ශුද්ධවූ අල් කුර්ආන් අර්ථ කථනය - චෙවා පරිවර්තනය * - පරිවර්තන පටුන


අර්ථ කථනය වාක්‍යය: (3) පරිච්ඡේදය: සූරා අල් අස්ර්
إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَتَوَاصَوۡاْ بِٱلۡحَقِّ وَتَوَاصَوۡاْ بِٱلصَّبۡرِ
Kupatula amene akhulupirira (mwa Allah) ndi kumachita zabwino, ndikumalangizana kutsatira choona ndiponso ndi kumalangizana za kupirira (potsatira malamulo a Allah ndi zina za mdziko).[481]
[481] Mgulu la otaika mwapatulidwa anthu olungama amene zochita zawo zili zolungama, omwe amalamulira kutsatira njira yolungama ndi kupilira. Anthu otere saataika, chifukwa chakuti nthawi yawo amaigwiritsira ntchito pa zinthu zabwino, zowathandiza padziko ndi pambuyo pa imfa. Kupilira kulipo mitundu inayi:-
(a) Kupilira pochita zinthu zabwino zomwe zili zovuta kwa munthu kuzipitiriza, monga kupemphera Swala zisanu.
(b) Kupilira posiya kuchita zoipa zimene zili zovuta kwa munthu kuti azileke.
(c) Kuwapilira anthu anzako; kupilira ndi zoipa zawo posawabwezera choipa chilichonse.
(d) Kupilira ndi mazunzo a padziko, monga njala, matenda, kusauka ndi zina zotero.
අල්කුර්ආන් අරාබි අර්ථ විවරණ:
 
අර්ථ කථනය වාක්‍යය: (3) පරිච්ඡේදය: සූරා අල් අස්ර්
සූරා පටුන පිටු අංක
 
ශුද්ධවූ අල් කුර්ආන් අර්ථ කථනය - චෙවා පරිවර්තනය - පරිවර්තන පටුන

ශුද්ධ වූ අල් කුර්ආනයේ අර්ථයන් හි චෙවා පරිවර්තනය. (ක)හාලිද් ඉබ්රාහීම් බීතාලා විසින් පරිවර්තනය කරන ලදී. 2020 මද්‍රණය

වසන්න