Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo - Firo siisiiwo * - Tippudi firooji ɗii


Firo maanaaji Aaya: (33) Simoore: Simoore Saba
وَقَالَ ٱلَّذِينَ ٱسۡتُضۡعِفُواْ لِلَّذِينَ ٱسۡتَكۡبَرُواْ بَلۡ مَكۡرُ ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ إِذۡ تَأۡمُرُونَنَآ أَن نَّكۡفُرَ بِٱللَّهِ وَنَجۡعَلَ لَهُۥٓ أَندَادٗاۚ وَأَسَرُّواْ ٱلنَّدَامَةَ لَمَّا رَأَوُاْ ٱلۡعَذَابَۚ وَجَعَلۡنَا ٱلۡأَغۡلَٰلَ فِيٓ أَعۡنَاقِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْۖ هَلۡ يُجۡزَوۡنَ إِلَّا مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Ndipo amene adaponderezedwa adzanena kwa amene adadzikweza: “Iyayi, koma (mumachita) ndale za usiku ndi usana (zotitsekereza nazo ku chikhulupiliro) pamene mumatilamula kuti tinkanire Allah ndikumpangira Iye milungu inzake.” Iwo adzabisa madandaulo pamene adzaona chilango. Ndipo tidzaika magoli m’makosi mwa amene sadakhulupirire; kodi angalipidwe china, osati zija ankachita?[337]
[337] M’ndime iyi, Allah akutifotokozera kuti pa tsiku la chimaliziro padzakhala kukangana pakati pa atsogeleri ndi anthu otsogoleredwa. Izi zidzachitika pamene otsogoleredwa adzatsimikiza kuti atsogoleri awo amawasokeza; ankangowalangiza zachabe. Potero adzakhala ndi madandaulo aakulu chifukwa chotsatira anthu osokera. Komatu madandaulo oterewa sadzawapindulira chilichonse popeza mwayi udzakhala utatha kale. Choncho nkofunika kuti potsata mtsogoleri aliyense tiyambe taganizira komwe akunka nafe; tisangokokedwa ngati nyama pakuti Allah adatipatsa dalitso lanzeru. Choncho tigwiritse ntchito bwino nzeru tsoka lisanatigwere.
Faccirooji aarabeeji:
 
Firo maanaaji Aaya: (33) Simoore: Simoore Saba
Tippudi cimooje Tonngoode hello ngoo
 
Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo - Firo siisiiwo - Tippudi firooji ɗii

Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo fayde e ɗemngal siisii, fari ɗum ko Kaaliid piitalaa. Tummbutere hitaande 2020

Uddude