ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: الإنشقاق
آية:
 

الإنشقاق

إِذَا ٱلسَّمَآءُ ٱنشَقَّتۡ
. Pamene thambo lidzang’ambike (kusonyeza mapeto ake),
التفاسير العربية:
وَأَذِنَتۡ لِرَبِّهَا وَحُقَّتۡ
“Ndikudzamvera lamulo la Mbuye wake; ndipo lidzayenera kutero,
التفاسير العربية:
وَإِذَا ٱلۡأَرۡضُ مُدَّتۡ
“Ndiponso pamene nthaka idzatambasulidwe (pogumuka mapiri ake ndikuchoka zitunda zake),
التفاسير العربية:
وَأَلۡقَتۡ مَا فِيهَا وَتَخَلَّتۡ
“Ndi kutaya zomwe zidali mkati mwake ndi kukhala yopanda kanthu,
Tanthauzo la “kuwazunza” apa ndiko kuwavutitsa ndi kuwathetsa mphamvu kuti asiye chikhulupiliro chawo; asakhulupirire mwa Allah. Mawuwa ngakhale akukhudzana ndi eni ngalande za moto, akukhudzanso akafiri a m’Makka omwe adali kuzunza Asilamu ndi mazunzo osiyanasiyana kuti abwelere kuchipembedzo cha mafano. Ndipo zimenezi zikhudzanso aliyense.
التفاسير العربية:
وَأَذِنَتۡ لِرَبِّهَا وَحُقَّتۡ
“Ndikudzamvera lamulo la Mbuye wake; ndipo lidzayenera kutero. (Choncho zikadzachitika zimenezi ndiye kuti munthu adzalandira mphoto ya zochita zake).
(Ndime 12-16) Allah pambuyo powatonthoza Asilamu pakuwauza zomwe zidawaonekera abale awo amene adatsogola, tsopanonso akuwatonthoza ndi ufumu Wake wolemekezeka kuti adziwe kuti awo akafiri omwe akudziona kuti ali ndi mphamvu zolangira anzawo, Iye sangamuthe. Akafuna adzawalanga ndi chilango cha dziko lapansi ndi cha tsiku lachimaliziro, kapena chimodzi mwa zilangozi; pakuti Iye Ngokhululuka kwambiri ndiponso Ngwachikondi zedi, awatembenula mitima yawo kuti achikhulupirire chimene adachikana. Chifukwa cha mphamvu Zake zoposa, Allah, adachita zonsezi ziwiri. Patapita zaka zochepa adawapatsa mphamvu omwe adali opanda mphamvu, kenaka adayamba kuwalanga osakhulupilira aja chilango cha padziko, monga Abu Jahl ndi anzake omwe adali kumutsutsa kwambiri Mtumiki (s.a.w) pamodzi ndi omutsatira ake. Ndipo ena adawatembenula mitima yawo nkulowa mchipembedzo cha Chisilamu; adaima ndikuchiteteza Chisilamu popereka nsembe ya mizimu yawo ndi chuma chawo.
التفاسير العربية:
يَـٰٓأَيُّهَا ٱلۡإِنسَٰنُ إِنَّكَ كَادِحٌ إِلَىٰ رَبِّكَ كَدۡحٗا فَمُلَٰقِيهِ
“E iwe munthu! Ndithudi iwe ukubwerera kwa Mbuye wako (ndi zochita zako zabwino kapena zoipa), kubwerera kotsimikizika, ndipo iwe ukumana (ndi zotsatira za zochitachita zako).
التفاسير العربية:
فَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِيَمِينِهِۦ
“Tsono amene adzapatsidwe kaundula wa zochita zake kudzanja la manja,
(Ndime15-16) Tanthauzo lake ndikuti akafiri (osakhulupilira) akuchita ndale kuti azimitse dangalira la Qur’an ndikuyesetsa kuti awabweze amene adakhulupilira ndiponso ndikufuna kumupha Mneneri (s.a.w). Naye Allah akuwachitira ndale powaonongera ziwembu zawo zomwe amazikonza.
التفاسير العربية:
فَسَوۡفَ يُحَاسَبُ حِسَابٗا يَسِيرٗا
“Basi iye, adzawerengedwa, kuwerengedwa kopepuka,
Tanthauzo lakulemekeza dzina la Allah ndiko kukhulupilira kuti iye ndiwopatulika ku mbiri zilizonse zoipa zosamuyenera, monga kumufanizira ndizolengedwa; monga kuti anabereka kapena adaberekedwa, kapena kuti ali ndi mkazi kapenanso kuti alipo omwe amathandizana naye pa Umulungu Wake.
التفاسير العربية:
وَيَنقَلِبُ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ مَسۡرُورٗا
“Ndipo adzabwerera kwa anthu ake (okhulupirira) ali wokondwa.
التفاسير العربية:
وَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ وَرَآءَ ظَهۡرِهِۦ
“Koma yemwe adzapatsidwe kaundula wa zochita zake chakumanzere kudzera kumbuyo kwa msana wake (chifukwa chomunyoza),
التفاسير العربية:
فَسَوۡفَ يَدۡعُواْ ثُبُورٗا
“Basi, iye adzaitana imfa (kuti imufikire; kuti afe apumule, koma siidzamufikira);
التفاسير العربية:
وَيَصۡلَىٰ سَعِيرًا
“Ndipo adzalowa ku Moto woyaka.
التفاسير العربية:
إِنَّهُۥ كَانَ فِيٓ أَهۡلِهِۦ مَسۡرُورًا
“Kamba kakuti iye adali wokondwa; (kukondwa kwa machimo) pamodzi ndi anthu ake (osaganizira za mathero ake).
التفاسير العربية:
إِنَّهُۥ ظَنَّ أَن لَّن يَحُورَ
“Ndithudi, amaganiza kuti sadzabwerera (kwa Allah ndiponso sadzawerengedwa).
التفاسير العربية:
بَلَىٰٓۚ إِنَّ رَبَّهُۥ كَانَ بِهِۦ بَصِيرٗا
“Chifukwa ninji (asabwelere)? Ndithu Mbuye wake adali kumuona. (Choncho alipidwa zimene adachita).
التفاسير العربية:
فَلَآ أُقۡسِمُ بِٱلشَّفَقِ
“Choncho ndikulumbilira kufiira kwa dzuwa (pamene likulowa).
التفاسير العربية:
وَٱلَّيۡلِ وَمَا وَسَقَ
“Ndi usiku ndi zimene wasonkhanitsa,
Allah pambuyo polenga zolengedwa Zake sadangozileka kuti zisadziwe chochita, koma cholengedwa chilichonse adachilamuliratu kuti chichite zoyenera nacho, ndipo pambuyo pake adachiongolera pa chinthu chimenecho; chidadziwa, ndipo chidachita. Munthu adamusonyeza zomwe zili ndi mazunzo mkati mwake kuti adzitalikitse nazo ndiponso adamusonyeza zabwino kuti azichite.
التفاسير العربية:
وَٱلۡقَمَرِ إِذَا ٱتَّسَقَ
“Ndi mwezi ukakwanira dangalira (lake),
التفاسير العربية:
لَتَرۡكَبُنَّ طَبَقًا عَن طَبَقٖ
“Ndithudi mudzachoka apa kunka apa (pa moyo uno mpakana umene uli nkudza).
التفاسير العربية:
فَمَا لَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
“Kodi nchiyani chikuwaletsa iwo (okanira) kukhulupirira (Allah ndi kuuka kumanda, zisonyezo zake zitaonekera poyera)?
التفاسير العربية:
وَإِذَا قُرِئَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡقُرۡءَانُ لَا يَسۡجُدُونَۤ۩
“Ndipo ikawerengedwa kwa iwo Qur’an, sagwetsa pansi nkhope zawo (modzichepetsa).
التفاسير العربية:
بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يُكَذِّبُونَ
“Koma amene sadakhulupirire akutsutsa basi (chifukwa cha makani ndi kudzikweza).
التفاسير العربية:
وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا يُوعُونَ
“Ndipo Allah akudziwa (bwinobwino) zimene akuzisonkhanitsa.
التفاسير العربية:
فَبَشِّرۡهُم بِعَذَابٍ أَلِيمٍ
“Choncho, auze nkhani yachilango chopweteka.
التفاسير العربية:

إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّـٰلِحَٰتِ لَهُمۡ أَجۡرٌ غَيۡرُ مَمۡنُونِۭ
“Kupatula awo amene akhulupirira ndikuchita ntchito zabwino, kwa iwo kuli malipiro osatha.
Mneneri Muhammad (s.a.w) adali munthu monga anthu ena ndipo adali ndi mbiri zonga anthu adalinazo, monga: kukonda ndi kusakonda, kuiwala ndi kukumbukira. Padapezeka kuti nthawi ina adaiwala ndi kupemphera maraka atatu m’Swala ya maraka anayi. Pachifukwa ichi pa nthawi yovumbulutsidwa Qur’an ndi Jibril, adali akubwereza bwereza mawu ovumbulutsidwawo kuopa kuti angaiwale. Choncho, apa Allah akumuletsa kuti asadzivutitse kumabwerezabwereza mawuwo pamene akuvumbulutsidwa ndipo adamupatsa lonjezo nthawi yomweyo kuti sadzaiwala. Ndipo adakwaniritsa lonjezo Lake. Mtumiki (s.a.w) adali kumtsikira ma surah aataliatali ndipo amatha kuwawerenga (molakatula) popanda kuonjezera kanthu kapena kuchepetsa, ngakhale kuti iye sadali kudziwa kuwerenga ndi kulemba. Kuwerenga kwake kudali kwakungolakatula pa mtima.
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: الإنشقاق
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق