(Bambo wake) adati: “E iwe mwana wanga! Usawasimbire abale ako maloto ako (kuopa kuti) angakuchitire chiwembu; ndithu satana kwa munthu, ndi mdani woonekera.”[228]
“Ndipo momwemo Mbuye wako akusankha komanso akuphunzitsa kumasulira nkhani (za maloto) ndi kukwaniritsa mtendere Wake pa iwe, ndi pa mbumba ya Ya’qub monga momwe adakwaniritsira kwa makolo ako kale, Ibrahim ndi Ishaq. Ndithu Mbuye wako Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya.”
Ndipo (mkaziyo) adaikira mtima pa iye (kuti achite naye kanthu), ndipo naye (Yûsuf) adaikira mtima pa iye (kuti ammenye). Pakadapanda kuona chisonyezo cha Mbuye wake (chakumzindikiritsa kuti asatero, akadammenya. Koma adamthawa). Tidachita izi kuti timchotsere chinthu choipa ndi chauve; ndithudi, iye adali mwa akapolo athu oyeretsedwa.[231]
[231] Musamchitire choipa amene wakuchitirani chabwino, ngakhalenso amene wakuchitrani choipa kumene. Makamaka amene sadakuchitireni choipa (ndiye chisimu). Koma alipo anthu ena oipitsitsa zedi amene amachitira zoipa yemwe akuwachitira zabwino. Anthu otero ngoipitsitsa kuposa nyama zamtchire, ndipo oterewa Allah adzawakhaulitsa koopsa. Ndipo machitidwe okhala mwamuna ndi mkazi kuseri kwaokha ngoletsedwa m’shariya ya Chisilamu chifukwa mwamuna kukhala ndi mkazi amene sali mnyazi wake kumalakwitsa. Musati awa ndi alamu ndikhoza kukhala nawo pawokha. Kukhala ndi mlamu wako kuseri, ndi ngozi imeneyo!
(Yûsuf) adati (podziteteza): “(Mkazi) uyu ndi yemwe wandifuna popanda ine kumufuna.” Ndipo mboni yochokera ku banja la mkaziyo idaikira umboni; (idati): “Ngati mkanjo wake wang’ambidwa cha kutsogolo, ndiye kuti (mkazi uyu) akunena zoona, ndipo iye (Yûsuf) ndi mmodzi mwa onena zabodza.”
Ndipo akazi a mu mzindamo (ataimva nkhaniyi) anati: “Mkazi wa nduna akulakalaka m’nyamata wake popanda kulakalakidwa ndi iye; ndithu chikondi chamufooketsa zedi; ndithudi, ife tikumuona (mkaziyu kuti) ali m’kusokera koonekera.”
(Yûsuf) adati: “(Kupyolera mu uneneri umene ndapatsidwa ndingathe kukumasulirani maloto anuwa ndi zinthu zina zobisika kwa inu), sichikudzerani chakudya cha mtundu uliwonse choti mungapatsidwe koma ndikhala nditakumasulirani tanthauzo lake chisanakufikeni; (ngati mukufunadi ndikuchitirani zimenezi). Izi ndi zina mwa zomwe Mbuye wanga wandiphunzitsa. Ndithudi, ine ndasiya njira za anthu osakhulupirira Allah ndiponso omwe akukana za tsiku la chimaliziro.”
“Ndipo ine ndatsata chipembedzo cha makolo anga Ibrahim, Ishâq ndi Ya’qub; ndipo sikudali koyenera kwa ife kumphatikiza Allah ndi chilichonse. (Ndipo kuzindikira) zimenezi ndi ubwino wa Allah umene uli pa ife ndi anthu ena, koma anthu ambiri sathokoza.”
“Simupembedza china kusiya Iye (Allah) koma ndi maina basi amene inu nokha mudawatcha ndi makolo anu, Allah sadatsitse umboni uliwonse pa zimenezo. Palibe lamulo lina koma ndi la Allah basi. Walamula kuti musampembedze aliyense koma Iye basi. Chimenecho ndicho chipembedzo choongoka, koma anthu ambiri sadziwa (monga inu mulili popembedza mafano).”
“E inu anzanga awiri a m’ndende! Tsono mmodzi wa inu (abwerera ku ntchito yake) azikamwetsa mowa bwana wake (monga zidalili poyamba); koma winayo aphedwa mopachikidwa, ndipo mbalame zidzadya mmutu wake. Chiweruzo chaweruzidwa kale (kwa Farawo) pa chinthu chomwe mudali kufunsa.”
(Adanka kundende ndikumpempha Yûsuf chikhululuko chifukwa cha kuiwala kwake. Ndipo adati): “Yûsuf! E iwe woona! Tiuze za ng’ombe zisanu ndi ziwiri zonenepa zikudyedwa ndi zisanu ndi ziwiri zoonda, ndi ngala zisanu ndi ziwiri zaziwisi ndi zina zouma; kuti ine ndibwelere kwa anthu kuti akadziwe.”
Choncho Mfumu idati: “Mubwere naye kwa ine kuti ine mwini ndimsankhe.” Ndipo pamene adayankhula naye, (Mfumu) idati: “Ndithu iwe lero kwa ife wakhala wolemekezeka, wokhulupirika.”
(Ya’qub) adati: “Kodi ndingakukhulupirireni pa iye kuposa momwe ndidakukhulupirirani pa m’bale wake kale (yemwe mudamsokeretsa)? Koma Allah ndi Yemwe ali Wabwino posunga, Ndipo Iye Ngwachifundo zedi kuposa achifundo onse.”
Adatinso: “E inu ana anga! Musakalowe (mu Iguputo) pachipata chimodzi koma kaloweni pa zipata zosiyanasiyana. Ndipo sindingakuthandizeni chilichonse kwa Allah. Lamulo ndi la Allah basi; kwa Iye ndiko ndatsamira; ndipo otsamira atsamire kwa Iye.”
Adati: “Mphoto yake ndi yemwe (chikhocho) chapezeka mu mtolo wake, iye ndiye mphoto yake. (Agwidwe monga kapolo kwa chaka chimodzi).” Umu ndi momwe timawalipirira anthu achinyengo.
Ndipo (mneneri Yûsuf) adayamba kufufuza m’mitolo mwawo asanafufuze mu mtolo wa m’bale wake; kenako adachitulutsa mu mtolo wa m’bale wake. Umu ndi momwe tidamlinganizira ndale Yûsuf (kuti ampeze m’bale wake). Mwachilamulo cha mfumu (ya m’dzikolo) sakadamutenga m’bale wake (monga kapolo) koma mmene Allah adafunira (powaonetsa abale ake za chilamulo cha kwawo chomuika mu ukapolo munthu wakuba). Timawakwezera pa ulemelero amene tawafuna. Ndipo pa wodziwa aliyense pali wodziwanso kuposa iye.
Ndipo adawachokera ndikunena (kuti): “Ha! kudandaula kwanga za Yûsuf!” Ndipo maso ake adayera chifukwa cha kudandaula ndipo iye adadzazidwa ndi chisoni.
“E ana anga! Pitani mukafufuzefufuze za Yûsuf ndi m’bale wake, ndipo musataye mtima pa chifundo cha Allah. Ndithu palibe amene amataya mtima za chifundo cha Allah koma anthu osakhulupirira.”
(Iwo) adati: “Kodi iwe ndiwe Yûsuf?” Adati: “Ine ndine Yûsuf, ndipo uyu ndi m’bale wanga; Allah watichitira zabwino. Ndithu amene aopa Allah ndikumapirira, (Allah amulipira). Ndithu Allah sasokoneza malipiro a ochita zabwino.”
(Kenako adathokoza ndi kupempha Allah kuti): “E Mbuye wanga! Ndithu mwandipatsako ufumu ndi kundiphunzitsako kumasulira nkhani (maloto). E Inu Mlengi wa thambo ndi nthaka! Inu ndiye Mtetezi wanga pa dziko lapansi ndi tsiku la chimaliziro. (Ndipo nthawi ya imfa yanga) mudzandipatse imfa ndili Msilamu ndipo kandikumanitseni ndi ochita zabwino.”
Ndipo ambiri a iwo sakhulupirira Allah koma momphatikiza. [234]
[234] Apa akutanthauza kuti ambiri a iwo amamphatikiza Allah ndi milungu yabodza. Iwo amavomereza kuti Allah ndiye Mlengi wopatsa zonse. Koma kuonjezera pachikhulupiliro choterechi, amapembedzanso mafano. Ndipo zoterezi masiku ano zikumachitika ndi Asilamu ena amene amafuulira mizimu ya anthu akufa kuti iwathangate pa mavuto amene awagwera, komwe nkumuphatikiza Allah ndi mizimu ya anthu akufa.
Nena: “Iyi ndi njira yanga. Ndikuitanira kwa Allah mwa nzeru zokwanira, ine ndi omwe akunditsata. Ndithu Allah wapatukana (ndi mbiri zopunguka). Ndipo ine sindili mwa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina).”[235]
[235] Apa Mtumiki (s.a.w) akuuzidwa kuti awauze anthu kuti iye pamodzi ndi amene akumutsata kuti amalalikira Chisilamu kwa anthu popereka kwa anthuwo mitsutso yanzeru, ndikuperekanso zisonyezo ndi maumboni amphamvu. Sibwino Msilamu kutsatira chinthu popanda kuchidziwa bwinobwino. Qur’an ikunenetsa kuti osatsatira chinthu popanda kuchidziwa bwinobwino pokhapokha chinthucho chitanenedwa ndi Allah kapena Mtumiki Wake.
Ndithu m’nkhani zawo izi muli phunziro kwa eni nzeru. (Qur’aniyi) simawu opekedwa, koma (iyi Qur’an) ndi chitsimikizo cha zomwe zidalipo patsogolo pake (m’mabuku ena a Allah), ndi kumasulira kwa tsatanetsatane pa chilichonse ndiponso chiongoko ndi mtendere kwa anthu okhulupirira.
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
検索結果:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".