وه‌رگێڕانی ماناكانی قورئانی پیرۆز - وەرگێڕاوی شیشوا * - پێڕستی وه‌رگێڕاوه‌كان


وه‌رگێڕانی ماناكان سوره‌تی: سورەتی الواقعة   ئایه‌تی:

سورەتی الواقعة

إِذَا وَقَعَتِ ٱلۡوَاقِعَةُ
Chikadzachitika chochitikacho (Qiyâma).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
لَيۡسَ لِوَقۡعَتِهَا كَاذِبَةٌ
Palibe wotsutsa za kuchitika kwake.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
خَافِضَةٞ رَّافِعَةٌ
Chidzatsitsa (oipa) ndi kutukula (abwino).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
إِذَا رُجَّتِ ٱلۡأَرۡضُ رَجّٗا
Nthaka ikadzagwedezeka kwamphamvu.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَبُسَّتِ ٱلۡجِبَالُ بَسّٗا
Ndipo mapiri akadzaperedwaperedwa.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَكَانَتۡ هَبَآءٗ مُّنۢبَثّٗا
Nkukhala fumbi longouluka.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَكُنتُمۡ أَزۡوَٰجٗا ثَلَٰثَةٗ
Choncho, inu mudzakhala m’magulu atatu (kulingana ndi zochita zanu).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَأَصۡحَٰبُ ٱلۡمَيۡمَنَةِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَيۡمَنَةِ
Anthu akumanja (abwino;) taonani kukula kwa ulemelero wa anthu akumanja!
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَأَصۡحَٰبُ ٱلۡمَشۡـَٔمَةِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَشۡـَٔمَةِ
Ndi anthu akumanzere (oipa;) taonani kuipa khalidwe la anthu akumanzere!
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَٱلسَّٰبِقُونَ ٱلسَّٰبِقُونَ
Ndipo otsogola (pochita zabwino pa dziko) adzakhalanso otsogola (polandira ulemu tsiku lachimaliziro).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلۡمُقَرَّبُونَ
Iwowo ndioyandikitsidwa (kwa Allah).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فِي جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ
M’minda yamtendere.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
ثُلَّةٞ مِّنَ ٱلۡأَوَّلِينَ
(Iwowo oyandikitsidwawo), gulu lalikulu lochokera kumibadwo yakale.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَقَلِيلٞ مِّنَ ٱلۡأٓخِرِينَ
Ndipo ochepa ochokera ku mbadwo wotsirizira.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
عَلَىٰ سُرُرٖ مَّوۡضُونَةٖ
Uku ali m’makama (m’mabedi) olukidwa ndi zingwe zagolide,
تەفسیرە عەرەبیەکان:
مُّتَّكِـِٔينَ عَلَيۡهَا مُتَقَٰبِلِينَ
Atatsamira m’makamawo uku akuyang’anizana (mwachikondi).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
يَطُوفُ عَلَيۡهِمۡ وِلۡدَٰنٞ مُّخَلَّدُونَ
Anyamata osasintha adzakhala akuwazungulira iwo (ndi kuwatumikira).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
بِأَكۡوَابٖ وَأَبَارِيقَ وَكَأۡسٖ مِّن مَّعِينٖ
Uku atatenga matambula ndi maketulo (odzaza ndi zakumwa za ku Jannah), ndi zipanda zodzaza ndi zakumwa zochokera mu akasupe oyenda;
تەفسیرە عەرەبیەکان:
لَّا يُصَدَّعُونَ عَنۡهَا وَلَا يُنزِفُونَ
(Zakumwa zake) zosapweteketsa mutu ndiponso zosaledzeretsa;
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَفَٰكِهَةٖ مِّمَّا يَتَخَيَّرُونَ
Ndi zipatso (zamitundumitundu) zimene azikazisankha;
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَلَحۡمِ طَيۡرٖ مِّمَّا يَشۡتَهُونَ
Ndi nyama yambalame imene mitima yawo izikafuna;
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَحُورٌ عِينٞ
Ndi akazi ophanuka maso mokongola,
تەفسیرە عەرەبیەکان:
كَأَمۡثَٰلِ ٱللُّؤۡلُوِٕ ٱلۡمَكۡنُونِ
(Kukongola kwawo) ndiye ngati ngale zosungidwa bwino mzigoba zake.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
جَزَآءَۢ بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Kukhala mphoto chifukwa cha zimene amachita (zabwino padziko lapansi).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
لَا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوٗا وَلَا تَأۡثِيمًا
M’menemo sakamva mawu achabe ngakhale (mawu a) machimo,
تەفسیرە عەرەبیەکان:
إِلَّا قِيلٗا سَلَٰمٗا سَلَٰمٗا
Koma mawu oti: “Mtendere! Mtendere!”
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَأَصۡحَٰبُ ٱلۡيَمِينِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡيَمِينِ
Anthu akudzanja lamanja. Taonani kukula malipiro a anthu akudzanja lamanja!
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فِي سِدۡرٖ مَّخۡضُودٖ
(Adzakhala m’mithunzi ya) mitengo ya masawu yopanda minga.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَطَلۡحٖ مَّنضُودٖ
Ndi mitengo ya nthochi yobereka kwambiri.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَظِلّٖ مَّمۡدُودٖ
Ndi m’mithunzi yotambasuka kwambiri, yosachoka,
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَمَآءٖ مَّسۡكُوبٖ
Ndi madzi oyenda mosalekeza,
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَفَٰكِهَةٖ كَثِيرَةٖ
Ndi zipatso zambiri,
تەفسیرە عەرەبیەکان:
لَّا مَقۡطُوعَةٖ وَلَا مَمۡنُوعَةٖ
Zopezeka mnyengo zonse, ndiponso zosaletsedwa (kwa amene akuzifuna).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَفُرُشٖ مَّرۡفُوعَةٍ
Ndi zoyala zapamwamba (zawofuwofu).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
إِنَّآ أَنشَأۡنَٰهُنَّ إِنشَآءٗ
Ndithu tidzawalenga (akazi okhulupirira) m’kalengedwe kapamwamba.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَجَعَلۡنَٰهُنَّ أَبۡكَارًا
Tidzawapanga kukhala anamwali.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
عُرُبًا أَتۡرَابٗا
Okondedwa ndi amuna awo; ofanana misinkhu,
تەفسیرە عەرەبیەکان:
لِّأَصۡحَٰبِ ٱلۡيَمِينِ
A anthu akudzanja la manja.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
ثُلَّةٞ مِّنَ ٱلۡأَوَّلِينَ
Gulu lalikulu lochokera ku m’badwo woyamba.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَثُلَّةٞ مِّنَ ٱلۡأٓخِرِينَ
Ndiponso gulu lalikulu lochokera ku mibadwo yotsiriza.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَأَصۡحَٰبُ ٱلشِّمَالِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلشِّمَالِ
Anthu akudzanja lakumanzere. Taonani chilango choopsa kwa anthu akudzanja lakumanzere!
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فِي سَمُومٖ وَحَمِيمٖ
Adzakhala mu mvuchi wamoto ndi m’madzi owira.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَظِلّٖ مِّن يَحۡمُومٖ
Ndi mumthunzi wa utsi wakuda.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
لَّا بَارِدٖ وَلَا كَرِيمٍ
Siwoziziritsa ndiponso siwosangalatsa.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَبۡلَ ذَٰلِكَ مُتۡرَفِينَ
Ndithu iwo amakhala kalelo mosangalala (samalabadira kumvera Allah),
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَكَانُواْ يُصِرُّونَ عَلَى ٱلۡحِنثِ ٱلۡعَظِيمِ
Ndipo amapitiriza kuchita machimo aakulu (polinga kuti palibe kuuka ku imfa).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَكَانُواْ يَقُولُونَ أَئِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابٗا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ
Ndipo amanena (motsutsa); “Kodi tikadzafa nkusanduka fumbi ndi mafupa ofumbwa, tidzaukitsidwanso?”
تەفسیرە عەرەبیەکان:
أَوَءَابَآؤُنَا ٱلۡأَوَّلُونَ
“Kodi ndi makolo athu akale (adzaukitsidwanso!)”
تەفسیرە عەرەبیەکان:
قُلۡ إِنَّ ٱلۡأَوَّلِينَ وَٱلۡأٓخِرِينَ
Nena kwa iwo (poyankha kutsutsa kwawo). Ndithudi, amibadwo yoyamba ndi mibadwo yomaliza (omwe inu muli m’gulu lawo),
تەفسیرە عەرەبیەکان:
لَمَجۡمُوعُونَ إِلَىٰ مِيقَٰتِ يَوۡمٖ مَّعۡلُومٖ
Adzasonkhanitsidwa m’nthawi ya tsiku lomwe lakhazikitsidwa.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
ثُمَّ إِنَّكُمۡ أَيُّهَا ٱلضَّآلُّونَ ٱلۡمُكَذِّبُونَ
Kenako inu osokera (njira yachilungamo), otsutsa (za kuuka,)
تەفسیرە عەرەبیەکان:
لَأٓكِلُونَ مِن شَجَرٖ مِّن زَقُّومٖ
Mudzadya (ku Jahannam) mtengo wa Zakkum, (mtengo wowawa wopezeka mu Jahannam).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَمَالِـُٔونَ مِنۡهَا ٱلۡبُطُونَ
Mudzakhutitsa mimba zanu ndi umenewu (chifukwa cha njala yadzaoneni).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَشَٰرِبُونَ عَلَيۡهِ مِنَ ٱلۡحَمِيمِ
(Mkhuto wa mtengowo) adzamwera madzi owira;
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَشَٰرِبُونَ شُرۡبَ ٱلۡهِيمِ
Adzamwa monga mmene imamwera ngamira yodwala matenda aludzu!
تەفسیرە عەرەبیەکان:
هَٰذَا نُزُلُهُمۡ يَوۡمَ ٱلدِّينِ
Ili ndi phwando lawo tsiku lamalipiro.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
نَحۡنُ خَلَقۡنَٰكُمۡ فَلَوۡلَا تُصَدِّقُونَ
Ife tidakulengani kodi nchifukwa ninji simukukhulupirira?
تەفسیرە عەرەبیەکان:
أَفَرَءَيۡتُم مَّا تُمۡنُونَ
Tandiuzani za madzi (ambewu ya munthu) amene mumawathira m’chiberekero,
تەفسیرە عەرەبیەکان:
ءَأَنتُمۡ تَخۡلُقُونَهُۥٓ أَمۡ نَحۡنُ ٱلۡخَٰلِقُونَ
Kodi inu ndiamene mumawalenga (madziwo ndi kumayang’anira mkusinthasintha kwake kuti akhale cholengedwa) kapena Ife ndiamene timawalenga?
تەفسیرە عەرەبیەکان:
نَحۡنُ قَدَّرۡنَا بَيۡنَكُمُ ٱلۡمَوۡتَ وَمَا نَحۡنُ بِمَسۡبُوقِينَ
Ife tidalamula imfa pakati panu ndipo Ife sitili wolephera,
تەفسیرە عەرەبیەکان:
عَلَىٰٓ أَن نُّبَدِّلَ أَمۡثَٰلَكُمۡ وَنُنشِئَكُمۡ فِي مَا لَا تَعۡلَمُونَ
Kubweretsa ena m’malo mwanu ndi kukulengani mwamaonekedwe ena omwe simumawadziwa.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَلَقَدۡ عَلِمۡتُمُ ٱلنَّشۡأَةَ ٱلۡأُولَىٰ فَلَوۡلَا تَذَكَّرُونَ
Ndipo ndithu mukdziwa kalengedwe koyamba; nanga bwanji simukukumbukira.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
أَفَرَءَيۡتُم مَّا تَحۡرُثُونَ
Tandiuzani za zimene mukubzala?
تەفسیرە عەرەبیەکان:
ءَأَنتُمۡ تَزۡرَعُونَهُۥٓ أَمۡ نَحۡنُ ٱلزَّٰرِعُونَ
Kodi ndinu amene mukuzimeretsa kapena ndife Amene tikuzimeretsa?
تەفسیرە عەرەبیەکان:
لَوۡ نَشَآءُ لَجَعَلۡنَٰهُ حُطَٰمٗا فَظَلۡتُمۡ تَفَكَّهُونَ
Tikadafuna tikadazitembenuza (mbewu zimenezo kukhala zouma isanakwane nthawi yake yozithyola) choncho mukadakhala mukudandaula.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
إِنَّا لَمُغۡرَمُونَ
(Uku mukunena:) “Ndithu ife tangotaya chuma chathu (padera);”
تەفسیرە عەرەبیەکان:
بَلۡ نَحۡنُ مَحۡرُومُونَ
“Koma ife tamanidwa (phindu la khama lathu).”
تەفسیرە عەرەبیەکان:
أَفَرَءَيۡتُمُ ٱلۡمَآءَ ٱلَّذِي تَشۡرَبُونَ
Kodi mukuwaona madzi amene mukumwa!
تەفسیرە عەرەبیەکان:
ءَأَنتُمۡ أَنزَلۡتُمُوهُ مِنَ ٱلۡمُزۡنِ أَمۡ نَحۡنُ ٱلۡمُنزِلُونَ
Kodi ndinu amene mudawatsitsa ku mitambo kapena ndife Amene timawatsitsa?
تەفسیرە عەرەبیەکان:
لَوۡ نَشَآءُ جَعَلۡنَٰهُ أُجَاجٗا فَلَوۡلَا تَشۡكُرُونَ
Tikadafuna tikadawapanga kukhala amchere; nanga nchifukwa ninji simuthokoza?
تەفسیرە عەرەبیەکان:
أَفَرَءَيۡتُمُ ٱلنَّارَ ٱلَّتِي تُورُونَ
Kodi mukuwuona moto umene mumaukoleza?
تەفسیرە عەرەبیەکان:
ءَأَنتُمۡ أَنشَأۡتُمۡ شَجَرَتَهَآ أَمۡ نَحۡنُ ٱلۡمُنشِـُٔونَ
Kodi ndinu amene mudameretsa mitengo yake kapena Ndife tidaipanga?
تەفسیرە عەرەبیەکان:
نَحۡنُ جَعَلۡنَٰهَا تَذۡكِرَةٗ وَمَتَٰعٗا لِّلۡمُقۡوِينَ
Ife taupanga kuti ukhale chikumbutso (cha Moto watsiku lachimaliziro akauona), ndikuti ukhale chothandiza kwa anthu apaulendo (amene akuyenda m’chipululu).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَسَبِّحۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلۡعَظِيمِ
Choncho, pitiriza kulemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
۞ فَلَآ أُقۡسِمُ بِمَوَٰقِعِ ٱلنُّجُومِ
Ndikulumbilira motsimikiza, mmene mumatsikira nyenyezi (pomwe zikulowa).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَإِنَّهُۥ لَقَسَمٞ لَّوۡ تَعۡلَمُونَ عَظِيمٌ
Ndithu kulumbira uku, mukadakhala olingalira, nkwakukulu kwabasi (pazimene kukusonya).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
إِنَّهُۥ لَقُرۡءَانٞ كَرِيمٞ
Ndithu iyi ndi Qur’an yolemekezeka (ndipo mkati mwake muli zithandizo zambiri).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فِي كِتَٰبٖ مَّكۡنُونٖ
Idachokera mu buku lotetezedwa.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
لَّا يَمَسُّهُۥٓ إِلَّا ٱلۡمُطَهَّرُونَ
Salikhudza kupatula okhawo oyeretsedwa (angelo).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
تَنزِيلٞ مِّن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Chivumbulutso chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa zonse.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
أَفَبِهَٰذَا ٱلۡحَدِيثِ أَنتُم مُّدۡهِنُونَ
Kodi nkhani iyi (ya Qur’an) ndiyomwe inu mukuinyozera?
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَتَجۡعَلُونَ رِزۡقَكُمۡ أَنَّكُمۡ تُكَذِّبُونَ
Kodi mwakuchita kukanira kukhala kuthokoza kwanu pa zimene wakupatsani?
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَلَوۡلَآ إِذَا بَلَغَتِ ٱلۡحُلۡقُومَ
Mmaona bwanji (mzimu wa mmodzi wa inu) ukafika kummero (panthawi ya imfa).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَأَنتُمۡ حِينَئِذٖ تَنظُرُونَ
Uku inu panthawi imeneyo mukuona zimenezo.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَنَحۡنُ أَقۡرَبُ إِلَيۡهِ مِنكُمۡ وَلَٰكِن لَّا تُبۡصِرُونَ
Pomwe Ife tili pafupi ndi iye kuposa inu, koma inu simuona,
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَلَوۡلَآ إِن كُنتُمۡ غَيۡرَ مَدِينِينَ
Mukadakhala kuti simuzalipidwa (pa zomwe mukuchita),
تەفسیرە عەرەبیەکان:
تَرۡجِعُونَهَآ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Bwenzi mukuubweza (mzimuwo) ngati mukunena zoona.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَأَمَّآ إِن كَانَ مِنَ ٱلۡمُقَرَّبِينَ
Ngati (amene yamfikira imfayo) adali mmodzi wa woyandikitsidwa (kwa Allah;)
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَرَوۡحٞ وَرَيۡحَانٞ وَجَنَّتُ نَعِيمٖ
Kobwerera kwake ndi kumpumulo ndi mtendere ndi kupatsidwa zonunkhira ndiponso Munda wamtendere.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَأَمَّآ إِن كَانَ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلۡيَمِينِ
Ndipo ngati adali mmodzi wa anthu akudzanja lamanja,
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَسَلَٰمٞ لَّكَ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلۡيَمِينِ
(Kudzanenedwa kwa iye:) “Mtendere ukhale pa iwe, amene udali m’gulu la anthu akudzanja lakumanja (anthu abwino).”
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَأَمَّآ إِن كَانَ مِنَ ٱلۡمُكَذِّبِينَ ٱلضَّآلِّينَ
Koma ngati adali mmodzi wa anthu otsutsa, osokera,
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَنُزُلٞ مِّنۡ حَمِيمٖ
Phwando lamadzi owira (ndilake).
تەفسیرە عەرەبیەکان:
وَتَصۡلِيَةُ جَحِيمٍ
Ndi kupsa m’moto wa Jahena.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ حَقُّ ٱلۡيَقِينِ
Ndithu izi ndizoona, zotsimikizika.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
فَسَبِّحۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلۡعَظِيمِ
Choncho lemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu.
تەفسیرە عەرەبیەکان:
 
وه‌رگێڕانی ماناكان سوره‌تی: سورەتی الواقعة
پێڕستی سوره‌ته‌كان ژمارەی پەڕە
 
وه‌رگێڕانی ماناكانی قورئانی پیرۆز - وەرگێڕاوی شیشوا - پێڕستی وه‌رگێڕاوه‌كان

وەرگێڕاوی ماناکانی قورئانی پیرۆز بۆ زمانی شیشیوا، وەرگێڕان: خالد إبراهيم بيتالا. چاپی ساڵی 2020ز.

داخستن