クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 * - 対訳の目次


対訳 節: (170) 章: 雌牛章
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ٱتَّبِعُواْ مَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ قَالُواْ بَلۡ نَتَّبِعُ مَآ أَلۡفَيۡنَا عَلَيۡهِ ءَابَآءَنَآۚ أَوَلَوۡ كَانَ ءَابَآؤُهُمۡ لَا يَعۡقِلُونَ شَيۡـٔٗا وَلَا يَهۡتَدُونَ
Ndipo kukanenedwa kwa iwo (kuti): “Tsatirani zimene Allah wavumbulutsa;” akunena: “Koma tikutsatira zimene tidawapeza nazo atate athu.” Kodi ngakhale kuti atate awo sadali kuzindikira chilichonse ndiponso sadali oongoka (awatsatirabe)?[12]
[12] Chikhulupiliro cha munthu kuti chikhale champhamvu ndi chopindula pafunika kuti achidziwe bwinobwino chimene akuchikhulupiliracho. Asangotsatira ndikuchikhulupilira chifukwa choti auje ndi auje adali kuchikhulupilira chimenecho. Zinthu zotere zimawasokeretsa anthu ambiri. Anthu ena amachikhulupilira chinthu chifukwa chakuti makolo awo adali kuchikhulupilira pomwe chinthucho chili chachabe.
Allah adatipatsa dalitso lanzeru kuti tizirigwilitsira ntchito pofuna choonadi cha zinthu, osati kumangotsatira ngati wakhungu.
アラビア語 クルアーン注釈:
 
対訳 節: (170) 章: 雌牛章
章名の目次 ページ番号
 
クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - 対訳の目次

クルアーン・チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

閉じる