Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 塔哈   段:
وَأَنَا ٱخۡتَرۡتُكَ فَٱسۡتَمِعۡ لِمَا يُوحَىٰٓ
Ndipo Ine ndakusankha (kuti ukhale Mtumiki); choncho mvera zonse zomwe zikuvumbulutsidwa (kwa iwe).
阿拉伯语经注:
إِنَّنِيٓ أَنَا ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّآ أَنَا۠ فَٱعۡبُدۡنِي وَأَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ لِذِكۡرِيٓ
Ndithu Ine ndine Allah palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine; choncho ndipembeze, pemphera Swala moyenera pondikumbukira.
阿拉伯语经注:
إِنَّ ٱلسَّاعَةَ ءَاتِيَةٌ أَكَادُ أُخۡفِيهَا لِتُجۡزَىٰ كُلُّ نَفۡسِۭ بِمَا تَسۡعَىٰ
Ndithu nthawi ya tsiku lachimaliziro idza; (choncho ikonzekere ndi ntchito zabwino); ndikuibisa dala (kwa anthu) kuti mzimu uliwonse udzalipidwe zimene udachita.[274]
[274] Womasulira Qur’an adati cholinga chakubisa kudza kwa tsiku la chimaliziro, ndi nthawi ya imfa ya munthu ndikuti Allah wapamwambamwamba adalamula kuti sangavomereze kulapa tsiku la chimaliziro litadza, ndi nthawi ya imfa itamufikira munthu. Anthu akadadziwa nthawi yeniyeni ya chimaliziro ndi nthawi yakudza kwa imfa yawo, akadakhala akuchita zinthu zoyipa naakhala ndi chiyembekezero choti adzalapa nthawi ikayandikira, nadzapulumuka kuchilango cha Allah. Koma Allah anabisa zimenezo kuti anthu akhale tcheru nthawi zonse ndikukhala okonzekera za imfa ndi za tsiku la chimaliziro kuti zingawadzere modzidzimutsa.
阿拉伯语经注:
فَلَا يَصُدَّنَّكَ عَنۡهَا مَن لَّا يُؤۡمِنُ بِهَا وَٱتَّبَعَ هَوَىٰهُ فَتَرۡدَىٰ
Ndipo asakutsekereze (ku khulupirira) zimenezo yemwe saikhulupirira (Kiyamayo), ndipo akungotsata zilakolako za mtima wake; kuopa kuti Ungadzaonongeke.”
阿拉伯语经注:
وَمَا تِلۡكَ بِيَمِينِكَ يَٰمُوسَىٰ
“Kodi nchiyani icho chili kudzanja Lako ladzanjadzanja, iwe Mûsa?”
阿拉伯语经注:
قَالَ هِيَ عَصَايَ أَتَوَكَّؤُاْ عَلَيۡهَا وَأَهُشُّ بِهَا عَلَىٰ غَنَمِي وَلِيَ فِيهَا مَـَٔارِبُ أُخۡرَىٰ
(Mûsa) adati: “Iyi ndi ndodo yanga, ndimaitsamira (poyenda) ndi kuphopholera masamba a mbuzi zanga; ndiponso (m’ndodomo) muli zina zondithandiza.”[275]
[275] Womasulira adati yankho lakuti: “Iyi ndi ndodo yanga,” lidali yankho lokwana. Koma iye adaonjezera payankho mawu ena amene sadamufunse chifukwa chakuti pomwe adalipo padali pamalo poyenera kutambasula mawu pakuti Allah ndiye adali kuyankhula naye popanda mkhalapakati. Uku kudali kuti amve kukoma koyankhulana ndi Allah. Pajatu mawu a wokondedwa amatonthoza moyo ndipo amachotsa kutopa kwa mtundu uliwonse.
阿拉伯语经注:
قَالَ أَلۡقِهَا يَٰمُوسَىٰ
(Allah) adati: “Iponye iwe Mûsa!”
阿拉伯语经注:
فَأَلۡقَىٰهَا فَإِذَا هِيَ حَيَّةٞ تَسۡعَىٰ
Ndipo adaiponya; pompo idasanduka njoka yoyenda mothamanga. [276]
[276] Ibun Abbas adati ndodoyi idasanduka chinjoka chachimuna chomwe chidali kumeza miyala ndi mitengo. Pamene Musa adachiona chikumeza chilichonse adachiopa. Nkhaniyi ikupezeka m’buku la Qurtubi, volume 11, tsamba la 190.
阿拉伯语经注:
قَالَ خُذۡهَا وَلَا تَخَفۡۖ سَنُعِيدُهَا سِيرَتَهَا ٱلۡأُولَىٰ
(Allah) adati: “Igwire, usaope. Tiibwezera m’chikhalidwe chake Choyamba.”
阿拉伯语经注:
وَٱضۡمُمۡ يَدَكَ إِلَىٰ جَنَاحِكَ تَخۡرُجۡ بَيۡضَآءَ مِنۡ غَيۡرِ سُوٓءٍ ءَايَةً أُخۡرَىٰ
“Ndipo lipane dzanja lako m’khwapa mwako lituluka lili loyera (ngati kuwala kwadzuwa ndi mwezi). Osati mwamatenda, (ichi chikhala) chozizwitsa china.”[277]
[277] Ibun Kathiri adati Musa ankati akalilowetsa dzanjalo mkhwapa mwake kenako nkulitulutsa, limatuluka lili kung’anima ngati chiditswa chamwezi popanda chonyansa chilichonse. Ichi chidali china mwa zozizwitsa zake.
阿拉伯语经注:
لِنُرِيَكَ مِنۡ ءَايَٰتِنَا ٱلۡكُبۡرَى
“Kuti tikusonyeze zina mwa zozizwitsa zathu, zazikuluzikulu.”
阿拉伯语经注:
ٱذۡهَبۡ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ إِنَّهُۥ طَغَىٰ
“Pita kwa Farawo, ndithu iye wapyola malire.”
阿拉伯语经注:
قَالَ رَبِّ ٱشۡرَحۡ لِي صَدۡرِي
(Mûsa) adati: “E Mbuye wanga! Nditsakulireni chifuwa changa.”
阿拉伯语经注:
وَيَسِّرۡ لِيٓ أَمۡرِي
“Ndi kundifewetsera ntchito yangayi (imene mwandipatsa kuti uthengawu ndikaufalitse m’njira yoyenera).”
阿拉伯语经注:
وَٱحۡلُلۡ عُقۡدَةٗ مِّن لِّسَانِي
“Ndipo masulani mfundo yomwe ili ku lirime kwanga, (ndimasulireni kumangika kwa lirime langa kuti mawu anga akakhale opanda chibwibwi).”[278]
[278] Musa adali wachibwibwi koma chibwibwi chake sichinali chachibadwa. Kuyamba kwa chibwibwi chake kudali motere: Kumayambiliro amoyo wake adali kukhala m’nyumba ya Farawo. Ndipo nthawi ina Farawo adamuika pamiyendo yake iye ali mwana. Musa adakoka ndevu za Farawo ndi dzanja lake. Ndipo Farawo adakwiya natsimikiza zomupha. Ndipo Asiya, mkazi wake, adati kwa iye: “Iyeyu sazindikira. Ndipo ndikusonyeza zimenezo kuti udziwe.Yandikitsani kwa iye makala awiri ndi ngale ziwiri. Ngati atola ngalezo ndiye kuti akuzindikira. Koma akatola khala lamoto, apo uzindikira kuti ameneyu sazindikira kanthu. Choncho Farawo adamuyandikizira zonsezo ndipo iye adatola khala lamoto nkuliponya mkamwa mwake. Potero palirime lake padali kachipsera. Nkhaniyi ikupezeka m’buku la Tabariyi, volume 16 tsamba 159.
阿拉伯语经注:
يَفۡقَهُواْ قَوۡلِي
“Kuti (anthu) akamvetse mawu anga.”
阿拉伯语经注:
وَٱجۡعَل لِّي وَزِيرٗا مِّنۡ أَهۡلِي
“Ndipo ndipatseni nduna (mthandizi) yochokera kubanja langa.”
阿拉伯语经注:
هَٰرُونَ أَخِي
“M’bale wanga Harun.”
阿拉伯语经注:
ٱشۡدُدۡ بِهِۦٓ أَزۡرِي
“Limbitsani nyonga zanga ndi iye.”
阿拉伯语经注:
وَأَشۡرِكۡهُ فِيٓ أَمۡرِي
“Ndipo mphatikeni ku ntchito yangayi.”
阿拉伯语经注:
كَيۡ نُسَبِّحَكَ كَثِيرٗا
“Kuti tikulemekezeni kwambiri.”
阿拉伯语经注:
وَنَذۡكُرَكَ كَثِيرًا
“Ndi kukutamandani kwabasi.”
阿拉伯语经注:
إِنَّكَ كُنتَ بِنَا بَصِيرٗا
“Ndithu inu (nthawi zonse) mumationa (ndi kutisunga).”
阿拉伯语经注:
قَالَ قَدۡ أُوتِيتَ سُؤۡلَكَ يَٰمُوسَىٰ
(Allah) adati: “Ndithu wapatsidwa zomwe wapempha, E, iwe Mûsa.”
阿拉伯语经注:
وَلَقَدۡ مَنَنَّا عَلَيۡكَ مَرَّةً أُخۡرَىٰٓ
“Ndipo ndithu tidakuchitira ubwino nthawi ina (popanda iwe kutipempha).”
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 塔哈
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭