Check out the new design

ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا * - لیست ترجمه ها


ترجمهٔ معانی سوره: انعام   آیه:

Al-An’âm

ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَجَعَلَ ٱلظُّلُمَٰتِ وَٱلنُّورَۖ ثُمَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِرَبِّهِمۡ يَعۡدِلُونَ
Kuyamikidwa konse kwabwino nkwa Allah, Yemwe adalenga thambo ndi nthaka, napanga mdima ndi kuunika pamwamba pa izi, kenako amene sadakhulupirire akumfanizira Mbuye wawo ndi milungu yabodza.
تفسیرهای عربی:
هُوَ ٱلَّذِي خَلَقَكُم مِّن طِينٖ ثُمَّ قَضَىٰٓ أَجَلٗاۖ وَأَجَلٞ مُّسَمًّى عِندَهُۥۖ ثُمَّ أَنتُمۡ تَمۡتَرُونَ
Iye ndi Yemwe adakulengani ndi dongo, kenako adaika nthawi (yothera cholengedwa chilichonse), ndi nthawi ina yodziwika kwa Iye (yomwe njoukitsira zolengedwa ku imfa). Ndipo pa izi inu (osakhulupirira) mukukaikira.
تفسیرهای عربی:
وَهُوَ ٱللَّهُ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَفِي ٱلۡأَرۡضِ يَعۡلَمُ سِرَّكُمۡ وَجَهۡرَكُمۡ وَيَعۡلَمُ مَا تَكۡسِبُونَ
Ndipo Iye ndi Allah (Wopembedzedwa) kumwamba ndi pansi. Akudziwa za mkati mwanu ndi zakunja kwanu, ndipo akudziwa zimene mukupeza (kuchokera mzochitachita zanu, zabwino kapena zoipa).
تفسیرهای عربی:
وَمَا تَأۡتِيهِم مِّنۡ ءَايَةٖ مِّنۡ ءَايَٰتِ رَبِّهِمۡ إِلَّا كَانُواْ عَنۡهَا مُعۡرِضِينَ
Ndipo palibe pamene chikuwadzera chisonyezo chilichonse mwa zisonyezo za Mbuye wawo koma akuzitembenukira kumbali.
تفسیرهای عربی:
فَقَدۡ كَذَّبُواْ بِٱلۡحَقِّ لَمَّا جَآءَهُمۡ فَسَوۡفَ يَأۡتِيهِمۡ أَنۢبَٰٓؤُاْ مَا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Ndithudi, atsutsa choonadi (Qur’an) pamene chawadzera. Posachedwapa ziwafika nkhani (za zilango) zimene adali kuzichitira chipongwe.
تفسیرهای عربی:
أَلَمۡ يَرَوۡاْ كَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِن قَبۡلِهِم مِّن قَرۡنٖ مَّكَّنَّٰهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ مَا لَمۡ نُمَكِّن لَّكُمۡ وَأَرۡسَلۡنَا ٱلسَّمَآءَ عَلَيۡهِم مِّدۡرَارٗا وَجَعَلۡنَا ٱلۡأَنۡهَٰرَ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهِمۡ فَأَهۡلَكۡنَٰهُم بِذُنُوبِهِمۡ وَأَنشَأۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِمۡ قَرۡنًا ءَاخَرِينَ
Kodi saona kuti ndi mibadwo ingati tidaiononga patsogolo pawo? Tidawapatsa mphamvu yopezera za m’dziko zomwe sitidakupatseni inu. Ndipo tidawavumbwitsira mvula yopitiriza (mwa ubwino choncho, adasangalala kopambana). Ndipo tidaipanga mitsinje kuyenda pansi pawo (pansi pa mitengo yawo ndi nyumba zawo). Kenako tidawaononga chifukwa cha machimo awo, ndipo pambuyo pawo tidalenga mibadwo ina.
تفسیرهای عربی:
وَلَوۡ نَزَّلۡنَا عَلَيۡكَ كِتَٰبٗا فِي قِرۡطَاسٖ فَلَمَسُوهُ بِأَيۡدِيهِمۡ لَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا سِحۡرٞ مُّبِينٞ
Ndipo ngati tikadakutsitsira malemba (olembedwa) m’mapepala, (monga momwe adakufunsira), nkuwakhudza ndi manja awo, amene sadakhulupirire akadati: “Ichi sichina koma ndi matsenga owoneka.”
تفسیرهای عربی:
وَقَالُواْ لَوۡلَآ أُنزِلَ عَلَيۡهِ مَلَكٞۖ وَلَوۡ أَنزَلۡنَا مَلَكٗا لَّقُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ ثُمَّ لَا يُنظَرُونَ
Ndipo amanena: “Bwanji iye osamtsitsira mngelo (kuti aziikira umboni kwa anthu za uneneri wake)?” Tikadakutsitsira mngelo (nkusakhulupirira), ndithu chiweruzo cha kuonongeka kwawo chikadakwaniritsidwa. Ndipo sakadapatsidwanso mpata.
تفسیرهای عربی:
 
ترجمهٔ معانی سوره: انعام
فهرست سوره ها شماره صفحه
 
ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا - لیست ترجمه ها

مترجم: خالد ابراهیم بیتالا.

بستن