Alif-Lam-Ra. Ili ndi buku lomwe ndime zake zakonzedwa bwino ndipo zafotokozedwa mwatsatanetsatane kuchokera kwa Allah Mwini nzeru zakuya Wodziwa chilichonse.
(Wachita zimenezi) kuti musampembedze wina wake koma Allah yekha. Ndithudi ine kwa inu ndimchenjezi wochokera kwa Iye ndiponso wokuuzani nkhani zabwino.
۞ Ndipo palibe nyama iliyonse panthaka koma rizq lake lili kwa Allah; ndipo (Iye) akudziwa mbuto yake yamuyaya ndi mbuto yake yakungodutsapo (yomwe ndi pano padziko lapansi). Zonse zili m’buku lofotokoza chilichonse.[219]
[219] Mawu oti “Riziki lake lili kwa Allah’’ nkuti Allah wapatsa chilichonse mphamvu zofunira riziki lake (zoyendetsa moyo wake). Ndimeyi siitanthauza kuti munthu angokhala popanda kugwira ntchito nayembekezera kuti riziki lichokera kumwamba. Koma munthu agwire ntchito molimbikira kuti apeze chuma cha Allah. Zotere nzimene Qur’an ikutilangiza.
Ndipo Iye ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo Arsh Yake (Mpando Wake wachifumu) idali pa madzi. (Adakulengani) kuti akuyeseni mayeso, ndani mwa inu ali wochita zabwino. Koma ukanena (kwa iwo kuti): “Inu mudzaukitsidwa pambuyo pa imfa,” amene sadakhulupirire akuti: “Izi sikanthu koma ndi matsenga oonekera.”[220]
[220] Kunena kwakuti thambo ndi nthaka zidalengedwa m’masiku asanu ndi limodzi, amene akudziwa za masiku asanu ndi limodziwo momwe adalili ndi Allah yekha. Ndiponso mpandowo sitikudziwa tsatanetsatane wake. Chimene chilipo kwa ife nkukhulupilira basi.
Mwina usiya zina mwa zomwe zikuvumbulutsidwa kwa iwe ndikubanika nazo mchifuwa mwako chifukwa chakuti akunena: “Bwanji sizidatsitsidwe kwa iye nkhokwe za chuma kapena bwanji mngelo osadza pamodzi ndi iye?” Koma ndithu iwe ndiwe mchenjezi basi ndipo Allah ndiye muyang’aniri wa chinthu chilichonse.[221]
[221] Ophatikiza Allah ndi zina zake adali kupereka maganizo kwa Mtumiki akuti ampemphe Allah kuti adzetse milumilu ya chuma kapena amutumizire angelo kuti aziyenda naye limodzi. Ndipo adalinso kumaichitira Qur’an chibwana Mtumiki akawawerengera. Potero Mtumiki (s.a.w) adali kubanika mu mtima mwake akafuna kufikitsa uthenga kwa iwo chifukwa chakuopa kutsutsidwa ndi kumchitira chibwana.
Nanga kodi munthu yemwe ali ndi chisonyezo choonekera chochokera kwa Mbuye wake (kotero kuti m’moyo mwake akuyenda molungama; yemwe ndi mneneri Muhammad {s.a.w}), ndipo Mboni ili naye pamodzi ikumtsata yochokera kwa Iye (Mbuye wake yomwe ndi Qur’an kapena Gaburiel), ndipo patsogolo pake padali buku la Mûsa lomwe lidali chitsanzo chabwino ndi mtendere, (wotereyu angafanane ndi yemwe ali mum’dima wa umbuli yemwenso sadziwa cholinga chakulengedwa kwake?) Awa (amene aongoka) akulikhulupirira (buku ili la Qur’an), ndipo amene ati asalikhulupirire m’magulu (a adani), Moto ndiwo malo awo alonjezo. Choncho, usakhale ndi chipeneko pa ichi; ndithudi ichi ndi choona chochokera kwa Mbuye Wako koma anthu ambiri sakhulupirira.
Ndipo palibe oipitsitsa kuposa yemwe wapeka bodza pakumnamizira Allah (kuti ali ndi mwana ndi athandizi). Iwo adzabweretsedwa kwa Mbuye wawo (tsiku la Qiyâma) ndipo mboni (zomwe ndi angelo) zidzanena: “Awa ndi omwe adapekera Mbuye wawo bodza. Mverani! Tembelero la Allah lili pa ochita zoipa.”
Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndi kumadzichepetsa kwa Mbuye wawo, iwowo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere. M’menemo adzakhala nthawi yaitali.
Ndipo pompo akuluakulu mwa omwe sadakhulupirire mwa anthu ake, adati: “Sitikukuona koma ndiwe munthu monga ife, ndipo sitikukuona koma kuti akutsata anthu a pansi pathu ofooka pa nzeru (omwe sadalingalire mozama za iwe). Ndipo sitikukuonani kuti muli ndi ulemelero ndi ubwino wochuluka kuposa ife. Koma tikukuganizirani kuti ndinu onama.”
“Ndipo E inu anthu anga! Ine sindikukupemphani chuma pa uthengawu. Palibe malipiro anga, koma ali kwa Allah basi. Ndipo ine sindingathamangitse amene akhulupirira (monga momwe mudandipemphera kuti ndiwathamangitse anthu ofooka kuti inu mulowe m’malo mwawo), ndithu iwo adzakumana ndi Mbuye wawo, ndipo ine ndikukuonani monga anthu osazindikira (mbuli).”
“Ndipo ine sindikukuuzani kuti ndili ndi nkhokwe za chuma cha Allah kapena kuti ine ndikudziwa zinthu zamseli, ndiponso sindikunena kuti ndine m’ngelo. Ndiponso sindikunena kwa omwe maso anu akuwachepetsa kuti Allah sadzawapatsa chabwino. Allah akudziwa zam’mitima mwawo. (Ngati nditatero) ndiye kuti ine pamenepo ndili m’gulu la oipa.”
“Ndipo kulangiza kwanga sikungakuthandizeni ngati ntafuna kukulangizani, ngati Allah akufuna kukulekelerani kusokera. Iye ndiye Mbuye wanu. Ndipo kwa Iye mudzabwezedwa.”
Kapena akunena (osakhulupirira a m’Makka kuti: “Muhammad) waipeka (Qur’an mwa iye yekha)?” Nena: “ngati ndayipeka ndiye kuti machimo ake (akupekawo) ali pa ine. Ndipo ine ndili kutali ndi zoipa zimene mukuchita.”
(Allah) adati: “E iwe Nuh! Ndithu iyeyo si (mwana) wa m’banja lako. Iye zochita zake sizili zabwino. Choncho usandipemphe zomwe siukuzidziwa, Ine ndikukulangiza kuti usakhale m’gulu la osazindikira (mbuli).”
Kudanenedwa: “E iwe Nuh! Tsika (pa nthaka youma) mwamtendere wochokera kwa Ife, ndipo madalitso ambiri akhale pa iwe ndi pa anthu omwe ali nawe; ndipo kudzakhala mibadwo ina (yoipa pambuyo pako) yomwe tidzaisangalatsa, ndipo kenako chidzaikhudza chilango chowawa chochokera kwa Ife.”
“Sitinena kanthu, koma kuti (mwina) milungu yathu ina yakulodza misala.” (Iye) adati: “Ndithu ine ndikupereka umboni kwa Allah ndipo inunso perekani umboni kuti ine ndili kutali ndi zimene mukumphatikiza nazo (Allah pomazipembedza).”
“Ndithu ine ndatsamira kwa Allah, Mbuye wanga yemwenso ali Mbuye wanu. Palibe chinyama chilichonse koma Allah wachigwira tsumba lake (ndikuchiyendetsa mmene akufunira). Ndithudi, Mbuye wanga Ngwachilungamo.”
[223] Chilangocho chidali chimphepo choononga chomwe chinagumula nyumba ndi kulowa m’mphuno za adani a Allah ndi kutulukira kokhalira kwawo. Chinkangowagwetsa chafufumimba kotero kuti anthu adali lambilambi ngati mathunthu a mitengo ya kanjedza.
Ndipo adatsatizidwa ndi tembelero pa moyo wapano padziko lapansi ndi tsiku la Qiyâma (tsiku la chiweruziro). Dziwani! Ndithu Âdi adakana Mbuye wawo. Ha! Adaonongeka Âdi, anthu a Hûd!.
(Iye) adati: “E inu anthu anga! Mukuona bwanji ngati ndili ndi chisonyezo choonekera chochokera kwa Mbuye wanga (chosonyeza kuona kwa zimenezi), nandipatsanso chifundo chochokera kwa Iye. Nanga ndi yani angandipulumutse ku chilango cha Allah ngati nditamunyoza? Choncho, simungandionjezere china chake koma kutaika basi.”
“Ndipo E inu anthu anga! Iyi ngamira ya Allah ndi chisonyezo kwa inu. Ilekeni izidya panthaka ya Allah, ndipo musaikhudze ndi choipa kuopa kuti chilango chomwe chili pafupi chingakuonongeni.”[224]
[224] Asamudu adampempha chozizwitsa Mneneri wawo Swalih chotsimikiza kuti iye adalidi Mneneri wa Allah. Chozizwitsa chomwe adampempha nkuti atulutse ngamira patanthwe. Choncho mwa mphamvu za Allah ngamira idatuluka m’tanthwemo. Ndipo adawauza kuti asaichitire choipa. Aisiye izingodzidyera m’dziko la Allah. Koma iwo adaipha, ndipo chilango cha Allah chidawatsikira.
(Angelowo) adati: “Ukudabwa ndi lamulo la Allah? Chisomo cha Allah ndi madalitso ake zili pa inu, E inu eni nyumba iyi! Iye Ngoyamikidwa, Mwini ulemelero!”
Ndipo atumiki athu pamene adafika kwa Luti, iye anadandaula za iwo ndi kubanika nao mu mtima (chifukwa chosowa njira yowatetezera kwa anthu oipa pomwe iye sadadziwe kuti alendowo ndi angelo), nati: “Lino ndi tsiku lovuta.”
(Athengawa) adati: “E iwe Luti! Ife ndi athenga a Mbuye wako. Safika kwa iwe (ndi chilichonse choipa). Ndipo choka pamodzi ndi banja lako m’gawo la usiku, ndipo aliyense wa inu asatembenuke (kuyang’ana m’mbuyo akamva mkokomo wa kudza kwa chilangocho), kupatula mkazi wako; iye chimpeza chimene chiwapeze anthu enawo. Ndithu lonjezo lawo ndi m’mawa. Kodi m’mawa suudayandikire?”
Ndipo sitidawachitire choipa (powaononga). Koma adadzichitira okha zoipa (pakusakhulupirira Allah ndi kupembedza mafano ndikuipitsa pa dziko), milungu yawo yomwe ankaipembedza kusiya Allah siidawathandize chilichonse pamene lidadza lamulo la Mbuye wako (la kuwaononga). Ndipo (milunguyo) siidawaonjezere (china chake) koma chionongeko basi.
Ndipo ndithu tidampatsa buku Mûsa, koma kusiyana kudabuka mmenemo (pakatanthauzidwe ka bukulo pambuyo pa Mûsa). Pakadapanda mawu a Mbuye wako omwe adatsogola (oti sadzawalanga nthawi isanafike), ndithu kukadaweruzidwa pakati pawo. Ndipo ndithu iwo ali m’kukaika ndi kupeneka (kwakukulu) pa zimenezo.
Choncho (E iwe Mtumiki!) Pitiriza kulungama monga momwe akulamulira (iwe) pamodzi ndi omwe atembenukira (kwa Allah), ndipo musapyole malire. Ndithu Iye akuona zonse zimene muchita.[226]
[226] Apa akutanthauza kuti ngati chikhalidwe cha mibadwo yakale chidali chonchi, mibadwo yomwe adaitumizira buku lake, natsutsana ndi bukuli, ena a iwo nalitaya kutali, iweyo pitiriza ndi Asilamu omwe uli nawo kugwira njira yolungama monga momwe Allah wakulamulira. Usapyole malire ponyozera chimene chili choyenera iwe kuchichita, kapena kudzikakamiza chimene sungathe kuchichita. Allah tu akudziwa zonse zomwe muchita ndipo adzakulipirani.
Ndipo pemphera Swala nsonga ziwiri za usana ndi nthawi za usiku zomwe zili pafupi ndi usana. Ndithu zabwino zimachotsa zoipa. Ichi ndi chikumbutso kwa okumbukira.
Zonse zobisika za kumwamba ndi pansi nza Allah ndipo zidzabwezedwa kwa Iye. Choncho, mpembedzeni ndi kutsamira kwa Iye. Ndithu Mbuye wako siwonyalanyaza zimene mukuchita.
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
Njeñtudi wiɗto ngoo:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".