Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 艾奈尔姆   段:
وَلَا تَقۡرَبُواْ مَالَ ٱلۡيَتِيمِ إِلَّا بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ حَتَّىٰ يَبۡلُغَ أَشُدَّهُۥۚ وَأَوۡفُواْ ٱلۡكَيۡلَ وَٱلۡمِيزَانَ بِٱلۡقِسۡطِۖ لَا نُكَلِّفُ نَفۡسًا إِلَّا وُسۡعَهَاۖ وَإِذَا قُلۡتُمۡ فَٱعۡدِلُواْ وَلَوۡ كَانَ ذَا قُرۡبَىٰۖ وَبِعَهۡدِ ٱللَّهِ أَوۡفُواْۚ ذَٰلِكُمۡ وَصَّىٰكُم بِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَذَكَّرُونَ
“Ndipo musachiyandikire chuma cha mwana wamasiye, koma m’njira yabwino (monga kuchichulukitsa ndi malonda) mpaka afike pansinkhu wokwanira. Ndipo kwaniritsani mwachilungamo miyeso ya mbale ndi masikelo; sitikakamiza munthu koma chimene angathe; ndipo pamene mukunena, (popereka umboni), nenani mwachilungamo ngakhale (umboniwo) uli wokhudza achibale. Ndipo kwaniritsani lonjezo la Allah. Izi ndi zomwe akukulangizani kuti mukumbukire.”
阿拉伯语经注:
وَأَنَّ هَٰذَا صِرَٰطِي مُسۡتَقِيمٗا فَٱتَّبِعُوهُۖ وَلَا تَتَّبِعُواْ ٱلسُّبُلَ فَتَفَرَّقَ بِكُمۡ عَن سَبِيلِهِۦۚ ذَٰلِكُمۡ وَصَّىٰكُم بِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَتَّقُونَ
(Auze kuti): “Ndithu iyi ndi njira yanga yoongoka. Choncho itsateni. Ndipo musatsate njira zina zambiri kuopera kuti zingakulekanitseni ndi njira Yake, (Allah) wakulangizani izi kuti mudziteteze kuzoipa.”
阿拉伯语经注:
ثُمَّ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ تَمَامًا عَلَى ٱلَّذِيٓ أَحۡسَنَ وَتَفۡصِيلٗا لِّكُلِّ شَيۡءٖ وَهُدٗى وَرَحۡمَةٗ لَّعَلَّهُم بِلِقَآءِ رَبِّهِمۡ يُؤۡمِنُونَ
Ndipo Mûsa tidampatsa buku (kukhala) lokwaniritsa (chisomo) kwa yemwe wachita zabwino, lofotokoza chinthu chilichonse, chiongoko ndi chifundo, kuti iwo akhulupirire za kukumana ndi Mbuye wawo.
阿拉伯语经注:
وَهَٰذَا كِتَٰبٌ أَنزَلۡنَٰهُ مُبَارَكٞ فَٱتَّبِعُوهُ وَٱتَّقُواْ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ
Ndipo iyi (Qur’an) ndi buku lodalitsika lomwe talivumbulutsa (kwa inu), choncho, litsateni ndi kuopa (Allah) kuti muchitiridwe chifundo;
阿拉伯语经注:
أَن تَقُولُوٓاْ إِنَّمَآ أُنزِلَ ٱلۡكِتَٰبُ عَلَىٰ طَآئِفَتَيۡنِ مِن قَبۡلِنَا وَإِن كُنَّا عَن دِرَاسَتِهِمۡ لَغَٰفِلِينَ
Kuti musadzanene (tsiku la Qiyâma) kuti: “Mabuku adavumbulutsidwa pa magulu awiri omwe adalipo patsogolo pathu, (Ayuda ndi Akhrisitu); ndipo ife sitidadziwe chilichonse pa zomwe adali kuwerenga ndi kuphunzira.”
阿拉伯语经注:
أَوۡ تَقُولُواْ لَوۡ أَنَّآ أُنزِلَ عَلَيۡنَا ٱلۡكِتَٰبُ لَكُنَّآ أَهۡدَىٰ مِنۡهُمۡۚ فَقَدۡ جَآءَكُم بَيِّنَةٞ مِّن رَّبِّكُمۡ وَهُدٗى وَرَحۡمَةٞۚ فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن كَذَّبَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَصَدَفَ عَنۡهَاۗ سَنَجۡزِي ٱلَّذِينَ يَصۡدِفُونَ عَنۡ ءَايَٰتِنَا سُوٓءَ ٱلۡعَذَابِ بِمَا كَانُواْ يَصۡدِفُونَ
Kapena kuti musadzati: “Likadavumbulutsidwa buku kwa ife, ndithudi, tikadakhala oongoka kuposa iwo.” Choncho, chakudzerani chizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu, ndi chiongoko ndi mtendere. Kodi ndani woipitsitsa kwambiri kuposa amene watsutsa zizindikiro za Allah ndi kutembenukira kutali Nazo? Tidzawalipira amene akutembenukira kutali ndi zizindikiro zathu, chilango choipa, chifukwa cha kudziika kwawo kutali.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 艾奈尔姆
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭