કુરઆન મજીદના શબ્દોનું ભાષાંતર - ચેવા ભાષાતર * - ભાષાંતરોની અનુક્રમણિકા


શબ્દોનું ભાષાંતર સૂરહ: અત્ તકવીર   આયત:

અત્ તકવીર

إِذَا ٱلشَّمۡسُ كُوِّرَتۡ
Pamene dzuwa lidzakulungidwe (ndikuchotsedwa kuwala kwake),[388]
[388] Surah zambiri zimene zidavumbulutsidwa ku Makka zimanena zododometsa za tsiku lachimaliziro.
અરબી તફસીરો:
وَإِذَا ٱلنُّجُومُ ٱنكَدَرَتۡ
Ndi pamene nyenyezi zidzathothoke (ndi kuchoka dangalira lake),
અરબી તફસીરો:
وَإِذَا ٱلۡجِبَالُ سُيِّرَتۡ
Ndi pamene mapiri adzayendetsedwe (kuchoka mmalo mwake),[389]
[389] Tsiku limenelo mapiri adzakhala osalimba ngati thonje limene likungouluka ndi mphepo.
અરબી તફસીરો:
وَإِذَا ٱلۡعِشَارُ عُطِّلَتۡ
Ndi pamene ngamira zabere lamiyezi khumi zidzasiidwe (zopanda oziyang’anira),[390]
[390] Ngamira za bere ndi chuma cha mtengo wapatali kwa Aarabu. Akuuzidwa apa kuti tsiku limenelo adzazisiya osazilabadira konse.
અરબી તફસીરો:
وَإِذَا ٱلۡوُحُوشُ حُشِرَتۡ
Ndi pamene nyama za mtchire zidzasonkhanitsidwe pamodzi (kuchokera mmalo osiyanasiyana chifukwa chakuopsa kwakukulu kwa tsikulo),[391]
[391] Mwa zina zododometsa pa tsiku limenelo ndi nyama za mtchire kusonkhanitsidwa pamodzi popanda kumenyana kapena kudyana.
અરબી તફસીરો:
وَإِذَا ٱلۡبِحَارُ سُجِّرَتۡ
Ndi pamene nyanja zidzayatsidwe moto,
અરબી તફસીરો:
وَإِذَا ٱلنُّفُوسُ زُوِّجَتۡ
Ndi pamene mizimu idzalumikizidwe (ndi matupi ake),
અરબી તફસીરો:
وَإِذَا ٱلۡمَوۡءُۥدَةُ سُئِلَتۡ
Ndi pamene mwana wamkazi yemwe adaikidwa m’manda wamoyo adzafunsidwe,[392]
[392] (Ndime 8-9) Ma Ayah awiriwa akufotokoza momwe Aarabu adalili Usilamu usadabwere. Munthu ankati akapatsidwa mphatso ya mwana wa mkazi adali kukhumudwa ndi kudandaula kwambiri. Ankanena kuti asungwana ngopanda phindu ndipo kuti kudali kuononga zinthu pakumulera, kumudyetsa, ndi kumuveka. Ndipo akadzakhala wachiwerewere adzakhala manyazi aakulu kwa makolo ake. Pamene chidadza chisilamu chidathetsa mkhalidwewu. Ndipo apa Allah akutisonyeza kuti patsiku limenelo, la chiweruziro, mwana uja adaikidwa wa moyo, adzafunsidwa kuti adaphedwa ndi tchimo lanji. Iye adzayankha kuti sadachite tchimo lililonse koma adaphedwa mopanda chilungamo.
અરબી તફસીરો:
بِأَيِّ ذَنۢبٖ قُتِلَتۡ
Ndi tchimo lanji adaphedwera?
અરબી તફસીરો:
وَإِذَا ٱلصُّحُفُ نُشِرَتۡ
Ndi pamene makalata (momwe mudalembedwa zochita za aliyense) adzatambasulidwe ndi kugawidwa (kuti awerengedwe),[393]
[393] Awa ndi makalata achiwerengero momwe mwalembedwa zabwino za munthu ndi zoipa zake. Tsiku limenelo munthu aliyense adzapatsidwa yake kalata kuti aone iye mwini zoipa ndi zabwino zake.
અરબી તફસીરો:
وَإِذَا ٱلسَّمَآءُ كُشِطَتۡ
Ndi pamene thambo lidzayalulidwe (kuchoka mmalo mwake),
અરબી તફસીરો:
وَإِذَا ٱلۡجَحِيمُ سُعِّرَتۡ
Ndi pamene Jahena idzasonkhezeredwe mwamphamvu,[394]
[394] (Ndime12-13) Tsiku limenelo Jannah idzayandikitsidwa kwa ochita zabwino ndiponso Moto udzayandikitsidwa kwa ochita zoipa kuti aone kumalo kwake.
અરબી તફસીરો:
وَإِذَا ٱلۡجَنَّةُ أُزۡلِفَتۡ
Ndi pamene Jannah idzayandikitsidwe,
અરબી તફસીરો:
عَلِمَتۡ نَفۡسٞ مَّآ أَحۡضَرَتۡ
(Zikadzachitika zimenezi) mzimu uliwonse udzadziwa zimene wabweretsa (zabwino ndi zoipa).
અરબી તફસીરો:
فَلَآ أُقۡسِمُ بِٱلۡخُنَّسِ
Ndikulumbilira nyenyezi zimene zimabwerera masana ndi kutulukanso usiku.
અરબી તફસીરો:
ٱلۡجَوَارِ ٱلۡكُنَّسِ
Zomwe zimayenda kenako nkubisika,
અરબી તફસીરો:
وَٱلَّيۡلِ إِذَا عَسۡعَسَ
Ndi usiku pamene ukulowa.
અરબી તફસીરો:
وَٱلصُّبۡحِ إِذَا تَنَفَّسَ
Ndi m’mawa kukamacha;
અરબી તફસીરો:
إِنَّهُۥ لَقَوۡلُ رَسُولٖ كَرِيمٖ
Ndithu iyi (Qur’an) ndi liwu la mthenga wa Allah (Jibril) wolemekezeka,[395]
[395] (Ndime 19-20) Mthenga wolemekezeka womveredwa uko kumwamba ndi Jibril (Gabriele) yemwe ndi wamkulu wa angelo onse. Iye ndiyemwe adali kubweretsa Qur’an mwa lamulo la Allah kwa Mneneri Wake Muhammad (s.a.w). Ndipo ulemelero wa Qur’an ndi ulemelero wa Mneneri (s.a.w) chifukwa choti munthu wolemekezeka amamutumizira mthenga wolemekezekanso. Ndipo uthenga wabwino umapatsidwa kwa Mneneri wabwino woposa onse.
અરબી તફસીરો:
ذِي قُوَّةٍ عِندَ ذِي ٱلۡعَرۡشِ مَكِينٖ
Mwini mphamvu ndi mwini ulemelero kwa Mwini Arsh (Mpando wa chifumu),
અરબી તફસીરો:
مُّطَاعٖ ثَمَّ أَمِينٖ
Womveredwa kumeneko ndiponso wokhulupirika (pachivumbulutso).
અરબી તફસીરો:
وَمَا صَاحِبُكُم بِمَجۡنُونٖ
Ndipo m’bale wanuyu siwamisala ayi.[396]
[396] (Ndime 22-25) Anthu okanira pamene adasowa chonena kwa mneneri (s.a.w) adali kunena nkhani zabodza kuti Mtumiki (s.a.w) wapenga ndikuti zomwe akuyankhula sadapatsidwe ndi Jibril.
અરબી તફસીરો:
وَلَقَدۡ رَءَاهُ بِٱلۡأُفُقِ ٱلۡمُبِينِ
Ndithu ndikulumbira kuti (iye Mtumiki) (s.a.w) adamuona (Jibril) mchizimezime (chakum’mawa) chooneka bwino.
અરબી તફસીરો:
وَمَا هُوَ عَلَى ٱلۡغَيۡبِ بِضَنِينٖ
Ndipo sali iye (Mtumiki) waumbombo ndi chivumbulutso (koma amafikitsa zonse ndi kuziphunzitsa kwa anthu).
અરબી તફસીરો:
وَمَا هُوَ بِقَوۡلِ شَيۡطَٰنٖ رَّجِيمٖ
(Chivumbulutso chomwe chavumbulutsidwachi kwa iye) si mawu a satana wothamangitsidwa (mchifundo cha Allah);
અરબી તફસીરો:
فَأَيۡنَ تَذۡهَبُونَ
Nanga mukupita kuti?
અરબી તફસીરો:
إِنۡ هُوَ إِلَّا ذِكۡرٞ لِّلۡعَٰلَمِينَ
(Qur’ani) iyi sichina koma ndi chikumbutso cha zolengedwa zonse.
અરબી તફસીરો:
لِمَن شَآءَ مِنكُمۡ أَن يَسۡتَقِيمَ
Kwa yemwe mwa inu akufuna kuyenda mu njira yoongoka.
અરબી તફસીરો:
وَمَا تَشَآءُونَ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُ رَبُّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Ndipo simungafune chinthu mwa inu nokha pokhapokha atafuna Allah Mbuye wa zolengedwa zonse.
અરબી તફસીરો:
 
શબ્દોનું ભાષાંતર સૂરહ: અત્ તકવીર
સૂરહ માટે અનુક્રમણિકા પેજ નંબર
 
કુરઆન મજીદના શબ્દોનું ભાષાંતર - ચેવા ભાષાતર - ભાષાંતરોની અનુક્રમણિકા

ચેવા ભાષાતરમાં

બંધ કરો