Traduction des sens du Noble Coran - Traduction en chewa * - Lexique des traductions


Traduction des sens Verset: (72) Sourate: AL ‘IMRÂN
وَقَالَت طَّآئِفَةٞ مِّنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ ءَامِنُواْ بِٱلَّذِيٓ أُنزِلَ عَلَى ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَجۡهَ ٱلنَّهَارِ وَٱكۡفُرُوٓاْ ءَاخِرَهُۥ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ
Ndipo gulu lina la amene adapatsidwa buku lidati (kwa anzawo): “Khulupirirani chomwe chavumbulutsidwa kwa Asilamu kumayambiliro kwa usana, ndipo chikaneni kumalekezero kwake (kwa usana) mwina angabwelere (kusiya Chisilamu).[73]
[73] Ena mwa anthu a mabuku adalangizana pakati pawo kuti chikhulupirire chipembedzo cha Chisilamu nthawi zakummawa zokha. Ikakwana nthawi yopemphera Swala akapemphere nawo. Koma ikafika nthawi yamadzulo atuluke m’chipembedzocho ncholinga choti asokoneze Asilamu maganizo, makamaka omwe adali ofooka pomwe aone kuti anthu anzeru adalowa m’chipembedzocho, koma kenako atulukamo, nawonso mwina atuluka poganiza kuti chikadakhala chipembedzo chenicheni anthu anzeru sakadatulukamo. Izi zidali ndale za Ayuda zomwe Allah adaziulula.
Les exégèses en arabe:
 
Traduction des sens Verset: (72) Sourate: AL ‘IMRÂN
Lexique des sourates Numéro de la page
 
Traduction des sens du Noble Coran - Traduction en chewa - Lexique des traductions

Traduction des sens du noble Coran en langue chewa, par Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ (édition 2020).

Fermeture