Check out the new design

ការបកប្រែអត្ថន័យគួរអាន - ការបកប្រែជាភាសាឆេវ៉ា - ខលីទ អុីប្រហុីម ប៊ីតាឡា * - សន្ទស្សន៍នៃការបកប្រែ


ការបកប្រែអត្ថន័យ ជំពូក​: អាល់អាន់អាម   អាយ៉ាត់:
۞ وَلَوۡ أَنَّنَا نَزَّلۡنَآ إِلَيۡهِمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ وَكَلَّمَهُمُ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَحَشَرۡنَا عَلَيۡهِمۡ كُلَّ شَيۡءٖ قُبُلٗا مَّا كَانُواْ لِيُؤۡمِنُوٓاْ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ يَجۡهَلُونَ
۞ Ndipo ngati tikadawatumizira angelo (kuti adzaikire umboni za uneneri wako), ndipo akufa nkuwayankhula, (naonso nkuvomereza kuti izi nzoona; kuonjezera apo) nkuwasonkhanitsira chinthu chilichonse pamaso pawo, sakadakhulupirira pokhapokha Allah akadafuna koma ambiri a iwo sazindikira.
តាហ្វសៀរជាភាសា​អារ៉ាប់ជាច្រេីន:
وَكَذَٰلِكَ جَعَلۡنَا لِكُلِّ نَبِيٍّ عَدُوّٗا شَيَٰطِينَ ٱلۡإِنسِ وَٱلۡجِنِّ يُوحِي بَعۡضُهُمۡ إِلَىٰ بَعۡضٖ زُخۡرُفَ ٱلۡقَوۡلِ غُرُورٗاۚ وَلَوۡ شَآءَ رَبُّكَ مَا فَعَلُوهُۖ فَذَرۡهُمۡ وَمَا يَفۡتَرُونَ
Ndipo nchomwechi tidamuikira adani mneneri aliyense (omwe) ndi asatana a mu anthu ndi asatana a m’ziwanda, (omwe) amadziwitsana wina ndi mnzake mawu okometsa ncholinga chonyenga. Ndipo Mbuye wako akadafuna, sakadatha kuchita zimenezi choncho asiye ndi zimene akupeka.
តាហ្វសៀរជាភាសា​អារ៉ាប់ជាច្រេីន:
وَلِتَصۡغَىٰٓ إِلَيۡهِ أَفۡـِٔدَةُ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ وَلِيَرۡضَوۡهُ وَلِيَقۡتَرِفُواْ مَا هُم مُّقۡتَرِفُونَ
Ndi kuti ipendekere ku mawu amenewo mitima ya anthu osakhulupirira tsiku la chimaliziro, ndi kuyanjana nawo (mawuo) ndikutinso apeze (machimo) omwe amawapeza.
តាហ្វសៀរជាភាសា​អារ៉ាប់ជាច្រេីន:
أَفَغَيۡرَ ٱللَّهِ أَبۡتَغِي حَكَمٗا وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَنزَلَ إِلَيۡكُمُ ٱلۡكِتَٰبَ مُفَصَّلٗاۚ وَٱلَّذِينَ ءَاتَيۡنَٰهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ يَعۡلَمُونَ أَنَّهُۥ مُنَزَّلٞ مِّن رَّبِّكَ بِٱلۡحَقِّۖ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُمۡتَرِينَ
(Nena:) “Kodi ndifune woweruza wina kusiya Allah, pomwe Iye ndi Yemwe adavumbulutsa buku kwa inu lofotokoza chilichonse?” Ndipo omwe tidawapatsa buku akudziwa kuti (Qur’an) yavumbulutsidwa ndi Mbuye wako mwachoonadi. Choncho, usakhale mwa okaikira.
តាហ្វសៀរជាភាសា​អារ៉ាប់ជាច្រេីន:
وَتَمَّتۡ كَلِمَتُ رَبِّكَ صِدۡقٗا وَعَدۡلٗاۚ لَّا مُبَدِّلَ لِكَلِمَٰتِهِۦۚ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
Ndipo mawu a Mbuye wako akwanira moona ndi mwachilungamo. Palibe amene angathe kusintha mawu Ake. Iye Ngwakumva, Ngodziwa.
តាហ្វសៀរជាភាសា​អារ៉ាប់ជាច្រេីន:
وَإِن تُطِعۡ أَكۡثَرَ مَن فِي ٱلۡأَرۡضِ يُضِلُّوكَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِۚ إِن يَتَّبِعُونَ إِلَّا ٱلظَّنَّ وَإِنۡ هُمۡ إِلَّا يَخۡرُصُونَ
Ngati umvera ambiri amene ali pa dziko lapansi, akusokeretsa pa njira ya Allah. Satsatira koma zakungoganizira. Ndipo sali chilichonse koma akungonama
តាហ្វសៀរជាភាសា​អារ៉ាប់ជាច្រេីន:
إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعۡلَمُ مَن يَضِلُّ عَن سَبِيلِهِۦۖ وَهُوَ أَعۡلَمُ بِٱلۡمُهۡتَدِينَ
Ndithu Mbuye wako ndi Yemwe akudziwa bwino amene asokera ku njira Yake, ndiponso Iye akudziwa bwino za oongoka.
តាហ្វសៀរជាភាសា​អារ៉ាប់ជាច្រេីន:
فَكُلُواْ مِمَّا ذُكِرَ ٱسۡمُ ٱللَّهِ عَلَيۡهِ إِن كُنتُم بِـَٔايَٰتِهِۦ مُؤۡمِنِينَ
Choncho, idyani (nyama) zomwe dzina la Allah latchulidwapo (pozizinga osati zofa zokha), ngati inu mukhulupiriradi Ayah (zizindikiro) Zake.
តាហ្វសៀរជាភាសា​អារ៉ាប់ជាច្រេីន:
 
ការបកប្រែអត្ថន័យ ជំពូក​: អាល់អាន់អាម
សន្ទស្សន៍នៃជំពូក លេខ​ទំព័រ
 
ការបកប្រែអត្ថន័យគួរអាន - ការបកប្រែជាភាសាឆេវ៉ា - ខលីទ អុីប្រហុីម ប៊ីតាឡា - សន្ទស្សន៍នៃការបកប្រែ

បកប្រែដោយលោកខលីទ អុីប្រហុីម ប៊ីតាឡា។

បិទ