ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: القلم
آية:
 

القلم

نٓۚ وَٱلۡقَلَمِ وَمَا يَسۡطُرُونَ
“Nûn. Ndikulumbilira cholembera (chimene akulembera angelo), ndi zimene amalemba.
التفاسير العربية:
مَآ أَنتَ بِنِعۡمَةِ رَبِّكَ بِمَجۡنُونٖ
“Pa chisomo cha Mbuye wako iwe sindiwe wamisala (pokupatsa uneneri).
التفاسير العربية:
وَإِنَّ لَكَ لَأَجۡرًا غَيۡرَ مَمۡنُونٖ
“Ndipo ndithu udzakhala ndi malipiro akulu osaduka, (onkerankera mtsogolo chifukwa cha mavuto amene ukukumana nawo pofikitsa uthenga).
التفاسير العربية:
وَإِنَّكَ لَعَلَىٰ خُلُقٍ عَظِيمٖ
“Ndipo ndithu uli nawo makhalidwe abwino kwambiri (omwe Allah adakulenga nawo).
التفاسير العربية:
فَسَتُبۡصِرُ وَيُبۡصِرُونَ
“Basi, posachedwapa uona, iwonso aona.
التفاسير العربية:
بِأَييِّكُمُ ٱلۡمَفۡتُونُ
“Kuti ndani mwa inu wamisala (iwe kapena iwo)?
التفاسير العربية:
إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعۡلَمُ بِمَن ضَلَّ عَن سَبِيلِهِۦ وَهُوَ أَعۡلَمُ بِٱلۡمُهۡتَدِينَ
“Ndithu Mbuye wako akum’dziwa bwino amene wasokera panjira yake. Ndiponso akuwadziwa bwino amene ali oongoka.
التفاسير العربية:
فَلَا تُطِعِ ٱلۡمُكَذِّبِينَ
“Choncho, usawamvere otsutsa; (usasiye zimene uli nazo ngakhale sakugwirizana nazo).
التفاسير العربية:
وَدُّواْ لَوۡ تُدۡهِنُ فَيُدۡهِنُونَ
“Akufuna kuti ukadakhala wofewa kwa iwo (pa zinthu zina) nawo akadakhala ofewa (kwa iwe).
التفاسير العربية:
وَلَا تُطِعۡ كُلَّ حَلَّافٖ مَّهِينٍ
“Ndipo usamumvere aliyense wochulukitsa kulumbira, woyaluka.
التفاسير العربية:
هَمَّازٖ مَّشَّآءِۭ بِنَمِيمٖ
“Wojeda, woyenda ndi ukazitape (ndi cholinga choononga umodzi wawo).
التفاسير العربية:
مَّنَّاعٖ لِّلۡخَيۡرِ مُعۡتَدٍ أَثِيمٍ
“Wotsekereza zabwino, wamtopola, wamachimo ambiri.
التفاسير العربية:
عُتُلِّۭ بَعۡدَ ذَٰلِكَ زَنِيمٍ
“Wouma mtima; pamwamba pa izi ndi wodzipachika mu mtundu wa ena (pomwe iye sali m’menemo).
التفاسير العربية:
أَن كَانَ ذَا مَالٖ وَبَنِينَ
“Chifukwa choti iye ndi mwini chuma ndi ana (ndi zimene ali kunyadira).
التفاسير العربية:
إِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ءَايَٰتُنَا قَالَ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ
“Zikawerengedwa kwa iye Ayah Zathu amanena: “Izi ndi nthano za akale (ndi zabodza zawo, zopeka).”
التفاسير العربية:
سَنَسِمُهُۥ عَلَى ٱلۡخُرۡطُومِ
“Timuika pamphuno pake chizindikiro (chosasiyana nacho kuti ayaluke nacho pamaso pa anthu).
التفاسير العربية:

إِنَّا بَلَوۡنَٰهُمۡ كَمَا بَلَوۡنَآ أَصۡحَٰبَ ٱلۡجَنَّةِ إِذۡ أَقۡسَمُواْ لَيَصۡرِمُنَّهَا مُصۡبِحِينَ
“Ndithu ife tidawayesa (eni mzinda wa Makka ndi mtendere omwe udali pa iwo, koma adakana monga) momwe tidawayesera eni munda, pamene adalumbira kuti akathyola (zipatso za m’munda wawozo) mbandakucha (kuti osauka asawaone angawapemphe).
التفاسير العربية:
وَلَا يَسۡتَثۡنُونَ
“Ndipo sadapatule (ngakhale wosauka ndi m’modzi yemwe ponena kuti uje timpatse, uje tisampatse, kapena sadanene kuti: “Ngati Allah afuna).”
التفاسير العربية:
فَطَافَ عَلَيۡهَا طَآئِفٞ مِّن رَّبِّكَ وَهُمۡ نَآئِمُونَ
“Mliri woopsa wochokera kwa Mbuye wako udauzinga (mundawo nthawi yausiku) iwo ali mtulo.
التفاسير العربية:
فَأَصۡبَحَتۡ كَٱلصَّرِيمِ
“Choncho udakhala ngati wokololedwa (chifukwa cha mliri uja).
التفاسير العربية:
فَتَنَادَوۡاْ مُصۡبِحِينَ
“Tero adaitanizana nthawi ya mbandakucha.
التفاسير العربية:
أَنِ ٱغۡدُواْ عَلَىٰ حَرۡثِكُمۡ إِن كُنتُمۡ صَٰرِمِينَ
““Lawilirani kumunda wanu kuja ngati mukufuna kukolola (kuopera kuti angakuoneni osauka).”
التفاسير العربية:
فَٱنطَلَقُواْ وَهُمۡ يَتَخَٰفَتُونَ
“Adanyamuka uku akunong’ onezana.
التفاسير العربية:
أَن لَّا يَدۡخُلَنَّهَا ٱلۡيَوۡمَ عَلَيۡكُم مِّسۡكِينٞ
“(Akunena kuti): “Asakulowelereni wosauka lero mmenemo.”
التفاسير العربية:
وَغَدَوۡاْ عَلَىٰ حَرۡدٖ قَٰدِرِينَ
“Ndipo adalawilira ali ndi chitsimikizo choti atha kuwamana (osauka).
التفاسير العربية:
فَلَمَّا رَأَوۡهَا قَالُوٓاْ إِنَّا لَضَآلُّونَ
“Choncho pamene adauona, adanena (uku akunjenjemera): “Ndithu ife tasokera (sikuno ayi, munda wathu uja siuno).”
التفاسير العربية:
بَلۡ نَحۡنُ مَحۡرُومُونَ
““Iyayi, ndiwomwewu; koma tamanidwa zinthu zake.”
التفاسير العربية:
قَالَ أَوۡسَطُهُمۡ أَلَمۡ أَقُل لَّكُمۡ لَوۡلَا تُسَبِّحُونَ
“Wolungama mwa iwo adanena: “Kodi sindinakuuzeni (pamene mudali kulangizana zomana osowa) kuti bwanji osamkumbukira Allah (ndi kusintha cholinga chanu)?”
التفاسير العربية:
قَالُواْ سُبۡحَٰنَ رَبِّنَآ إِنَّا كُنَّا ظَٰلِمِينَ
“(Iwo) adanena: “Alemekezeke Mbuye wathu ndithu ife tidali achinyengo (chifukwa cha kuipa kwa cholinga chathu).”
التفاسير العربية:
فَأَقۡبَلَ بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖ يَتَلَٰوَمُونَ
“Ndipo adatembenukirana ndikuyamba kudzudzulana.
التفاسير العربية:
قَالُواْ يَٰوَيۡلَنَآ إِنَّا كُنَّا طَٰغِينَ
“Adati: “E chionongeko chathu! Ndithu Ife tidapyola malire (m’chinyengo chathu).”
التفاسير العربية:
عَسَىٰ رَبُّنَآ أَن يُبۡدِلَنَا خَيۡرٗا مِّنۡهَآ إِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا رَٰغِبُونَ
““Mwina Mbuye wathu angatipatse zabwino m’malo mwa munda wathuwu. Ndithu ife tikufunitsitsa kwa Mbuye wathu (chikhululuko Chake).”
التفاسير العربية:
كَذَٰلِكَ ٱلۡعَذَابُۖ وَلَعَذَابُ ٱلۡأٓخِرَةِ أَكۡبَرُۚ لَوۡ كَانُواْ يَعۡلَمُونَ
“Umo ndi mmene chimakhalira chilango (Changa chomwe ndimachitsitsa pa dziko lapansi kwa amene chamuyenera); koma chilango cha tsiku lachimaliziro nchachikulu zedi, akadakhala akudziwa.
التفاسير العربية:
إِنَّ لِلۡمُتَّقِينَ عِندَ رَبِّهِمۡ جَنَّـٰتِ ٱلنَّعِيمِ
“Ndithu oopa Allah adzakhala ndi Minda ya mtendere kwa Mbuye wawo.
التفاسير العربية:
أَفَنَجۡعَلُ ٱلۡمُسۡلِمِينَ كَٱلۡمُجۡرِمِينَ
“Kodi tiwachite Asilamu monga ochimwa.
التفاسير العربية:
مَا لَكُمۡ كَيۡفَ تَحۡكُمُونَ
“Kodi nchiyani chakupezani! Nanga mukuweruza bwanji (maweruzo opanda chilungamo)?
التفاسير العربية:
أَمۡ لَكُمۡ كِتَٰبٞ فِيهِ تَدۡرُسُونَ
“Kapena muli ndi buku limene mukuwerenga.
التفاسير العربية:
إِنَّ لَكُمۡ فِيهِ لَمَا تَخَيَّرُونَ
“Kuti ndithu mulinazo mmenemo zomwe mukudzisankhira.
التفاسير العربية:
أَمۡ لَكُمۡ أَيۡمَٰنٌ عَلَيۡنَا بَٰلِغَةٌ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ إِنَّ لَكُمۡ لَمَا تَحۡكُمُونَ
“Kapena muli nawo mapangano ndi Ife okafika mpaka tsiku lachimaliziro akuti inu mudzapeza zimene mukudziweruzira?
التفاسير العربية:
سَلۡهُمۡ أَيُّهُم بِذَٰلِكَ زَعِيمٌ
“Afunse (iwe Mtumiki) ndani mwa iwo amene ali mtsogoleri (pa malamulo amenewa)?
التفاسير العربية:
أَمۡ لَهُمۡ شُرَكَآءُ فَلۡيَأۡتُواْ بِشُرَكَآئِهِمۡ إِن كَانُواْ صَٰدِقِينَ
“Kapena iwo ali nawo othandidzana nawo (pa mau awa)? Chomwecho atabweretsa othandizana nawo ngati akunena zowona!
التفاسير العربية:
يَوۡمَ يُكۡشَفُ عَن سَاقٖ وَيُدۡعَوۡنَ إِلَى ٱلسُّجُودِ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ
“(Akumbukire) tsiku la mavuto okhwima, ndipo adzaitanidwa (akafiri) kuti achite sijida (polambira Allah) koma sadzatha.
التفاسير العربية:

خَٰشِعَةً أَبۡصَٰرُهُمۡ تَرۡهَقُهُمۡ ذِلَّةٞۖ وَقَدۡ كَانُواْ يُدۡعَوۡنَ إِلَى ٱلسُّجُودِ وَهُمۡ سَٰلِمُونَ
“Maso awo adzangoti pansi zyoli, manyazi ndi kunyozeka kudzawaphimba; chikhalirecho adali kuitanidwa (pa dziko lapansi) kuti agwetse nkhope pansi pomwe iwo adali ndi moyo wa ngwiro (koma ankakana).
التفاسير العربية:
فَذَرۡنِي وَمَن يُكَذِّبُ بِهَٰذَا ٱلۡحَدِيثِۖ سَنَسۡتَدۡرِجُهُم مِّنۡ حَيۡثُ لَا يَعۡلَمُونَ
“Choncho ndisiye, (iwe Mtumiki), ndi amene akukanira nkhani iyi tiwakokera kuchilango pang’onopang’ono pamene iwo sakudziwa (mmene chiti chiwadzere chilangochi).
التفاسير العربية:
وَأُمۡلِي لَهُمۡۚ إِنَّ كَيۡدِي مَتِينٌ
“Ndipo ndikuwalekelera (pochedwetsa chilango); ndithudi makonzedwe Anga ngokhwima, (palibe angapulumuke mmenemo).
التفاسير العربية:
أَمۡ تَسۡـَٔلُهُمۡ أَجۡرٗا فَهُم مِّن مَّغۡرَمٖ مُّثۡقَلُونَ
“Kapena ukuwapempha malipiro (pofikitsa uthenga) kotero kuti iwo akulemedwa ndi kulipira?
التفاسير العربية:
أَمۡ عِندَهُمُ ٱلۡغَيۡبُ فَهُمۡ يَكۡتُبُونَ
“Kapena ali nazo (nzeru) zobisika kotero kuti iwo akulemba (zimene akuweruzazo)!
التفاسير العربية:
فَٱصۡبِرۡ لِحُكۡمِ رَبِّكَ وَلَا تَكُن كَصَاحِبِ ٱلۡحُوتِ إِذۡ نَادَىٰ وَهُوَ مَكۡظُومٞ
“Choncho pirira ndi lamulo la Mbuye wako (chifukwa chowalekelera ndi kuchedwetsa chipulumutso chako); ndipo usakhale ngati mwini nsomba (Yunusu pa changu ndi mkwiyo kwa anthu ake) pamene adaitana (Mbuye wake) uku ali wodzazidwa ndi mkwiyo (kupempha kuti chidze mwachangu chilango kwa anthu ake).
التفاسير العربية:
لَّوۡلَآ أَن تَدَٰرَكَهُۥ نِعۡمَةٞ مِّن رَّبِّهِۦ لَنُبِذَ بِٱلۡعَرَآءِ وَهُوَ مَذۡمُومٞ
“Chikadapanda kumfikira chisomo chochokera kwa Mbuye wake (ndi kuvomera kulapa kwake), akadaponyedwa (kuchokera m’mimba mwa chinsomba chija) pagombe (popanda kanthu) ali wodzudzulidwa.
التفاسير العربية:
فَٱجۡتَبَٰهُ رَبُّهُۥ فَجَعَلَهُۥ مِنَ ٱلصَّـٰلِحِينَ
“Koma adamsankha Mbuye wake (povomera kulapa kwake) ndipo adamchita kukhala mmodzi wa anthu abwino.
التفاسير العربية:
وَإِن يَكَادُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَيُزۡلِقُونَكَ بِأَبۡصَٰرِهِمۡ لَمَّا سَمِعُواْ ٱلذِّكۡرَ وَيَقُولُونَ إِنَّهُۥ لَمَجۡنُونٞ
“Ndithudi anthu amene sadakhulupirire adayandikira kukuteleretsa ndi kunyogodola kwa maso awo (chifukwa chachidani ndi mkwiyo) pamene adamva chikumbutso (Qur’an), ndipo akunena kuti iyeyo ngwamisala.
التفاسير العربية:
وَمَا هُوَ إِلَّا ذِكۡرٞ لِّلۡعَٰلَمِينَ
“Ndipo ichi sichina, koma (ndi phunziro, ndi nzeru) ndi chikumbutso kwa zolengedwa zonse.
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: القلم
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق