Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 玛仪戴   段:
قَالُواْ يَٰمُوسَىٰٓ إِنَّا لَن نَّدۡخُلَهَآ أَبَدٗا مَّا دَامُواْ فِيهَا فَٱذۡهَبۡ أَنتَ وَرَبُّكَ فَقَٰتِلَآ إِنَّا هَٰهُنَا قَٰعِدُونَ
(Iwo) adati: “Iwe Mûsa, ife sitikalowamo mpang’ono pomwe, pomwe iwo ali momwemo. Choncho pita iwe ndi Mbuye wako, ukamenyane nawo; ife tikhala pompano.”
阿拉伯语经注:
قَالَ رَبِّ إِنِّي لَآ أَمۡلِكُ إِلَّا نَفۡسِي وَأَخِيۖ فَٱفۡرُقۡ بَيۡنَنَا وَبَيۡنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلۡفَٰسِقِينَ
(Mûsa) adati: “E Mbuye wanga! Ndithudi, ine ndilibe nyonga (yokakamizira aliyense kutsatira lamulo Lanu) koma pa ine ndekha ndi pa m’bale wanga. Choncho tisiyanitseni ndi anthu awa opandukira chilamulo.”
阿拉伯语经注:
قَالَ فَإِنَّهَا مُحَرَّمَةٌ عَلَيۡهِمۡۛ أَرۡبَعِينَ سَنَةٗۛ يَتِيهُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِۚ فَلَا تَأۡسَ عَلَى ٱلۡقَوۡمِ ٱلۡفَٰسِقِينَ
Allah adati: “Choncho laletsedwa dzikolo kwa iwo kulilowa kwa zaka makumi anayi. Akhala akuyendayenda pa dziko. Tero, usawadandaulire anthu opandukira chilamulo.”
阿拉伯语经注:
۞ وَٱتۡلُ عَلَيۡهِمۡ نَبَأَ ٱبۡنَيۡ ءَادَمَ بِٱلۡحَقِّ إِذۡ قَرَّبَا قُرۡبَانٗا فَتُقُبِّلَ مِنۡ أَحَدِهِمَا وَلَمۡ يُتَقَبَّلۡ مِنَ ٱلۡأٓخَرِ قَالَ لَأَقۡتُلَنَّكَۖ قَالَ إِنَّمَا يَتَقَبَّلُ ٱللَّهُ مِنَ ٱلۡمُتَّقِينَ
Ndipo awerengere nkhani mwachoonadi ya ana awiri a Adam, pamene adapereka nsembe. Ndipo idalandiridwa ya mmodzi wawo, koma ya winayo siidalandiridwe. (Amene nsembe yake siidalandiridwe) adati (kwa mnzake): “Ndithudi ndikupha.” Mnzakeyo adati: “Ndithudi, Allah amalandira nsembe ya amene akuopa (Allah).”[163]
[163] Iyi ndinkhani yoyamba ya munthu wopha mnzake. Ndipo amene adaphedwayu ndiye munthu woyamba kulawa imfa. Wopha mnzakeyo ataona kuti mnzake wafadi, iye adangoti kakasi, kusowa chochita naye. Tero adangomsenza kumsana nkumangozungilirazungulira naye, kuopa kubwera naye kunyumba kuti anzake angamdziwe kuti ndiye wamupha. Makolo awo adali Adam ndi Hava. Mwamwayi, khwangwala adatulukira nayamba kumenyana ndimnzake mpaka kumupha. Kenako namkwilira m’nthaka. Tsono naye uja wopha mnzake adatsanzira zomwe khwangwala adachita. Nakumba dzenje nkukwilira mnzakeyo. N.B! Munthu ncholengedwa chomalizira kudza pa dziko. Zidamtsogolera zolengedwa zonse ndi zaka miyandamiyanda.
阿拉伯语经注:
لَئِنۢ بَسَطتَ إِلَيَّ يَدَكَ لِتَقۡتُلَنِي مَآ أَنَا۠ بِبَاسِطٖ يَدِيَ إِلَيۡكَ لِأَقۡتُلَكَۖ إِنِّيٓ أَخَافُ ٱللَّهَ رَبَّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
“Ngati utambasula dzanja lako pa ine kuti undiphe, ine sinditambasula dzanja langa pa iwe kuti ndikuphe. Ndithudi, ine ndikuopa Allah Mbuye wa zolengedwa.”
阿拉伯语经注:
إِنِّيٓ أُرِيدُ أَن تَبُوٓأَ بِإِثۡمِي وَإِثۡمِكَ فَتَكُونَ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلنَّارِۚ وَذَٰلِكَ جَزَٰٓؤُاْ ٱلظَّٰلِمِينَ
“Ine ndikufuna kuti usenze machimo anga pamodzi ndi machimo ako, choncho ukakhale m’gulu la anthu a ku Moto. Ndipo awo ndio malipiro a anthu ochita zoipa.”
阿拉伯语经注:
فَطَوَّعَتۡ لَهُۥ نَفۡسُهُۥ قَتۡلَ أَخِيهِ فَقَتَلَهُۥ فَأَصۡبَحَ مِنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ
Choncho mtima wake udamkometsera kupha m’bale wake, ndipo adamuphadi. Tero adali wotaika.
阿拉伯语经注:
فَبَعَثَ ٱللَّهُ غُرَابٗا يَبۡحَثُ فِي ٱلۡأَرۡضِ لِيُرِيَهُۥ كَيۡفَ يُوَٰرِي سَوۡءَةَ أَخِيهِۚ قَالَ يَٰوَيۡلَتَىٰٓ أَعَجَزۡتُ أَنۡ أَكُونَ مِثۡلَ هَٰذَا ٱلۡغُرَابِ فَأُوَٰرِيَ سَوۡءَةَ أَخِيۖ فَأَصۡبَحَ مِنَ ٱلنَّٰدِمِينَ
Pamenepo Allah adatumiza khwangwala yemwe amafukula pansi kuti amusonyeze mmene angakwililire mtembo wa m’bale wake. (Wopha mnzake) adati: “Kalanga ine! Ndalephera kuti ndifanane ndi khwangwala uyu, kuti ndikwilire mtembo wa m’bale wanga.” Choncho adali mmodzi mwa odzinena.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 玛仪戴
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭