《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 * - 译解目录


含义的翻译 章: 盖拉姆   段:

盖拉姆

نٓۚ وَٱلۡقَلَمِ وَمَا يَسۡطُرُونَ
Nûn. Ndikulumbilira cholembera (chimene akulembera angelo), ndi zimene amalemba.
阿拉伯语经注:
مَآ أَنتَ بِنِعۡمَةِ رَبِّكَ بِمَجۡنُونٖ
Pa chisomo cha Mbuye wako iwe sindiwe wamisala (pokupatsa uneneri).
阿拉伯语经注:
وَإِنَّ لَكَ لَأَجۡرًا غَيۡرَ مَمۡنُونٖ
Ndipo ndithu udzakhala ndi malipiro akulu osaduka, (onkerankera mtsogolo chifukwa cha mavuto amene ukukumana nawo pofikitsa uthenga).
阿拉伯语经注:
وَإِنَّكَ لَعَلَىٰ خُلُقٍ عَظِيمٖ
Ndipo ndithu uli nawo makhalidwe abwino kwambiri (omwe Allah adakulenga nawo).
阿拉伯语经注:
فَسَتُبۡصِرُ وَيُبۡصِرُونَ
Basi, posachedwapa uona, iwonso aona.
阿拉伯语经注:
بِأَييِّكُمُ ٱلۡمَفۡتُونُ
Kuti ndani mwa inu wamisala (iwe kapena iwo)?
阿拉伯语经注:
إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعۡلَمُ بِمَن ضَلَّ عَن سَبِيلِهِۦ وَهُوَ أَعۡلَمُ بِٱلۡمُهۡتَدِينَ
Ndithu Mbuye wako akum’dziwa bwino amene wasokera panjira yake. Ndiponso akuwadziwa bwino amene ali oongoka.
阿拉伯语经注:
فَلَا تُطِعِ ٱلۡمُكَذِّبِينَ
Choncho, usawamvere otsutsa; (usasiye zimene uli nazo ngakhale sakugwirizana nazo).
阿拉伯语经注:
وَدُّواْ لَوۡ تُدۡهِنُ فَيُدۡهِنُونَ
Akufuna kuti ukadakhala wofewa kwa iwo (pa zinthu zina) nawo akadakhala ofewa (kwa iwe).
阿拉伯语经注:
وَلَا تُطِعۡ كُلَّ حَلَّافٖ مَّهِينٍ
Ndipo usamumvere aliyense wochulukitsa kulumbira, woyaluka.
阿拉伯语经注:
هَمَّازٖ مَّشَّآءِۭ بِنَمِيمٖ
Wojeda, woyenda ndi ukazitape (ndi cholinga choononga umodzi wawo).
阿拉伯语经注:
مَّنَّاعٖ لِّلۡخَيۡرِ مُعۡتَدٍ أَثِيمٍ
Wotsekereza zabwino, wamtopola, wamachimo ambiri.
阿拉伯语经注:
عُتُلِّۭ بَعۡدَ ذَٰلِكَ زَنِيمٍ
Wouma mtima; pamwamba pa izi ndi wodzipachika mu mtundu wa ena (pomwe iye sali m’menemo).
阿拉伯语经注:
أَن كَانَ ذَا مَالٖ وَبَنِينَ
Chifukwa choti iye ndi mwini chuma ndi ana (ndi zimene ali kunyadira).
阿拉伯语经注:
إِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ءَايَٰتُنَا قَالَ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Zikawerengedwa kwa iye Ayah Zathu amanena: “Izi ndi nthano za akale (ndi zabodza zawo, zopeka).”
阿拉伯语经注:
سَنَسِمُهُۥ عَلَى ٱلۡخُرۡطُومِ
Timuika pamphuno pake chizindikiro (chosasiyana nacho kuti ayaluke nacho pamaso pa anthu).
阿拉伯语经注:
إِنَّا بَلَوۡنَٰهُمۡ كَمَا بَلَوۡنَآ أَصۡحَٰبَ ٱلۡجَنَّةِ إِذۡ أَقۡسَمُواْ لَيَصۡرِمُنَّهَا مُصۡبِحِينَ
Ndithu ife tidawayesa (eni mzinda wa Makka ndi mtendere omwe udali pa iwo, koma adakana monga) momwe tidawayesera eni munda, pamene adalumbira kuti akathyola (zipatso za m’munda wawozo) mbandakucha (kuti osauka asawaone angawapemphe).
阿拉伯语经注:
وَلَا يَسۡتَثۡنُونَ
Ndipo sadapatule (ngakhale wosauka ndi m’modzi yemwe ponena kuti uje timpatse, uje tisampatse, kapena sadanene kuti: “Ngati Allah afuna).”
阿拉伯语经注:
فَطَافَ عَلَيۡهَا طَآئِفٞ مِّن رَّبِّكَ وَهُمۡ نَآئِمُونَ
Mliri woopsa wochokera kwa Mbuye wako udauzinga (mundawo nthawi yausiku) iwo ali mtulo.
阿拉伯语经注:
فَأَصۡبَحَتۡ كَٱلصَّرِيمِ
Choncho udakhala ngati wokololedwa (chifukwa cha mliri uja).
阿拉伯语经注:
فَتَنَادَوۡاْ مُصۡبِحِينَ
Tero adaitanizana nthawi ya mbandakucha.
阿拉伯语经注:
أَنِ ٱغۡدُواْ عَلَىٰ حَرۡثِكُمۡ إِن كُنتُمۡ صَٰرِمِينَ
“Lawilirani kumunda wanu kuja ngati mukufuna kukolola (kuopera kuti angakuoneni osauka).”
阿拉伯语经注:
فَٱنطَلَقُواْ وَهُمۡ يَتَخَٰفَتُونَ
Adanyamuka uku akunong’ onezana.
阿拉伯语经注:
أَن لَّا يَدۡخُلَنَّهَا ٱلۡيَوۡمَ عَلَيۡكُم مِّسۡكِينٞ
(Akunena kuti): “Asakulowelereni wosauka lero mmenemo.”
阿拉伯语经注:
وَغَدَوۡاْ عَلَىٰ حَرۡدٖ قَٰدِرِينَ
Ndipo adalawilira ali ndi chitsimikizo choti atha kuwamana (osauka).
阿拉伯语经注:
فَلَمَّا رَأَوۡهَا قَالُوٓاْ إِنَّا لَضَآلُّونَ
Choncho pamene adauona, adanena (uku akunjenjemera): “Ndithu ife tasokera (sikuno ayi, munda wathu uja siuno).”
阿拉伯语经注:
بَلۡ نَحۡنُ مَحۡرُومُونَ
“Iyayi, ndiwomwewu; koma tamanidwa zinthu zake.”
阿拉伯语经注:
قَالَ أَوۡسَطُهُمۡ أَلَمۡ أَقُل لَّكُمۡ لَوۡلَا تُسَبِّحُونَ
Wolungama mwa iwo adanena: “Kodi sindinakuuzeni (pamene mudali kulangizana zomana osowa) kuti bwanji osamkumbukira Allah (ndi kusintha cholinga chanu)?”
阿拉伯语经注:
قَالُواْ سُبۡحَٰنَ رَبِّنَآ إِنَّا كُنَّا ظَٰلِمِينَ
(Iwo) adanena: “Alemekezeke Mbuye wathu ndithu ife tidali achinyengo (chifukwa cha kuipa kwa cholinga chathu).”
阿拉伯语经注:
فَأَقۡبَلَ بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖ يَتَلَٰوَمُونَ
Ndipo adatembenukirana ndikuyamba kudzudzulana.
阿拉伯语经注:
قَالُواْ يَٰوَيۡلَنَآ إِنَّا كُنَّا طَٰغِينَ
Adati: “E chionongeko chathu! Ndithu Ife tidapyola malire (m’chinyengo chathu).”
阿拉伯语经注:
عَسَىٰ رَبُّنَآ أَن يُبۡدِلَنَا خَيۡرٗا مِّنۡهَآ إِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا رَٰغِبُونَ
“Mwina Mbuye wathu angatipatse zabwino m’malo mwa munda wathuwu. Ndithu ife tikufunitsitsa kwa Mbuye wathu (chikhululuko Chake).”
阿拉伯语经注:
كَذَٰلِكَ ٱلۡعَذَابُۖ وَلَعَذَابُ ٱلۡأٓخِرَةِ أَكۡبَرُۚ لَوۡ كَانُواْ يَعۡلَمُونَ
Umo ndi mmene chimakhalira chilango (Changa chomwe ndimachitsitsa pa dziko lapansi kwa amene chamuyenera); koma chilango cha tsiku lachimaliziro nchachikulu zedi, akadakhala akudziwa.
阿拉伯语经注:
إِنَّ لِلۡمُتَّقِينَ عِندَ رَبِّهِمۡ جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ
Ndithu oopa Allah adzakhala ndi Minda ya mtendere kwa Mbuye wawo.
阿拉伯语经注:
أَفَنَجۡعَلُ ٱلۡمُسۡلِمِينَ كَٱلۡمُجۡرِمِينَ
Kodi tiwachite Asilamu monga ochimwa.
阿拉伯语经注:
مَا لَكُمۡ كَيۡفَ تَحۡكُمُونَ
Kodi nchiyani chakupezani! Nanga mukuweruza bwanji (maweruzo opanda chilungamo)?
阿拉伯语经注:
أَمۡ لَكُمۡ كِتَٰبٞ فِيهِ تَدۡرُسُونَ
Kapena muli ndi buku limene mukuwerenga.
阿拉伯语经注:
إِنَّ لَكُمۡ فِيهِ لَمَا تَخَيَّرُونَ
Kuti ndithu mulinazo mmenemo zomwe mukudzisankhira.
阿拉伯语经注:
أَمۡ لَكُمۡ أَيۡمَٰنٌ عَلَيۡنَا بَٰلِغَةٌ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ إِنَّ لَكُمۡ لَمَا تَحۡكُمُونَ
Kapena muli nawo mapangano ndi Ife okafika mpaka tsiku lachimaliziro akuti inu mudzapeza zimene mukudziweruzira?
阿拉伯语经注:
سَلۡهُمۡ أَيُّهُم بِذَٰلِكَ زَعِيمٌ
Afunse (iwe Mtumiki) ndani mwa iwo amene ali mtsogoleri (pa malamulo amenewa)?
阿拉伯语经注:
أَمۡ لَهُمۡ شُرَكَآءُ فَلۡيَأۡتُواْ بِشُرَكَآئِهِمۡ إِن كَانُواْ صَٰدِقِينَ
Kapena iwo ali nawo othandidzana nawo (pa mau awa)? Chomwecho atabweretsa othandizana nawo ngati akunena zowona!
阿拉伯语经注:
يَوۡمَ يُكۡشَفُ عَن سَاقٖ وَيُدۡعَوۡنَ إِلَى ٱلسُّجُودِ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ
(Akumbukire) tsiku la mavuto okhwima, ndipo adzaitanidwa (akafiri) kuti achite sijida (polambira Allah) koma sadzatha.
阿拉伯语经注:
خَٰشِعَةً أَبۡصَٰرُهُمۡ تَرۡهَقُهُمۡ ذِلَّةٞۖ وَقَدۡ كَانُواْ يُدۡعَوۡنَ إِلَى ٱلسُّجُودِ وَهُمۡ سَٰلِمُونَ
Maso awo adzangoti pansi zyoli, manyazi ndi kunyozeka kudzawaphimba; chikhalirecho adali kuitanidwa (pa dziko lapansi) kuti agwetse nkhope pansi pomwe iwo adali ndi moyo wa ngwiro (koma ankakana).
阿拉伯语经注:
فَذَرۡنِي وَمَن يُكَذِّبُ بِهَٰذَا ٱلۡحَدِيثِۖ سَنَسۡتَدۡرِجُهُم مِّنۡ حَيۡثُ لَا يَعۡلَمُونَ
Choncho ndisiye, (iwe Mtumiki), ndi amene akukanira nkhani iyi tiwakokera kuchilango pang’onopang’ono pamene iwo sakudziwa (mmene chiti chiwadzere chilangochi).
阿拉伯语经注:
وَأُمۡلِي لَهُمۡۚ إِنَّ كَيۡدِي مَتِينٌ
Ndipo ndikuwalekelera (pochedwetsa chilango); ndithudi makonzedwe Anga ngokhwima, (palibe angapulumuke mmenemo).
阿拉伯语经注:
أَمۡ تَسۡـَٔلُهُمۡ أَجۡرٗا فَهُم مِّن مَّغۡرَمٖ مُّثۡقَلُونَ
Kapena ukuwapempha malipiro (pofikitsa uthenga) kotero kuti iwo akulemedwa ndi kulipira?
阿拉伯语经注:
أَمۡ عِندَهُمُ ٱلۡغَيۡبُ فَهُمۡ يَكۡتُبُونَ
Kapena ali nazo (nzeru) zobisika kotero kuti iwo akulemba (zimene akuweruzazo)!
阿拉伯语经注:
فَٱصۡبِرۡ لِحُكۡمِ رَبِّكَ وَلَا تَكُن كَصَاحِبِ ٱلۡحُوتِ إِذۡ نَادَىٰ وَهُوَ مَكۡظُومٞ
Choncho pirira ndi lamulo la Mbuye wako (chifukwa chowalekelera ndi kuchedwetsa chipulumutso chako); ndipo usakhale ngati mwini nsomba (Yunusu pa changu ndi mkwiyo kwa anthu ake) pamene adaitana (Mbuye wake) uku ali wodzazidwa ndi mkwiyo (kupempha kuti chidze mwachangu chilango kwa anthu ake).
阿拉伯语经注:
لَّوۡلَآ أَن تَدَٰرَكَهُۥ نِعۡمَةٞ مِّن رَّبِّهِۦ لَنُبِذَ بِٱلۡعَرَآءِ وَهُوَ مَذۡمُومٞ
Chikadapanda kumfikira chisomo chochokera kwa Mbuye wake (ndi kuvomera kulapa kwake), akadaponyedwa (kuchokera m’mimba mwa chinsomba chija) pagombe (popanda kanthu) ali wodzudzulidwa.
阿拉伯语经注:
فَٱجۡتَبَٰهُ رَبُّهُۥ فَجَعَلَهُۥ مِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ
Koma adamsankha Mbuye wake (povomera kulapa kwake) ndipo adamchita kukhala mmodzi wa anthu abwino.
阿拉伯语经注:
وَإِن يَكَادُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَيُزۡلِقُونَكَ بِأَبۡصَٰرِهِمۡ لَمَّا سَمِعُواْ ٱلذِّكۡرَ وَيَقُولُونَ إِنَّهُۥ لَمَجۡنُونٞ
Ndithudi anthu amene sadakhulupirire adayandikira kukuteleretsa ndi kunyogodola kwa maso awo (chifukwa chachidani ndi mkwiyo) pamene adamva chikumbutso (Qur’an), ndipo akunena kuti iyeyo ngwamisala.
阿拉伯语经注:
وَمَا هُوَ إِلَّا ذِكۡرٞ لِّلۡعَٰلَمِينَ
Ndipo ichi sichina, koma (ndi phunziro, ndi nzeru) ndi chikumbutso kwa zolengedwa zonse.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 盖拉姆
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 译解目录

古兰经契瓦文译解,哈利德·伊布拉欣·比德拉翻译,2020年版

关闭