Check out the new design

क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला * - अनुवादों की सूची


अर्थों का अनुवाद सूरा: अल्-आराफ़   आयत:
قَالَ مَا مَنَعَكَ أَلَّا تَسۡجُدَ إِذۡ أَمَرۡتُكَۖ قَالَ أَنَا۠ خَيۡرٞ مِّنۡهُ خَلَقۡتَنِي مِن نَّارٖ وَخَلَقۡتَهُۥ مِن طِينٖ
(Allah) adati: “Nchiyani chakuletsa kumgwadira pamene ndakulamula?” (Satana) anati: “Ine ndine wabwino kuposa iye. Ine munandilenga ndi moto koma iye mudamulenga ndi dongo.”
अरबी तफ़सीरें:
قَالَ فَٱهۡبِطۡ مِنۡهَا فَمَا يَكُونُ لَكَ أَن تَتَكَبَّرَ فِيهَا فَٱخۡرُجۡ إِنَّكَ مِنَ ٱلصَّٰغِرِينَ
(Allah) adati: “Choncho, choka m’menemo ndi kutsikira pansi. Sikofunika kwa iwe kudzitama m’menemo. Tuluka, ndithu iwe ndiwe mmodzi wa onyozeka.”[179]
[179] Allah anamtulutsa m’nyumba ya ulemelero Wake chifukwa cha kudzitama ndi kunyoza lamulo la Allah.
अरबी तफ़सीरें:
قَالَ أَنظِرۡنِيٓ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ
(Satana) adati: “Ndipatseni nthawi mpaka tsiku limene adzaukitsidwa (akapolo anu ku imfa).”
अरबी तफ़सीरें:
قَالَ إِنَّكَ مِنَ ٱلۡمُنظَرِينَ
(Allah) adati: “Ndithudi iwe ndi mmodzi wa opatsidwa nthawi.”
अरबी तफ़सीरें:
قَالَ فَبِمَآ أَغۡوَيۡتَنِي لَأَقۡعُدَنَّ لَهُمۡ صِرَٰطَكَ ٱلۡمُسۡتَقِيمَ
Iye (chifukwa cha njiru yake yoopsa pa Adam) adati: “Tsono chifukwa chakuti mwandichita ine kukhala wopotoka, ndidzawakhalira (akapolo Anu ndi kuwabisalira) pa njira Yanu yoongoka (ndi cholinga chowasokeretsa).”
अरबी तफ़सीरें:
ثُمَّ لَأٓتِيَنَّهُم مِّنۢ بَيۡنِ أَيۡدِيهِمۡ وَمِنۡ خَلۡفِهِمۡ وَعَنۡ أَيۡمَٰنِهِمۡ وَعَن شَمَآئِلِهِمۡۖ وَلَا تَجِدُ أَكۡثَرَهُمۡ شَٰكِرِينَ
Kenako ndidzawadzera (mbali ya) kutsogolo kwawo, m’mbuyo mwawo, kumbali yakumanja kwawo ndi kumanzere kwawo, mwakuti simudzapeza ambiri a iwo oyamika.
अरबी तफ़सीरें:
قَالَ ٱخۡرُجۡ مِنۡهَا مَذۡءُومٗا مَّدۡحُورٗاۖ لَّمَن تَبِعَكَ مِنۡهُمۡ لَأَمۡلَأَنَّ جَهَنَّمَ مِنكُمۡ أَجۡمَعِينَ
(Allah) adati: “Tuluka m’menemo, uli wonyozeka ndi wothamangitsidwa. Amene adzakutsata iwe mwa iwo, ndithudi, (ndikamponya ku Moto). Ndipo ndikaidzadzitsa Jahannam ndi inu nonse.”
अरबी तफ़सीरें:
وَيَٰٓـَٔادَمُ ٱسۡكُنۡ أَنتَ وَزَوۡجُكَ ٱلۡجَنَّةَ فَكُلَا مِنۡ حَيۡثُ شِئۡتُمَا وَلَا تَقۡرَبَا هَٰذِهِ ٱلشَّجَرَةَ فَتَكُونَا مِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ
(Kenako Allah adanena kwa Adam) “E iwe Adam! Khala ndi mkazi wako m’Munda wamtendere (sangalalani ndi zomwe zili m’menemo), idyani paliponse pamene mwafuna. Koma mtego uwu musawuyandikire kuopera kuti mungakhale m’gulu la odzichitira okha zoipa.”
अरबी तफ़सीरें:
فَوَسۡوَسَ لَهُمَا ٱلشَّيۡطَٰنُ لِيُبۡدِيَ لَهُمَا مَا وُۥرِيَ عَنۡهُمَا مِن سَوۡءَٰتِهِمَا وَقَالَ مَا نَهَىٰكُمَا رَبُّكُمَا عَنۡ هَٰذِهِ ٱلشَّجَرَةِ إِلَّآ أَن تَكُونَا مَلَكَيۡنِ أَوۡ تَكُونَا مِنَ ٱلۡخَٰلِدِينَ
Choncho satana adawanong’oneza (zoipa) kuti awaonetsere zomwe zidabisika kwa iwo za maliseche awo. Ndipo (satana) adati: “Mbuye wanu sadakuletseni mtengo uwu, koma pachifukwa chakuti mungasanduke angelo awiri, kapena kuti mungakhale okhala nthawi yaitali.”
अरबी तफ़सीरें:
وَقَاسَمَهُمَآ إِنِّي لَكُمَا لَمِنَ ٱلنَّٰصِحِينَ
Ndipo adawalumbilira onse awiri kuti: “Ndithudi, ine ndine mmodzi mwa olangiza (ndikukufunirani zabwino).”
अरबी तफ़सीरें:
فَدَلَّىٰهُمَا بِغُرُورٖۚ فَلَمَّا ذَاقَا ٱلشَّجَرَةَ بَدَتۡ لَهُمَا سَوۡءَٰتُهُمَا وَطَفِقَا يَخۡصِفَانِ عَلَيۡهِمَا مِن وَرَقِ ٱلۡجَنَّةِۖ وَنَادَىٰهُمَا رَبُّهُمَآ أَلَمۡ أَنۡهَكُمَا عَن تِلۡكُمَا ٱلشَّجَرَةِ وَأَقُل لَّكُمَآ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ لَكُمَا عَدُوّٞ مُّبِينٞ
Tero adawakopa mwachinyengo. Ndipo pamene adalawa zipatso za mtengowo umaliseche wawo udaoneka kwa iwo nayamba kudziphatika masamba (a mitengo) a m’mundamo. Ndipo Mbuye wawo adawaitana (mowadzudzula) nati: “Kodi sindinakuletseni mtengowu ndi kukuuzani kuti satana ndi mdani wanu woonekeratu?”
अरबी तफ़सीरें:
 
अर्थों का अनुवाद सूरा: अल्-आराफ़
सूरों की सूची पृष्ठ संख्या
 
क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला - अनुवादों की सूची

अनुवाद ख़ालिद इबराहीम बेताला।

बंद करें