Check out the new design

क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला * - अनुवादों की सूची


अर्थों का अनुवाद सूरा: अल्-आराफ़   आयत:
إِنَّ وَلِـِّۧيَ ٱللَّهُ ٱلَّذِي نَزَّلَ ٱلۡكِتَٰبَۖ وَهُوَ يَتَوَلَّى ٱلصَّٰلِحِينَ
“Ndithu Mtetezi wanga ndi Allah, Yemwe wavumbulutsa buku (ili lopatulika). Ndipo Iye amawateteza ochita zabwino.”
अरबी तफ़सीरें:
وَٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ لَا يَسۡتَطِيعُونَ نَصۡرَكُمۡ وَلَآ أَنفُسَهُمۡ يَنصُرُونَ
“Ndipo omwe mukuwapembedza kusiya Iye (Allah,) sangathe kukupulumutsani ndiponso sangathe kudzipulumutsa okha.”
अरबी तफ़सीरें:
وَإِن تَدۡعُوهُمۡ إِلَى ٱلۡهُدَىٰ لَا يَسۡمَعُواْۖ وَتَرَىٰهُمۡ يَنظُرُونَ إِلَيۡكَ وَهُمۡ لَا يُبۡصِرُونَ
Ngati mutawaitanira ku chiwongoko, sangamve; koma uwaona akukuyang’ana koma pomwe iwo sakuona.
अरबी तफ़सीरें:
خُذِ ٱلۡعَفۡوَ وَأۡمُرۡ بِٱلۡعُرۡفِ وَأَعۡرِضۡ عَنِ ٱلۡجَٰهِلِينَ
Khala ndi khalidwe lokhululuka, lamula zabwino ndipo dzipatule ku mbuli.
अरबी तफ़सीरें:
وَإِمَّا يَنزَغَنَّكَ مِنَ ٱلشَّيۡطَٰنِ نَزۡغٞ فَٱسۡتَعِذۡ بِٱللَّهِۚ إِنَّهُۥ سَمِيعٌ عَلِيمٌ
Ndipo ngati manong’onong’o a satana atakuvutitsa, dzitchinjirize ndi Allah. Ndithu Iye Ngwakumva, Ngodziwa.
अरबी तफ़सीरें:
إِنَّ ٱلَّذِينَ ٱتَّقَوۡاْ إِذَا مَسَّهُمۡ طَٰٓئِفٞ مِّنَ ٱلشَّيۡطَٰنِ تَذَكَّرُواْ فَإِذَا هُم مُّبۡصِرُونَ
Ndithu amene akuopa (Allah), udyerekezi wa satana ukawakhudza amakumbukira (Allah), nkuona (njira yotulukira muudyerekezi wakewo).
अरबी तफ़सीरें:
وَإِخۡوَٰنُهُمۡ يَمُدُّونَهُمۡ فِي ٱلۡغَيِّ ثُمَّ لَا يُقۡصِرُونَ
Koma anzawo (omwe ali oipa) amawalimbikitsa m’machimo, ndipo kenako saleka (kupitiriza machimowo).
अरबी तफ़सीरें:
وَإِذَا لَمۡ تَأۡتِهِم بِـَٔايَةٖ قَالُواْ لَوۡلَا ٱجۡتَبَيۡتَهَاۚ قُلۡ إِنَّمَآ أَتَّبِعُ مَا يُوحَىٰٓ إِلَيَّ مِن رَّبِّيۚ هَٰذَا بَصَآئِرُ مِن رَّبِّكُمۡ وَهُدٗى وَرَحۡمَةٞ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ
Ngati siudawabweretsere chozizwitsa, akunena: “Bwanji wosachibweretsa pa iwe wekha? Nena: “Ndithudi ndikutsatira zimene zikuvumbulitsidwa kwa ine kuchokera kwa Mbuye wanga. (Sindichita chinthu mwa ine ndekha). Iyi (Qur’an) ndi umboni (waukulu pa zoyankhula zanga) kuchokera kwa Mbuye wanu. (Izo) ndi chiongoko ndi chifundo kwa anthu okhulupirira.”
अरबी तफ़सीरें:
وَإِذَا قُرِئَ ٱلۡقُرۡءَانُ فَٱسۡتَمِعُواْ لَهُۥ وَأَنصِتُواْ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ
Ndipo Qur’an ikamawerengedwa, mvetserani (mwatcheru) ndi kukhala chete, kuti muchitiridwe chifundo.
अरबी तफ़सीरें:
وَٱذۡكُر رَّبَّكَ فِي نَفۡسِكَ تَضَرُّعٗا وَخِيفَةٗ وَدُونَ ٱلۡجَهۡرِ مِنَ ٱلۡقَوۡلِ بِٱلۡغُدُوِّ وَٱلۡأٓصَالِ وَلَا تَكُن مِّنَ ٱلۡغَٰفِلِينَ
Ndipo mtchule Mbuye wako mu mtima mwako modzichepetsa, mwa mantha ndi mosakweza mawu m’mawa ndi madzulo; ndipo usakhale mwa osalabadila (malamulo a Allah).
अरबी तफ़सीरें:
إِنَّ ٱلَّذِينَ عِندَ رَبِّكَ لَا يَسۡتَكۡبِرُونَ عَنۡ عِبَادَتِهِۦ وَيُسَبِّحُونَهُۥ وَلَهُۥ يَسۡجُدُونَۤ۩
Ndithu amene ali kwa Mbuye wako, (angelo), sadzitukumula posiya kumpembedza (Mbuye wawo, koma iwo) amam’lemekeza ndi kumlambira.
अरबी तफ़सीरें:
 
अर्थों का अनुवाद सूरा: अल्-आराफ़
सूरों की सूची पृष्ठ संख्या
 
क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला - अनुवादों की सूची

अनुवाद ख़ालिद इबराहीम बेताला।

बंद करें