《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 * - 译解目录


含义的翻译 章: 阿苏尔   段:

阿苏尔

وَٱلۡعَصۡرِ
Ndikuilumbilira nthawi.[480]
[480] Chinthu cha mtengo wapatali kwa munthu pa dziko lino ndi moyo wake. Choncho mphindi iliyonse imene akuigwiritsa ntchito pa zinthu zabwino ndiyo imene idzamuthandiza. Ndipo mphindi iliyonse imene akuigwiritsa ntchito mu zinthu zoipa kapena zopanda pake, kumeneko ndiko kutaika kwake; (kuluza).
阿拉伯语经注:
إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لَفِي خُسۡرٍ
Ndithu munthu aliyense ndi wotaika (chifukwa chakugonjetsedwa ndi zilakolako zake).
阿拉伯语经注:
إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَتَوَاصَوۡاْ بِٱلۡحَقِّ وَتَوَاصَوۡاْ بِٱلصَّبۡرِ
Kupatula amene akhulupirira (mwa Allah) ndi kumachita zabwino, ndikumalangizana kutsatira choona ndiponso ndi kumalangizana za kupirira (potsatira malamulo a Allah ndi zina za mdziko).[481]
[481] Mgulu la otaika mwapatulidwa anthu olungama amene zochita zawo zili zolungama, omwe amalamulira kutsatira njira yolungama ndi kupilira. Anthu otere saataika, chifukwa chakuti nthawi yawo amaigwiritsira ntchito pa zinthu zabwino, zowathandiza padziko ndi pambuyo pa imfa. Kupilira kulipo mitundu inayi:-
(a) Kupilira pochita zinthu zabwino zomwe zili zovuta kwa munthu kuzipitiriza, monga kupemphera Swala zisanu.
(b) Kupilira posiya kuchita zoipa zimene zili zovuta kwa munthu kuti azileke.
(c) Kuwapilira anthu anzako; kupilira ndi zoipa zawo posawabwezera choipa chilichonse.
(d) Kupilira ndi mazunzo a padziko, monga njala, matenda, kusauka ndi zina zotero.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 阿苏尔
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 译解目录

古兰经契瓦文译解,哈利德·伊布拉欣·比德拉翻译,2020年版

关闭