Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 赛拜艾   段:
وَلَا تَنفَعُ ٱلشَّفَٰعَةُ عِندَهُۥٓ إِلَّا لِمَنۡ أَذِنَ لَهُۥۚ حَتَّىٰٓ إِذَا فُزِّعَ عَن قُلُوبِهِمۡ قَالُواْ مَاذَا قَالَ رَبُّكُمۡۖ قَالُواْ ٱلۡحَقَّۖ وَهُوَ ٱلۡعَلِيُّ ٱلۡكَبِيرُ
Ndipo uwomboli sudzathandiza kwa Iye (Allah) kupatula amene wamuloleza. Kufikira pamene mantha adzachotsedwa m’mitima mwawo (popatsidwa chilolezo choti apulumutse ena), adzanena pakati pawo (mosangalala): “Kodi wanena chiyani Mbuye wanu?” (Adzayankha): “Ndithu Iye wanena choona; Iye Ngotukuka Ngwamkulu.”
阿拉伯语经注:
۞ قُلۡ مَن يَرۡزُقُكُم مِّنَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ قُلِ ٱللَّهُۖ وَإِنَّآ أَوۡ إِيَّاكُمۡ لَعَلَىٰ هُدًى أَوۡ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ
Nena (kwa iwo, iwe Mneneri {s.a.w}): “Kodi ndani amakupatsani rizq (zaulere) kuchokera kumwamba ndi pansi?” (Ngati sakuyankha chifukwa chodzitukumula), nena (kwa iwo): “Ndi Allah (Mmodzi, amene akukupatsani zopatsa zaulere zochokera kumwamba ndi pansi); ndipo ife kapena inu, tili pachiongoko kapena mkusokera koonekera.”
阿拉伯语经注:
قُل لَّا تُسۡـَٔلُونَ عَمَّآ أَجۡرَمۡنَا وَلَا نُسۡـَٔلُ عَمَّا تَعۡمَلُونَ
Nena: “Simudzafunsidwa pa zimene (ife) talakwa, nafenso sitidzafunsidwa pazimene mukuchita.”
阿拉伯语经注:
قُلۡ يَجۡمَعُ بَيۡنَنَا رَبُّنَا ثُمَّ يَفۡتَحُ بَيۡنَنَا بِٱلۡحَقِّ وَهُوَ ٱلۡفَتَّاحُ ٱلۡعَلِيمُ
Nena (kwa iwo): “Mbuye wathu adzatisonkhanitsa pakati pathu (pa tsiku la chiweruziro). Kenako adzaweruza pakati pathu mwa choonadi; Iye ndi Muweruzi Wodziwa kwambiri.
阿拉伯语经注:
قُلۡ أَرُونِيَ ٱلَّذِينَ أَلۡحَقۡتُم بِهِۦ شُرَكَآءَۖ كَلَّاۚ بَلۡ هُوَ ٱللَّهُ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
Nena (kwa iwo): “Ndisonyezeni amene mwawalumikiza ndi Iye monga othandizana Naye; iyayi, sizingatheke (Iye kukhala ndi anzake), koma Iye (Yekha) ndiye Allah, Mwini Mphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.”
阿拉伯语经注:
وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا كَآفَّةٗ لِّلنَّاسِ بَشِيرٗا وَنَذِيرٗا وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ
Ndipo sitidakutumize (iwe, Mtumiki{s.a.w} kwa Arabu okha) koma kwa anthu onse, kuti ukhale wouza (okhulupirira) nkhani zabwino ndi wochenjeza otsutsa. Koma anthu ambiri sadziwa (za uthenga wako).
阿拉伯语经注:
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Eti akunena: “Nliti lidzakwaniritsidwe lonjezo ili (lakudza kwa chiweruziro) ngati mukunenadi zoona?”
阿拉伯语经注:
قُل لَّكُم مِّيعَادُ يَوۡمٖ لَّا تَسۡتَـٔۡخِرُونَ عَنۡهُ سَاعَةٗ وَلَا تَسۡتَقۡدِمُونَ
Nena: “Muli nalo pangano (lotsimikizika) la tsiku limene simungathe kulichedwetsa ngakhale ola limodzi, kapena kulifulumizitsa.”
阿拉伯语经注:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَن نُّؤۡمِنَ بِهَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ وَلَا بِٱلَّذِي بَيۡنَ يَدَيۡهِۗ وَلَوۡ تَرَىٰٓ إِذِ ٱلظَّٰلِمُونَ مَوۡقُوفُونَ عِندَ رَبِّهِمۡ يَرۡجِعُ بَعۡضُهُمۡ إِلَىٰ بَعۡضٍ ٱلۡقَوۡلَ يَقُولُ ٱلَّذِينَ ٱسۡتُضۡعِفُواْ لِلَّذِينَ ٱسۡتَكۡبَرُواْ لَوۡلَآ أَنتُمۡ لَكُنَّا مُؤۡمِنِينَ
Ndipo amene sadakhulupirire akunena: “Sitiikhulupirira Qur’an iyi, ngakhalenso (mabuku) aja apatsogolo pake.” Ndipo ukadawaona achinyengo pamene azikaimiritsidwa pamaso pa Mbuye wawo, (ukadaona zoopsa zazikulu), uku pakati pawo akubwezerana mawu. Amene adaponderezedwa adzanena kwa amene adadzikweza: “Kukadapanda inu (kutipondereza), tikadakhala okhulupirira.”
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 赛拜艾
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭