Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 艾尔拉   段:
وَيَتَجَنَّبُهَا ٱلۡأَشۡقَى
Ndipo wamavuto ambiri, (wamakani ndi wokanira), adzitalikitsa ndi ulalikiwo.[422]
[422] “Wamavuto ambiri” apa, ndiko kuzunzika ndi matsoka. Allah akumutcha kafiri kuti “Wamavuto ambiri” chifukwa chakuti ali ndi mavuto padziko lino lapansi mpaka pa tsiku lachimaliziro. Mazunzo a tsiku lachimaliziro monga momwe tidziwira ndi chilango cha Moto chomwe chikumuyembekeza. Tsono “chilango cha padziko lapansi” ndiko kuti alibe chinthu chomutonthoza likampeza tsoka kapena vuto lililonse. Msilamu likampeza vuto amadzitonthoza ndi chikhulupiliro chake chakuti moyo wa munthu suwonjezeka ndiponso suchepa, ndikuti munthu amamwalira akamaliza moyo wake. Koma kafiri saganiza choncho; amangokukuta zala ndi kuwatukwana ma dokotala kuti sadziwa kanthu akadachita mwakutimwakuti munthuyo sakadafa. Msilamu kukampeza kusauka amadzitonthoza ndi kupilira pamodzi ndi chikhulupiliro choti “chilichonse chimachitika mchifuniro cha Allah.” Ndipo amakhala woyembekezera kuti lero kapena mawa, Allah amupatsa chisomo Chake. Koma anthu opanda chikhulupiliro amangoona kuti aponderezedwa; amayesetsa kufunafuna chuma mnjira zosayenera, ndipo akalephera amadzudzula uyu kapena kumenyana ndi uyu, ndipo amangodziona ngati wonyozeka kwambiri pa maso pa munthu wolemera.
Kotero kuti atauzidwa kuti amulambire wolemera uja kuti amupatse ndalama akhoza kuchita zotero. Ndipo tsiku lililonse njiru imamuondetsa; mwina amangodzipha monga momwe tionera masiku ano. Palibe mazunzo aakulu kuposa amenewa. Ngati muyang’ana ma Ayah 16 ndi 17 muona kuti akuthilira umboni pa zimene talongosolazi.
阿拉伯语经注:
ٱلَّذِي يَصۡلَى ٱلنَّارَ ٱلۡكُبۡرَىٰ
Amene adzalowa ku moto waukulu (umene wakonzedwa kuti udzakhale malipiro ake).
阿拉伯语经注:
ثُمَّ لَا يَمُوتُ فِيهَا وَلَا يَحۡيَىٰ
Ndipo sakafa m’menemo (ndikupumula kumazunzo), ndiponso sakakhala ndi moyo (wamtendere).
阿拉伯语经注:
قَدۡ أَفۡلَحَ مَن تَزَكَّىٰ
Ndithu wapambana amene wadziyeretsa (ku machimo),[423]
[423] Tanthauzo lake ndikuti amene wadziyeretsa posiya kumuphatikiza Allah ndi zolengedwa ndi kumchimwira ndi machimo onse. Machimo amaletsa ulaliki wabwino kulowa mu mtima wa munthu. (yang’anani ndemanga ya 14 mu surat ya Al-Mutaffifin).
阿拉伯语经注:
وَذَكَرَ ٱسۡمَ رَبِّهِۦ فَصَلَّىٰ
Ndikukumbukira dzina la Mbuye wake (ndi mtima wake, ndi lirime lake) uku akumapemphera.
阿拉伯语经注:
بَلۡ تُؤۡثِرُونَ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا
Koma inu mukukonda kwambiri moyo wa dziko lapansi.
阿拉伯语经注:
وَٱلۡأٓخِرَةُ خَيۡرٞ وَأَبۡقَىٰٓ
Pamene moyo wa tsiku lachimaliziro ndiwabwino kwambiri ndiponso wamuyaya.
阿拉伯语经注:
إِنَّ هَٰذَا لَفِي ٱلصُّحُفِ ٱلۡأُولَىٰ
Ndithu izi (mukuuzidwa m’Qur’an) zilipo m’mabuku oyamba, akale,[424]
[424] Mawu akuti “wapambana amene wadziyeretsa ndi kumkumbukira Mbuye wake ndi kumapemphera,” ndiponso kuti: “ tsiku lachimaliziro ndilabwino kuposa dziko lapansi” mawuwa adanenedwanso m’mabuku oyamba; sikuti Qur’an ndiyo yayamba kunena zimenezi.
阿拉伯语经注:
صُحُفِ إِبۡرَٰهِيمَ وَمُوسَىٰ
Mabuku a Ibrahim ndi Mûsa.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 艾尔拉
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭