Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 穆资米拉   段:

AL-Muzzammil

يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمُزَّمِّلُ
E iwe wadzifunditsa (ndi nsalu!)
阿拉伯语经注:
قُمِ ٱلَّيۡلَ إِلَّا قَلِيلٗا
Imilira usiku (upemphere), kupatula nthawi yochepa.
阿拉伯语经注:
نِّصۡفَهُۥٓ أَوِ ٱنقُصۡ مِنۡهُ قَلِيلًا
Theka lake kapena chepetsa thekalo pang’ono (mpaka ufike chimodzi mwa zigawo zitatu za usiku).
阿拉伯语经注:
أَوۡ زِدۡ عَلَيۡهِ وَرَتِّلِ ٱلۡقُرۡءَانَ تَرۡتِيلًا
Kapena wonjezapo (mpaka ufike zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za usiku;) ndipo werenga Qur’an mofatsa (lemba ndi lemba).
阿拉伯语经注:
إِنَّا سَنُلۡقِي عَلَيۡكَ قَوۡلٗا ثَقِيلًا
Ife tikuvumbulutsira iwe (Mneneri) mawu olemera (yomwe ndi Qur’an).
阿拉伯语经注:
إِنَّ نَاشِئَةَ ٱلَّيۡلِ هِيَ أَشَدُّ وَطۡـٔٗا وَأَقۡوَمُ قِيلًا
Ndithu kudzuka usiku ndi kuchita mapemphero kumalowelera (mu mtima) kwambiri, ndipo zoyankhula zake zimakhala zoongoka ndi zolunjika bwino (kuposa mapemphero amasana).
阿拉伯语经注:
إِنَّ لَكَ فِي ٱلنَّهَارِ سَبۡحٗا طَوِيلٗا
Ndithu masana uli ndi zochitachita zambiri; (umatanganidwa ndi ntchito yauthenga; dzipatse danga usiku polimbika kupemphera).
阿拉伯语经注:
وَٱذۡكُرِ ٱسۡمَ رَبِّكَ وَتَبَتَّلۡ إِلَيۡهِ تَبۡتِيلٗا
Ndipo tchula dzina la Mbuye wako (Amene adalenga ndi kulera zinthu), ndipo udzipereke kwathunthu kwa Iye.
阿拉伯语经注:
رَّبُّ ٱلۡمَشۡرِقِ وَٱلۡمَغۡرِبِ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ فَٱتَّخِذۡهُ وَكِيلٗا
(Iye ndiye) Mbuye wa kuvuma ndi kuzambwe; palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Mchiteni kukhala Mtetezi (wanu pa zinthu zanu zonse).
阿拉伯语经注:
وَٱصۡبِرۡ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَٱهۡجُرۡهُمۡ هَجۡرٗا جَمِيلٗا
Ndipo pirira pa zimene akunena. Ndipo apewe (ndi mtima wako); kupewa kwabwino.
阿拉伯语经注:
وَذَرۡنِي وَٱلۡمُكَذِّبِينَ أُوْلِي ٱلنَّعۡمَةِ وَمَهِّلۡهُمۡ قَلِيلًا
Ndisiye Ine ndi otsutsa eni kupeza bwino; ndipo alekelere kanthawi kochepa.
阿拉伯语经注:
إِنَّ لَدَيۡنَآ أَنكَالٗا وَجَحِيمٗا
Ndithudi, tili ndi mitundumitundu ya unyolo ndi Moto woyaka,
阿拉伯语经注:
وَطَعَامٗا ذَا غُصَّةٖ وَعَذَابًا أَلِيمٗا
Ndi chakudya chotsamwitsa ndi chilango chowawa.
阿拉伯语经注:
يَوۡمَ تَرۡجُفُ ٱلۡأَرۡضُ وَٱلۡجِبَالُ وَكَانَتِ ٱلۡجِبَالُ كَثِيبٗا مَّهِيلًا
Tsiku limene nthaka ndi mapiri zidzagwedezeka; (kugwedezeka kwa mphamvu kotero kuti) mapiri adzakhala ngati mulu wa mchenga woyoyoka.
阿拉伯语经注:
إِنَّآ أَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡكُمۡ رَسُولٗا شَٰهِدًا عَلَيۡكُمۡ كَمَآ أَرۡسَلۡنَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ رَسُولٗا
Ndithu Ife takutumizirani Mthenga amene adzakhala mboni yanu (tsiku la chimaliziro; monga momwe tidamtumizira (Mûsa) kukhala Mtumiki kwa Firiauni.
阿拉伯语经注:
فَعَصَىٰ فِرۡعَوۡنُ ٱلرَّسُولَ فَأَخَذۡنَٰهُ أَخۡذٗا وَبِيلٗا
Koma Firiauni adamnyoza Mtumikiyo; ndipo tidamulanga chilango chokhwima.
阿拉伯语经注:
فَكَيۡفَ تَتَّقُونَ إِن كَفَرۡتُمۡ يَوۡمٗا يَجۡعَلُ ٱلۡوِلۡدَٰنَ شِيبًا
Kodi mungadzitchinjirize chotani ngati mukana (chilango cha) tsiku (lomwe) lidzachititsa ana kukhala ndi imvi?
阿拉伯语经注:
ٱلسَّمَآءُ مُنفَطِرُۢ بِهِۦۚ كَانَ وَعۡدُهُۥ مَفۡعُولًا
Thambo (pamodzi ndi mphamvu zake ndi kukula kwake), lidzang’ambika (tsiku limenelo) chifukwa cha kuopsa kwa tsikulo, lonjezo la (Allah) lidzakwaniritsidwa (palibe wolipinga).
阿拉伯语经注:
إِنَّ هَٰذِهِۦ تَذۡكِرَةٞۖ فَمَن شَآءَ ٱتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ سَبِيلًا
Ndithudi, ma Ayah awa (amene akunena za kuwopsa kwa Qiyâma) ndichikumbutso. Choncho amene akufuna (kuthandizika nawo) ayende panjira ya Mbuye wake (pokwaniritsa malamulo Ake ndi kuleka zoipa).
阿拉伯语经注:
۞ إِنَّ رَبَّكَ يَعۡلَمُ أَنَّكَ تَقُومُ أَدۡنَىٰ مِن ثُلُثَيِ ٱلَّيۡلِ وَنِصۡفَهُۥ وَثُلُثَهُۥ وَطَآئِفَةٞ مِّنَ ٱلَّذِينَ مَعَكَۚ وَٱللَّهُ يُقَدِّرُ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَۚ عَلِمَ أَن لَّن تُحۡصُوهُ فَتَابَ عَلَيۡكُمۡۖ فَٱقۡرَءُواْ مَا تَيَسَّرَ مِنَ ٱلۡقُرۡءَانِۚ عَلِمَ أَن سَيَكُونُ مِنكُم مَّرۡضَىٰ وَءَاخَرُونَ يَضۡرِبُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ يَبۡتَغُونَ مِن فَضۡلِ ٱللَّهِ وَءَاخَرُونَ يُقَٰتِلُونَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِۖ فَٱقۡرَءُواْ مَا تَيَسَّرَ مِنۡهُۚ وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَ وَأَقۡرِضُواْ ٱللَّهَ قَرۡضًا حَسَنٗاۚ وَمَا تُقَدِّمُواْ لِأَنفُسِكُم مِّنۡ خَيۡرٖ تَجِدُوهُ عِندَ ٱللَّهِ هُوَ خَيۡرٗا وَأَعۡظَمَ أَجۡرٗاۚ وَٱسۡتَغۡفِرُواْ ٱللَّهَۖ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمُۢ
Ndithu Mbuye wako akudziwa kuti iwe ukuima (kupemphera) pafupifupi magawo awiri mwa magawo atatu a usiku kapena theka lake, kape’nanso gawo limodzi mwa magawo atatu a usiku, pamodzi ndi gulu la omwe uli nawo. Ndipo Allah ndi Amene amadziwa bwino muyeso wa (nthawi za) usiku ndi usana, wadziwa kuti simungathe kuwerengera zimenezo, choncho wakukhululukirani. Werengani ndime imene yapepuka yochokera m’Qur’an. Wadziwa kuti ena mwa inu adzakhala odwala; (kudzawavuta kuimilira ndi kuchezera usiku), ndipo ena adzakhala akuyendayenda pa dziko (ndi cholinga cha malonda ndi ntchito) kunka nafunafuna ubwino wa Allah. Ndipo ena adzakhala akumenya nkhondo pa njira ya Allah (ncholinga chotukula mawu Ake), werengani chimene chapepuka chochokera mmenemo (m’Qur’an). Ndipo pitirizani kupemphera Swala, perekani chopereka (chimene chakakamizidwa kwa inu). Ndipo mkongozeni Allah ngongole yabwino. Ndipo chilichonse chabwino chimene mwadzitsogozera mudzachipeza kwa Allah chili chabwino (kuposa zomwe mudazisiya m’mbuyo) ndi malipiro akulu zedi ndipo mpempheni Allah chikhululuko (pa uchimo wanu ndi chikhululuko pakunyozera kwanu kuchita zabwino). Ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 穆资米拉
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭