அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - الترجمة الشيشيوا * - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை


மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: ஸூரா அல்காஷியா
வசனம்:
 

ஸூரா அல்காஷியா

هَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ ٱلۡغَٰشِيَةِ
“Kodi yakudzera, (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Qiyâma (imene idzaphimba anthu ndi zoopsa zake)?
அரபு விரிவுரைகள்:
وُجُوهٞ يَوۡمَئِذٍ خَٰشِعَةٌ
“Nkhope zina tsiku limenelo, zidzakhala zonyozeka,
Apa ndikuti Allah akuwaona anthu Ake nthawi ili yonse. Palibe chimene iwo achita popanda Iye kuchiona ndi kuchilemba.
அரபு விரிவுரைகள்:
عَامِلَةٞ نَّاصِبَةٞ
“Zogwira ntchito yotopetsa kwambiri.
அரபு விரிவுரைகள்:
تَصۡلَىٰ نَارًا حَامِيَةٗ
“Zikalowa ku Moto wotentha kwambiri.
அரபு விரிவுரைகள்:
تُسۡقَىٰ مِنۡ عَيۡنٍ ءَانِيَةٖ
“Zikamwetsedwa mu kasupe wotentha kwabasi.
அரபு விரிவுரைகள்:
لَّيۡسَ لَهُمۡ طَعَامٌ إِلَّا مِن ضَرِيعٖ
“Sadzakhala ndichakudya koma minga.
அரபு விரிவுரைகள்:
لَّا يُسۡمِنُ وَلَا يُغۡنِي مِن جُوعٖ
“Yosanenepetsa (thupi) ndiponso yosathetsa njala.
அரபு விரிவுரைகள்:
وُجُوهٞ يَوۡمَئِذٖ نَّاعِمَةٞ
“Nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zosangalala.
அரபு விரிவுரைகள்:
لِّسَعۡيِهَا رَاضِيَةٞ
“Zidzakondwera ndi malipiro a zochita zake (za pa dziko lapansi).
Arabu asadalowe m’Chisilamu akazi sadali kugawiridwa chuma cha masiye kudzanso ana aang’onoang’ono a masiye sadali kuchiona chumacho.
அரபு விரிவுரைகள்:
فِي جَنَّةٍ عَالِيَةٖ
“M’minda ya pamwamba (Jannah).
அரபு விரிவுரைகள்:
لَّا تَسۡمَعُ فِيهَا لَٰغِيَةٗ
“Sizikamva m’menemo mawu oipa, (otukwana ndi kulaula).
அரபு விரிவுரைகள்:
فِيهَا عَيۡنٞ جَارِيَةٞ
“Mmenemo muli kasupe woyenda (mokongola).
(Ndime 25-26) Tanthauzo lake ndikuti palibe chofanizira chilango cha Allah chomwe chidzaperekedwe kwa akafiri ndiponso ndi kunjata komwe akafiri adzanjatidwe.
அரபு விரிவுரைகள்:
فِيهَا سُرُرٞ مَّرۡفُوعَةٞ
“Mmenemo muli makama a pamwamba,
அரபு விரிவுரைகள்:
وَأَكۡوَابٞ مَّوۡضُوعَةٞ
“Ndi zikho zoikidwa bwino (pamaso pawo),
அரபு விரிவுரைகள்:
وَنَمَارِقُ مَصۡفُوفَةٞ
“Ndi misamiro yoikidwa bwino m’mizeremizere
அரபு விரிவுரைகள்:
وَزَرَابِيُّ مَبۡثُوثَةٌ
“Ndi mphasa (zamtengo wapatali, carpet) zoyalidwa ponseponse.
அரபு விரிவுரைகள்:
أَفَلَا يَنظُرُونَ إِلَى ٱلۡإِبِلِ كَيۡفَ خُلِقَتۡ
“Kodi (akunyozera kulingalira zisonyezo za Allah), sakulingalira kungamira idalengedwa motani?
“Mzimu wokhazikika” ndi mzimu wa munthu wokhulupilira amene akuchita zomwe walamulidwa ndi kusiya zimene waletsedwa. Umenewo ndiwo mzimu umene udzakhale wodekha pa tsiku lachimaliziro chifukwa chakuti pa tsikulo sudzakhala ndi mantha kapena kudandaula.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِلَى ٱلسَّمَآءِ كَيۡفَ رُفِعَتۡ
“Ndi thambo (limene akuliona nthawi zonse) m’mene lidatukulidwira (kutali popanda mzati)?
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِلَى ٱلۡجِبَالِ كَيۡفَ نُصِبَتۡ
“Ndi mapiri momwe adakhazikitsidwira (molimba)?
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِلَى ٱلۡأَرۡضِ كَيۡفَ سُطِحَتۡ
“Ndi nthaka momwe idayalidwira.
அரபு விரிவுரைகள்:
فَذَكِّرۡ إِنَّمَآ أَنتَ مُذَكِّرٞ
“Basi, kumbutsa (anthu) ndithu iwe, ndiwe mkumbutsi.
அரபு விரிவுரைகள்:
لَّسۡتَ عَلَيۡهِم بِمُصَيۡطِرٍ
“Sindiwe wokakamiza anthu (kuti akhulupirire).
Tanthauzo lake nkuti mzimu wokhazikika udzakondwera ndi zimene udzalandira kwa Allah tsiku limenelo ndipo naye Allah adzakondwera nawo.
அரபு விரிவுரைகள்:

إِلَّا مَن تَوَلَّىٰ وَكَفَرَ
“Koma amene anyoza ndi kukanira (ulaliki wako),
அரபு விரிவுரைகள்:
فَيُعَذِّبُهُ ٱللَّهُ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَكۡبَرَ
“Allah amulanga chilango chachikulu zedi.
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّ إِلَيۡنَآ إِيَابَهُمۡ
“Ndithu kobwerera kwawo ndi kwa Ife basi.
அரபு விரிவுரைகள்:
ثُمَّ إِنَّ عَلَيۡنَا حِسَابَهُم
“Ndipo ndithu kuwerengedwa kwawo kuli kwa Ife.
அரபு விரிவுரைகள்:

 
மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: ஸூரா அல்காஷியா
அத்தியாயங்களின் அட்டவணை பக்க எண்
 
அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - الترجمة الشيشيوا - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

மூடுக