Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - Dịch thuật tiếng Chichio * - Mục lục các bản dịch


Ý nghĩa nội dung Câu: (159) Chương: Chương Al-Baqarah
إِنَّ ٱلَّذِينَ يَكۡتُمُونَ مَآ أَنزَلۡنَا مِنَ ٱلۡبَيِّنَٰتِ وَٱلۡهُدَىٰ مِنۢ بَعۡدِ مَا بَيَّنَّٰهُ لِلنَّاسِ فِي ٱلۡكِتَٰبِ أُوْلَٰٓئِكَ يَلۡعَنُهُمُ ٱللَّهُ وَيَلۡعَنُهُمُ ٱللَّٰعِنُونَ
Ndithudi, amene akubisa zimene tavumbulutsa zomwe ndi zisonyezo zoonekera poyera, ndi chiongoko pambuyo pozifotokoza mwatsatanetsatane kwa anthu m’Buku, Allah akuwatembelera iwo. Ndiponso akuwatembelera otembelera.[9]
[9] Nkofunika kwa munthu aliyense amene wachidziwa choona kuchita izi:-
a) Kuchivomereza choonacho.
b) Kuchitsata.
c) Kuchifalitsa.
d) Kuchiphunzitsa.
Choncho, masheikh ndi maulama ali ndi mwawi pokhala ndi ntchito yapamwambayi. Achite ntchitoyi modzipereka kwatunthu, mwaulere kapena molandira malipiro ngati alipo. Apitirize kuigwira ntchitoyi pamoyo wawo wonse ngakhale atakumana ndi zovuta pa ntchitoyi. Ntchitoyi njomwe aneneri a Allah adali kugwira. Tero aigwire motsanzira momwe aneneri a Allah adali kuigwilira ntchitoyi pamakhalidwe awo ndi machitidwe awo onse. Kubisa komwe kwanenedwa m’ndimeyi sikubisa mawu a Allah kokha, komanso kubisa maphunziro a zam’dziko ofunika kwa anthu.
Chisilamu chikulimbikitsa kuti ngati munthu akudziwa chilichonse chomwe chili ndi phindu kwa anthu awaphunzitse anzake, asawabisire chifukwa choopa kuti nzeruyo angaitulukire anthu ambiri ndi kuti iye sadzapatsidwa ulemu kapena kuopa kuti ena angampose. Maganizo otere ngosafunika m’Chisilamu.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
 
Ý nghĩa nội dung Câu: (159) Chương: Chương Al-Baqarah
Mục lục các chương Kinh Số trang
 
Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - Dịch thuật tiếng Chichio - Mục lục các bản dịch

Bản dịch ý nghĩa nội dung Kinh Qur'an bằng tiếng Chichio, do Khalid Ibrahim Petala dịch thuật, bản dịch năm 2020.

Đóng lại