Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 艾奈尔姆   段:
وَقَالُواْ هَٰذِهِۦٓ أَنۡعَٰمٞ وَحَرۡثٌ حِجۡرٞ لَّا يَطۡعَمُهَآ إِلَّا مَن نَّشَآءُ بِزَعۡمِهِمۡ وَأَنۡعَٰمٌ حُرِّمَتۡ ظُهُورُهَا وَأَنۡعَٰمٞ لَّا يَذۡكُرُونَ ٱسۡمَ ٱللَّهِ عَلَيۡهَا ٱفۡتِرَآءً عَلَيۡهِۚ سَيَجۡزِيهِم بِمَا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ
Iwo akuti: “Ziweto izi ndi mbewu izi, nzoletsedwa; palibe angazidye koma amene tawafuna (kuti adye),” zonsezi mkuyankhula kwawo kwachabe. Ndipo (amanenanso): “Ziweto izi, misana yake njoletsedwa (kukwerapo).” Ndipo pa ziweto zina satchula dzina la Allah pozizinga; kungompekera bodza Iye. Ndipo posachedwa adzawalipira pa zomwe adali kupeka.
阿拉伯语经注:
وَقَالُواْ مَا فِي بُطُونِ هَٰذِهِ ٱلۡأَنۡعَٰمِ خَالِصَةٞ لِّذُكُورِنَا وَمُحَرَّمٌ عَلَىٰٓ أَزۡوَٰجِنَاۖ وَإِن يَكُن مَّيۡتَةٗ فَهُمۡ فِيهِ شُرَكَآءُۚ سَيَجۡزِيهِمۡ وَصۡفَهُمۡۚ إِنَّهُۥ حَكِيمٌ عَلِيمٞ
Ndipo amanenanso: “Zimene zili m’mimba mwa ziweto izi, ndi za amuna okha; ndipo nzoletsedwa kwa akazi athu.” Koma ngati chili chibudu, onse adali kugawana (amuna ndi akazi). Ndithudi, adzawalipira ndi zonena zawozo. Ndithu Iye (Allah), Ngwanzeru zakuya, Wodziwa kwambiri.
阿拉伯语经注:
قَدۡ خَسِرَ ٱلَّذِينَ قَتَلُوٓاْ أَوۡلَٰدَهُمۡ سَفَهَۢا بِغَيۡرِ عِلۡمٖ وَحَرَّمُواْ مَا رَزَقَهُمُ ٱللَّهُ ٱفۡتِرَآءً عَلَى ٱللَّهِۚ قَدۡ ضَلُّواْ وَمَا كَانُواْ مُهۡتَدِينَ
Ndithu adaluza amene adapha ana awo mwa umbuli popanda kudziwa, ndi kuletsa (chakudya) chimene Allah awapatsa, pakungompekera bodza Allah. Ndithu adasokera ndipo sadali oongoka.
阿拉伯语经注:
۞ وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَنشَأَ جَنَّٰتٖ مَّعۡرُوشَٰتٖ وَغَيۡرَ مَعۡرُوشَٰتٖ وَٱلنَّخۡلَ وَٱلزَّرۡعَ مُخۡتَلِفًا أُكُلُهُۥ وَٱلزَّيۡتُونَ وَٱلرُّمَّانَ مُتَشَٰبِهٗا وَغَيۡرَ مُتَشَٰبِهٖۚ كُلُواْ مِن ثَمَرِهِۦٓ إِذَآ أَثۡمَرَ وَءَاتُواْ حَقَّهُۥ يَوۡمَ حَصَادِهِۦۖ وَلَا تُسۡرِفُوٓاْۚ إِنَّهُۥ لَا يُحِبُّ ٱلۡمُسۡرِفِينَ
Ndipo Iye (Allah) ndi amene adapanga minda (ya mitengo) yothaza ndi yosathaza; ndipo (adapanga) mitengo yakanjedza ndi mmera wazipatso zosiyanasiyana makomedwe ake ndipo adapanganso mzitona ndi makomamanga, zofanana (mmaonekedwe) ndi zosiyana (mmakomemedwe). Idyani zipatso zake pamene zikupatsa. Ndipo perekani chopereka chake tsiku lokolola (powapatsa masikini ndi ogundizana nawo nyumba). Ndipo musaziononge pakudya mopyoza muyeso. Ndithu Iye (Allah) sakonda opyoza muyeso.
阿拉伯语经注:
وَمِنَ ٱلۡأَنۡعَٰمِ حَمُولَةٗ وَفَرۡشٗاۚ كُلُواْ مِمَّا رَزَقَكُمُ ٱللَّهُ وَلَا تَتَّبِعُواْ خُطُوَٰتِ ٱلشَّيۡطَٰنِۚ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوّٞ مُّبِينٞ
Ndipo m’gulu la nyama, (Allah adalenga) zonyamulira katundu ndi zopangira choyala (bweya bwake). Idyani zimene Allah wakupatsani ndipo musatsate mapazi a satana (ndi abwenzi ake pozichita halali kapena haramu zomwe Allah sadalamule. Satana sakufunirani zabwino); ndithu iye ndi mdani wanu woonekera.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 艾奈尔姆
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭