ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: النبإ
آية:
 

النبإ

عَمَّ يَتَسَآءَلُونَ
“۞ Kodi akufunsana zachiyani?
التفاسير العربية:
عَنِ ٱلنَّبَإِ ٱلۡعَظِيمِ
“Za nkhani yayikulu ija.
التفاسير العربية:
ٱلَّذِي هُمۡ فِيهِ مُخۡتَلِفُونَ
“Imene iwo akusiyana (maganizo).
Tanthauzo lake ndikuti: “Kodi chilengedwe chanu nchovuta kwambiri kuposa chilengedwe cha thambo pamene inu mukuganiza kuti Allah sangathe kukudzutsani pambuyo pa imfa?”
التفاسير العربية:
كَلَّا سَيَعۡلَمُونَ
“Aleke (zimenezo) adzadziwa posachedwapa.
Mu Ayah iyi Allah akusonyeza kuti Iye ndi Mwini mphamvu zonse zochitira chinthu chilichonse chachikulu kuposa kuwaukitsa akufa; ndiponso akukumbutsa ufulu Wake waukulu womwe adatichitira potipatsa zinthu zonsezo kuti tithandizike nazo.
التفاسير العربية:
ثُمَّ كَلَّا سَيَعۡلَمُونَ
“Ayi, ndithu aleke (zimenezo); posachedwapa adzadziwa zoona zake (pamene chilango chidzawatsikira).
Apa tanthauzo lake ndikuti adzaona masiku onse amene adakhala m’dziko ngati lidali ola limodzi.
التفاسير العربية:
أَلَمۡ نَجۡعَلِ ٱلۡأَرۡضَ مِهَٰدٗا
“Kodi sitidachite nthaka kukhala ngati choyala?
Tsiku lina Mneneri (s.a.w) atakhala ndi akuluakulu a Aquraishi. Adali kuwalalikira za chipembedzo mwachidwi, ndipo adali kuyembekezera kuti akavomereza Chisilamu iwo, ndiye kuti anthu owatsatira naonso avomereza. Chifukwa anthu ambiri sadalowe Chisilamu poopa atsogoleri awo. Pa nthawi imeneyi adatulukira wakhungu wina yemwe ankatchedwa Ibn Ummu Maktum. Sadadziwe kuti Mneneri (s.a.w) ali wotanganidwa. Adamukuwira: “E Iwe Mneneri wa Allah! Ndiphunzitse inenso zimene wakuphunzitsa Allah.” Ndipo ankangomubwerezera-bwerezera mawu amenewa. Mneneri (s.a.w) pakuti adali ndi chidwi ndi kulalikira akuluakulu aja, adamchitira tsinya wakhungu uja chifukwa chomuonongera ntchito yake; sadamumvere. Basi pamenepa Allah akumdzudzula Mneneri Wake pa zomwe adachita posiya kumumvera amene adamubwerera kudzafuna chiongoko.
التفاسير العربية:
وَٱلۡجِبَالَ أَوۡتَادٗا
“Ndi mapiri ngati zichiri (zolimbitsa nthaka)?
التفاسير العربية:
وَخَلَقۡنَٰكُمۡ أَزۡوَٰجٗا
“Ndipo takulengani mitundu iwiri (amuna ndi akazi).
التفاسير العربية:
وَجَعَلۡنَا نَوۡمَكُمۡ سُبَاتٗا
“Ndipo tidachita tulo tanu kukhala mpumulo (ku mavuto a ntchito).
التفاسير العربية:
وَجَعَلۡنَا ٱلَّيۡلَ لِبَاسٗا
“Ndipo taupanga usiku kukhala ngati chovala (pokuvindikirani ndi mdima wake).
التفاسير العربية:
وَجَعَلۡنَا ٱلنَّهَارَ مَعَاشٗا
“Ndipo tapanga masana kukhala nthawi yopezera zofunika pa moyo;
التفاسير العربية:
وَبَنَيۡنَا فَوۡقَكُمۡ سَبۡعٗا شِدَادٗا
“Ndipo tamanga pamwamba panu thambo zisanu ndi ziwiri zolimba;
التفاسير العربية:
وَجَعَلۡنَا سِرَاجٗا وَهَّاجٗا
“Ndipo tidapanga nyali yowala ndi yotentha kwambiri (dzuwa);
التفاسير العربية:
وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلۡمُعۡصِرَٰتِ مَآءٗ ثَجَّاجٗا
“Ndipo tawatsitsa madzi otsika mwamphamvu kuchokera ku mitambo, ya mvula;
التفاسير العربية:
لِّنُخۡرِجَ بِهِۦ حَبّٗا وَنَبَاتٗا
“Kuti titulutse ndi madziwo mbewu ndi m’mera, (chomwe ndi chakudya cha anthu ndi nyama).
التفاسير العربية:
وَجَنَّـٰتٍ أَلۡفَافًا
“Ndi minda yothothana nthambi za mitengo.
التفاسير العربية:
إِنَّ يَوۡمَ ٱلۡفَصۡلِ كَانَ مِيقَٰتٗا
“Ndithu tsiku la chiweruziro ndinthawi imene idakhazikitsidwa kale.
التفاسير العربية:
يَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِ فَتَأۡتُونَ أَفۡوَاجٗا
“Tsiku limene lipenga (lakuuka) lidzaimbidwa ndipo inu mudzabwera (kubwalo losonkhanirana) muli magulumagulu.
التفاسير العربية:
وَفُتِحَتِ ٱلسَّمَآءُ فَكَانَتۡ أَبۡوَٰبٗا
“Ndipo thambo lidzatsegulidwa (mbali zonse): choncho lidzakhala makomomakomo.
التفاسير العربية:
وَسُيِّرَتِ ٱلۡجِبَالُ فَكَانَتۡ سَرَابًا
“Ndipo mapiri adzachotsedwa m’malo mwake, adzakhala ngati zideruderu.
(Ndime 11-16) Apa Allah akumuletsa Mtumiki Wake kuti asachitenso zonga adachitazo ndi kumuuza kuti Qur’an ndi ulaliki chabe, amene afuna kulingalira za ulalikiwo, umuthandiza, ndipo amene safuna, kutaika ndi kwake. Ndiponso adamufotokozera kuti Qur’an idachokera m’mabuku olemekezeka; idachokera ku “Lauhil-Mahfudh” mabuku omwe ali m’manja mwa Angelo olemba, olemekezeka, ochita zabwino omwe ndi abwino kuposa Aquraishi.
التفاسير العربية:
إِنَّ جَهَنَّمَ كَانَتۡ مِرۡصَادٗا
“Ndithu moto wa Jahannam ukuwadikilira (oipa).
التفاسير العربية:
لِّلطَّـٰغِينَ مَـَٔابٗا
“Mbuto ya opyola malire.
Ngati munthu sakumbuka chilengedwe chake, ayang’ane chakudya chimene akudya momwe chimapezekera. Azindikira mphamvu za Allah.
التفاسير العربية:
لَّـٰبِثِينَ فِيهَآ أَحۡقَابٗا
“Adzakhala m’menemo muyaya.
التفاسير العربية:
لَّا يَذُوقُونَ فِيهَا بَرۡدٗا وَلَا شَرَابًا
“Sadzalawa m’menemo kuzizira (kowachotsera kutentha), kapena chakumwa (chowachotsera ludzu lawo);
التفاسير العربية:
إِلَّا حَمِيمٗا وَغَسَّاقٗا
“Kupatula madzi otentha kwambiri ndi mafinya (otuluka mmatupi a anthu a ku Moto);
التفاسير العربية:
جَزَآءٗ وِفَاقًا
“Kukhala malipiro olingana ndi ntchito zawo.
التفاسير العربية:
إِنَّهُمۡ كَانُواْ لَا يَرۡجُونَ حِسَابٗا
“Ndithu iwo sadali kuyembekezera chiwerengero (cha Allah);
التفاسير العربية:
وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا كِذَّابٗا
“Adatsutsa zizindikiro Zathu (zosonyeza kuuka kwa akufa) ndi mtsutso waukulu.
التفاسير العربية:
وَكُلَّ شَيۡءٍ أَحۡصَيۡنَٰهُ كِتَٰبٗا
“Ndipo chinthu chilichonse tachisunga mochilemba.
التفاسير العربية:
فَذُوقُواْ فَلَن نَّزِيدَكُمۡ إِلَّا عَذَابًا
“Basi, lawani (lero chilango Changa); sitikuonjezerani chinthu china koma chilango pamwamba pa chilango.
التفاسير العربية:

إِنَّ لِلۡمُتَّقِينَ مَفَازًا
“Ndithu anthu oopa Allah adzakhala ndi malo wopambana.
التفاسير العربية:
حَدَآئِقَ وَأَعۡنَٰبٗا
“Minda ndi zipatso za mphesa.
التفاسير العربية:
وَكَوَاعِبَ أَتۡرَابٗا
“Ndi mabuthu (anamwali) ofanana misinkhu.
التفاسير العربية:
وَكَأۡسٗا دِهَاقٗا
“Ndi zipanda zodzaza ndi zakumwa.
التفاسير العربية:
لَّا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوٗا وَلَا كِذَّـٰبٗا
“Sakamva m’menemo mawu opanda pake kapena bodza.
التفاسير العربية:
جَزَآءٗ مِّن رَّبِّكَ عَطَآءً حِسَابٗا
“Amenewa ndi malipiro ochokera kwa Mbuye wako zopereka zokwanira.
(Ndime 38-39) Tsiku limenelo anthu adzakhala kakhalidwe ka mitundu iwiri: amene adakhulupilira ndi kuchita ntchito zabwino nkhope zawo zidzawala ndi chimwemwe, ndipo amene adakanira ndikumachita zoipa, nkhope zawo zidzakhala zafumbi ndi zakuda monga momwe anenera ma Ayah 40 ndi 42.
التفاسير العربية:
رَّبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا ٱلرَّحۡمَٰنِۖ لَا يَمۡلِكُونَ مِنۡهُ خِطَابٗا
“Mbuye wa kumwamba ndi pansi ndi zimene zili pakati pake; Wachifundo chambiri. Palibe amene adzakhala ndi mphamvu yolankhulana naye (pa tsiku limenero);
التفاسير العربية:
يَوۡمَ يَقُومُ ٱلرُّوحُ وَٱلۡمَلَـٰٓئِكَةُ صَفّٗاۖ لَّا يَتَكَلَّمُونَ إِلَّا مَنۡ أَذِنَ لَهُ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَقَالَ صَوَابٗا
“Tsiku limene adzaima Jibril ndi angelo pa mzere (ali odzichepetsa); sadzayankhula aliyense mwa iwo kupatula yekhayo amene adzaloledwa ndi (Allah) Wachifundo chambiri (kuyankhula) ndipo adzanena zolondola.
التفاسير العربية:
ذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمُ ٱلۡحَقُّۖ فَمَن شَآءَ ٱتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ مَـَٔابًا
“Limenelo ndi tsiku loona, (lopanda chikaiko); choncho amene akufuna adzipezere malo (njira yonkera) kwa Mbuye wake. (Pomugonjera Iye pa moyo uno wadziko lapansi).
التفاسير العربية:
إِنَّآ أَنذَرۡنَٰكُمۡ عَذَابٗا قَرِيبٗا يَوۡمَ يَنظُرُ ٱلۡمَرۡءُ مَا قَدَّمَتۡ يَدَاهُ وَيَقُولُ ٱلۡكَافِرُ يَٰلَيۡتَنِي كُنتُ تُرَٰبَۢا
“Ndithu tikukuchenjezani zachilango chomwe chili pafupi kudza; tsiku limene munthu adzayang’ana zimene adatsogoza manja ake, ndipo wosakhulupirira adzanena: Kalanga ine! Ndikadakhala dothi, (kuti ndisalangidwe chilango chikundiyembekezachi).
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: النبإ
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق