Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 舒拉   段:
وَمِنۡ ءَايَٰتِهِ ٱلۡجَوَارِ فِي ٱلۡبَحۡرِ كَٱلۡأَعۡلَٰمِ
Ndipo zina mwa zisonyezo Zake ndi zombo zoyenda panyanja zonga mapiri ataliatali (koma osabira).
阿拉伯语经注:
إِن يَشَأۡ يُسۡكِنِ ٱلرِّيحَ فَيَظۡلَلۡنَ رَوَاكِدَ عَلَىٰ ظَهۡرِهِۦٓۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّكُلِّ صَبَّارٖ شَكُورٍ
Atafuna akhoza kuiyimitsa mphepo choncho nkungokhala duu, (osayenda) pamwamba pake (panyanja). Ndithu mzimenezi muli zisonyezo kwa aliyense wopirira ndi wothokoza.
阿拉伯语经注:
أَوۡ يُوبِقۡهُنَّ بِمَا كَسَبُواْ وَيَعۡفُ عَن كَثِيرٖ
Kapena akhoza kuziononga (potumiza mphepo yamkuntho) chifukwa cha machimo amene adawachita. Koma amakhululuka zambiri.
阿拉伯语经注:
وَيَعۡلَمَ ٱلَّذِينَ يُجَٰدِلُونَ فِيٓ ءَايَٰتِنَا مَا لَهُم مِّن مَّحِيصٖ
Ndipo adzadziwa (tsiku la Qiyâma) amene akutsutsana ndi zisonyezo Zathu kuti alibe pothawira (kuchilango cha Allah).
阿拉伯语经注:
فَمَآ أُوتِيتُم مِّن شَيۡءٖ فَمَتَٰعُ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَمَا عِندَ ٱللَّهِ خَيۡرٞ وَأَبۡقَىٰ لِلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَلَىٰ رَبِّهِمۡ يَتَوَكَّلُونَ
Ndipo chilichonse chimene mwapatsidwa, nzosangalatsa za moyo wa pa dziko. Koma zimene zili kwa Allah ndi zabwino ndiponso zamuyaya za amene akhulupirira ndi kutsamira kwa Mbuye wawo.
阿拉伯语经注:
وَٱلَّذِينَ يَجۡتَنِبُونَ كَبَٰٓئِرَ ٱلۡإِثۡمِ وَٱلۡفَوَٰحِشَ وَإِذَا مَا غَضِبُواْ هُمۡ يَغۡفِرُونَ
Ndipo amene akupewa machimo akuluakulu omwe Allah waletsa ndi machimo onse oipitsitsa; ndipo iwo akakwiya (chifukwa choputidwa) iwo amakhululuka;
阿拉伯语经注:
وَٱلَّذِينَ ٱسۡتَجَابُواْ لِرَبِّهِمۡ وَأَقَامُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَأَمۡرُهُمۡ شُورَىٰ بَيۡنَهُمۡ وَمِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ يُنفِقُونَ
Ndipo amene adayankha kuitana kwa Mbuye wawo ndi kusunga mapemphero (popemphera mnthawi yake mkapempheredwe koyenera); ndipo zinthu zawo zonse zimakhala zokambirana pakati pawo; ndipo mzimene tawapatsa amapereka (pa njira ya Allah);
阿拉伯语经注:
وَٱلَّذِينَ إِذَآ أَصَابَهُمُ ٱلۡبَغۡيُ هُمۡ يَنتَصِرُونَ
Ndi amene amati akachitiridwa mtopola amadzipulumutsa.
阿拉伯语经注:
وَجَزَٰٓؤُاْ سَيِّئَةٖ سَيِّئَةٞ مِّثۡلُهَاۖ فَمَنۡ عَفَا وَأَصۡلَحَ فَأَجۡرُهُۥ عَلَى ٱللَّهِۚ إِنَّهُۥ لَا يُحِبُّ ٱلظَّٰلِمِينَ
Malipiro a choipa ndi choipa chonga icho; (wochita choipa alipidwe choipa chonga chimene wachita). Koma amene wakhululukira wochita choipa (pomwe akhoza kubwezera), ndi kuyanjana naye (mdani wakeyo), malipiro ake ali kwa Allah; ndithu Allah sakonda ochitira anzawo mtopola.
阿拉伯语经注:
وَلَمَنِ ٱنتَصَرَ بَعۡدَ ظُلۡمِهِۦ فَأُوْلَٰٓئِكَ مَا عَلَيۡهِم مِّن سَبِيلٍ
Koma amene abwezera pambuyo pakuchitiridwa mtopola, kwa iwo palibe njira yowadzudzulira.
阿拉伯语经注:
إِنَّمَا ٱلسَّبِيلُ عَلَى ٱلَّذِينَ يَظۡلِمُونَ ٱلنَّاسَ وَيَبۡغُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّۚ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ
Ndithu njira yodzudzulidwira ili kwa amene akupondereza anthu ndi kuchita mtopola pa dziko popanda chifukwa choyenera. Iwowo ndi amene adzalandira chilango chowawa.
阿拉伯语经注:
وَلَمَن صَبَرَ وَغَفَرَ إِنَّ ذَٰلِكَ لَمِنۡ عَزۡمِ ٱلۡأُمُورِ
Ndipo amene akupirira ndi kukhululuka, (Allah adzamlipira mphoto yaikulu); ndithu kupirirako ndi chimodzi mwa zinthu zazikulu (chofunika kudzilimbikitsa nacho Msilamu pa chikhalidwe chake.)
阿拉伯语经注:
وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِن وَلِيّٖ مِّنۢ بَعۡدِهِۦۗ وَتَرَى ٱلظَّٰلِمِينَ لَمَّا رَأَوُاْ ٱلۡعَذَابَ يَقُولُونَ هَلۡ إِلَىٰ مَرَدّٖ مِّن سَبِيلٖ
Ndipo amene Allah wamsiya kuti asokere, alibe mthandizi (wina) kupatula Iye (Allah). ndipo udzawaona osalungama pamene adzachiona (masomphenya) chilango, adzanena (modandaula): “Kodi pali njira yobwerera (padziko lapansi kuti tikachite zabwino tidzalowe ku Jannah)?”
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 舒拉
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭