કુરઆન મજીદના શબ્દોનું ભાષાંતર - ચેવા ભાષાતર * - ભાષાંતરોની અનુક્રમણિકા


શબ્દોનું ભાષાંતર સૂરહ: અસ્ સોફ્ફાત   આયત:

અસ્ સોફ્ફાત

وَٱلصَّٰٓفَّٰتِ صَفّٗا
Ndikulumbira (angelo) amene amandanda m’mizere yondondozana, (popembedza ndi kugonjera Mbuye wawo).
અરબી તફસીરો:
فَٱلزَّٰجِرَٰتِ زَجۡرٗا
Ndi omwe amaletsa zoipa.
અરબી તફસીરો:
فَٱلتَّٰلِيَٰتِ ذِكۡرًا
Ndi omwe amalalika ulaliki (wa Allah ndi kumtamanda mochulukira).
અરબી તફસીરો:
إِنَّ إِلَٰهَكُمۡ لَوَٰحِدٞ
Ndithu Mulungu wanu ndi mmodzi basi.
અરબી તફસીરો:
رَّبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا وَرَبُّ ٱلۡمَشَٰرِقِ
Mbuye wathambo ndi nthaka, ndi zapakati pake; ndiponso Mbuye wa kuvuma konse.
અરબી તફસીરો:
إِنَّا زَيَّنَّا ٱلسَّمَآءَ ٱلدُّنۡيَا بِزِينَةٍ ٱلۡكَوَاكِبِ
Ndithu tidalikongoletsa thambo lapafupi (ndi inu) ndi chokongoletsa cha nyenyezi (zowala).
અરબી તફસીરો:
وَحِفۡظٗا مِّن كُلِّ شَيۡطَٰنٖ مَّارِدٖ
Ndi kuti lisungidwe ku satana aliyense wogalukira (lamulo la Allah).
અરબી તફસીરો:
لَّا يَسَّمَّعُونَ إِلَى ٱلۡمَلَإِ ٱلۡأَعۡلَىٰ وَيُقۡذَفُونَ مِن كُلِّ جَانِبٖ
Kuti asamvere (zomwe zikunenedwa ndi) gulu lolemekezeka (la angelo). Ndipo akugendedwa (ndi kupirikitsidwa) mbali zonse.
અરબી તફસીરો:
دُحُورٗاۖ وَلَهُمۡ عَذَابٞ وَاصِبٌ
Kuthamangitsidwa mwamphamvu; ndipo chilango chonkerankera patsogolo chili pa iwo.
અરબી તફસીરો:
إِلَّا مَنۡ خَطِفَ ٱلۡخَطۡفَةَ فَأَتۡبَعَهُۥ شِهَابٞ ثَاقِبٞ
Kupatula amene wazembetsa mawu (akumwamba), ndipo chikumtsatira iye chenje cha moto chowala kwambiri.
અરબી તફસીરો:
فَٱسۡتَفۡتِهِمۡ أَهُمۡ أَشَدُّ خَلۡقًا أَم مَّنۡ خَلَقۡنَآۚ إِنَّا خَلَقۡنَٰهُم مِّن طِينٖ لَّازِبِۭ
Tawafunsa (otsutsa zouka ku imfa): “Kodi iwo ngovuta kuwalenga kuposa zimene tidalenga, (monga: thambo, nthaka, nyenyezi ndi zina zotere)?” Ndithu Ife tidawalenga kuchokera ku dongo lonyata.
અરબી તફસીરો:
بَلۡ عَجِبۡتَ وَيَسۡخَرُونَ
Koma iwe (Mneneri) ukudabwa (za kutsutsa kwawo kuuka ku imfa pomwe zisonyezo zilipo zambirimbiri), ndipo akukuchitira chipongwe (kudabwa kwako).
અરબી તફસીરો:
وَإِذَا ذُكِّرُواْ لَا يَذۡكُرُونَ
Ndipo akalalikiridwa, salalikirika.
અરબી તફસીરો:
وَإِذَا رَأَوۡاْ ءَايَةٗ يَسۡتَسۡخِرُونَ
Ndipo akachiona chisonyezo (chosonyeza kukhoza kwa Allah,) amachichitira chipongwe.
અરબી તફસીરો:
وَقَالُوٓاْ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا سِحۡرٞ مُّبِينٌ
Ndipo osakhulupirira amanena: “Palibe chilipo apa, koma ndi matsenga woonekera poyera.”
અરબી તફસીરો:
أَءِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابٗا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ
“Kodi tikadzafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, tidzatulutsidwanso (kuchokera m’manda tili amoyo)?”
અરબી તફસીરો:
أَوَءَابَآؤُنَا ٱلۡأَوَّلُونَ
“Pamodzi ndi makolo athu akale?”
અરબી તફસીરો:
قُلۡ نَعَمۡ وَأَنتُمۡ دَٰخِرُونَ
Nena (iwe Mneneri): “Inde (mudzaukitsidwa inu pamodzi ndi makolo anu) uku inu muli onyozeka.”
અરબી તફસીરો:
فَإِنَّمَا هِيَ زَجۡرَةٞ وَٰحِدَةٞ فَإِذَا هُمۡ يَنظُرُونَ
Ndithu (kuukako) ndimkuwe umodzi adzangodzidzimuka ali moyo, akuyang’ana.
અરબી તફસીરો:
وَقَالُواْ يَٰوَيۡلَنَا هَٰذَا يَوۡمُ ٱلدِّينِ
Ndipo adzanena (okanawo): “Kalanga ife! Kuonongeka nkwathu! Ili nditsiku lija lamalipiro!”
અરબી તફસીરો:
هَٰذَا يَوۡمُ ٱلۡفَصۡلِ ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تُكَذِّبُونَ
(Adzawauza): “Ili nditsiku la chiweruziro lomwe mumalitsutsa lija.”
અરબી તફસીરો:
۞ ٱحۡشُرُواْ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ وَأَزۡوَٰجَهُمۡ وَمَا كَانُواْ يَعۡبُدُونَ
(Kudzanenedwa kwa angelo): “Asonkhanitseni amene adali osalungama pamodzi ndi akazi awo (okana Allah) ndi milungu yawo imene amaipembedza,”
અરબી તફસીરો:
مِن دُونِ ٱللَّهِ فَٱهۡدُوهُمۡ إِلَىٰ صِرَٰطِ ٱلۡجَحِيمِ
“Kusiya Allah, ndipo asonyezeni njira ya ku Jahannam.”
અરબી તફસીરો:
وَقِفُوهُمۡۖ إِنَّهُم مَّسۡـُٔولُونَ
“Koma aimikeni pano chifukwa iwo afunsidwa (za chikhulupiliro chawo ndi zochita zawo):”
અરબી તફસીરો:
مَا لَكُمۡ لَا تَنَاصَرُونَ
“Kodi nchifukwa ninji inu (opembedza mafano) simukupulumutsana (monga mumanenera pa dziko lapansi kuti mudzapulumutsana)?”
અરબી તફસીરો:
بَلۡ هُمُ ٱلۡيَوۡمَ مُسۡتَسۡلِمُونَ
Koma iwo pa tsikulo adzagonjera ndi kudzipereka (ku lamulo la Allah).
અરબી તફસીરો:
وَأَقۡبَلَ بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖ يَتَسَآءَلُونَ
Ndipo adzatembenukirana ndi kuyamba kufunsana (ndi kudzudzulana).
અરબી તફસીરો:
قَالُوٓاْ إِنَّكُمۡ كُنتُمۡ تَأۡتُونَنَا عَنِ ٱلۡيَمِينِ
Ndipo (ofooka) adzanena (kwa odzikweza): “Inu mumatidzera kumbali komwe timakuganizira kuti nkwabwino (ndi kutichotsako kunka nafe ku njira yopotoka).
અરબી તફસીરો:
قَالُواْ بَل لَّمۡ تَكُونُواْ مُؤۡمِنِينَ
(Odzikweza) adzayankha: “Koma simudali okhulupirira.”
અરબી તફસીરો:
وَمَا كَانَ لَنَا عَلَيۡكُم مِّن سُلۡطَٰنِۭۖ بَلۡ كُنتُمۡ قَوۡمٗا طَٰغِينَ
“Ndipo tidalibe nyonga zokuponderezerani inu, koma mudali anthu opyola malire (ndi kutuluka ku choonadi cha Allah).”
અરબી તફસીરો:
فَحَقَّ عَلَيۡنَا قَوۡلُ رَبِّنَآۖ إِنَّا لَذَآئِقُونَ
“Choncho mawu a Mbuye wathu (onena za chilango) atsimikizika pa ife; ndithu ife tichilawa (chilango).”
અરબી તફસીરો:
فَأَغۡوَيۡنَٰكُمۡ إِنَّا كُنَّا غَٰوِينَ
“Tidakusokeretsani; nafenso tidali osokera. (Choncho musatidzudzule).”
અરબી તફસીરો:
فَإِنَّهُمۡ يَوۡمَئِذٖ فِي ٱلۡعَذَابِ مُشۡتَرِكُونَ
Ndithu iwo akathandizana chilango tsiku limenelo (la chiweruziro).
અરબી તફસીરો:
إِنَّا كَذَٰلِكَ نَفۡعَلُ بِٱلۡمُجۡرِمِينَ
Ndithu (chilango chonga chimenecho) ndimomwe timawachitira olakwira (Allah).
અરબી તફસીરો:
إِنَّهُمۡ كَانُوٓاْ إِذَا قِيلَ لَهُمۡ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا ٱللَّهُ يَسۡتَكۡبِرُونَ
Ndithu iwo ankati akauzidwa kuti palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Allah ankadzitukumula.
અરબી તફસીરો:
وَيَقُولُونَ أَئِنَّا لَتَارِكُوٓاْ ءَالِهَتِنَا لِشَاعِرٖ مَّجۡنُونِۭ
Ndipo ankanena: “Kodi ife tisiye kupembedza milungu yathu chifukwa cha zonena za mlakatuli, wopenga?”
અરબી તફસીરો:
بَلۡ جَآءَ بِٱلۡحَقِّ وَصَدَّقَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Iyayi koma adawadzera ndi choonadi (Mthenga wawo Muhammad yemwe siwamisala kapena wolakatula zopeka) ndipo adawatsimikizira za atumiki.
અરબી તફસીરો:
إِنَّكُمۡ لَذَآئِقُواْ ٱلۡعَذَابِ ٱلۡأَلِيمِ
Ndithu inu (osakhulupirira) mudzalawa chilango chowawa.
અરબી તફસીરો:
وَمَا تُجۡزَوۡنَ إِلَّا مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Ndipo simudzalipidwa kupatula zokhazo zimene mumachita.
અરબી તફસીરો:
إِلَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ
Kupatula akapolo a Allah oyeretsedwa.
અરબી તફસીરો:
أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ رِزۡقٞ مَّعۡلُومٞ
Kwa iwo kuli zopatsidwa zodziwika (ndi Mbuye wawo Allah),
અરબી તફસીરો:
فَوَٰكِهُ وَهُم مُّكۡرَمُونَ
Zipatso (zamtundu uliwonse); ndipo iwo adzalandira ulemu (waukulu),
અરબી તફસીરો:
فِي جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ
M’minda ya mtendere.
અરબી તફસીરો:
عَلَىٰ سُرُرٖ مُّتَقَٰبِلِينَ
Adzakhala pa makama (a mtengo wapatali) uku akuyang’anizana.
અરબી તફસીરો:
يُطَافُ عَلَيۡهِم بِكَأۡسٖ مِّن مَّعِينِۭ
Uku zikuwazungulira zikho zodzazidwa ndi zakumwa zochokera m’kasupe woyenda nthawi zonse.
અરબી તફસીરો:
بَيۡضَآءَ لَذَّةٖ لِّلشَّٰرِبِينَ
Woyera, wokoma kwa akumwa (zakumwazo).
અરબી તફસીરો:
لَا فِيهَا غَوۡلٞ وَلَا هُمۡ عَنۡهَا يُنزَفُونَ
(M’zakumwazo) mulibe zopweteketsa mutu (kwa ozimwa) ndiponso iwo sadzaledzera nazo.
અરબી તફસીરો:
وَعِندَهُمۡ قَٰصِرَٰتُ ٱلطَّرۡفِ عِينٞ
Ndipo kwa iwo kudzakhala akazi oyang’ana iwo okha, ophanuka maso (okongola).
અરબી તફસીરો:
كَأَنَّهُنَّ بَيۡضٞ مَّكۡنُونٞ
Onga ngati dzira (la nthiwatiwa) losungidwa (m’mapiko).
અરબી તફસીરો:
فَأَقۡبَلَ بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖ يَتَسَآءَلُونَ
Ndipo adzayang’anizana ndi kuyamba kufunsana (pakati pawo.)
અરબી તફસીરો:
قَالَ قَآئِلٞ مِّنۡهُمۡ إِنِّي كَانَ لِي قَرِينٞ
Adzanena wonena mmodzi wa iwo: “Ine ndidali ndi mnzanga (wopembedza mafano amene amatsutsana nane za chipembedzo ndi zophunzitsa za Qur’an yolemekezeka).”
અરબી તફસીરો:
يَقُولُ أَءِنَّكَ لَمِنَ ٱلۡمُصَدِّقِينَ
Yemwe amandiuza: “Kodi iwe ndiwe mmodzi wa ovomereza?”
અરબી તફસીરો:
أَءِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابٗا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَدِينُونَ
“Zakuti tikadzafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, (tidzaukanso) ndi kulandira malipiro (pa zochita zathu)?”
અરબી તફસીરો:
قَالَ هَلۡ أَنتُم مُّطَّلِعُونَ
(Wokhulupirira) adzanena (kwa anzake: “Inu anthu a kumtendere) kodi simungasuzumire (nane ku moto kuti timuone)?”
અરબી તફસીરો:
فَٱطَّلَعَ فَرَءَاهُ فِي سَوَآءِ ٱلۡجَحِيمِ
Choncho adzayang’ana ndipo adzamuona ali mkatikati mwa moto.
અરબી તફસીરો:
قَالَ تَٱللَّهِ إِن كِدتَّ لَتُرۡدِينِ
Adzanena: “Ndikulumbilira Allah! Udatsala pang’ono kuti undiononge (ndikadakuvomera paja pa dziko lapansi).”
અરબી તફસીરો:
وَلَوۡلَا نِعۡمَةُ رَبِّي لَكُنتُ مِنَ ٱلۡمُحۡضَرِينَ
“Ndipo pakadapanda chisomo cha Mbuye wanga, ndikadakhala mmodzi mwa opezeka ku Moto.”
અરબી તફસીરો:
أَفَمَا نَحۡنُ بِمَيِّتِينَ
“Kodi zili choncho kuti sitidzafanso (tizingosangalala m’Munda wamtendere).”
અરબી તફસીરો:
إِلَّا مَوۡتَتَنَا ٱلۡأُولَىٰ وَمَا نَحۡنُ بِمُعَذَّبِينَ
“Kupatula imfa yathu yoyamba ija, ndi kutinso ife sitilangidwa?”
અરબી તફસીરો:
إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ
Ndithu izi (zimene Allah waika m’Munda wamtendere) ndiko kupambana kwakukulu.
અરબી તફસીરો:
لِمِثۡلِ هَٰذَا فَلۡيَعۡمَلِ ٱلۡعَٰمِلُونَ
(Pofuna kupeza) zonga zimenezi ogwira ntchito agwire.
અરબી તફસીરો:
أَذَٰلِكَ خَيۡرٞ نُّزُلًا أَمۡ شَجَرَةُ ٱلزَّقُّومِ
Kodi zimenezo ndilo phwando labwino kapena mtengo wa Zaqqum (wowawa kwambiri womwe anthu a ku Moto azikadya)?
અરબી તફસીરો:
إِنَّا جَعَلۡنَٰهَا فِتۡنَةٗ لِّلظَّٰلِمِينَ
Ndithu Ife taupanga (mtengo umenewu) kukhala mayeso ndi chilango cha anthu ochimwa (podzichitira okha chinyengo ndi kupembedza mafano.)
અરબી તફસીરો:
إِنَّهَا شَجَرَةٞ تَخۡرُجُ فِيٓ أَصۡلِ ٱلۡجَحِيمِ
Umenewu ndimtengo omwe umatuluka pakatikati pa Jahannam (adaulenga kuchokera ku Moto).
અરબી તફસીરો:
طَلۡعُهَا كَأَنَّهُۥ رُءُوسُ ٱلشَّيَٰطِينِ
Zipatso zake (nzoipa) ngati mitu ya asatana.
અરબી તફસીરો:
فَإِنَّهُمۡ لَأٓكِلُونَ مِنۡهَا فَمَالِـُٔونَ مِنۡهَا ٱلۡبُطُونَ
Ndithu iwo akadya mtengowo ndi kudzaza mimba zawo ndi zipatso zake (pakuti sakapeza chakudya china kupatula zipatso za mtengowo).
અરબી તફસીરો:
ثُمَّ إِنَّ لَهُمۡ عَلَيۡهَا لَشَوۡبٗا مِّنۡ حَمِيمٖ
Kenako, ndithu kuwawa kwa mtengowo kosakanikirana ndi madzi owira kuzakhala pa iwo.
અરબી તફસીરો:
ثُمَّ إِنَّ مَرۡجِعَهُمۡ لَإِلَى ٱلۡجَحِيمِ
Kenako ndithu kobwerera kwawo ndi ku Jahannam.
અરબી તફસીરો:
إِنَّهُمۡ أَلۡفَوۡاْ ءَابَآءَهُمۡ ضَآلِّينَ
Ndithu iwo adapeza makolo awo ali osokera.
અરબી તફસીરો:
فَهُمۡ عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِمۡ يُهۡرَعُونَ
Ndipo iwonso adatsata mapazi awo mothamanga.
અરબી તફસીરો:
وَلَقَدۡ ضَلَّ قَبۡلَهُمۡ أَكۡثَرُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Ndipo, ndithu akale ambiri adasokera patsogolo pawo.
અરબી તફસીરો:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا فِيهِم مُّنذِرِينَ
Ndipo, ndithu tidatuma achenjezi kwa iwo.
અરબી તફસીરો:
فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُنذَرِينَ
Tapenya momwe adalili mapeto a omwe adachenjezedwa.
અરબી તફસીરો:
إِلَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ
Kupatula akapolo a Allah, oyeretsedwa (iwo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere).
અરબી તફસીરો:
وَلَقَدۡ نَادَىٰنَا نُوحٞ فَلَنِعۡمَ ٱلۡمُجِيبُونَ
Ndithu Nuh adatiitana, (ndipo tidamuyankha mayankho abwino), taonani kukhala bwino Ife Oyankha.
અરબી તફસીરો:
وَنَجَّيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥ مِنَ ٱلۡكَرۡبِ ٱلۡعَظِيمِ
Ndipo tidampulumutsa iye ndi anthu ake ku vuto lalikulu.
અરબી તફસીરો:
وَجَعَلۡنَا ذُرِّيَّتَهُۥ هُمُ ٱلۡبَاقِينَ
Ndipo tidazichita zidzukulu zake kukhala zotsala (pa dziko, oipa ataonongeka).
અરબી તફસીરો:
وَتَرَكۡنَا عَلَيۡهِ فِي ٱلۡأٓخِرِينَ
Ndipo tidamsiira mbiri yabwino kwa mibadwo yodza pambuyo pake.
અરબી તફસીરો:
سَلَٰمٌ عَلَىٰ نُوحٖ فِي ٱلۡعَٰلَمِينَ
Mtendere ukhale pa Nuh pa zolengedwa zonse.
અરબી તફસીરો:
إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ
Ndithu umu ndimomwe Ife tilipirira ochita zabwino.
અરબી તફસીરો:
إِنَّهُۥ مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndithu iye ndi mmodzi mwa akapolo Athu okhulupirira.
અરબી તફસીરો:
ثُمَّ أَغۡرَقۡنَا ٱلۡأٓخَرِينَ
Kenako tidawamiza enawo.
અરબી તફસીરો:
۞ وَإِنَّ مِن شِيعَتِهِۦ لَإِبۡرَٰهِيمَ
Ndipo ndithu m’gulu lake (la Nuh) muli Ibrahim.
અરબી તફસીરો:
إِذۡ جَآءَ رَبَّهُۥ بِقَلۡبٖ سَلِيمٍ
Kumbuka pamene adadza kwa Mbuye wake ndi mtima wabwino (wogonjera malamulo).
અરબી તફસીરો:
إِذۡ قَالَ لِأَبِيهِ وَقَوۡمِهِۦ مَاذَا تَعۡبُدُونَ
Pomwe adanena kwa bambo wake ndi anthu ake: “Mukupembedza chiyani?”
અરબી તફસીરો:
أَئِفۡكًا ءَالِهَةٗ دُونَ ٱللَّهِ تُرِيدُونَ
“Ha! Milungu yopeka kusiya Allah, ndi imene mukuifuna?”
અરબી તફસીરો:
فَمَا ظَنُّكُم بِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
“Kodi maganizo anu ngotani pa Mbuye wa zolengedwa zonse?”
અરબી તફસીરો:
فَنَظَرَ نَظۡرَةٗ فِي ٱلنُّجُومِ
Ndipo adayang’ana nyenyezi mozama.
અરબી તફસીરો:
فَقَالَ إِنِّي سَقِيمٞ
Ndipo adanena: “Ine ndine wodwala!”
અરબી તફસીરો:
فَتَوَلَّوۡاْ عَنۡهُ مُدۡبِرِينَ
Choncho iwo adatembenuka ndi kumsiya.
અરબી તફસીરો:
فَرَاغَ إِلَىٰٓ ءَالِهَتِهِمۡ فَقَالَ أَلَا تَأۡكُلُونَ
(Ibrahim) adapita mozemba ku mafano awo, ndipo adawauza (mwachipongwe:) “Bwanji simukudya (chakudya chomwe chaikidwa patsogolo panupo)?”
અરબી તફસીરો:
مَا لَكُمۡ لَا تَنطِقُونَ
“Bwanji simukuyankhula?”
અરબી તફસીરો:
فَرَاغَ عَلَيۡهِمۡ ضَرۡبَۢا بِٱلۡيَمِينِ
Atatero adawatembenukira ndi kuwamenya (mwamphamvu) ndi dzanja lamanja.
અરબી તફસીરો:
فَأَقۡبَلُوٓاْ إِلَيۡهِ يَزِفُّونَ
(Pamene adamva eni mafanowo) adadza kwa iye akuthamanga.
અરબી તફસીરો:
قَالَ أَتَعۡبُدُونَ مَا تَنۡحِتُونَ
Anati: “Kodi mukupembedza (miyala) imene mwasema?”
અરબી તફસીરો:
وَٱللَّهُ خَلَقَكُمۡ وَمَا تَعۡمَلُونَ
“Chikhalirecho Allah ndiye adakulengani ndi zimene mukuchita!”
અરબી તફસીરો:
قَالُواْ ٱبۡنُواْ لَهُۥ بُنۡيَٰنٗا فَأَلۡقُوهُ فِي ٱلۡجَحِيمِ
Iwo adati: “Mmangireni ng’anjo, ndipo mponyeni m’motowo.”
અરબી તફસીરો:
فَأَرَادُواْ بِهِۦ كَيۡدٗا فَجَعَلۡنَٰهُمُ ٱلۡأَسۡفَلِينَ
Adafuna kumchita chiwembu (kuti amuphe ndi moto), koma tidawachita kukhala onyozeka.
અરબી તફસીરો:
وَقَالَ إِنِّي ذَاهِبٌ إِلَىٰ رَبِّي سَيَهۡدِينِ
Ndipo (Ibrahim) adati: “Ndithu ine ndikupita kwa Mbuye wanga, Iye andiongolera.”
અરબી તફસીરો:
رَبِّ هَبۡ لِي مِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ
“E Mbuye wanga! Ndipatseni mwana yemwe adzakhale (mmodzi) mwa olungama!”
અરબી તફસીરો:
فَبَشَّرۡنَٰهُ بِغُلَٰمٍ حَلِيمٖ
Ndipo tidamuuza nkhani yabwino ya mwana wofatsa, (mwanayo ndi Ismaila).
અરબી તફસીરો:
فَلَمَّا بَلَغَ مَعَهُ ٱلسَّعۡيَ قَالَ يَٰبُنَيَّ إِنِّيٓ أَرَىٰ فِي ٱلۡمَنَامِ أَنِّيٓ أَذۡبَحُكَ فَٱنظُرۡ مَاذَا تَرَىٰۚ قَالَ يَٰٓأَبَتِ ٱفۡعَلۡ مَا تُؤۡمَرُۖ سَتَجِدُنِيٓ إِن شَآءَ ٱللَّهُ مِنَ ٱلصَّٰبِرِينَ
Ndipo (adabadwa ndi kuyamba kukula.) Pamene adakwana nsinkhu woyenda pamodzi ndi tate wake pochitachita za m’dziko (Ibrahim adayesedwa mayeso kupyolera m’maloto omwe adalota). Adati: “E mwana wanga! Ine kutulo ndikuona maloto (owona ochokera kwa Allah omwe akundilamula) kuti ndikuzinge (monga nsembe yopereka kwa Allah). Nanga ukuti bwanji?” (Mwana wabwino) adanena: “Bambo wanga! Kwaniritsani chimene mukulamulidwa. Ngati Allah afuna, mundipeza ndili mmodzi mwa opirira.”
અરબી તફસીરો:
فَلَمَّآ أَسۡلَمَا وَتَلَّهُۥ لِلۡجَبِينِ
Pamene adagonjera onse awiri (chofuna cha Allah), ndipo (Ibrahim) adam’goneka chakumphumi (ndipo adatsimikiza kumupha).
અરબી તફસીરો:
وَنَٰدَيۡنَٰهُ أَن يَٰٓإِبۡرَٰهِيمُ
Ndipo tidamuitana: “E iwe Ibrahim!”
અરબી તફસીરો:
قَدۡ صَدَّقۡتَ ٱلرُّءۡيَآۚ إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ
“Ndithu wavomereza maloto! (Choncho usamuphe mwana wakoyo).” Umo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino.
અરબી તફસીરો:
إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ ٱلۡبَلَٰٓؤُاْ ٱلۡمُبِينُ
Ndithu amenewa ndimayeso oonekera.
અરબી તફસીરો:
وَفَدَيۡنَٰهُ بِذِبۡحٍ عَظِيمٖ
Ndipo tidampulumutsa pompatsa nyama yayikulu (yoti apereke nsembe).
અરબી તફસીરો:
وَتَرَكۡنَا عَلَيۡهِ فِي ٱلۡأٓخِرِينَ
Ndipo tidamsiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pake).
અરબી તફસીરો:
سَلَٰمٌ عَلَىٰٓ إِبۡرَٰهِيمَ
Mtendere ukhale pa Ibrahim!
અરબી તફસીરો:
كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ
M’menemo ndi mornwe timawalipirira ochita zabwino.
અરબી તફસીરો:
إِنَّهُۥ مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndithu iye adali mmodzi mwa akapolo Athu okhulupirira.
અરબી તફસીરો:
وَبَشَّرۡنَٰهُ بِإِسۡحَٰقَ نَبِيّٗا مِّنَ ٱلصَّٰلِحِينَ
Ndiponso tidamuuza nkhani yabwino (yoti akhala ndi mwana wotchedwa) Isihaqa; mneneri; wam’gulu la olungama.
અરબી તફસીરો:
وَبَٰرَكۡنَا عَلَيۡهِ وَعَلَىٰٓ إِسۡحَٰقَۚ وَمِن ذُرِّيَّتِهِمَا مُحۡسِنٞ وَظَالِمٞ لِّنَفۡسِهِۦ مُبِينٞ
Ndipo tidamdalitsa iye ndi (mwana wake) Isihaqa; ndipo m’mbumba ya awiriwa mudapezeka abwino ndi odzichitira zoipa owonekera.
અરબી તફસીરો:
وَلَقَدۡ مَنَنَّا عَلَىٰ مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ
Ndipo ndithu tidawachitira zabwino Mûsa ndi Haruna, (powapatsa uneneri ndi madalitso ambiri).
અરબી તફસીરો:
وَنَجَّيۡنَٰهُمَا وَقَوۡمَهُمَا مِنَ ٱلۡكَرۡبِ ٱلۡعَظِيمِ
Ndipo tidawapulumutsa (awiriwa) ndi anthu awo ku vuto lalikulu.
અરબી તફસીરો:
وَنَصَرۡنَٰهُمۡ فَكَانُواْ هُمُ ٱلۡغَٰلِبِينَ
Ndipo tidawathangata (powagonjetsera adani awo), ndipo iwo adali opambana.
અરબી તફસીરો:
وَءَاتَيۡنَٰهُمَا ٱلۡكِتَٰبَ ٱلۡمُسۡتَبِينَ
Ndipo tidawapatsa (Mûsa ndi Haruna) buku losonyeza poyera (malamulo).
અરબી તફસીરો:
وَهَدَيۡنَٰهُمَا ٱلصِّرَٰطَ ٱلۡمُسۡتَقِيمَ
Ndipo tidawaongolera ku njira yolunjika.
અરબી તફસીરો:
وَتَرَكۡنَا عَلَيۡهِمَا فِي ٱلۡأٓخِرِينَ
Ndiponso tidawasiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pawo).
અરબી તફસીરો:
سَلَٰمٌ عَلَىٰ مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ
Mtendere ukhale pa Mûsa ndi Haruna!
અરબી તફસીરો:
إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ
Ndithu umu ndi momwe Ife timawalipirira ochita zabwino.
અરબી તફસીરો:
إِنَّهُمَا مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndithu awiriwa adali m’gulu la akapoio Athu okhulupirira.
અરબી તફસીરો:
وَإِنَّ إِلۡيَاسَ لَمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Ndipo ndithu Iliyasa ndi mmodzi wa atumiki.
અરબી તફસીરો:
إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِۦٓ أَلَا تَتَّقُونَ
(Kumbuka) pamene adanena kwa anthu ake: “Bwanji simuopa (Allah)?”
અરબી તફસીરો:
أَتَدۡعُونَ بَعۡلٗا وَتَذَرُونَ أَحۡسَنَ ٱلۡخَٰلِقِينَ
“Mukupembedza (fano lotchedwa) Ba’la ndi kusiya (kupembedza) Wabwino zedi mwa olenga onse.”
અરબી તફસીરો:
ٱللَّهَ رَبَّكُمۡ وَرَبَّ ءَابَآئِكُمُ ٱلۡأَوَّلِينَ
“Allah, Mbuye wanu ndi Mbuye wa makolo anu akale?”
અરબી તફસીરો:
فَكَذَّبُوهُ فَإِنَّهُمۡ لَمُحۡضَرُونَ
Koma adamtsutsa; ndithu iwo adzaonekera (ku Moto).
અરબી તફસીરો:
إِلَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ
Kupatula akapolo a Allah amene ayeretsedwa (ndi Allah).
અરબી તફસીરો:
وَتَرَكۡنَا عَلَيۡهِ فِي ٱلۡأٓخِرِينَ
Ndipo tidamsiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pake).
અરબી તફસીરો:
سَلَٰمٌ عَلَىٰٓ إِلۡ يَاسِينَ
Mtendere ukhale pa Iliyasiin!
અરબી તફસીરો:
إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ
Ndithu umo ndi mmene Ife timawalipirira ochita zabwino.
અરબી તફસીરો:
إِنَّهُۥ مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndithu iye ndimmodzi mwa akapolo Athu okhulupirira.
અરબી તફસીરો:
وَإِنَّ لُوطٗا لَّمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Ndithu Luti ndi mmodzi wa atumiki.
અરબી તફસીરો:
إِذۡ نَجَّيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥٓ أَجۡمَعِينَ
(Kumbuka) pamene tidampulumutsa iye ndi anthu ake onse.
અરબી તફસીરો:
إِلَّا عَجُوزٗا فِي ٱلۡغَٰبِرِينَ
Kupatula nkhalamba yachikazi; idali mwa otsalira.
અરબી તફસીરો:
ثُمَّ دَمَّرۡنَا ٱلۡأٓخَرِينَ
Kenako tidawaononga enawo (omwe adali oipa).
અરબી તફસીરો:
وَإِنَّكُمۡ لَتَمُرُّونَ عَلَيۡهِم مُّصۡبِحِينَ
Ndithu inu (a mumzinda wa Makka) mumadutsa pa malo pawopo m’mawa,
અરબી તફસીરો:
وَبِٱلَّيۡلِۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ
Ndi usiku. Kodi bwanji simuzindikira?
અરબી તફસીરો:
وَإِنَّ يُونُسَ لَمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Ndithu Yunusu ndi mmodzi wa atumiki.
અરબી તફસીરો:
إِذۡ أَبَقَ إِلَى ٱلۡفُلۡكِ ٱلۡمَشۡحُونِ
(Kumbuka) pamene adathawira m’chombo chodzazidwa (ndi katundu).
અરબી તફસીરો:
فَسَاهَمَ فَكَانَ مِنَ ٱلۡمُدۡحَضِينَ
Choncho adachita mayere, ndipo adali m’gulu la omgwera (mayerewo).
અરબી તફસીરો:
فَٱلۡتَقَمَهُ ٱلۡحُوتُ وَهُوَ مُلِيمٞ
Choncho nsomba idammeza uku ali wodzudzulidwa.
અરબી તફસીરો:
فَلَوۡلَآ أَنَّهُۥ كَانَ مِنَ ٱلۡمُسَبِّحِينَ
Kukadapanda kuti iye adali m’modzi mwa otamanda ndi kulemekeza Allah).
અરબી તફસીરો:
لَلَبِثَ فِي بَطۡنِهِۦٓ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ
Akadakhala m’mimba mwake mpaka tsiku loukitsidwa (zolengedwa ku imfa).
અરબી તફસીરો:
۞ فَنَبَذۡنَٰهُ بِٱلۡعَرَآءِ وَهُوَ سَقِيمٞ
Koma tidamponya pa gombe uku ali wodwala.
અરબી તફસીરો:
وَأَنۢبَتۡنَا عَلَيۡهِ شَجَرَةٗ مِّن يَقۡطِينٖ
Ndipo tidammeretsera mmera wa mtundu wa nkhaka.
અરબી તફસીરો:
وَأَرۡسَلۡنَٰهُ إِلَىٰ مِاْئَةِ أَلۡفٍ أَوۡ يَزِيدُونَ
Ndipo (atachira) tidamtuma ku anthu okwana zikwi zana limodzi (100,000) kapena kupambana apa.
અરબી તફસીરો:
فَـَٔامَنُواْ فَمَتَّعۡنَٰهُمۡ إِلَىٰ حِينٖ
Ndipo adakhulupirira (ndi kuvomereza ulaliki wake); choncho tidawapatsa chisangalalo kufikira nthawi (ya imfa yawo).
અરબી તફસીરો:
فَٱسۡتَفۡتِهِمۡ أَلِرَبِّكَ ٱلۡبَنَاتُ وَلَهُمُ ٱلۡبَنُونَ
Choncho afunse: “Kodi Mbuye wako ndiye woyenera ana aakazi, ndipo iwo aamuna? (Pomwe iwo akabereka mwana wamkazi amanyansidwa naye)!”
અરબી તફસીરો:
أَمۡ خَلَقۡنَا ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ إِنَٰثٗا وَهُمۡ شَٰهِدُونَ
Kapena kuti tidalenga angelo kukhala akazi, iwo akuona?
અરબી તફસીરો:
أَلَآ إِنَّهُم مِّنۡ إِفۡكِهِمۡ لَيَقُولُونَ
Chenjera ndi bodza lawolo, ndithu iwo akunena:
અરબી તફસીરો:
وَلَدَ ٱللَّهُ وَإِنَّهُمۡ لَكَٰذِبُونَ
“Allah wabereka.” Ndithu iwo ndi abodza.
અરબી તફસીરો:
أَصۡطَفَى ٱلۡبَنَاتِ عَلَى ٱلۡبَنِينَ
Kodi Iye adasankha ana aakazi kusiya aamuna?
અરબી તફસીરો:
مَا لَكُمۡ كَيۡفَ تَحۡكُمُونَ
Kodi nchiyani chakupezani (kuti muweruze mopanda chilungamo); nanga mukuweruza bwanji (zimenezi)?
અરબી તફસીરો:
أَفَلَا تَذَكَّرُونَ
Kodi bwanji simukumbukira, (mwaiwala zisonyezo Zake zodabwitsa ndi kupatukana kwake ndi zimenezo)?
અરબી તફસીરો:
أَمۡ لَكُمۡ سُلۡطَٰنٞ مُّبِينٞ
Kapena inu muli ndi umboni woonekera (wochokera kumwamba)?
અરબી તફસીરો:
فَأۡتُواْ بِكِتَٰبِكُمۡ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Tabweretsani buku lanulo (momwe mwalembedwa zimenezi) ngati mukunena zoona.
અરબી તફસીરો:
وَجَعَلُواْ بَيۡنَهُۥ وَبَيۡنَ ٱلۡجِنَّةِ نَسَبٗاۚ وَلَقَدۡ عَلِمَتِ ٱلۡجِنَّةُ إِنَّهُمۡ لَمُحۡضَرُونَ
Ndipo adapeka chibale pakati pa Iye (Allah) ndi ziwanda; (pomwe ziwanda nzobisika kwa iwo). Ndithu ziwanda zimadziwa kuti iwo osakhulupirira akaonekera (kwa Allah kuti aweruzidwe)!
અરબી તફસીરો:
سُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ عَمَّا يَصِفُونَ
Walemekezeka Allah! Ndi kupatukana ndi zimene akumnamizira!
અરબી તફસીરો:
إِلَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ
Koma akapolo a Allah oyeretsedwa (ali kutali ndi zimene akusimba osakhulupirirazi).
અરબી તફસીરો:
فَإِنَّكُمۡ وَمَا تَعۡبُدُونَ
Ndithu inu (osakhulupirira) ndi zimene mukuzipembedza (kusiya Allah),
અરબી તફસીરો:
مَآ أَنتُمۡ عَلَيۡهِ بِفَٰتِنِينَ
Ndi zimenezo simungamsokeretse aliyense.
અરબી તફસીરો:
إِلَّا مَنۡ هُوَ صَالِ ٱلۡجَحِيمِ
Kupatula yemwe (Allah adadziwa kuti) ngolowa ku Jahannam.
અરબી તફસીરો:
وَمَا مِنَّآ إِلَّا لَهُۥ مَقَامٞ مَّعۡلُومٞ
Ndipo (angelo adanena): “Aliyense mwa ife ali ndi malo ake odziwika.”
અરબી તફસીરો:
وَإِنَّا لَنَحۡنُ ٱلصَّآفُّونَ
“Ndipo ndithu (ena mwa) ife ngondanda m’mizere (ya mapemphero nthawi zonse).”
અરબી તફસીરો:
وَإِنَّا لَنَحۡنُ ٱلۡمُسَبِّحُونَ
“Ndipo (ena mwa) ife ngolemekeza (Allah nthawi zonse ndi kumtamanda ndi kumpatula ku zinthu zosayenerana ndi ulemelero wake).”
અરબી તફસીરો:
وَإِن كَانُواْ لَيَقُولُونَ
Ndipo (osakhulupirira) ankati:
અરબી તફસીરો:
لَوۡ أَنَّ عِندَنَا ذِكۡرٗا مِّنَ ٱلۡأَوَّلِينَ
“Tikadakhala ndi buku monga lomwe anthu akale adali nalo.”
અરબી તફસીરો:
لَكُنَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ
“Tikadakhala akapolo a Allah, oyeretsedwa.”
અરબી તફસીરો:
فَكَفَرُواْ بِهِۦۖ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ
Koma (pamene lidawadzera bukulo), adalikana; choncho posachedwa adziwa (zotsatira zake).
અરબી તફસીરો:
وَلَقَدۡ سَبَقَتۡ كَلِمَتُنَا لِعِبَادِنَا ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Ndipo ndithu liwu lathu lidatsogola kwa akapolo athu otumidwa.
અરબી તફસીરો:
إِنَّهُمۡ لَهُمُ ٱلۡمَنصُورُونَ
(Kuti) ndithu iwo ngopulumutsidwa.
અરબી તફસીરો:
وَإِنَّ جُندَنَا لَهُمُ ٱلۡغَٰلِبُونَ
Ndipo ndithu asilikali Athu ndi opambana.
અરબી તફસીરો:
فَتَوَلَّ عَنۡهُمۡ حَتَّىٰ حِينٖ
Choncho, asiye kwa kanthawi kochepa.
અરબી તફસીરો:
وَأَبۡصِرۡهُمۡ فَسَوۡفَ يُبۡصِرُونَ
Ndipo ingowayang’ana basi; posachedwapa aona!
અરબી તફસીરો:
أَفَبِعَذَابِنَا يَسۡتَعۡجِلُونَ
Kodi chilango chathu akuchifulumizitsa?
અરબી તફસીરો:
فَإِذَا نَزَلَ بِسَاحَتِهِمۡ فَسَآءَ صَبَاحُ ٱلۡمُنذَرِينَ
Choncho chikadzatsika pabwalo lawo, udzakhala mmawa woipa kwa ochenjezedwa!
અરબી તફસીરો:
وَتَوَلَّ عَنۡهُمۡ حَتَّىٰ حِينٖ
Ndipo asiye kwa kanthawi kochepa.
અરબી તફસીરો:
وَأَبۡصِرۡ فَسَوۡفَ يُبۡصِرُونَ
Ndipo ingowayang’ana basi; posachedwapa aona.
અરબી તફસીરો:
سُبۡحَٰنَ رَبِّكَ رَبِّ ٱلۡعِزَّةِ عَمَّا يَصِفُونَ
Mbuye wako, Mwini ulemelero, wapatukana ndi zimene akumnamizira (osakhulupirira).
અરબી તફસીરો:
وَسَلَٰمٌ عَلَى ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Ndipo mtendere ukhale pa atumiki onse.
અરબી તફસીરો:
وَٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Ndipo kuyamikidwa konse nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa zonse.
અરબી તફસીરો:
 
શબ્દોનું ભાષાંતર સૂરહ: અસ્ સોફ્ફાત
સૂરહ માટે અનુક્રમણિકા પેજ નંબર
 
કુરઆન મજીદના શબ્દોનું ભાષાંતર - ચેવા ભાષાતર - ભાષાંતરોની અનુક્રમણિકા

ચેવા ભાષાતરમાં

બંધ કરો