ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: الإنفطار
آية:
 

الإنفطار

إِذَا ٱلسَّمَآءُ ٱنفَطَرَتۡ
“Pamene thambo lidzasweke,
Allah pambuyo ponena zimenezi sadanene kuti chidzachitika chiyani. Alekera munthu mwini wake kuti aganizire chomwe chidzachitika zikadzapezeka zoopsa kuti aope kwambiri.
التفاسير العربية:
وَإِذَا ٱلۡكَوَاكِبُ ٱنتَثَرَتۡ
“Ndi pamene nyenyezi zidzayoyoke (ndi kumwazikana),
التفاسير العربية:
وَإِذَا ٱلۡبِحَارُ فُجِّرَتۡ
“Pamenenso nyanja zikuluzikulu zidzaphwasulidwe.
التفاسير العربية:
وَإِذَا ٱلۡقُبُورُ بُعۡثِرَتۡ
“Ndiponso pamene manda adzafukulidwe (ndikutuluka akufa omwe adali mmenemo),
التفاسير العربية:
عَلِمَتۡ نَفۡسٞ مَّا قَدَّمَتۡ وَأَخَّرَتۡ
“(Panthawiyo) mzimu uliwonse udzadziwa zimene udatsogoza (zabwino ndi zoipa) ndi zimene udasiya m’mbuyo.
Tsiku la chiweruziro munthu adzapatsidwa kaundula wake monga momwe zanenedwa mu Ayah 10 Surah Takwir, choncho ena adzapatsidwa ndi dzanja la kumanja; iwo ndiwo anthu abwino. Pomwe ena adzapatsidwa ndi dzanja la kumanzere, chakumbali yakumsana; iwowo ndiwo anthu oipa.
التفاسير العربية:
يَـٰٓأَيُّهَا ٱلۡإِنسَٰنُ مَا غَرَّكَ بِرَبِّكَ ٱلۡكَرِيمِ
“E iwe munthu! Nchiani chakunyenga kumsiya Mbuye wako wa ufulu (kufikira pomnyoza)?
التفاسير العربية:
ٱلَّذِي خَلَقَكَ فَسَوَّىٰكَ فَعَدَلَكَ
“Amene adalenga iwe nakulinganiza (ziwalo zako) ndi kukulongosola (moyenera);
التفاسير العربية:
فِيٓ أَيِّ صُورَةٖ مَّا شَآءَ رَكَّبَكَ
“Ndipo maonekedwe amtundu uliwonse omwe adawafuna adakuveka (popanda chifuniro chako).
التفاسير العربية:
كَلَّا بَلۡ تُكَذِّبُونَ بِٱلدِّينِ
“Ayi, sichoncho! Koma inu mukutsutsa za (tsiku) lamalipiro.
التفاسير العربية:
وَإِنَّ عَلَيۡكُمۡ لَحَٰفِظِينَ
“Ndithu pa inu alipo okuyang’ anirani,
Anthu ena adzawerengedwa popanda kufunsidwa mafunso pa zimene adachita, koma adzangowauza zabwino zawo ndi zoipa zawo ndipo pambuyo pake adzawakhululukira zoipazo ndi kudzawalipira pa zabwinozo. Iwowa ndiwo anthu abwino; chimenechi ndicho chiweruzo chofewa. Ena adzaweruzidwa pofunsidwa pa chilichonse m’zimene ankachita monga kuti “Bwanji ichi udachita? Bwanji ichi sudachite”? Iwowa ndiwo anthu oipa; chiwerengero chawo chidzakhala chokhwima.
التفاسير العربية:
كِرَامٗا كَٰتِبِينَ
“Olemekezeka, olemba (zochita zanu.)
التفاسير العربية:
يَعۡلَمُونَ مَا تَفۡعَلُونَ
“Akudziwa (zonse) zimene mukuchita (zabwino ndi zoipa).
التفاسير العربية:
إِنَّ ٱلۡأَبۡرَارَ لَفِي نَعِيمٖ
“Ndithudi ochita zabwino adzakhala mu mtendere.
التفاسير العربية:
وَإِنَّ ٱلۡفُجَّارَ لَفِي جَحِيمٖ
“Ndipo ndithu amene ali olakwira malamulo a Allah adzakhala ku Moto wopsereza.
التفاسير العربية:
يَصۡلَوۡنَهَا يَوۡمَ ٱلدِّينِ
“Adzaulowa tsiku la malipiro.
التفاسير العربية:
وَمَا هُمۡ عَنۡهَا بِغَآئِبِينَ
“Ndipo iwo kumeneko sadzachokako.
التفاسير العربية:
وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا يَوۡمُ ٱلدِّينِ
“Kodi nchiyani chingakudziwitse za tsiku la malipiro?
التفاسير العربية:
ثُمَّ مَآ أَدۡرَىٰكَ مَا يَوۡمُ ٱلدِّينِ
“Ndipo nchiyani chingakudziwitse za tsiku lamalipiro?
التفاسير العربية:
يَوۡمَ لَا تَمۡلِكُ نَفۡسٞ لِّنَفۡسٖ شَيۡـٔٗاۖ وَٱلۡأَمۡرُ يَوۡمَئِذٖ لِّلَّهِ
“Limeneli ndi tsiku limene mzimu uliwonse sudzakhala ndi mphamvu (yodzetsa mtendere kapena yochotsa chovuta) pa mzimu wina. Ndipo lamulo pa tsiku limeneli ndi la Allah yekha.
Kubalalikana masana ndi chizolowezi cha anthu ndi nyama chifukwa chofunafuna zinthu zothandiza pa moyo wawo. Tsono usiku ukabwera amasonkhana ndi kukhala pamodzi. Ndipo ili ndilo tanthauzo la: “Usiku ndi zimene wasonkhanitsa.”
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: الإنفطار
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق