ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: الضحى
آية:
 

الضحى

وَٱلضُّحَىٰ
“Ndikulumbilira mmawa dzuwa litakwera (imene ili nthawi yantchito),
التفاسير العربية:
وَٱلَّيۡلِ إِذَا سَجَىٰ
“Ndi usiku pamene ukuvindikira.
التفاسير العربية:
مَا وَدَّعَكَ رَبُّكَ وَمَا قَلَىٰ
“Sadakusiye Mbuye wako (iwe Mneneri) (s.a.w) ndiponso sadakude.
Madzi ambewu ya munthu, pambuyo pokhazikika mchiberekero kwa masiku makumi anayi, amatembenuka ndikukhala magazi. Ili ndilo tanthauzo la Ayah imeneyi.
التفاسير العربية:
وَلَلۡأٓخِرَةُ خَيۡرٞ لَّكَ مِنَ ٱلۡأُولَىٰ
“Ndithu moyo watsiku lirimkudza ndi wabwino kwa iwe kuposa umoyo woyambawu.
التفاسير العربية:
وَلَسَوۡفَ يُعۡطِيكَ رَبُّكَ فَتَرۡضَىٰٓ
“Ndithu posachedwapa akupatsa Mbuye wako (zabwino zamdziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro) ndipo ukondwera.
Ayah 3 ndi 5 Mtumiki (s.a.w) akuyankhidwa pa kunena kwake kwa kuti: “Ine sindidziwa kuwerenga.” Choncho Allah akumuuza kuti Iye ndi Mfulu weniweni, ndi Yemwe adawaphunzitsa anthu kulemba ndi cholembera ndi zonse zomwe sadali kuzidziwa. Kwa ufulu Wake wochuluka ndi mphamvu Zake pa chilichonse, sichovuta kwa Iye (Allah) kumphunzitsa Mtumiki Wake kuwerenga molakatula.
التفاسير العربية:
أَلَمۡ يَجِدۡكَ يَتِيمٗا فَـَٔاوَىٰ
“Kodi sadakupeze uli wa masiye ndipo adakupatsa pokhala pabwino?
التفاسير العربية:
وَوَجَدَكَ ضَآلّٗا فَهَدَىٰ
“Ndipo adakupeza uli wosazindikira (Qur’an) nakuongola (pokuzindikiritsa Qur’aniyo ndi malamulo a chipembedzo)?
Tanthauzo lake nkuti musanyengedwe ndi chumacho chifukwa chakuti, popanda chikaiko, mubwerera kwa Mbuye wanu ndipo chumacho sichidzakuthandizani chilichonse pa maso Pake.
التفاسير العربية:
وَوَجَدَكَ عَآئِلٗا فَأَغۡنَىٰ
“Ndiponso adakupeza uli wosauka nakulemeretsa?
التفاسير العربية:
فَأَمَّا ٱلۡيَتِيمَ فَلَا تَقۡهَرۡ
“Basi, wamasiye usamchitire nkhanza.
التفاسير العربية:
وَأَمَّا ٱلسَّآئِلَ فَلَا تَنۡهَرۡ
“Ndiponso wopempha usamukalipire.
التفاسير العربية:
وَأَمَّا بِنِعۡمَةِ رَبِّكَ فَحَدِّثۡ
“Tsono mtendere wa Mbuye wako uwutchule (pothokoza ndi kugwira ntchito zabwino).
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: الضحى
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق