《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 * - 译解目录


含义的翻译 段: (256) 章: 拜格勒
لَآ إِكۡرَاهَ فِي ٱلدِّينِۖ قَد تَّبَيَّنَ ٱلرُّشۡدُ مِنَ ٱلۡغَيِّۚ فَمَن يَكۡفُرۡ بِٱلطَّٰغُوتِ وَيُؤۡمِنۢ بِٱللَّهِ فَقَدِ ٱسۡتَمۡسَكَ بِٱلۡعُرۡوَةِ ٱلۡوُثۡقَىٰ لَا ٱنفِصَامَ لَهَاۗ وَٱللَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٌ
Palibe kukakamiza (munthu kulowa) m’chipembedzo; kulungama kwaonekera poyera kusiyana ndi kusalungama. Choncho amene akumkana satana nakhulupirira Allah, ndiye kuti wagwira chigwiliro cholimba, chomwe sichisweka. Ndipo Allah Ngwakumva; Ngodziwa.[49]
[49] Arabu ena a mu Mzinda wa Madina, Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) asanasamukireko adali kutsata chipembedzo cha Chiyuda. Koma ambiri a iwo adali kupembedza mafano. Pamene chidadza Chisilamu pafupifupi onse omwe ankapembedza mafano adalowa m’ Chisilamu. Koma amene adali m’chipembedzo cha Chiyuda ndiochepa okha omwe adalowa m’Chisilamu. Ndipo ena ngakhale anali Arabu adatsalirabe m’chipembedzo cha Chiyuda. Choncho, omwe adali asilamu adafuna kukakamiza mwamphamvu amene adali m’chipembedzo cha Chiyuda kuti alowe m’Chisilamu. Koma Allah adawaletsa kuti palibe kumkakamiza kuti alowe m’Chisilamu yemwe sakufuna. Munthu aliyense adapatsidwa nzeru yomzindikiritsa chabwino ndi choipa. Ngati afuna kusokera nkufuna kwake iye mwini. Ndipo Allah adzamulanga pa tsiku lachimaliziro osati pano padziko lapansi.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 段: (256) 章: 拜格勒
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 译解目录

古兰经契瓦文译解,哈利德·伊布拉欣·比德拉翻译,2020年版

关闭