クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 * - 対訳の目次


対訳 節: (153) 章: 雌牛章
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱسۡتَعِينُواْ بِٱلصَّبۡرِ وَٱلصَّلَوٰةِۚ إِنَّ ٱللَّهَ مَعَ ٱلصَّٰبِرِينَ
E inu amene mwakhulupirira! Dzithandizeni (pa zinthu zanu) popirira, ndi popemphera Swala. Ndithudi, Allah ali pamodzi ndi opirira. [7]
[7] M’ndimeyi Allah akulangiza Asilamu kuti akhale opilira pa masautso amtundu uliwonse amene akukumana nawo. Kupilira ndi chida chakuthwa chopambanitsa munthu ndi kugonjetsera masautso. Munthu wosapilira ndi zopweteka sangapambane pa zofuna zake. Allah akutilangizanso kuti tifunefune chithandizo pochulukitsa Swala chifukwa chakuti imalimbitsa mtima wa munthu pa masautso. Mtumiki (s.a.w) ankati masautso akamukhudza amachita changu kukapemphera Swala. Ndipo ankayankhula kuti: “Allah waupanga mpumulo wanga kukhala mkati mwa Swala.”
アラビア語 クルアーン注釈:
 
対訳 節: (153) 章: 雌牛章
章名の目次 ページ番号
 
クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - 対訳の目次

クルアーン・チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

閉じる