Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 拉哈迈尼   段:

Ar-Rahmân

ٱلرَّحۡمَٰنُ
(Allah) Wachifundo chochuluka!
阿拉伯语经注:
عَلَّمَ ٱلۡقُرۡءَانَ
Waphunzitsa Qur’an.
阿拉伯语经注:
خَلَقَ ٱلۡإِنسَٰنَ
Adalenga munthu.
阿拉伯语经注:
عَلَّمَهُ ٱلۡبَيَانَ
Adamphunzitsa kuyankhula.
阿拉伯语经注:
ٱلشَّمۡسُ وَٱلۡقَمَرُ بِحُسۡبَانٖ
Dzuwa ndi mwezi zikuyenda mwachiwerengero.
阿拉伯语经注:
وَٱلنَّجۡمُ وَٱلشَّجَرُ يَسۡجُدَانِ
Zomera zopanda tsinde ndi mitengo, zikulambira (Allah pachilichonse chimene wafuna mwa izo).
阿拉伯语经注:
وَٱلسَّمَآءَ رَفَعَهَا وَوَضَعَ ٱلۡمِيزَانَ
Ndipo thambo adalitukula kumwamba ndipo adakhazikitsa sikelo (ya chilungamo).
阿拉伯语经注:
أَلَّا تَطۡغَوۡاْ فِي ٱلۡمِيزَانِ
Kuti musapyole malire ndi kuchita chinyengo poyesa.
阿拉伯语经注:
وَأَقِيمُواْ ٱلۡوَزۡنَ بِٱلۡقِسۡطِ وَلَا تُخۡسِرُواْ ٱلۡمِيزَانَ
Choncho yesani sikelo mwachilungamo ndipo musapungule muyeso.
阿拉伯语经注:
وَٱلۡأَرۡضَ وَضَعَهَا لِلۡأَنَامِ
Ndipo nthaka adaiyala (ndi kuikonza) kuti ikhale ya zolengedwa.
阿拉伯语经注:
فِيهَا فَٰكِهَةٞ وَٱلنَّخۡلُ ذَاتُ ٱلۡأَكۡمَامِ
M’menemo muli zipatso ndi mitengo ya kanjedza yokhala ndi mapava (a zipatso).
阿拉伯语经注:
وَٱلۡحَبُّ ذُو ٱلۡعَصۡفِ وَٱلرَّيۡحَانُ
Ndi mbewu zamakoko (kuti chikhale chakudya cha inu ndi ziweto zanu), ndipo mulinso m’menemo mmera wafungo labwino.
阿拉伯语经注:
فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
阿拉伯语经注:
خَلَقَ ٱلۡإِنسَٰنَ مِن صَلۡصَٰلٖ كَٱلۡفَخَّارِ
Adalenga munthu kuchokera ku dongo lolira monga ziwiya zadongo.
阿拉伯语经注:
وَخَلَقَ ٱلۡجَآنَّ مِن مَّارِجٖ مِّن نَّارٖ
Ndipo adalenga ziwanda kuchokera ku malawi a moto (wopanda utsi.)
阿拉伯语经注:
فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
阿拉伯语经注:
رَبُّ ٱلۡمَشۡرِقَيۡنِ وَرَبُّ ٱلۡمَغۡرِبَيۡنِ
Mbuye wa kuvuma kuwiri ndiponso Mbuye wa kuzambwe kuwiri.
阿拉伯语经注:
فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ
(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?)
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 拉哈迈尼
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭