Check out the new design

ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا * - لیست ترجمه ها


ترجمهٔ معانی سوره: انعام   آیه:
۞ إِنَّمَا يَسۡتَجِيبُ ٱلَّذِينَ يَسۡمَعُونَۘ وَٱلۡمَوۡتَىٰ يَبۡعَثُهُمُ ٱللَّهُ ثُمَّ إِلَيۡهِ يُرۡجَعُونَ
Ndithudi amene akuvomereza, ngomwe akumva (ndipo anthu awa amene safuna kumvera chilichonse ndi akufa ngakhale ali moyo). Ndipo akufa Allah adzawaukitsa (m’manda mwawo) kenako adzabwezedwa kwa Iye.
تفسیرهای عربی:
وَقَالُواْ لَوۡلَا نُزِّلَ عَلَيۡهِ ءَايَةٞ مِّن رَّبِّهِۦۚ قُلۡ إِنَّ ٱللَّهَ قَادِرٌ عَلَىٰٓ أَن يُنَزِّلَ ءَايَةٗ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
Ndipo akumanena: “Bwanji sichinatsitsidwe chozizwitsa kwa iye kuchokera kwa Mbuye wake?” Nena: “Ndithudi, Allah Ngokhoza kutsitsa chozizwitsa koma ambiri a iwo sadziwa (zomwe Allah afuna).”
تفسیرهای عربی:
وَمَا مِن دَآبَّةٖ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا طَٰٓئِرٖ يَطِيرُ بِجَنَاحَيۡهِ إِلَّآ أُمَمٌ أَمۡثَالُكُمۚ مَّا فَرَّطۡنَا فِي ٱلۡكِتَٰبِ مِن شَيۡءٖۚ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّهِمۡ يُحۡشَرُونَ
Ndipo palibe nyama ili yonse pa nthaka, ngakhale mbalame yowuluka ndi mapiko ake awiri koma ndi magulu a zolengedwa ngati inu (zomwe Allah adazilenga). Sitinasiye chinthu chilichonse kapena kuchinyozera chilichonse m’buku (chomwe nchofunika koma tachifotokoza). Ndipo tero kwa Mbuye wawo adzasonkhanitsidwa.
تفسیرهای عربی:
وَٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا صُمّٞ وَبُكۡمٞ فِي ٱلظُّلُمَٰتِۗ مَن يَشَإِ ٱللَّهُ يُضۡلِلۡهُ وَمَن يَشَأۡ يَجۡعَلۡهُ عَلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
Ndipo amene atsutsa zizindikiro Zathu, ndiagonthi ndiponso abubu, ali mu m’dima (wa umbuli). Amene Allah wamfuna amamlekelera kusokera. Ndipo amene wamfuna amamuika pa njira yolunjika (yomwe ndi njira ya Chisilamu).
تفسیرهای عربی:
قُلۡ أَرَءَيۡتَكُمۡ إِنۡ أَتَىٰكُمۡ عَذَابُ ٱللَّهِ أَوۡ أَتَتۡكُمُ ٱلسَّاعَةُ أَغَيۡرَ ٱللَّهِ تَدۡعُونَ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Nena: “Tandiuzani ngati mazunzo a Allah atakufikani (pompano pa dziko lapansi), kapena kukufikani nthawi (ya chilango cha tsiku lachimaliziro) kodi mudzaitana yemwe sali Allah (kuti akupulumutseni) ngati inu muli owona.”
تفسیرهای عربی:
بَلۡ إِيَّاهُ تَدۡعُونَ فَيَكۡشِفُ مَا تَدۡعُونَ إِلَيۡهِ إِن شَآءَ وَتَنسَوۡنَ مَا تُشۡرِكُونَ
“Koma Iye yekha ndi Yemwe mudzampempha, ndipo Iye adzakuchotserani zomwe mukumpempha (kuti akuchotsereni) ngati atafuna. Ndipo mudzaiwala zomwe mudali kuziphatikiza (ndi Allah).”
تفسیرهای عربی:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَآ إِلَىٰٓ أُمَمٖ مِّن قَبۡلِكَ فَأَخَذۡنَٰهُم بِٱلۡبَأۡسَآءِ وَٱلضَّرَّآءِ لَعَلَّهُمۡ يَتَضَرَّعُونَ
Ndithu tidawatumiza (atumiki) ku mibadwo yomwe idalipo iwe usadadze. Ndipo tidaikhaulitsa (mibadwoyo) ndi mazunzo ndi masautso kuti iyo idzichepetse (pambuyo podzikuza).
تفسیرهای عربی:
فَلَوۡلَآ إِذۡ جَآءَهُم بَأۡسُنَا تَضَرَّعُواْ وَلَٰكِن قَسَتۡ قُلُوبُهُمۡ وَزَيَّنَ لَهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Pamene masautso adawafika kuchokera kwa Ife, bwanji sadaphunzire kudzichepetsa? Koma mitima yawo idali youma, ndipo satana adawakometsera machimo omwe iwo adali kuchita.
تفسیرهای عربی:
فَلَمَّا نَسُواْ مَا ذُكِّرُواْ بِهِۦ فَتَحۡنَا عَلَيۡهِمۡ أَبۡوَٰبَ كُلِّ شَيۡءٍ حَتَّىٰٓ إِذَا فَرِحُواْ بِمَآ أُوتُوٓاْ أَخَذۡنَٰهُم بَغۡتَةٗ فَإِذَا هُم مُّبۡلِسُونَ
Ndipo pamene adanyozera zimene ankakumbutsidwa tidawatsekulira makomo a chinthu chilichonse (chimene adali kuchifuna) kufikira pamene adasangalala ndi zomwe adapatsidwa, tidawagwira mwadzidzidzi; pompo adataya mtima.
تفسیرهای عربی:
 
ترجمهٔ معانی سوره: انعام
فهرست سوره ها شماره صفحه
 
ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا - لیست ترجمه ها

مترجم: خالد ابراهیم بیتالا.

بستن