Check out the new design

ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا * - لیست ترجمه ها


ترجمهٔ معانی سوره: انعام   آیه:
فَقُطِعَ دَابِرُ ٱلۡقَوۡمِ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْۚ وَٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Choncho mizu ya anthu oipa idadulidwa. Ndipo kuyamikidwa konse kwabwino nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa.
تفسیرهای عربی:
قُلۡ أَرَءَيۡتُمۡ إِنۡ أَخَذَ ٱللَّهُ سَمۡعَكُمۡ وَأَبۡصَٰرَكُمۡ وَخَتَمَ عَلَىٰ قُلُوبِكُم مَّنۡ إِلَٰهٌ غَيۡرُ ٱللَّهِ يَأۡتِيكُم بِهِۗ ٱنظُرۡ كَيۡفَ نُصَرِّفُ ٱلۡأٓيَٰتِ ثُمَّ هُمۡ يَصۡدِفُونَ
Nena: “Tandiuzani, ngati Allah atakuchotserani kumva kwanu ndi kupenya kwanu, nadinda chidindo m’mitima yanu (kuti asalowemo mawu amalangizo a mtundu uliwonse), kodi ndi mulungu uti, kupatula Allah, amene angakubwezereninso (zimenezi)?” Taona momwe tikufotokozera mwatsatanetsatane zizindikiro kenako iwo akunyozera.
تفسیرهای عربی:
قُلۡ أَرَءَيۡتَكُمۡ إِنۡ أَتَىٰكُمۡ عَذَابُ ٱللَّهِ بَغۡتَةً أَوۡ جَهۡرَةً هَلۡ يُهۡلَكُ إِلَّا ٱلۡقَوۡمُ ٱلظَّٰلِمُونَ
Nena: “Tandiuzani, ngati masautso a Allah atakufikani mwadzidzidzi kapena moonekera, kodi angaonongeke ndi ena osati anthu ochita zoipa?”
تفسیرهای عربی:
وَمَا نُرۡسِلُ ٱلۡمُرۡسَلِينَ إِلَّا مُبَشِّرِينَ وَمُنذِرِينَۖ فَمَنۡ ءَامَنَ وَأَصۡلَحَ فَلَا خَوۡفٌ عَلَيۡهِمۡ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ
Ndipo sititumiza atumiki koma kuti akhale ouza nkhani zabwino ndi ochenjeza. Choncho amene akhulupirira nakonza zinthu, pa iwo sipadzakhala mantha ndiponso sadzadandaula.
تفسیرهای عربی:
وَٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يَمَسُّهُمُ ٱلۡعَذَابُ بِمَا كَانُواْ يَفۡسُقُونَ
Ndipo amene atsutsa zizindikiro zathu, chilango chidzawakhudza chifukwa chakupandukira kwawo chilamulo.
تفسیرهای عربی:
قُل لَّآ أَقُولُ لَكُمۡ عِندِي خَزَآئِنُ ٱللَّهِ وَلَآ أَعۡلَمُ ٱلۡغَيۡبَ وَلَآ أَقُولُ لَكُمۡ إِنِّي مَلَكٌۖ إِنۡ أَتَّبِعُ إِلَّا مَا يُوحَىٰٓ إِلَيَّۚ قُلۡ هَلۡ يَسۡتَوِي ٱلۡأَعۡمَىٰ وَٱلۡبَصِيرُۚ أَفَلَا تَتَفَكَّرُونَ
Nena: “Ine sindikukuuzani kuti ndili nazo nkhokwe za Allah kapena kuti ndikudziwa zamseri, ndiponso sindikukuuzani kuti ine ndine mngelo. Ine sinditsata china koma zomwe zikuvumbulutsidwa kwa ine.” Nena: “Kodi wakhungu ndi wopenya angafanane? Bwanji simukuganizira?”
تفسیرهای عربی:
وَأَنذِرۡ بِهِ ٱلَّذِينَ يَخَافُونَ أَن يُحۡشَرُوٓاْ إِلَىٰ رَبِّهِمۡ لَيۡسَ لَهُم مِّن دُونِهِۦ وَلِيّٞ وَلَا شَفِيعٞ لَّعَلَّهُمۡ يَتَّقُونَ
Achenjeze ndi Qur’an iyi omwe akuopa kuti adzasonkhanitsidwa kwa Mbuye wawo pomwe ali opanda mtetezi ngakhale muomboli aliyense kupatula Iye, kuti iwo aope (Allah).
تفسیرهای عربی:
وَلَا تَطۡرُدِ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ رَبَّهُم بِٱلۡغَدَوٰةِ وَٱلۡعَشِيِّ يُرِيدُونَ وَجۡهَهُۥۖ مَا عَلَيۡكَ مِنۡ حِسَابِهِم مِّن شَيۡءٖ وَمَا مِنۡ حِسَابِكَ عَلَيۡهِم مِّن شَيۡءٖ فَتَطۡرُدَهُمۡ فَتَكُونَ مِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ
Ndipo usawathamangitse omwe akupembedza Mbuye wawo m’mawa ndi madzulo pofuna chiyanjo Chake. Chiwerengero chawo sichili pa iwe ngakhale pang’ono, ndipo chiwerengero chako sichili pa iwo ngakhale pang’ono kotero kuti nkwathamangitsa. (Ngati uwapirikitsa) ukhala m’gulu la anthu ochita zoipa.
تفسیرهای عربی:
 
ترجمهٔ معانی سوره: انعام
فهرست سوره ها شماره صفحه
 
ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا - لیست ترجمه ها

مترجم: خالد ابراهیم بیتالا.

بستن