Traduction des sens du Noble Coran - Traduction en chewa * - Lexique des traductions


Traduction des sens Sourate: AZ-ZOUKHROUF   Verset:

AZ-ZOUKHROUF

حمٓ
. Hâ-Mîm.
Les exégèses en arabe:
وَٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُبِينِ
Ndikulumbilira buku lofotokoza momveka.
Les exégèses en arabe:
إِنَّا جَعَلۡنَٰهُ قُرۡءَٰنًا عَرَبِيّٗا لَّعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ
Ndithu Ife talichita bukuli (Qur’an) kukhala chowerengedwa m’Chiarabu kuti muzindikire.
Les exégèses en arabe:
وَإِنَّهُۥ فِيٓ أُمِّ ٱلۡكِتَٰبِ لَدَيۡنَا لَعَلِيٌّ حَكِيمٌ
Ndipo ndithu bukuli (Qur’an) lili m’manthu wa mabuku onse (Lawhi Mahfudh) limene lili kwa Ife; (ndipo ndi buku) lotukuka, la mawu anzeru.
Les exégèses en arabe:
أَفَنَضۡرِبُ عَنكُمُ ٱلذِّكۡرَ صَفۡحًا أَن كُنتُمۡ قَوۡمٗا مُّسۡرِفِينَ
Kodi tisiye kukukumbutsani chifukwa chakuti ndinu anthu opyola malire (pochita zoipa)?
Les exégèses en arabe:
وَكَمۡ أَرۡسَلۡنَا مِن نَّبِيّٖ فِي ٱلۡأَوَّلِينَ
Ndipo tidatumiza aneneri ambiri kwa anthu akale.
Les exégèses en arabe:
وَمَا يَأۡتِيهِم مِّن نَّبِيٍّ إِلَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Ndipo palibe mneneri aliyense amene amawadzera koma amam’chitira chipongwe.
Les exégèses en arabe:
فَأَهۡلَكۡنَآ أَشَدَّ مِنۡهُم بَطۡشٗا وَمَضَىٰ مَثَلُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Choncho tidawaononga amene adali amphamvu kuposa iwo (Aquraish) ndipo ladutsa fanizo la (zilango zomwe zidawapeza) anthu akale.
Les exégèses en arabe:
وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ لَيَقُولُنَّ خَلَقَهُنَّ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡعَلِيمُ
Ndipo ukawafunsa: “Ndani adalenga thambo ndi nthaka?” Ndithu ayankha kuti: “Adazilenga (Allah) Mwini Mphamvu, Wodziwa.”
Les exégèses en arabe:
ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ مَهۡدٗا وَجَعَلَ لَكُمۡ فِيهَا سُبُلٗا لَّعَلَّكُمۡ تَهۡتَدُونَ
Amene wakupangirani nthaka kukhala choyala ndipo adakupangirani njira mmenemo kuti muongoke (ndikukafika kumene mukufuna).
Les exégèses en arabe:
وَٱلَّذِي نَزَّلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءَۢ بِقَدَرٖ فَأَنشَرۡنَا بِهِۦ بَلۡدَةٗ مَّيۡتٗاۚ كَذَٰلِكَ تُخۡرَجُونَ
Ndiponso amene watsitsa madzi kuchokera kumwamba mwamuyeso; chifukwa cha madziwo tidaukitsa mudzi wakufa. Momwemonso inu mudzatulutsidwa (mmanda);
Les exégèses en arabe:
وَٱلَّذِي خَلَقَ ٱلۡأَزۡوَٰجَ كُلَّهَا وَجَعَلَ لَكُم مِّنَ ٱلۡفُلۡكِ وَٱلۡأَنۡعَٰمِ مَا تَرۡكَبُونَ
Ndiponso amene walenga zinthu zonse ziwiriziwiri (chachimuna ndi chachikazi). Ndipo adakupangirani zombo ndi ziweto zimene mukukwera,
Les exégèses en arabe:
لِتَسۡتَوُۥاْ عَلَىٰ ظُهُورِهِۦ ثُمَّ تَذۡكُرُواْ نِعۡمَةَ رَبِّكُمۡ إِذَا ٱسۡتَوَيۡتُمۡ عَلَيۡهِ وَتَقُولُواْ سُبۡحَٰنَ ٱلَّذِي سَخَّرَ لَنَا هَٰذَا وَمَا كُنَّا لَهُۥ مُقۡرِنِينَ
Kuti mukhazikike mwaubwino pamisana paizo, kenako mukumbukire mtendere wa Mbuye wanu mukakhazikika pamenepo, ndipo munene: “Walemekezeka Amene watifewetsera ichi; ndipo sitikadatha kuchifewetsa ndi kuchigwiritsa ntchito.”
Les exégèses en arabe:
وَإِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا لَمُنقَلِبُونَ
“Ndipo ndithu ife kwa Mbuye wathu ndiko kobwerera.”
Les exégèses en arabe:
وَجَعَلُواْ لَهُۥ مِنۡ عِبَادِهِۦ جُزۡءًاۚ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لَكَفُورٞ مُّبِينٌ
Ndipo amuikira gawo mwa akapolo Ake. (Kuti ndi ana a Allah.) Ndithu munthu, ngwamsulizo woonekera poyera!
Les exégèses en arabe:
أَمِ ٱتَّخَذَ مِمَّا يَخۡلُقُ بَنَاتٖ وَأَصۡفَىٰكُم بِٱلۡبَنِينَ
Kodi wadzichitira ana achikazi mzimene wazilenga ndipo wakusankhirani inu ana achimuna?
Les exégèses en arabe:
وَإِذَا بُشِّرَ أَحَدُهُم بِمَا ضَرَبَ لِلرَّحۡمَٰنِ مَثَلٗا ظَلَّ وَجۡهُهُۥ مُسۡوَدّٗا وَهُوَ كَظِيمٌ
Koma akauzidwa (kuti wabereka mwana wamkazi) mmodzi wa iwo chomwe amamfanizira (Allah) Wachifundo chambiri, nkhope yake imakhala yakuda ndi kudandaula kwambiri!
Les exégèses en arabe:
أَوَمَن يُنَشَّؤُاْ فِي ٱلۡحِلۡيَةِ وَهُوَ فِي ٱلۡخِصَامِ غَيۡرُ مُبِينٖ
Ha! Kodi amene waleredwa monga chokongoletsa, potsutsana iye sangathe kunena momveka? (Ameneyo ndiye mwampatsa Allah; omwe ndi ana aakazi).
Les exégèses en arabe:
وَجَعَلُواْ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ ٱلَّذِينَ هُمۡ عِبَٰدُ ٱلرَّحۡمَٰنِ إِنَٰثًاۚ أَشَهِدُواْ خَلۡقَهُمۡۚ سَتُكۡتَبُ شَهَٰدَتُهُمۡ وَيُسۡـَٔلُونَ
Ndipo angelo omwe ndi akapolo a (Allah) Wachifundo chambiri akuwatcha akazi. Kodi adaona kalengedwe kawo? Umboni wawo ulembedwa ndipo adzafunsidwa (pazimenezo)!
Les exégèses en arabe:
وَقَالُواْ لَوۡ شَآءَ ٱلرَّحۡمَٰنُ مَا عَبَدۡنَٰهُمۗ مَّا لَهُم بِذَٰلِكَ مِنۡ عِلۡمٍۖ إِنۡ هُمۡ إِلَّا يَخۡرُصُونَ
Ndipo (otsutsa) akunena: “Akadafuna (Allah) Wachifundo chambiri (kuti tisamapembedze mafano awa), sitikadawapembedza!” Iwo alibe kudziwa pa zimenezi (zomwe akunenazi). Koma akungonena mawu opeka.
Les exégèses en arabe:
أَمۡ ءَاتَيۡنَٰهُمۡ كِتَٰبٗا مِّن قَبۡلِهِۦ فَهُم بِهِۦ مُسۡتَمۡسِكُونَ
Kapena tidawapatsa buku lina tisadapereke ili, kotero kuti iwo agwiritsitsa limenelo (ndi kugwirizana nazo zili mmenemo)?
Les exégèses en arabe:
بَلۡ قَالُوٓاْ إِنَّا وَجَدۡنَآ ءَابَآءَنَا عَلَىٰٓ أُمَّةٖ وَإِنَّا عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِم مُّهۡتَدُونَ
Koma akunena: “Ndithu ife tidawapeza makolo athu pa chipembedzo chimenechi, ndipo ife tikutsatira mapazi awo.”
Les exégèses en arabe:
وَكَذَٰلِكَ مَآ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ فِي قَرۡيَةٖ مِّن نَّذِيرٍ إِلَّا قَالَ مُتۡرَفُوهَآ إِنَّا وَجَدۡنَآ ءَابَآءَنَا عَلَىٰٓ أُمَّةٖ وَإِنَّا عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِم مُّقۡتَدُونَ
Ndipo momwemo, sitidatumize mchenjezi patsogolo ku mudzi uliwonse koma olemera ammenemo adanena: “Ndithu tidawapeza makolo athu pa chipembedzochi (akuchita mmene tikuchitiramu), ndipo ife titsatira mmapazi awo.”
Les exégèses en arabe:
۞ قَٰلَ أَوَلَوۡ جِئۡتُكُم بِأَهۡدَىٰ مِمَّا وَجَدتُّمۡ عَلَيۡهِ ءَابَآءَكُمۡۖ قَالُوٓاْ إِنَّا بِمَآ أُرۡسِلۡتُم بِهِۦ كَٰفِرُونَ
Adanena (mneneri wawo): “Ngakhale ndakubweretserani chipembedzo chabwino kuposa chomwe mudawapeza nacho makolo anu (mupitirizabe kutsatira chipembedzo cha makolo anucho)?” Adanena: “Ife tikuzikana zimene mwatumidwa nazozi.”
Les exégèses en arabe:
فَٱنتَقَمۡنَا مِنۡهُمۡۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُكَذِّبِينَ
Choncho tidawalanga iwo. Taona m’mene adalili mapeto a otsutsa aja.
Les exégèses en arabe:
وَإِذۡ قَالَ إِبۡرَٰهِيمُ لِأَبِيهِ وَقَوۡمِهِۦٓ إِنَّنِي بَرَآءٞ مِّمَّا تَعۡبُدُونَ
Ndipo (kumbuka) pamene Ibrahim adauza bambo wake ndi anthu ake (kuti): “Ndithu ine ndadzipatula ku zimene mukuzipembedzazi.”
Les exégèses en arabe:
إِلَّا ٱلَّذِي فَطَرَنِي فَإِنَّهُۥ سَيَهۡدِينِ
“Kupatula Amene adandilenga; ndithu Iye andiongola.”
Les exégèses en arabe:
وَجَعَلَهَا كَلِمَةَۢ بَاقِيَةٗ فِي عَقِبِهِۦ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ
Ndipo adalichita liwu ili kukhala losatha ku mtundu wake, kuti abwelere (ku malankhulidwe amenewa).
Les exégèses en arabe:
بَلۡ مَتَّعۡتُ هَٰٓؤُلَآءِ وَءَابَآءَهُمۡ حَتَّىٰ جَآءَهُمُ ٱلۡحَقُّ وَرَسُولٞ مُّبِينٞ
Koma ndidawasangalatsa awa (Aquraish) pamodzi ndi makolo awo kufikira choonadi chawadzera ndi Mtumiki wolongosola (za choonadichi).
Les exégèses en arabe:
وَلَمَّا جَآءَهُمُ ٱلۡحَقُّ قَالُواْ هَٰذَا سِحۡرٞ وَإِنَّا بِهِۦ كَٰفِرُونَ
Ndipo pamene choonadi (Qur’an) chidawadzera, adanena: “Awa ndi matsenga; ndithu ife tikuwakana.”
Les exégèses en arabe:
وَقَالُواْ لَوۡلَا نُزِّلَ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانُ عَلَىٰ رَجُلٖ مِّنَ ٱلۡقَرۡيَتَيۡنِ عَظِيمٍ
Ndipo adatinso: “Nchifukwa ninji Qur’an iyi siidavumbulutsidwe pa munthu wamkulu mmidzi iwiriyi (Makka ndi Twaif).”
Les exégèses en arabe:
أَهُمۡ يَقۡسِمُونَ رَحۡمَتَ رَبِّكَۚ نَحۡنُ قَسَمۡنَا بَيۡنَهُم مَّعِيشَتَهُمۡ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَرَفَعۡنَا بَعۡضَهُمۡ فَوۡقَ بَعۡضٖ دَرَجَٰتٖ لِّيَتَّخِذَ بَعۡضُهُم بَعۡضٗا سُخۡرِيّٗاۗ وَرَحۡمَتُ رَبِّكَ خَيۡرٞ مِّمَّا يَجۡمَعُونَ
(Choncho Allah akunena): “Kodi iwo ndi amene akugawa mtendere wa Mbuye wako (kumpatsa amene wamfuna ndi kummana amene sakumfuna? Chikhalirecho) Ife ndi Amene timagawa pakati pawo zofunika pa moyo wawo mu moyo wadziko lapansi; ndipo tawatukula ena mwa iwo pa ulemelero pamwamba pa ena, choncho ena mwa iwo akuwachita anzawo kukhala antchito awo koma mtendere wa Mbuye wako ndi wabwino kuposa zimene akusonkhanitsa.”
Les exégèses en arabe:
وَلَوۡلَآ أَن يَكُونَ ٱلنَّاسُ أُمَّةٗ وَٰحِدَةٗ لَّجَعَلۡنَا لِمَن يَكۡفُرُ بِٱلرَّحۡمَٰنِ لِبُيُوتِهِمۡ سُقُفٗا مِّن فِضَّةٖ وَمَعَارِجَ عَلَيۡهَا يَظۡهَرُونَ
Ndipo pakadapanda kuopera kuti anthu adzakhala gulu limodzi (lokanira Allah), ndithu tikadazichita nyumba za amene akumkana (Allah) Wachifundo chambiri kukhala ndi madenga a Siliva, ndi makwelero amene amakwelera (kukhalanso a Siliva).
Les exégèses en arabe:
وَلِبُيُوتِهِمۡ أَبۡوَٰبٗا وَسُرُرًا عَلَيۡهَا يَتَّكِـُٔونَ
Ndipo nyumba zawo kukhala ndi zitseko ndi makama (mabedi) omwe amayadzamira (zonsezo kukhala za Siliva).
Les exégèses en arabe:
وَزُخۡرُفٗاۚ وَإِن كُلُّ ذَٰلِكَ لَمَّا مَتَٰعُ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَٱلۡأٓخِرَةُ عِندَ رَبِّكَ لِلۡمُتَّقِينَ
Ndiponso ndi zokongoletsa za golide. Koma zonsezo sikanthu ayi, ndi chisangalalo chabe cha dziko lapansi (chosakhalira kutha); ndipo tsiku lachimaliziro lomwe lili kwa Mbuye wako ndi la oopa Allah (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa).
Les exégèses en arabe:
وَمَن يَعۡشُ عَن ذِكۡرِ ٱلرَّحۡمَٰنِ نُقَيِّضۡ لَهُۥ شَيۡطَٰنٗا فَهُوَ لَهُۥ قَرِينٞ
Ndipo amene akunyozera kukumbukira (Allah) Wachifundo chambiri, timpatsa satana, kuti iye akhale bwenzi lake (lotsagana nalo).
Les exégèses en arabe:
وَإِنَّهُمۡ لَيَصُدُّونَهُمۡ عَنِ ٱلسَّبِيلِ وَيَحۡسَبُونَ أَنَّهُم مُّهۡتَدُونَ
Ndipo iwo amawatsekereza ku njira zabwino ndi kumaganiza kuti iwo ngoongoka.
Les exégèses en arabe:
حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَنَا قَالَ يَٰلَيۡتَ بَيۡنِي وَبَيۡنَكَ بُعۡدَ ٱلۡمَشۡرِقَيۡنِ فَبِئۡسَ ٱلۡقَرِينُ
Kufikira pamene adzatidzera (tsiku la Qiyâma, uku akulowetsedwa ku Moto). Adzati (kumuuza satana): “Kalanga ine! Pakati pa ine ndi iwe pakadakhala ntunda wa pakati pa kuvuma ndi kuzambwe (kutalikirana kwathu).” Ha! Taonani kuipa kwa bwenzi!
Les exégèses en arabe:
وَلَن يَنفَعَكُمُ ٱلۡيَوۡمَ إِذ ظَّلَمۡتُمۡ أَنَّكُمۡ فِي ٱلۡعَذَابِ مُشۡتَرِكُونَ
(Allah adzawauza kuti): “Ndipo lero sikukuthandizani kukhala limodzi kwanu m’chilango pakuti mudadzichitira nokha zoipa.”
Les exégèses en arabe:
أَفَأَنتَ تُسۡمِعُ ٱلصُّمَّ أَوۡ تَهۡدِي ٱلۡعُمۡيَ وَمَن كَانَ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ
Kodi ungathe kuwamveretsa agonthi, kapena ungathe kuwaongola akhungu ndi amene ali mkusokera koonekera?
Les exégèses en arabe:
فَإِمَّا نَذۡهَبَنَّ بِكَ فَإِنَّا مِنۡهُم مُّنتَقِمُونَ
Ngati titakuchotsa (padziko usadaone chilango chawo, usakhale ndi chikaiko), ndithu Ife tiwalanga iwo.
Les exégèses en arabe:
أَوۡ نُرِيَنَّكَ ٱلَّذِي وَعَدۡنَٰهُمۡ فَإِنَّا عَلَيۡهِم مُّقۡتَدِرُونَ
Kapena tikusonyeza zimene tidawalonjeza (uona ndi maso ako usadafe). Ndithu Ife tili ndi mphamvu pa iwo.
Les exégèses en arabe:
فَٱسۡتَمۡسِكۡ بِٱلَّذِيٓ أُوحِيَ إِلَيۡكَۖ إِنَّكَ عَلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
Choncho, gwiritsa zimene zavumbulutsidwa kwa iwe, ndithu iwe uli pa njira yolunjika.
Les exégèses en arabe:
وَإِنَّهُۥ لَذِكۡرٞ لَّكَ وَلِقَوۡمِكَۖ وَسَوۡفَ تُسۡـَٔلُونَ
Ndithu iyi (Qur’an) ndi ulemelero wako ndi anthu ako; ndipo posachedwa mufunsidwa (za ulemelero umenewu).
Les exégèses en arabe:
وَسۡـَٔلۡ مَنۡ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ مِن رُّسُلِنَآ أَجَعَلۡنَا مِن دُونِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ءَالِهَةٗ يُعۡبَدُونَ
Ndipo afunse atumiki Athu amene tidawatumiza iwe usadadze: “Kodi tidapanga milungu ina kuti ipembedzedwe, osati (Allah) Wachifundo chambiri?”
Les exégèses en arabe:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ فَقَالَ إِنِّي رَسُولُ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Ndithu tidamtumiza Mûsa pamodzi ndi zozizwitsa Zathu kwa Farawo ndi nduna zake; ndipo adati: “Ndithu ine ndine Mtumiki wa Mbuye wa zolengedwa.”
Les exégèses en arabe:
فَلَمَّا جَآءَهُم بِـَٔايَٰتِنَآ إِذَا هُم مِّنۡهَا يَضۡحَكُونَ
Koma pamene adawadzera ndi zisonyezo zathu, basi iwo adali kuziseka.
Les exégèses en arabe:
وَمَا نُرِيهِم مِّنۡ ءَايَةٍ إِلَّا هِيَ أَكۡبَرُ مِنۡ أُخۡتِهَاۖ وَأَخَذۡنَٰهُم بِٱلۡعَذَابِ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ
Ndipo chisonyezo chilichonse chomwe tidawasonyeza chidali chachikulu kuposa chinzake (komabe sadakhulupirire). Ndipo tidawalanga ndi chilango kuti abwelere (kwa Ife).
Les exégèses en arabe:
وَقَالُواْ يَٰٓأَيُّهَ ٱلسَّاحِرُ ٱدۡعُ لَنَا رَبَّكَ بِمَا عَهِدَ عِندَكَ إِنَّنَا لَمُهۡتَدُونَ
Ndipo adati (kwa Mûsa): “E iwe wamatsenga! Tipemphere kwa Mbuye wako pa chomwe adakulonjeza; ndithu ife tiongoka, (tikhulupirira).”
Les exégèses en arabe:
فَلَمَّا كَشَفۡنَا عَنۡهُمُ ٱلۡعَذَابَ إِذَا هُمۡ يَنكُثُونَ
Choncho, pamene tidawachotsera chilangocho, basi iwo adayamba kuswa pangano.
Les exégèses en arabe:
وَنَادَىٰ فِرۡعَوۡنُ فِي قَوۡمِهِۦ قَالَ يَٰقَوۡمِ أَلَيۡسَ لِي مُلۡكُ مِصۡرَ وَهَٰذِهِ ٱلۡأَنۡهَٰرُ تَجۡرِي مِن تَحۡتِيٓۚ أَفَلَا تُبۡصِرُونَ
Ndipo Farawo adaitana anthu ake, adati: “E inu anthu anga! Kodi ulamuliro wa mu Iguputo siwanga pamodzi ndi mitsinje iyi imene ikuyenda pansi panga (pa nyumba zanga?) Kodi simukuona?”
Les exégèses en arabe:
أَمۡ أَنَا۠ خَيۡرٞ مِّنۡ هَٰذَا ٱلَّذِي هُوَ مَهِينٞ وَلَا يَكَادُ يُبِينُ
“Kodi kapena ine sindine woposa uyu (Mûsa) wonyozeka, ndipo sangathe kuyankhula momveka?”
Les exégèses en arabe:
فَلَوۡلَآ أُلۡقِيَ عَلَيۡهِ أَسۡوِرَةٞ مِّن ذَهَبٍ أَوۡ جَآءَ مَعَهُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ مُقۡتَرِنِينَ
“Nanga bwanji sadavekedwe zibangiri zagolide kapena angelo kudza pamodzi ndi iye uku akumtsatira?”
Les exégèses en arabe:
فَٱسۡتَخَفَّ قَوۡمَهُۥ فَأَطَاعُوهُۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمٗا فَٰسِقِينَ
Adawapeputsa anthu ake. Ndipo adamvera; iwo adali anthu otuluka mchilamulo (cha Allah).
Les exégèses en arabe:
فَلَمَّآ ءَاسَفُونَا ٱنتَقَمۡنَا مِنۡهُمۡ فَأَغۡرَقۡنَٰهُمۡ أَجۡمَعِينَ
Pamene adatikwiitsa, tidawalanga ndipo tidawamiza onse mmadzi.
Les exégèses en arabe:
فَجَعَلۡنَٰهُمۡ سَلَفٗا وَمَثَلٗا لِّلۡأٓخِرِينَ
Tidawachita (Farawo ndi anthu ake) kukhala chitsanzo cha okanira a pambuyo pawo ndikukhala mbiri kwa anthu amene akudza.
Les exégèses en arabe:
۞ وَلَمَّا ضُرِبَ ٱبۡنُ مَرۡيَمَ مَثَلًا إِذَا قَوۡمُكَ مِنۡهُ يَصِدُّونَ
Ndipo pamene lidaperekedwa fanizo la mwana wa Mariya, pamenepo anthu anu adali kufuula (monyoza).[344]
[344] Fanizo lomwe likunenedwa apa ndi lomufanizira Isa (Yesu) ndi zomwe zikupembedzedwa kusiya Allah. Akafiri adamfanizira iye pambuyo povumbulutsidwa Ayah yakuti: “Ndithu inu ndi zomwe mukuzipembedza kusiya Allah ndi nkhuni za ku Jahannam.” Choncho adati Isa (Yesu) nayenso akalowa ku Moto chifukwa chakuti Akhrisitu amamupembedza kusiya Allah. Koma Allah adamyeretsa ponena kuti: “Ndithu awo amene ubwino wochokera kwa Ife watsogola kwa iwo, iwowo akatalikitsidwa ndi motowo” Choncho Isa (Yesu) sakalowa ku Moto chifukwa iye sadalamule anthu kuti amupembedze komanso sakudziwa kuti pali aliyense amene akupembedza iye.
Les exégèses en arabe:
وَقَالُوٓاْ ءَأَٰلِهَتُنَا خَيۡرٌ أَمۡ هُوَۚ مَا ضَرَبُوهُ لَكَ إِلَّا جَدَلَۢاۚ بَلۡ هُمۡ قَوۡمٌ خَصِمُونَ
Ndipo adati: “Kodi milungu yathu ndi yabwino, kapena iye?” Sadamfanizire kwa iwe koma kufuna kutsutsana basi (kopanda kufuna choona). Koma iwo ndi anthu amtsutso.
Les exégèses en arabe:
إِنۡ هُوَ إِلَّا عَبۡدٌ أَنۡعَمۡنَا عَلَيۡهِ وَجَعَلۡنَٰهُ مَثَلٗا لِّبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ
Iye sadali kanthu koma ndi kapolo amene tidampatsa mtendere; ndipo tidamchita kukhala chitsanzo (chodabwitsa) cha ana a Israyeli.
Les exégèses en arabe:
وَلَوۡ نَشَآءُ لَجَعَلۡنَا مِنكُم مَّلَٰٓئِكَةٗ فِي ٱلۡأَرۡضِ يَخۡلُفُونَ
Ndipo tikadafuna tikadawachita angelo kukhala pa dziko mmalo mwa inu ndi kumasiirana iwo kwa iwo (kuti mudziwe kuti angelo akugonjera malamulo a Allah. Iwo siAllah).
Les exégèses en arabe:
وَإِنَّهُۥ لَعِلۡمٞ لِّلسَّاعَةِ فَلَا تَمۡتَرُنَّ بِهَا وَٱتَّبِعُونِۚ هَٰذَا صِرَٰطٞ مُّسۡتَقِيمٞ
Ndipo iye (Isa (Yesu) adzakhala chizindikiro cha Qiyâma (kuti yayandikira). Choncho musaikaikire, koma nditsatireni. Imeneyi ndi njira yolunjika.
Les exégèses en arabe:
وَلَا يَصُدَّنَّكُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُۖ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوّٞ مُّبِينٞ
Asakutsekerezeni satana; iye kwa inu ndi mdani woonekera.
Les exégèses en arabe:
وَلَمَّا جَآءَ عِيسَىٰ بِٱلۡبَيِّنَٰتِ قَالَ قَدۡ جِئۡتُكُم بِٱلۡحِكۡمَةِ وَلِأُبَيِّنَ لَكُم بَعۡضَ ٱلَّذِي تَخۡتَلِفُونَ فِيهِۖ فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ
Ndipo pamene Isa (Yesu) adadza ndi zisonyezo zoonekera poyera, adati: “Ndakudzerani ndi nzeru (yopindulitsa), ndikuti ndikulongosolereni zina zimene mudali kusiyana mu izo; choncho, muopeni Allah ndiponso ndimvereni.”
Les exégèses en arabe:
إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ رَبِّي وَرَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُوهُۚ هَٰذَا صِرَٰطٞ مُّسۡتَقِيمٞ
“Ndithu Allah ndiye Mbuye wanga ndi Mbuye wanunso; choncho mupembedzeni; imeneyi ndiyo njira yolunjika.”
Les exégèses en arabe:
فَٱخۡتَلَفَ ٱلۡأَحۡزَابُ مِنۢ بَيۡنِهِمۡۖ فَوَيۡلٞ لِّلَّذِينَ ظَلَمُواْ مِنۡ عَذَابِ يَوۡمٍ أَلِيمٍ
Koma magulu adasemphana pakati pawo. Ndipo kuonongeka kuchokera mu chilango cha tsiku lowawa kudzakhala pa amene adzichitira okha zoipa.
Les exégèses en arabe:
هَلۡ يَنظُرُونَ إِلَّا ٱلسَّاعَةَ أَن تَأۡتِيَهُم بَغۡتَةٗ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ
Palibe chimene akuyembekeza, koma Qiyâma basi yomwe iwadzera mwadzidzidzi pomwe iwo sakuzindikira (ali otanganidwa ndi za m’dziko).
Les exégèses en arabe:
ٱلۡأَخِلَّآءُ يَوۡمَئِذِۭ بَعۡضُهُمۡ لِبَعۡضٍ عَدُوٌّ إِلَّا ٱلۡمُتَّقِينَ
Abwenzi tsiku limenelo adzakhala odana, wina ndi mnzake, (chifukwa chakuti adali kuthandizana pa zinthu zosalungama ndi zamachimo) kupatula oopa Allah (amene adachita chibwenzi mwa Allah, pothandizana kukwaniritsa malamulo a Allah ndi kusiya zimene Allah waletsa).
Les exégèses en arabe:
يَٰعِبَادِ لَا خَوۡفٌ عَلَيۡكُمُ ٱلۡيَوۡمَ وَلَآ أَنتُمۡ تَحۡزَنُونَ
(Allah adzati): E inu akapolo Anga (abwino)! Palibe kuopa kwa inu lerolino ndiponso simudandaula.
Les exégèses en arabe:
ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَكَانُواْ مُسۡلِمِينَ
Amene adakhulupirira zisonyezo Zathu ndipo adali Asilamu (ogonjera Allah).
Les exégèses en arabe:
ٱدۡخُلُواْ ٱلۡجَنَّةَ أَنتُمۡ وَأَزۡوَٰجُكُمۡ تُحۡبَرُونَ
Lowani ku Munda wamtendere, inu ndi akazi anu musangalatsidwa.
Les exégèses en arabe:
يُطَافُ عَلَيۡهِم بِصِحَافٖ مِّن ذَهَبٖ وَأَكۡوَابٖۖ وَفِيهَا مَا تَشۡتَهِيهِ ٱلۡأَنفُسُ وَتَلَذُّ ٱلۡأَعۡيُنُۖ وَأَنتُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ
Adzakhala akupititsidwa mbale zagolide ndi matambula (agolide); zonse zokomera moyo zidzakhala mmenemo ndi zokomera maso, ndipo inu mudzakhala mmenemo nthawi yaitali.
Les exégèses en arabe:
وَتِلۡكَ ٱلۡجَنَّةُ ٱلَّتِيٓ أُورِثۡتُمُوهَا بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Ndipo umeneo ndi munda umene mwapatsidwa chifukwa cha (zabwino) zimene munkachita.
Les exégèses en arabe:
لَكُمۡ فِيهَا فَٰكِهَةٞ كَثِيرَةٞ مِّنۡهَا تَأۡكُلُونَ
Inu mupeza mmenemo zipatso zambiri zomwe muzidya.
Les exégèses en arabe:
إِنَّ ٱلۡمُجۡرِمِينَ فِي عَذَابِ جَهَنَّمَ خَٰلِدُونَ
Ndithu ochimwa (okanira) adzakhala m’chilango cha Jahannam nthawi yaitali.
Les exégèses en arabe:
لَا يُفَتَّرُ عَنۡهُمۡ وَهُمۡ فِيهِ مُبۡلِسُونَ
Sadzapatsidwa nthawi yopumula, ndipo mmenemo iwo akataya mtima (zakupeza moyo wabwino).
Les exégèses en arabe:
وَمَا ظَلَمۡنَٰهُمۡ وَلَٰكِن كَانُواْ هُمُ ٱلظَّٰلِمِينَ
Ndipo sitidawapondereze koma adali kudzipondereza okha.
Les exégèses en arabe:
وَنَادَوۡاْ يَٰمَٰلِكُ لِيَقۡضِ عَلَيۡنَا رَبُّكَۖ قَالَ إِنَّكُم مَّٰكِثُونَ
Ndipo (okanira) adzaitana E iwe Malik! (yemwe ndi mngelo woyang’anira moto): ‘‘Mbuye wako atipatse imfa (kuti tipumule kuchilangochi!)” Adzanena (Malik): “Ndithu inu mukhala momwemo!”
Les exégèses en arabe:
لَقَدۡ جِئۡنَٰكُم بِٱلۡحَقِّ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَكُمۡ لِلۡحَقِّ كَٰرِهُونَ
Ndithu tidakubweretserani choona; koma ambiri a inu mudali kuchida choona.
Les exégèses en arabe:
أَمۡ أَبۡرَمُوٓاْ أَمۡرٗا فَإِنَّا مُبۡرِمُونَ
Kodi akonza bwino chikonzero (chawocho chomwe ndi chiwembu chofuna kumupha Mtumiki {s.a.w})? Ndithu nafenso ndife okonza chikonzero chabwino (cholepheretsa chiwembu chawocho).
Les exégèses en arabe:
أَمۡ يَحۡسَبُونَ أَنَّا لَا نَسۡمَعُ سِرَّهُمۡ وَنَجۡوَىٰهُمۚ بَلَىٰ وَرُسُلُنَا لَدَيۡهِمۡ يَكۡتُبُونَ
Kodi akuganiza kuti sitikumva zobisa zawo ndi zonong’oneza zawo? Iyayi, (tikuzimva zonse), ndipo atumiki Athu (angelo) ali nawo pamodzi; akulemba.
Les exégèses en arabe:
قُلۡ إِن كَانَ لِلرَّحۡمَٰنِ وَلَدٞ فَأَنَا۠ أَوَّلُ ٱلۡعَٰبِدِينَ
Nena (kwa omphatikiza Allah ndi mafano): “Zikadakhala kuti (Allah) Wachifundo chambiri ali ndi mwana, ndiye kuti ine ndikadakhala woyamba kumpembedza (mwanayo).”
Les exégèses en arabe:
سُبۡحَٰنَ رَبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ رَبِّ ٱلۡعَرۡشِ عَمَّا يَصِفُونَ
Mbuye wa kumwamba ndi pansi, Mbuye wa Arsh (Mpando wachifumu), Wapatukana ndi mbiri zimene akum’nenerazo (zoti Allah ali ndi mwana).
Les exégèses en arabe:
فَذَرۡهُمۡ يَخُوضُواْ وَيَلۡعَبُواْ حَتَّىٰ يُلَٰقُواْ يَوۡمَهُمُ ٱلَّذِي يُوعَدُونَ
Asiye azingonena zachabezo ndi kusewera kufikira adzakumana ndi tsiku lawo limene akulonjezedwa.
Les exégèses en arabe:
وَهُوَ ٱلَّذِي فِي ٱلسَّمَآءِ إِلَٰهٞ وَفِي ٱلۡأَرۡضِ إِلَٰهٞۚ وَهُوَ ٱلۡحَكِيمُ ٱلۡعَلِيمُ
Ndipo Iye ndiamene akupembedzedwa kumwamba, ndiponso ndi Iye Amene akupembedzedwa pansi. Iye ndi Wanzeru zakuya, Wodziwa kwambiri.
Les exégèses en arabe:
وَتَبَارَكَ ٱلَّذِي لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا وَعِندَهُۥ عِلۡمُ ٱلسَّاعَةِ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Ndipo watukuka kwambiri Yemwe ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi pakati pa zimenezi ndi Wake. Ndiponso kwa Iye ndiko kuli kudziwa kudza kwa tsiku la Qiyâma; ndipo kwa Iye Yekha ndi kumene m’dzabwezedwa.
Les exégèses en arabe:
وَلَا يَمۡلِكُ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ مِن دُونِهِ ٱلشَّفَٰعَةَ إِلَّا مَن شَهِدَ بِٱلۡحَقِّ وَهُمۡ يَعۡلَمُونَ
Ndipo omwe akuwapembedzawo kusiya Iye (Allah), sangathe kupulumutsa (aliyense) kupatula amene akuikira umboni choonachi, pomwe iwo akuchidziwa bwino.
Les exégèses en arabe:
وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَهُمۡ لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُۖ فَأَنَّىٰ يُؤۡفَكُونَ
Ndipo ngati utawafunsa: “Ndani adawalenga?” Anena motsimikiza kuti: “Ndi Allah.” Nanga akutembenuzidwa bwanji (kusiya choona)?
Les exégèses en arabe:
وَقِيلِهِۦ يَٰرَبِّ إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ قَوۡمٞ لَّا يُؤۡمِنُونَ
Ndipo zonena zake (Mneneri Muhammad{s.a.w} nthawi zonse): “E Mbuye Wanga! Ndithu awa ndi anthu osakhulupirira (nditani nao)?”
Les exégèses en arabe:
فَٱصۡفَحۡ عَنۡهُمۡ وَقُلۡ سَلَٰمٞۚ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ
Choncho, akhululukire, ndipo auze mawu a mtendere. Posachedwa adzadziwa!
Les exégèses en arabe:
 
Traduction des sens Sourate: AZ-ZOUKHROUF
Lexique des sourates Numéro de la page
 
Traduction des sens du Noble Coran - Traduction en chewa - Lexique des traductions

Traduction des sens du noble Coran en langue chewa, par Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ (édition 2020).

Fermeture