Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 宰哈柔福   段:

Az-Zukhruf

حمٓ
. Hâ-Mîm.
阿拉伯语经注:
وَٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُبِينِ
Ndikulumbilira buku lofotokoza momveka.
阿拉伯语经注:
إِنَّا جَعَلۡنَٰهُ قُرۡءَٰنًا عَرَبِيّٗا لَّعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ
Ndithu Ife talichita bukuli (Qur’an) kukhala chowerengedwa m’Chiarabu kuti muzindikire.
阿拉伯语经注:
وَإِنَّهُۥ فِيٓ أُمِّ ٱلۡكِتَٰبِ لَدَيۡنَا لَعَلِيٌّ حَكِيمٌ
Ndipo ndithu bukuli (Qur’an) lili m’manthu wa mabuku onse (Lawhi Mahfudh) limene lili kwa Ife; (ndipo ndi buku) lotukuka, la mawu anzeru.
阿拉伯语经注:
أَفَنَضۡرِبُ عَنكُمُ ٱلذِّكۡرَ صَفۡحًا أَن كُنتُمۡ قَوۡمٗا مُّسۡرِفِينَ
Kodi tisiye kukukumbutsani chifukwa chakuti ndinu anthu opyola malire (pochita zoipa)?
阿拉伯语经注:
وَكَمۡ أَرۡسَلۡنَا مِن نَّبِيّٖ فِي ٱلۡأَوَّلِينَ
Ndipo tidatumiza aneneri ambiri kwa anthu akale.
阿拉伯语经注:
وَمَا يَأۡتِيهِم مِّن نَّبِيٍّ إِلَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Ndipo palibe mneneri aliyense amene amawadzera koma amam’chitira chipongwe.
阿拉伯语经注:
فَأَهۡلَكۡنَآ أَشَدَّ مِنۡهُم بَطۡشٗا وَمَضَىٰ مَثَلُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Choncho tidawaononga amene adali amphamvu kuposa iwo (Aquraish) ndipo ladutsa fanizo la (zilango zomwe zidawapeza) anthu akale.
阿拉伯语经注:
وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ لَيَقُولُنَّ خَلَقَهُنَّ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡعَلِيمُ
Ndipo ukawafunsa: “Ndani adalenga thambo ndi nthaka?” Ndithu ayankha kuti: “Adazilenga (Allah) Mwini Mphamvu, Wodziwa.”
阿拉伯语经注:
ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ مَهۡدٗا وَجَعَلَ لَكُمۡ فِيهَا سُبُلٗا لَّعَلَّكُمۡ تَهۡتَدُونَ
Amene wakupangirani nthaka kukhala choyala ndipo adakupangirani njira mmenemo kuti muongoke (ndikukafika kumene mukufuna).
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 宰哈柔福
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭