Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима * - Таржималар мундарижаси


Маънолар таржимаси Сура: Маъориж сураси   Оят:

Маъориж сураси

سَأَلَ سَآئِلُۢ بِعَذَابٖ وَاقِعٖ
Wopempha adapempha kuti chiwadzere msanga chilango chopezekacho, (m’kupempha kwa chipongwe ndi kotsutsa).
Арабча тафсирлар:
لِّلۡكَٰفِرِينَ لَيۡسَ لَهُۥ دَافِعٞ
Kwa okanira palibe angachitsekereze.
Арабча тафсирлар:
مِّنَ ٱللَّهِ ذِي ٱلۡمَعَارِجِ
Chochokera kwa Allah Mwini makwelero.
Арабча тафсирлар:
تَعۡرُجُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ وَٱلرُّوحُ إِلَيۡهِ فِي يَوۡمٖ كَانَ مِقۡدَارُهُۥ خَمۡسِينَ أَلۡفَ سَنَةٖ
Angelo ndi Jiburil amakwera kwa Iye (Allah) m’tsiku lomwe kutalika kwake kuli ngati zaka zikwi makumi asanu (50 000).
Арабча тафсирлар:
فَٱصۡبِرۡ صَبۡرٗا جَمِيلًا
Choncho, pirira (iwe Mtumiki (s.a.w) kupirira kwabwino,
Арабча тафсирлар:
إِنَّهُمۡ يَرَوۡنَهُۥ بَعِيدٗا
Ndithu iwo akuliona (tsiku la Qiyâma) kuti lili kutali (silingachitike).
Арабча тафсирлар:
وَنَرَىٰهُ قَرِيبٗا
Koma Ife tikuliona kuti lilipafupi (ndilochitika).
Арабча тафсирлар:
يَوۡمَ تَكُونُ ٱلسَّمَآءُ كَٱلۡمُهۡلِ
Tsiku limene thambo lidzakhala ngati mtovu wosungunuka.
Арабча тафсирлар:
وَتَكُونُ ٱلۡجِبَالُ كَٱلۡعِهۡنِ
Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya (wongouluka wokha).
Арабча тафсирлар:
وَلَا يَسۡـَٔلُ حَمِيمٌ حَمِيمٗا
Ndipo m’bale sadzafunsa za m’bale wake.
Арабча тафсирлар:
يُبَصَّرُونَهُمۡۚ يَوَدُّ ٱلۡمُجۡرِمُ لَوۡ يَفۡتَدِي مِنۡ عَذَابِ يَوۡمِئِذِۭ بِبَنِيهِ
Ngakhale adzawalole kuti aonane ndi kudziwana pakati pawo (sadzafunsana). Wochimwa adzalakalaka kuti akadaziwombola ku chilango cha tsiku limenelo ndi ana ake.
Арабча тафсирлар:
وَصَٰحِبَتِهِۦ وَأَخِيهِ
Ndi mkazi wake, ndi m’bale wake.
Арабча тафсирлар:
وَفَصِيلَتِهِ ٱلَّتِي تُـٔۡوِيهِ
Ndi akumtundu wake amene amamsunga.
Арабча тафсирлар:
وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ جَمِيعٗا ثُمَّ يُنجِيهِ
Ndi (kulipira) zonse za m’dziko, kuti zimpulumutse.
Арабча тафсирлар:
كَلَّآۖ إِنَّهَا لَظَىٰ
Iyayi, (siya iwe wamachimo zimene ukulakalakazo)! Ndithu umenewu ndi Moto wa malawi.
Арабча тафсирлар:
نَزَّاعَةٗ لِّلشَّوَىٰ
Wosupula mwamphamvu khungu.
Арабча тафсирлар:
تَدۡعُواْ مَنۡ أَدۡبَرَ وَتَوَلَّىٰ
Udzaitana (potchula dzina la aliyense) amene adachitembenuzira msana choona ndi kunyoza.
Арабча тафсирлар:
وَجَمَعَ فَأَوۡعَىٰٓ
Adasonkhanitsa (chuma) ndi kusunga (m’nkhokwe zake popanda kuperekera chopereka cha Allah).
Арабча тафсирлар:
۞ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ خُلِقَ هَلُوعًا
Ndithu munthu walengedwa kukhala wosapirira.
Арабча тафсирлар:
إِذَا مَسَّهُ ٱلشَّرُّ جَزُوعٗا
Mavuto akamkhudza amada nkhawa.
Арабча тафсирлар:
وَإِذَا مَسَّهُ ٱلۡخَيۡرُ مَنُوعًا
Koma zabwino zikamkhudza amamana (ena ndi kuiwala mavuto amene adali nawo).
Арабча тафсирлар:
إِلَّا ٱلۡمُصَلِّينَ
Kupatula opemphera Swala, (iwo alibe mbiri zoipazi).
Арабча тафсирлар:
ٱلَّذِينَ هُمۡ عَلَىٰ صَلَاتِهِمۡ دَآئِمُونَ
Iwo amene sadukiza mapemphero awo a swala; (sakuwaleka ngakhale zivute chotani).
Арабча тафсирлар:
وَٱلَّذِينَ فِيٓ أَمۡوَٰلِهِمۡ حَقّٞ مَّعۡلُومٞ
Ndi amene mchuma chawo muli gawo lodziwika (Zakaat),
Арабча тафсирлар:
لِّلسَّآئِلِ وَٱلۡمَحۡرُومِ
La wopempha ndi wosapempha.
Арабча тафсирлар:
وَٱلَّذِينَ يُصَدِّقُونَ بِيَوۡمِ ٱلدِّينِ
Ndi amene akuvomereza za tsiku la malipiro (ndi kumalikonzekera.)
Арабча тафсирлар:
وَٱلَّذِينَ هُم مِّنۡ عَذَابِ رَبِّهِم مُّشۡفِقُونَ
Ndi iwo amene akuopa chilango chochokera kwa Mbuye wawo.
Арабча тафсирлар:
إِنَّ عَذَابَ رَبِّهِمۡ غَيۡرُ مَأۡمُونٖ
Ndithu chilango cha Mbuye wawo nchosapulumuka nacho (munthu woipa).
Арабча тафсирлар:
وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِفُرُوجِهِمۡ حَٰفِظُونَ
Ndiponso iwo amene akusunga umaliseche wawo (posachita chiwerewere),
Арабча тафсирлар:
إِلَّا عَلَىٰٓ أَزۡوَٰجِهِمۡ أَوۡ مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُهُمۡ فَإِنَّهُمۡ غَيۡرُ مَلُومِينَ
Kupatula kwa akazi awo ndi amene manja awo akumanja apeza; ndithu pazimenezo iwo sangadzudzulidwe.
Арабча тафсирлар:
فَمَنِ ٱبۡتَغَىٰ وَرَآءَ ذَٰلِكَ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡعَادُونَ
Koma amene angafune (zina) kusiya zimenezi iwowo ndiwo olumpha malire.
Арабча тафсирлар:
وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِأَمَٰنَٰتِهِمۡ وَعَهۡدِهِمۡ رَٰعُونَ
Ndi iwo amene amasunga mwaubwino zimene amasungitsidwa ndi zimene alonjeza.
Арабча тафсирлар:
وَٱلَّذِينَ هُم بِشَهَٰدَٰتِهِمۡ قَآئِمُونَ
Ndi iwo amene amaima molungama popereka umboni wawo.
Арабча тафсирлар:
وَٱلَّذِينَ هُمۡ عَلَىٰ صَلَاتِهِمۡ يُحَافِظُونَ
Ndiponso iwo amene amasunga (mwaubwino) mapemphero awo a swala.
Арабча тафсирлар:
أُوْلَٰٓئِكَ فِي جَنَّٰتٖ مُّكۡرَمُونَ
Amene ali ndi mbiri zimenezi adzakhala m’Minda (yamtendere) ali olemekezedwa.
Арабча тафсирлар:
فَمَالِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ قِبَلَكَ مُهۡطِعِينَ
Kodi kuli chiyani kwa amene akana (chikhulupiliro) akuthamangira kwa iwe (maso ali pamtunda)?
Арабча тафсирлар:
عَنِ ٱلۡيَمِينِ وَعَنِ ٱلشِّمَالِ عِزِينَ
Atakuzungulira ena chakumanja ena chakumanzere.
Арабча тафсирлар:
أَيَطۡمَعُ كُلُّ ٱمۡرِيٕٖ مِّنۡهُمۡ أَن يُدۡخَلَ جَنَّةَ نَعِيمٖ
Kodi akulakalaka aliyense mwa iwo kuti akalowetsedwe ku Munda wamtendere?
Арабча тафсирлар:
كَلَّآۖ إِنَّا خَلَقۡنَٰهُم مِّمَّا يَعۡلَمُونَ
Asiye (kukhumba kwawo kokalowa ku Munda wamtendere)! Ndithu Ife tidawalenga kuchokera m’zimene akudziwa (madzi opanda pake).
Арабча тафсирлар:
فَلَآ أُقۡسِمُ بِرَبِّ ٱلۡمَشَٰرِقِ وَٱلۡمَغَٰرِبِ إِنَّا لَقَٰدِرُونَ
Ndikulumbilira Mbuye wa kuvuma ndi kuzambwe konse ndithu Ndife Wokhoza.
Арабча тафсирлар:
عَلَىٰٓ أَن نُّبَدِّلَ خَيۡرٗا مِّنۡهُمۡ وَمَا نَحۡنُ بِمَسۡبُوقِينَ
Kuwasintha ndi kudzetsa abwino kuposa iwo; Ife palibe (chilichonse) chotipambana.
Арабча тафсирлар:
فَذَرۡهُمۡ يَخُوضُواْ وَيَلۡعَبُواْ حَتَّىٰ يُلَٰقُواْ يَوۡمَهُمُ ٱلَّذِي يُوعَدُونَ
Asiye azingolankhula zopanda pake ndi kumangosewera mpaka adzakumane ndi tsiku lawo limene akulonjezedwa.
Арабча тафсирлар:
يَوۡمَ يَخۡرُجُونَ مِنَ ٱلۡأَجۡدَاثِ سِرَاعٗا كَأَنَّهُمۡ إِلَىٰ نُصُبٖ يُوفِضُونَ
Tsiku limene adzatuluke m’manda uku akuthamanga (kudza kwa woitana) ngati kuti akuthamangira kumafano awo (amene adali kuwapembedza).
Арабча тафсирлар:
خَٰشِعَةً أَبۡصَٰرُهُمۡ تَرۡهَقُهُمۡ ذِلَّةٞۚ ذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمُ ٱلَّذِي كَانُواْ يُوعَدُونَ
Maso awo ali zyoli, (osatha kuwakweza); kuyaluka kutawaphimba! Limenelo ndilo tsiku lomwe adali kulonjezedwa (pomwe adali padziko lapansi.
Арабча тафсирлар:
 
Маънолар таржимаси Сура: Маъориж сураси
Суралар мундарижаси Бет рақами
 
Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима - Таржималар мундарижаси

Қуръон Карим маъноларининг чевача таржимаси, мутаржим: Холид Иброҳим Бетала, 2020 йилда нашр қилинган

Ёпиш