Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 舒拉   段:

Ash-Shûra

حمٓ
Hâ-Mîm.
阿拉伯语经注:
عٓسٓقٓ
‘Aîn-Sîn-Qâf.
阿拉伯语经注:
كَذَٰلِكَ يُوحِيٓ إِلَيۡكَ وَإِلَى ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِكَ ٱللَّهُ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
Chomwecho akukuvumbulutsira iwe ndi atumiki amene adadza kale, Allah Ngopambana Wanzeru zakuya.
阿拉伯语经注:
لَهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۖ وَهُوَ ٱلۡعَلِيُّ ٱلۡعَظِيمُ
Zonse za kumwamba ndi pansi ndi za Iye Yekha. Ndipo Iye ndi Wotukuka, Wamkulu.
阿拉伯语经注:
تَكَادُ ٱلسَّمَٰوَٰتُ يَتَفَطَّرۡنَ مِن فَوۡقِهِنَّۚ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ يُسَبِّحُونَ بِحَمۡدِ رَبِّهِمۡ وَيَسۡتَغۡفِرُونَ لِمَن فِي ٱلۡأَرۡضِۗ أَلَآ إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ
(Chifukwa chakukula Kwake ndi ulemelero Wake) mitambo ikuyandikira kuphwasuka pamwamba pa iyo. Ndipo angelo akulemekeza ndi kutamanda Mbuye wawo, ndi kuwapemphera chikhululuko amene ali pa dziko lapansi. Dziwani kuti ndithu Allah Yekha ndiye Wokhululuka kwabasi, Wachisoni chosatha.
阿拉伯语经注:
وَٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَ ٱللَّهُ حَفِيظٌ عَلَيۡهِمۡ وَمَآ أَنتَ عَلَيۡهِم بِوَكِيلٖ
Ndipo awo amene adzipangira athandizi (a mafano) kusiya Allah, Allah ndi Wolondera (zochita) zawo; ndipo iwe si muyang’anili wawo (wosunga zochita zawo).
阿拉伯语经注:
وَكَذَٰلِكَ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ قُرۡءَانًا عَرَبِيّٗا لِّتُنذِرَ أُمَّ ٱلۡقُرَىٰ وَمَنۡ حَوۡلَهَا وَتُنذِرَ يَوۡمَ ٱلۡجَمۡعِ لَا رَيۡبَ فِيهِۚ فَرِيقٞ فِي ٱلۡجَنَّةِ وَفَرِيقٞ فِي ٱلسَّعِيرِ
Chomwechonso (monga chilili chivumbulutso chapoyerachi) takuvumbulutsira Qur’an m’Chiarabu (popanda chikaiko) kuti uchenjeze (eni) manthu wa mizinda (Makka) ndi amene ali m’mbali mwake, ndikutinso uchenjeze (anthu) za tsiku la msonkhano, lopanda chikaiko. (Pa tsikulo anthu adzagawikana mmagulu awiri): gulu lina ku Jannah, ndipo gulu lina ku Moto.
阿拉伯语经注:
وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَجَعَلَهُمۡ أُمَّةٗ وَٰحِدَةٗ وَلَٰكِن يُدۡخِلُ مَن يَشَآءُ فِي رَحۡمَتِهِۦۚ وَٱلظَّٰلِمُونَ مَا لَهُم مِّن وَلِيّٖ وَلَا نَصِيرٍ
Ndipo akadafuna Allah akadawachita iwo kukhala mpingo umodzi; koma amamulowetsa ku chifundo Chake amene wamfuna ndipo odzichitira okha chinyengo (pokana Allah) alibe mtetezi kapena mthandizi.
阿拉伯语经注:
أَمِ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَۖ فَٱللَّهُ هُوَ ٱلۡوَلِيُّ وَهُوَ يُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
Kapena adzichitira athandizi ena kusiya Iye (Allah)? Pomwe Allah Yekha ndiye Mthandizi woona ndipo Iye amaukitsa akufa. Ndipo Iye ndi Wokhoza pa chilichonse.
阿拉伯语经注:
وَمَا ٱخۡتَلَفۡتُمۡ فِيهِ مِن شَيۡءٖ فَحُكۡمُهُۥٓ إِلَى ٱللَّهِۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبِّي عَلَيۡهِ تَوَكَّلۡتُ وَإِلَيۡهِ أُنِيبُ
Ndipo chilichonse chimene mwasiyana mmenemo (mchipembedzo: za kukhulupirira ndi kusakhulupirira) chiweruzo chake nkwa Allah; (bwererani ku Buku la Allah ndi Hadith za mtumiki Wake). Ndipo Ameneyo ndi Allah, Mbuye wanga; kwa Iye Yekha ndatsamira, ndipo kwa Iye Yekha (ndiko) ndikutembenukira.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 舒拉
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭