《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 * - 译解目录


含义的翻译 章: 舒拉   段:

舒拉

حمٓ
Hâ-Mîm.
阿拉伯语经注:
عٓسٓقٓ
‘Aîn-Sîn-Qâf.
阿拉伯语经注:
كَذَٰلِكَ يُوحِيٓ إِلَيۡكَ وَإِلَى ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِكَ ٱللَّهُ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
Chomwecho akukuvumbulutsira iwe ndi atumiki amene adadza kale, Allah Ngopambana Wanzeru zakuya.
阿拉伯语经注:
لَهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۖ وَهُوَ ٱلۡعَلِيُّ ٱلۡعَظِيمُ
Zonse za kumwamba ndi pansi ndi za Iye Yekha. Ndipo Iye ndi Wotukuka, Wamkulu.
阿拉伯语经注:
تَكَادُ ٱلسَّمَٰوَٰتُ يَتَفَطَّرۡنَ مِن فَوۡقِهِنَّۚ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ يُسَبِّحُونَ بِحَمۡدِ رَبِّهِمۡ وَيَسۡتَغۡفِرُونَ لِمَن فِي ٱلۡأَرۡضِۗ أَلَآ إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ
(Chifukwa chakukula Kwake ndi ulemelero Wake) mitambo ikuyandikira kuphwasuka pamwamba pa iyo. Ndipo angelo akulemekeza ndi kutamanda Mbuye wawo, ndi kuwapemphera chikhululuko amene ali pa dziko lapansi. Dziwani kuti ndithu Allah Yekha ndiye Wokhululuka kwabasi, Wachisoni chosatha.
阿拉伯语经注:
وَٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَ ٱللَّهُ حَفِيظٌ عَلَيۡهِمۡ وَمَآ أَنتَ عَلَيۡهِم بِوَكِيلٖ
Ndipo awo amene adzipangira athandizi (a mafano) kusiya Allah, Allah ndi Wolondera (zochita) zawo; ndipo iwe si muyang’anili wawo (wosunga zochita zawo).
阿拉伯语经注:
وَكَذَٰلِكَ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ قُرۡءَانًا عَرَبِيّٗا لِّتُنذِرَ أُمَّ ٱلۡقُرَىٰ وَمَنۡ حَوۡلَهَا وَتُنذِرَ يَوۡمَ ٱلۡجَمۡعِ لَا رَيۡبَ فِيهِۚ فَرِيقٞ فِي ٱلۡجَنَّةِ وَفَرِيقٞ فِي ٱلسَّعِيرِ
Chomwechonso (monga chilili chivumbulutso chapoyerachi) takuvumbulutsira Qur’an m’Chiarabu (popanda chikaiko) kuti uchenjeze (eni) manthu wa mizinda (Makka) ndi amene ali m’mbali mwake, ndikutinso uchenjeze (anthu) za tsiku la msonkhano, lopanda chikaiko. (Pa tsikulo anthu adzagawikana mmagulu awiri): gulu lina ku Jannah, ndipo gulu lina ku Moto.
阿拉伯语经注:
وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَجَعَلَهُمۡ أُمَّةٗ وَٰحِدَةٗ وَلَٰكِن يُدۡخِلُ مَن يَشَآءُ فِي رَحۡمَتِهِۦۚ وَٱلظَّٰلِمُونَ مَا لَهُم مِّن وَلِيّٖ وَلَا نَصِيرٍ
Ndipo akadafuna Allah akadawachita iwo kukhala mpingo umodzi; koma amamulowetsa ku chifundo Chake amene wamfuna ndipo odzichitira okha chinyengo (pokana Allah) alibe mtetezi kapena mthandizi.
阿拉伯语经注:
أَمِ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَۖ فَٱللَّهُ هُوَ ٱلۡوَلِيُّ وَهُوَ يُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
Kapena adzichitira athandizi ena kusiya Iye (Allah)? Pomwe Allah Yekha ndiye Mthandizi woona ndipo Iye amaukitsa akufa. Ndipo Iye ndi Wokhoza pa chilichonse.
阿拉伯语经注:
وَمَا ٱخۡتَلَفۡتُمۡ فِيهِ مِن شَيۡءٖ فَحُكۡمُهُۥٓ إِلَى ٱللَّهِۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبِّي عَلَيۡهِ تَوَكَّلۡتُ وَإِلَيۡهِ أُنِيبُ
Ndipo chilichonse chimene mwasiyana mmenemo (mchipembedzo: za kukhulupirira ndi kusakhulupirira) chiweruzo chake nkwa Allah; (bwererani ku Buku la Allah ndi Hadith za mtumiki Wake). Ndipo Ameneyo ndi Allah, Mbuye wanga; kwa Iye Yekha ndatsamira, ndipo kwa Iye Yekha (ndiko) ndikutembenukira.
阿拉伯语经注:
فَاطِرُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ جَعَلَ لَكُم مِّنۡ أَنفُسِكُمۡ أَزۡوَٰجٗا وَمِنَ ٱلۡأَنۡعَٰمِ أَزۡوَٰجٗا يَذۡرَؤُكُمۡ فِيهِۚ لَيۡسَ كَمِثۡلِهِۦ شَيۡءٞۖ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡبَصِيرُ
(Iye ndi) Mlengi wa kumwamba ndi pansi. Adakupangirani akazi kuchokera mwa inu nomwe, ndipo nazo ziweto mitundu iwiri, (zazimuna ndi zazikazi. Choncho) akukuchulukitsani mmenemo (mchikonzero Chake chanzeru) palibe chilichonse chofanana ndi Iye. Iye ndi Wakumva zonse ndiponso Woona zonse.
阿拉伯语经注:
لَهُۥ مَقَالِيدُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ وَيَقۡدِرُۚ إِنَّهُۥ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٞ
Makiyi a kumwamba ndi pansi ndi Ake. Amamchulukitsira rizq amene wamfuna ndipo amamchepetsera amene wamfuna. Ndithu Iye Ngodziwa chilichonse (pochiika pamalo oyenera).
阿拉伯语经注:
۞ شَرَعَ لَكُم مِّنَ ٱلدِّينِ مَا وَصَّىٰ بِهِۦ نُوحٗا وَٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ وَمَا وَصَّيۡنَا بِهِۦٓ إِبۡرَٰهِيمَ وَمُوسَىٰ وَعِيسَىٰٓۖ أَنۡ أَقِيمُواْ ٱلدِّينَ وَلَا تَتَفَرَّقُواْ فِيهِۚ كَبُرَ عَلَى ٱلۡمُشۡرِكِينَ مَا تَدۡعُوهُمۡ إِلَيۡهِۚ ٱللَّهُ يَجۡتَبِيٓ إِلَيۡهِ مَن يَشَآءُ وَيَهۡدِيٓ إِلَيۡهِ مَن يُنِيبُ
Wakhazikitsa kwa inu chipembedzo chonga chomwe adam’langiza Nuh. Ndipo chimene takuvumbulutsira iwe ndi chimenenso tidavumbulutsira Ibrahim, Mûsa, ndi Isa (Yesu) kuti: Mulimbike chipembedzo (potsatira malamulo) ndikuti musalekane pa chipembedzo. Koma ndizovuta kwa opembedza mafano (kuvomera) zimene ukuwaitanira. Allah amadzisankhira amene wam’funa ndipo amamuongolera amene akutembenukira kwa Iye.
阿拉伯语经注:
وَمَا تَفَرَّقُوٓاْ إِلَّا مِنۢ بَعۡدِ مَا جَآءَهُمُ ٱلۡعِلۡمُ بَغۡيَۢا بَيۡنَهُمۡۚ وَلَوۡلَا كَلِمَةٞ سَبَقَتۡ مِن رَّبِّكَ إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمّٗى لَّقُضِيَ بَيۡنَهُمۡۚ وَإِنَّ ٱلَّذِينَ أُورِثُواْ ٱلۡكِتَٰبَ مِنۢ بَعۡدِهِمۡ لَفِي شَكّٖ مِّنۡهُ مُرِيبٖ
Ndipo sadagawikane (pa chipembedzo otsatira a aneneri oyamba) kufikira pamene kudawadzera kudziwa kwa choonadi, chifukwa chachidani ndi dumbo pakati pawo. Kukadapanda liwu lochokera kwa Mbuye wako pachiyambi (lowachedwetsera chilango) mpaka nthawi yoikidwa kukadaweruzidwa pakati pawo koma ndithu amene adalandira buku pambuyo pawo (makolo awo, ndipo ndikukumana ndi nthawi yako,) ali mchikaiko cholikaikira (buku lawo).
阿拉伯语经注:
فَلِذَٰلِكَ فَٱدۡعُۖ وَٱسۡتَقِمۡ كَمَآ أُمِرۡتَۖ وَلَا تَتَّبِعۡ أَهۡوَآءَهُمۡۖ وَقُلۡ ءَامَنتُ بِمَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ مِن كِتَٰبٖۖ وَأُمِرۡتُ لِأَعۡدِلَ بَيۡنَكُمُۖ ٱللَّهُ رَبُّنَا وَرَبُّكُمۡۖ لَنَآ أَعۡمَٰلُنَا وَلَكُمۡ أَعۡمَٰلُكُمۡۖ لَا حُجَّةَ بَيۡنَنَا وَبَيۡنَكُمُۖ ٱللَّهُ يَجۡمَعُ بَيۡنَنَاۖ وَإِلَيۡهِ ٱلۡمَصِيرُ
(Chifukwa cha umodzi wa zipembedzo ndikuti pasakhale kugawikana pa chipembedzo) choncho aitanire (ku chipembedzo chimodzi); ndipo lungama (poitanapo) monga momwe walamulidwira. Ndipo usatsatire zofuna zawo. Ndipo nena: “Ndakhulupirira mmabuku onse omwe adawavumbulutsa Allah; ndipo ndalamulidwa kuchita chilungamo pakati panu. Allah ndiye Mbuye wathu ndiponso Mbuye wanu; ife tili ndi ntchito zathu (zomwe tidzalipidwa nazo); inunso muli ndi ntchito zanu (zomwe mudzalipidwa nazo). Palibe kukangana pakati pa ife ndi inu (chifukwa chakuonekera poyera choona). Allah adzatisonkhanitsa (kuti atiweruze); kwa Iye yekha ndiko kobwerera.
阿拉伯语经注:
وَٱلَّذِينَ يُحَآجُّونَ فِي ٱللَّهِ مِنۢ بَعۡدِ مَا ٱسۡتُجِيبَ لَهُۥ حُجَّتُهُمۡ دَاحِضَةٌ عِندَ رَبِّهِمۡ وَعَلَيۡهِمۡ غَضَبٞ وَلَهُمۡ عَذَابٞ شَدِيدٌ
Ndipo amene akutsutsana ndi Allah pambuyo povomerezedwa (ndi anthu ambiri), mtsutso wawo ndiwachabe kwa Mbuye wawo; mkwiyo waukulu (wa Allah) uli pa iwo. Ndipo iwo adzakhala ndi chilango chokhwima.
阿拉伯语经注:
ٱللَّهُ ٱلَّذِيٓ أَنزَلَ ٱلۡكِتَٰبَ بِٱلۡحَقِّ وَٱلۡمِيزَانَۗ وَمَا يُدۡرِيكَ لَعَلَّ ٱلسَّاعَةَ قَرِيبٞ
Allah ndi Amene wavumbulutsa buku (la Qur’an ndi mabuku ena) moona ndi mwachilungamo. Nanga nchiyani chikudziwitse kuti mwina Qiyâma ili pafupi?
阿拉伯语经注:
يَسۡتَعۡجِلُ بِهَا ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِهَاۖ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مُشۡفِقُونَ مِنۡهَا وَيَعۡلَمُونَ أَنَّهَا ٱلۡحَقُّۗ أَلَآ إِنَّ ٱلَّذِينَ يُمَارُونَ فِي ٱلسَّاعَةِ لَفِي ضَلَٰلِۭ بَعِيدٍ
Akuifulumizitsa amene sakuikhulupirira; koma amene akhulupirira ali oopa za iyo, ndipo akudziwa kuti imeneyo ndiyoonadi, (za kupezeka kwake palibe chikaiko). Dziwani kuti ndithu amene akutsutsana za nthawi (ya Qiyâma) ali mkusokera konka nako kutali.
阿拉伯语经注:
ٱللَّهُ لَطِيفُۢ بِعِبَادِهِۦ يَرۡزُقُ مَن يَشَآءُۖ وَهُوَ ٱلۡقَوِيُّ ٱلۡعَزِيزُ
Allah Ngoleza kwa akapolo (Ake). Amapereka rizq kwa amene wamfuna. Ndipo Iye ndi Wamphamvu zoposa, Wopambana.
阿拉伯语经注:
مَن كَانَ يُرِيدُ حَرۡثَ ٱلۡأٓخِرَةِ نَزِدۡ لَهُۥ فِي حَرۡثِهِۦۖ وَمَن كَانَ يُرِيدُ حَرۡثَ ٱلدُّنۡيَا نُؤۡتِهِۦ مِنۡهَا وَمَا لَهُۥ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ مِن نَّصِيبٍ
Amene akufuna (pantchito yake) zokolola za tsiku lachimaliziro, timuonjezera zokolola zakezo; ndipo amene akufuna pa ntchito yake yabwino zokolola za chisangalalo cha m’dziko lapansi timpatsa chimene chidagawidwa kwa iye, ndipo iye sadzakhala ndi gawo (la zabwino) pa tsiku lachimaliziro.
阿拉伯语经注:
أَمۡ لَهُمۡ شُرَكَٰٓؤُاْ شَرَعُواْ لَهُم مِّنَ ٱلدِّينِ مَا لَمۡ يَأۡذَنۢ بِهِ ٱللَّهُۚ وَلَوۡلَا كَلِمَةُ ٱلۡفَصۡلِ لَقُضِيَ بَيۡنَهُمۡۗ وَإِنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ لَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ
Kodi iwo alinayo milungu imene idawakhazikitsira m’zipembedzo zimene Allah sadaziloleze? Ndipo pakadapanda kutsogola (lonjezo lochedwetsa) liwu la chiweruziro (mpaka pa tsiku la Qiyâma); pakadaweruzidwa pakati pawo (okanira ndi okhulupirira pompano pa dziko lapansi). Ndipo ndithu opondereza chawo nchilango chowawa.
阿拉伯语经注:
تَرَى ٱلظَّٰلِمِينَ مُشۡفِقِينَ مِمَّا كَسَبُواْ وَهُوَ وَاقِعُۢ بِهِمۡۗ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فِي رَوۡضَاتِ ٱلۡجَنَّاتِۖ لَهُم مَّا يَشَآءُونَ عِندَ رَبِّهِمۡۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَضۡلُ ٱلۡكَبِيرُ
Udzawaona (tsiku la Qiyâma) amene adadzichitira okha zoipa (popembedza mafano) akuopa chifukwa cha (zoipa) zomwe adachita, ndipo (chilangocho) chidzawapezabe. Koma amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino (udzawaona akusangalala) m’Madimba abwino a ku Minda ya mtendere. Iwo akapeza chilichonse chimene akafune kwa Mbuye wawo. Umenewo ndiwo ulemelero wawukulu.
阿拉伯语经注:
ذَٰلِكَ ٱلَّذِي يُبَشِّرُ ٱللَّهُ عِبَادَهُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِۗ قُل لَّآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ أَجۡرًا إِلَّا ٱلۡمَوَدَّةَ فِي ٱلۡقُرۡبَىٰۗ وَمَن يَقۡتَرِفۡ حَسَنَةٗ نَّزِدۡ لَهُۥ فِيهَا حُسۡنًاۚ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ شَكُورٌ
Umenewu ndi (ulemelero) umene Allah akuwasangalatsira akapolo Ake nkhani yabwino; amene akhulupirira ndi kuchita zabwino. Nena (iwe Mtumiki {s.a.w} kwa iwo): “Sindikupemphani malipiro (kapena chuma) pofikitsa uthenga (kwa inu), koma kuti musunge chikondi pachibale chimene chili pakati pathu. (Musandizunze kufikira ndifikitse kwa inu uthenga wa Mbuye wanga.)” Amene achita chabwino timuonjezera pachabwinocho ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngolandira kuthokoza.
阿拉伯语经注:
أَمۡ يَقُولُونَ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبٗاۖ فَإِن يَشَإِ ٱللَّهُ يَخۡتِمۡ عَلَىٰ قَلۡبِكَۗ وَيَمۡحُ ٱللَّهُ ٱلۡبَٰطِلَ وَيُحِقُّ ٱلۡحَقَّ بِكَلِمَٰتِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ
Kapena akunena kuti: “Wampekera Allah bodza?”Allah akadafuna akadadinda mu mtima mwako (kuti usathe kunena chilichonse; koma kuti chilichonse chimene ukunena chikuchokera kwa Iye). Ndipo Allah amachotsa chabodza (shirik), ndi kuchilimbikitsa choona (Chisilamu), ndi mau Ake (amene adawavumbulutsa kwa Mneneri Wake). Ndithu Iye Ngodziwa (zobisika) za mmitima.
阿拉伯语经注:
وَهُوَ ٱلَّذِي يَقۡبَلُ ٱلتَّوۡبَةَ عَنۡ عِبَادِهِۦ وَيَعۡفُواْ عَنِ ٱلسَّيِّـَٔاتِ وَيَعۡلَمُ مَا تَفۡعَلُونَ
Ndipo Iye (Yekha) ndi amene amalandira kulapa (kuchokera) kwa akapolo Ake. Ndipo amakhululuka machimo (awo); komanso akudziwa zimene mukuchita.
阿拉伯语经注:
وَيَسۡتَجِيبُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَيَزِيدُهُم مِّن فَضۡلِهِۦۚ وَٱلۡكَٰفِرُونَ لَهُمۡ عَذَابٞ شَدِيدٞ
Ndipo Iye (Allah) akuwayankha amene akhulupirira ndi kuchita zabwino; ndi kuwaonjezera ubwino Wake. Ndipo okana, chilango chaukali chili pa iwo.
阿拉伯语经注:
۞ وَلَوۡ بَسَطَ ٱللَّهُ ٱلرِّزۡقَ لِعِبَادِهِۦ لَبَغَوۡاْ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَٰكِن يُنَزِّلُ بِقَدَرٖ مَّا يَشَآءُۚ إِنَّهُۥ بِعِبَادِهِۦ خَبِيرُۢ بَصِيرٞ
Allah akadachulukitsa rizq (chuma) kwa akapolo Ake onse (monga anthuwo akufunira), akadapyola malire poononga pa dziko; koma (Allah) akutsitsa (chumacho) mwamuyeso monga momwe Iye afunira. Ndithu Iye pa za akapolo Ake Ngodziwa, Ngopenya.
阿拉伯语经注:
وَهُوَ ٱلَّذِي يُنَزِّلُ ٱلۡغَيۡثَ مِنۢ بَعۡدِ مَا قَنَطُواْ وَيَنشُرُ رَحۡمَتَهُۥۚ وَهُوَ ٱلۡوَلِيُّ ٱلۡحَمِيدُ
Ndipo Iye yekha ndi amene akutsitsa mvula (pambuyo poti anthu)atataya mtima (pa zamvulayo); ndipo amafalitsa madalitso Ake ndipo ndi Mthandizi Wotamandidwa.
阿拉伯语经注:
وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦ خَلۡقُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَثَّ فِيهِمَا مِن دَآبَّةٖۚ وَهُوَ عَلَىٰ جَمۡعِهِمۡ إِذَا يَشَآءُ قَدِيرٞ
Ndipo zina mwa zisonyezo zake ndi kulenga kwa thambo ndi nthaka, ndi zamoyo zimene wazifalitsa mmenemo (zooneka ndi zosaoneka). Ndipo Iye ndi Wamphamvu zowasonkhanitsira (anthu kuchokera ku imfa) akadzafuna.
阿拉伯语经注:
وَمَآ أَصَٰبَكُم مِّن مُّصِيبَةٖ فَبِمَا كَسَبَتۡ أَيۡدِيكُمۡ وَيَعۡفُواْ عَن كَثِيرٖ
Ndipo mavuto amtundu uliwonse amene akukupezani nchifukwa cha (zochita zoipa) zimene achita manja anu, koma (Allah) akukhululuka zambiri.
阿拉伯语经注:
وَمَآ أَنتُم بِمُعۡجِزِينَ فِي ٱلۡأَرۡضِۖ وَمَا لَكُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ مِن وَلِيّٖ وَلَا نَصِيرٖ
Ndipo simungathe kum’lepheretsa (Allah kukutsitsirani mavuto) padziko lapansi (ngati mutachimwa); ndipo inu mulibenso mthandizi kapena mpulumutsi kupatula Allah.
阿拉伯语经注:
وَمِنۡ ءَايَٰتِهِ ٱلۡجَوَارِ فِي ٱلۡبَحۡرِ كَٱلۡأَعۡلَٰمِ
Ndipo zina mwa zisonyezo Zake ndi zombo zoyenda panyanja zonga mapiri ataliatali (koma osabira).
阿拉伯语经注:
إِن يَشَأۡ يُسۡكِنِ ٱلرِّيحَ فَيَظۡلَلۡنَ رَوَاكِدَ عَلَىٰ ظَهۡرِهِۦٓۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّكُلِّ صَبَّارٖ شَكُورٍ
Atafuna akhoza kuiyimitsa mphepo choncho nkungokhala duu, (osayenda) pamwamba pake (panyanja). Ndithu mzimenezi muli zisonyezo kwa aliyense wopirira ndi wothokoza.
阿拉伯语经注:
أَوۡ يُوبِقۡهُنَّ بِمَا كَسَبُواْ وَيَعۡفُ عَن كَثِيرٖ
Kapena akhoza kuziononga (potumiza mphepo yamkuntho) chifukwa cha machimo amene adawachita. Koma amakhululuka zambiri.
阿拉伯语经注:
وَيَعۡلَمَ ٱلَّذِينَ يُجَٰدِلُونَ فِيٓ ءَايَٰتِنَا مَا لَهُم مِّن مَّحِيصٖ
Ndipo adzadziwa (tsiku la Qiyâma) amene akutsutsana ndi zisonyezo Zathu kuti alibe pothawira (kuchilango cha Allah).
阿拉伯语经注:
فَمَآ أُوتِيتُم مِّن شَيۡءٖ فَمَتَٰعُ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَمَا عِندَ ٱللَّهِ خَيۡرٞ وَأَبۡقَىٰ لِلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَلَىٰ رَبِّهِمۡ يَتَوَكَّلُونَ
Ndipo chilichonse chimene mwapatsidwa, nzosangalatsa za moyo wa pa dziko. Koma zimene zili kwa Allah ndi zabwino ndiponso zamuyaya za amene akhulupirira ndi kutsamira kwa Mbuye wawo.
阿拉伯语经注:
وَٱلَّذِينَ يَجۡتَنِبُونَ كَبَٰٓئِرَ ٱلۡإِثۡمِ وَٱلۡفَوَٰحِشَ وَإِذَا مَا غَضِبُواْ هُمۡ يَغۡفِرُونَ
Ndipo amene akupewa machimo akuluakulu omwe Allah waletsa ndi machimo onse oipitsitsa; ndipo iwo akakwiya (chifukwa choputidwa) iwo amakhululuka;
阿拉伯语经注:
وَٱلَّذِينَ ٱسۡتَجَابُواْ لِرَبِّهِمۡ وَأَقَامُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَأَمۡرُهُمۡ شُورَىٰ بَيۡنَهُمۡ وَمِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ يُنفِقُونَ
Ndipo amene adayankha kuitana kwa Mbuye wawo ndi kusunga mapemphero (popemphera mnthawi yake mkapempheredwe koyenera); ndipo zinthu zawo zonse zimakhala zokambirana pakati pawo; ndipo mzimene tawapatsa amapereka (pa njira ya Allah);
阿拉伯语经注:
وَٱلَّذِينَ إِذَآ أَصَابَهُمُ ٱلۡبَغۡيُ هُمۡ يَنتَصِرُونَ
Ndi amene amati akachitiridwa mtopola amadzipulumutsa.
阿拉伯语经注:
وَجَزَٰٓؤُاْ سَيِّئَةٖ سَيِّئَةٞ مِّثۡلُهَاۖ فَمَنۡ عَفَا وَأَصۡلَحَ فَأَجۡرُهُۥ عَلَى ٱللَّهِۚ إِنَّهُۥ لَا يُحِبُّ ٱلظَّٰلِمِينَ
Malipiro a choipa ndi choipa chonga icho; (wochita choipa alipidwe choipa chonga chimene wachita). Koma amene wakhululukira wochita choipa (pomwe akhoza kubwezera), ndi kuyanjana naye (mdani wakeyo), malipiro ake ali kwa Allah; ndithu Allah sakonda ochitira anzawo mtopola.
阿拉伯语经注:
وَلَمَنِ ٱنتَصَرَ بَعۡدَ ظُلۡمِهِۦ فَأُوْلَٰٓئِكَ مَا عَلَيۡهِم مِّن سَبِيلٍ
Koma amene abwezera pambuyo pakuchitiridwa mtopola, kwa iwo palibe njira yowadzudzulira.
阿拉伯语经注:
إِنَّمَا ٱلسَّبِيلُ عَلَى ٱلَّذِينَ يَظۡلِمُونَ ٱلنَّاسَ وَيَبۡغُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّۚ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ
Ndithu njira yodzudzulidwira ili kwa amene akupondereza anthu ndi kuchita mtopola pa dziko popanda chifukwa choyenera. Iwowo ndi amene adzalandira chilango chowawa.
阿拉伯语经注:
وَلَمَن صَبَرَ وَغَفَرَ إِنَّ ذَٰلِكَ لَمِنۡ عَزۡمِ ٱلۡأُمُورِ
Ndipo amene akupirira ndi kukhululuka, (Allah adzamlipira mphoto yaikulu); ndithu kupirirako ndi chimodzi mwa zinthu zazikulu (chofunika kudzilimbikitsa nacho Msilamu pa chikhalidwe chake.)
阿拉伯语经注:
وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِن وَلِيّٖ مِّنۢ بَعۡدِهِۦۗ وَتَرَى ٱلظَّٰلِمِينَ لَمَّا رَأَوُاْ ٱلۡعَذَابَ يَقُولُونَ هَلۡ إِلَىٰ مَرَدّٖ مِّن سَبِيلٖ
Ndipo amene Allah wamsiya kuti asokere, alibe mthandizi (wina) kupatula Iye (Allah). ndipo udzawaona osalungama pamene adzachiona (masomphenya) chilango, adzanena (modandaula): “Kodi pali njira yobwerera (padziko lapansi kuti tikachite zabwino tidzalowe ku Jannah)?”
阿拉伯语经注:
وَتَرَىٰهُمۡ يُعۡرَضُونَ عَلَيۡهَا خَٰشِعِينَ مِنَ ٱلذُّلِّ يَنظُرُونَ مِن طَرۡفٍ خَفِيّٖۗ وَقَالَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِنَّ ٱلۡخَٰسِرِينَ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ وَأَهۡلِيهِمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۗ أَلَآ إِنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ فِي عَذَابٖ مُّقِيمٖ
Udzawaona (osalungama) akusonyezedwa ku Moto ali okhumata chifukwa chakunyozeka uku akuyang’ana (Moto) mkayang’anidwe kobisa (kotsinzina). Ndipo amene adakhulupirira adzanena pa tsiku la Qiyâma: “Ndithu otaika ndi amene adadzitaya okha pamodzi ndi maanja awo.” Dziwani kuti osalungama adzakhala mchilango chamuyaya.
阿拉伯语经注:
وَمَا كَانَ لَهُم مِّنۡ أَوۡلِيَآءَ يَنصُرُونَهُم مِّن دُونِ ٱللَّهِۗ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِن سَبِيلٍ
Ndipo sadzakhala ndi athangati owapulumutsa (kuchilango cha Moto) kupatula Allah. Ndipo amene Allah wamusiya kuti asokere (chifukwa cha zochita zake zoipa) sangapeze njira (yopezera kulungama.)
阿拉伯语经注:
ٱسۡتَجِيبُواْ لِرَبِّكُم مِّن قَبۡلِ أَن يَأۡتِيَ يَوۡمٞ لَّا مَرَدَّ لَهُۥ مِنَ ٱللَّهِۚ مَا لَكُم مِّن مَّلۡجَإٖ يَوۡمَئِذٖ وَمَا لَكُم مِّن نَّكِيرٖ
Muyankheni Mbuye wanu lisadadze tsiku losapeweka lochokera kwa Allah; tsiku limenelo simudzapeza pothawira, ndipo simudzakhala ndi njira (yokanira zimene mudzachitidwa).
阿拉伯语经注:
فَإِنۡ أَعۡرَضُواْ فَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ عَلَيۡهِمۡ حَفِيظًاۖ إِنۡ عَلَيۡكَ إِلَّا ٱلۡبَلَٰغُۗ وَإِنَّآ إِذَآ أَذَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِنَّا رَحۡمَةٗ فَرِحَ بِهَاۖ وَإِن تُصِبۡهُمۡ سَيِّئَةُۢ بِمَا قَدَّمَتۡ أَيۡدِيهِمۡ فَإِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ كَفُورٞ
Ngati anyalanyaza (Allah awalanga) sitidakutume kwa iwo kukhala muyang’aniri. Udindo wako ndikufalitsa uthenga. Ndipo ndithu tikamulawitsa munthu mtendere wochokera kwa Ife, akuunyadira (modzikweza), koma choipa chikawapeza kupyolera mzoipa zimene manja awo adatsogoza, pompo munthuyo sathokoza (Allah).
阿拉伯语经注:
لِّلَّهِ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ يَخۡلُقُ مَا يَشَآءُۚ يَهَبُ لِمَن يَشَآءُ إِنَٰثٗا وَيَهَبُ لِمَن يَشَآءُ ٱلذُّكُورَ
Ufumu wakumwamba ndi pa dziko lapansi ngwa Allah; amalenga zimene wafuna; amene wam’funa amampatsa ana achikazi (okhaokha) ndiponso amene wamfuna amampatsa ana achimuna (okhaokha).
阿拉伯语经注:
أَوۡ يُزَوِّجُهُمۡ ذُكۡرَانٗا وَإِنَٰثٗاۖ وَيَجۡعَلُ مَن يَشَآءُ عَقِيمًاۚ إِنَّهُۥ عَلِيمٞ قَدِيرٞ
Kapena kuphatikiza (ana) achimuna ndi achikazi, ndipo amene wam’funa amamchita kukhala chumba. Ndithu Iye Ngodziwa, Wokhoza (chilichonse).
阿拉伯语经注:
۞ وَمَا كَانَ لِبَشَرٍ أَن يُكَلِّمَهُ ٱللَّهُ إِلَّا وَحۡيًا أَوۡ مِن وَرَآيِٕ حِجَابٍ أَوۡ يُرۡسِلَ رَسُولٗا فَيُوحِيَ بِإِذۡنِهِۦ مَا يَشَآءُۚ إِنَّهُۥ عَلِيٌّ حَكِيمٞ
Nkosayenera kwa munthu kuti Allah alankhule naye koma kupyolera mkumzindikiritsa, kapena kuchokera kuseri kwa chotsekereza, kapena pomtuma mtumiki (Jiburil) kuti amvumbulutsire zimene Iye akufuna mwa chilolezo Chake. Ndithu Iye Ngwapamwamba, Ngwanzeru zakuya.
阿拉伯语经注:
وَكَذَٰلِكَ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ رُوحٗا مِّنۡ أَمۡرِنَاۚ مَا كُنتَ تَدۡرِي مَا ٱلۡكِتَٰبُ وَلَا ٱلۡإِيمَٰنُ وَلَٰكِن جَعَلۡنَٰهُ نُورٗا نَّهۡدِي بِهِۦ مَن نَّشَآءُ مِنۡ عِبَادِنَاۚ وَإِنَّكَ لَتَهۡدِيٓ إِلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
Momwemonso takuvumbulutsira chivumbulutso (Chathu) mwa lamulo Lathu. Siudali kudziwa kuti buku ndi chiyani, chikhulupiliro ndi chiyani; koma bukuli (Qur’an) talichita kukhala kuunika; ndi kuunikaku tikumuongola amene tam’funa mwa akapolo Athu. Ndithu iwe ukuongolera kunjira yoongoka.
阿拉伯语经注:
صِرَٰطِ ٱللَّهِ ٱلَّذِي لَهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۗ أَلَآ إِلَى ٱللَّهِ تَصِيرُ ٱلۡأُمُورُ
Njira ya Allah Amene zonse za kumwamba ndi za mdziko lapansi ndi Zake. Dziwani kuti zinthu zonse zimabwerera kwa Allah.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 舒拉
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 译解目录

古兰经契瓦文译解,哈利德·伊布拉欣·比德拉翻译,2020年版

关闭