Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 艾尔拉夫   段:
قَالَا رَبَّنَا ظَلَمۡنَآ أَنفُسَنَا وَإِن لَّمۡ تَغۡفِرۡ لَنَا وَتَرۡحَمۡنَا لَنَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ
Iwo (Adam ndi mkazi wake) adati (modzichepetsa): “E Mbuye wathu! Tadzichitira tokha zoipa, ngati simutikhululukira ndi kuchita nafe chifundo ndiye kuti tikhala mwa otaika.”
阿拉伯语经注:
قَالَ ٱهۡبِطُواْ بَعۡضُكُمۡ لِبَعۡضٍ عَدُوّٞۖ وَلَكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُسۡتَقَرّٞ وَمَتَٰعٌ إِلَىٰ حِينٖ
(Allah) adati: “Tsikani pansi uku pali chidani pakati panu. Ndipo padziko lapansi ndipokhala panu ndi kusangalala kwanu mpaka m’nthawi yoikidwayo.”
阿拉伯语经注:
قَالَ فِيهَا تَحۡيَوۡنَ وَفِيهَا تَمُوتُونَ وَمِنۡهَا تُخۡرَجُونَ
(Allah) adatinso: “Muzikakhala moyo pamenepo, ndipo muzikafa pamenepo; ndipo momwemo mudzatulutsidwa (mutauka kwa akufa).”
阿拉伯语经注:
يَٰبَنِيٓ ءَادَمَ قَدۡ أَنزَلۡنَا عَلَيۡكُمۡ لِبَاسٗا يُوَٰرِي سَوۡءَٰتِكُمۡ وَرِيشٗاۖ وَلِبَاسُ ٱلتَّقۡوَىٰ ذَٰلِكَ خَيۡرٞۚ ذَٰلِكَ مِنۡ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ لَعَلَّهُمۡ يَذَّكَّرُونَ
E inu ana a Adam! Ndithu tatsitsa kwa inu chovala chobisa umaliseche wanu ndi chodzikongoletsera nacho. Koma chovala choopa nacho Allah (pakudziyeretsa ku zoletsedwa) chimenecho ndicho chabwino koposa. Zimenezo ndi zizindikiro za (chisomo cha) Allah kuti iwo akumbukire.[180]
[180] Allah akutiuza kuti tivale nsalu zomwe Allah adatipangira kuti zikongoletse matupi athu. Komatu akutilamulanso kuti tivale nsalu zokongoletsa mitima yathu; nsalu yomwe njotsatira nayo malamulo a Allah ndi kusiya zomwe Iye waletsa; ndi kuchita zokhazo zomwe Allah walamula. Nsalu imeneyi ndi “takuwa” (kuopa Allah). Sibwino kukongoletsa kunja kwa thupi kokha pomwe mu mtima mwadzaza zauve.
阿拉伯语经注:
يَٰبَنِيٓ ءَادَمَ لَا يَفۡتِنَنَّكُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ كَمَآ أَخۡرَجَ أَبَوَيۡكُم مِّنَ ٱلۡجَنَّةِ يَنزِعُ عَنۡهُمَا لِبَاسَهُمَا لِيُرِيَهُمَا سَوۡءَٰتِهِمَآۚ إِنَّهُۥ يَرَىٰكُمۡ هُوَ وَقَبِيلُهُۥ مِنۡ حَيۡثُ لَا تَرَوۡنَهُمۡۗ إِنَّا جَعَلۡنَا ٱلشَّيَٰطِينَ أَوۡلِيَآءَ لِلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ
E inu ana a Adam! Satana asakusokonezeni monga momwe adawatulutsira makolo anu m’Munda wamtendere ndi kuwavula onse awiri chovala chawo kuti awasonyeze umaliseche wawo. Ndithu iye ndi mtundu wake akukuonani pomwe inu simukuwaona. Ndithu asatana tawachita kukhala abwenzi a osakhulupirira.
阿拉伯语经注:
وَإِذَا فَعَلُواْ فَٰحِشَةٗ قَالُواْ وَجَدۡنَا عَلَيۡهَآ ءَابَآءَنَا وَٱللَّهُ أَمَرَنَا بِهَاۗ قُلۡ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَأۡمُرُ بِٱلۡفَحۡشَآءِۖ أَتَقُولُونَ عَلَى ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ
Ndipo (osakhulupirira) akachita chauve amanena: “(Ichi) tidawapeza nacho makolo athu (akuchichita), ndiponso Allah watilamula chimenechi.” Nena: “Ndithu Allah salamula zonyansa. Kodi mukumunenera Allah zomwe simukuzidziwa?”
阿拉伯语经注:
قُلۡ أَمَرَ رَبِّي بِٱلۡقِسۡطِۖ وَأَقِيمُواْ وُجُوهَكُمۡ عِندَ كُلِّ مَسۡجِدٖ وَٱدۡعُوهُ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَۚ كَمَا بَدَأَكُمۡ تَعُودُونَ
Nena: “Mbuye wanga walamula chilungamo; ndiponso (wandiuza kuti ndikuuzeni kuti) lungamitsani nkhope zanu (kwa Iye) m’nthawi ya Swala iliyonse, ndipo mpembedzeni Iye Yekha momuyeretsera chipembedzo monga Iye adakulengani pachiyambi, momwemonso mudzabwerera kwa Iye.”
阿拉伯语经注:
فَرِيقًا هَدَىٰ وَفَرِيقًا حَقَّ عَلَيۡهِمُ ٱلضَّلَٰلَةُۚ إِنَّهُمُ ٱتَّخَذُواْ ٱلشَّيَٰطِينَ أَوۡلِيَآءَ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَيَحۡسَبُونَ أَنَّهُم مُّهۡتَدُونَ
Gulu lina waliongola, pomwe gulu lina patsimikizika pa ilo kusokera chifukwa chakuti iwo adasankha asatana kukhala atetezi (awo) kusiya Allah; ndipo akuganiza kuti iwo ngoongoka.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 艾尔拉夫
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭