Ndithu takugonjetsera (iwe Mtumiki{s.a.w}mzinda wa Makka) kugonjetsa kwakukulu koonekera poyera.[346]
[346] M’chaka cha chisanu ndi chimodzi chisamukire Mtumiki (s.a.w), Mtumiki (s.a.w) adapita ku Makka kuchokera ku Madina pamodzi ndi omtsatira ake kuti akachite Umrah imene ndi Hajj yaing’ono. Koma atayandikira ku Makka, Aquraish adamuletsa kulowa mu mzindamo kuti asachite mapemphero a Umrah. Ndipo atakambiranakambirana adamvana mfundo zingapo, zina mwa izo ndi:-
(i) Asamenyane nthawi imeneyo.
(ii) Abwelere ndipo adzabwere chaka chotsatiracho mwezi wonga umenewo kudzachita mapemphero. Panthawiyo sadzawaletsa kulowa mu mzindawo.
(iii) Asiye kumenyana pakati pawo kwa zaka khumi, ndi kumayenderana m’mene angafunire; Aquraish azipita ku Madina ngati atafuna, popanda kuzunzidwa.
(iv) Mafuko ena a Arabu adaloledwa kulowa nawo m’pangano limeneli kuti asamthire nkhondo Mtumiki (s.a.w), ndipo iyenso asawathire nkhondo.
Ndi kuti awalange achiphamaso aamuna ndi aakazi ndi omphatikiza Allah aamuna ndi aakazi oganizira Allah maganizo achabe. Kutembenuka koipa kuli kwa iwo ndipo Allah wawakwiyira ndiponso wawatembelera ndi kuwakonzera Jahannamu. Ndipo kumeneko nkobwerera koipa.
Ncholinga choti mumkhulupirire Allah ndi Mtumiki Wake, ndi kuti mumtukule ndi kumulemekeza (Mtumiki) ndi kutinso mumtamande (Allah) m’mawa ndi madzulo.
Ndithu amene akukulonjeza, ndiye kuti akulonjeza Allah. Dzanja la Allah lili pamwamba pa manja awo. Amene ati aswe lonjezo, ndiye kuti wadziswera yekha (mavuto ali pa iye). Koma yemwe akwaniritse zomwe adalonjeza kwa Allah, amulipira malipiro aakulu.
Adzanena kwa iwe Arabu am’midzi otsala (ku nkhondo, amene adalibe zifukwa zomveka m’kutsala kwawo): “Chuma ndi ana athu zidatitangwanitsa; choncho tipemphereni chikhululuko.” Akunena ndi malirime awo (mawu) omwe m’mitima mwawo mulibe. Nena: “Kodi ndani angathe kukuthandizani chilichonse kwa Allah ngati atafuna kukupatsani masautso, kapena atafuna kukupatsani zabwino? Koma Allah Akudziwa zonse zimene mukuchita.”
Nena kwa otsala (kunkhondo) mwa Arabu a m’midzi: “Mudzaitanidwa (kukamenyana) ndi anthu eni mphamvu zaukali; mudzamenyana nawo kapena adzagonja (ndi kulowa m’Chisilamu). Ngati mudzamvera, Allah adzakulipirani malipiro abwino, koma ngati mutembenuka monga mudatembenukira kale adzakulangani ndi chilango chowawa.”
Ndipo Iye ndi amene adatsekereza manja awo pa inu; ndi manja anu pa iwo, pa chigwa cha Makka, pambuyo pokupambanitsani pa iwo. Ndipo Allah akuona zonse zimene mukuchita.
Pamene omwe sadakhulupirire adaika mkwiyo m’mitima, mkwiyo waumbuli, Allah adatsitsa chikhazikiko Chake ndi kudekha pa Mtumiki Wake ndi pa okhulupirira, ndipo adawalimbikitsa ndi mawu woopa Allah; ndipo adali eni mawuwo ndi oyenerana nawo. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse.
Iye ndi Yemwe adatumiza Mtumiki Wake ndi chiongoko ndi chipembedzo choona kuti achiike pamwamba pa zipembedzo zonse. Ndipo Allah akukwanira kukhala mboni (yake).
Muhammad (s.a.w) ndi Mtumiki wa Allah; ndipo amene ali pamodzi ndi iye ngamphamvu kwa osakhulupirira (Allah), ngachifundo chambiri pakati pawo. Uwaona akugwira m’maondo ndi kugwetsa nkhope zawo pansi ncholinga chofuna zabwino za Allah ndi chikondi (Chake). Zizindikiro zawo zili pa nkhope zawo zosonyeza kulambira kwawo. Ili ndi fanizo lawo m’Chipangano chakale, Ndipo fanizo lawo m’Chipangano chatsopano nkuti iwo ali monga mmera womwe watulutsa nthambi zake; kenako (nthambizo) nkuulimbitsa ndi kukhala waukulu ndi kuima bwinobwino ndi tsinde lake, nkuwasangalatsa omwe adaubzala. (Choncho) zotsatira zake, nkuwakwiyitsa osakhulupirira chifukwa cha iwo. Allah walonjeza chikhululuko ndi malipiro aakulu (kwa) amene akhulupirira ndi kuchita zabwino mwa iwo.
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
搜索结果:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".