《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 * - 译解目录


含义的翻译 章: 哈格   段:

哈格

ٱلۡحَآقَّةُ
Chakudza cha choonadi (chomwe ndi Qiyâma).
阿拉伯语经注:
مَا ٱلۡحَآقَّةُ
Kodi chakudza cha choonadi nchiyani?
阿拉伯语经注:
وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلۡحَآقَّةُ
Nanga nchiyani chikudziwitse za chakudza cha choonadicho?
阿拉伯语经注:
كَذَّبَتۡ ثَمُودُ وَعَادُۢ بِٱلۡقَارِعَةِ
Asamudu ndi Âdi adatsutsa zakudza kwa Qiyâma (yomwe idzadzidzimutsa zolengedwa mwamphamvu ndi zoopsa zake).
阿拉伯语经注:
فَأَمَّا ثَمُودُ فَأُهۡلِكُواْ بِٱلطَّاغِيَةِ
Tsono Asamudu adaonongedwa ndi phokoso lopyola muyeso, (lamphamvu kwambiri).
阿拉伯语经注:
وَأَمَّا عَادٞ فَأُهۡلِكُواْ بِرِيحٖ صَرۡصَرٍ عَاتِيَةٖ
Ndipo Âdi adaonongedwa ndi chimphepo cha mkuntho, chozizira, champhamvu kwambiri.
阿拉伯语经注:
سَخَّرَهَا عَلَيۡهِمۡ سَبۡعَ لَيَالٖ وَثَمَٰنِيَةَ أَيَّامٍ حُسُومٗاۖ فَتَرَى ٱلۡقَوۡمَ فِيهَا صَرۡعَىٰ كَأَنَّهُمۡ أَعۡجَازُ نَخۡلٍ خَاوِيَةٖ
Allah adachitumiza kwa iwo pa usiku usanu ndi uwiri ndi masana asanu ndi atatu mosadukiza; kotero ukadawaona ali lambalamba mmenemo ngati mathunthu a mitengo ya kanjedza yopanda kanthu m’kati mwake.
阿拉伯语经注:
فَهَلۡ تَرَىٰ لَهُم مِّنۢ بَاقِيَةٖ
Kodi nanga ukumuona wotsala mwa iwo?
阿拉伯语经注:
وَجَآءَ فِرۡعَوۡنُ وَمَن قَبۡلَهُۥ وَٱلۡمُؤۡتَفِكَٰتُ بِٱلۡخَاطِئَةِ
Ndipo Firiaun ndi amene adalipo iye asadabadwe, ndi khamu la anthu amidzi yotembenuzidwa (anthu a Luti) adadza ndi machimo (akulu).
阿拉伯语经注:
فَعَصَوۡاْ رَسُولَ رَبِّهِمۡ فَأَخَذَهُمۡ أَخۡذَةٗ رَّابِيَةً
Ndipo (yense wa iwowa) adanyoza Mtumiki wa Mbuye wawo; choncho adawalanga chilango chopitilira muyeso.
阿拉伯语经注:
إِنَّا لَمَّا طَغَا ٱلۡمَآءُ حَمَلۡنَٰكُمۡ فِي ٱلۡجَارِيَةِ
Ndithu pamene madzi adasefukira mopyola muyeso (mpaka kumeza mapiri nthawi ya chigumula cha Nowa) Ife tidakukwezani mchombo choyandama ndi kuyenda.
阿拉伯语经注:
لِنَجۡعَلَهَا لَكُمۡ تَذۡكِرَةٗ وَتَعِيَهَآ أُذُنٞ وَٰعِيَةٞ
Kuti tichichite (chochitikacho chomwe okhulupirira adapulumuka nacho; osakhulupirira adaonongeka nacho) kukhala lingaliro ndi phunziro kwa inu, ndikuti lisunge (nkhaniyi) khutu losunga.
阿拉伯语经注:
فَإِذَا نُفِخَ فِي ٱلصُّورِ نَفۡخَةٞ وَٰحِدَةٞ
Choncho likadzaimbidwa lipenga, kuimba kumodzi kokha (zamoyo zonse zidzafa).
阿拉伯语经注:
وَحُمِلَتِ ٱلۡأَرۡضُ وَٱلۡجِبَالُ فَدُكَّتَا دَكَّةٗ وَٰحِدَةٗ
Ndipo nthaka ndi mapiri nkuchotsedwa m’malo mwake ndi kuphwanyidwa kamodzi nkamodzi.
阿拉伯语经注:
فَيَوۡمَئِذٖ وَقَعَتِ ٱلۡوَاقِعَةُ
Chomwecho tsiku limenelo, chochitika chidzachitika (imene ili Qiyâma).
阿拉伯语经注:
وَٱنشَقَّتِ ٱلسَّمَآءُ فَهِيَ يَوۡمَئِذٖ وَاهِيَةٞ
Ndipo thambo lidzasweka choncho ilo tsiku limenelo lidzakhala lofooka (pamene lidali lolimba).
阿拉伯语经注:
وَٱلۡمَلَكُ عَلَىٰٓ أَرۡجَآئِهَاۚ وَيَحۡمِلُ عَرۡشَ رَبِّكَ فَوۡقَهُمۡ يَوۡمَئِذٖ ثَمَٰنِيَةٞ
Ndipo angelo adzakhala m’mphepete mwake, ndipo pamwamba pawo tsiku limenero (angelo) asanu ndi atatu adzasenza Arsh (Mpando wachifumu) ya Mbuye wako.
阿拉伯语经注:
يَوۡمَئِذٖ تُعۡرَضُونَ لَا تَخۡفَىٰ مِنكُمۡ خَافِيَةٞ
Tsiku limenelo mudzabweretsedwa ku chiweruzo; sichidzabisika chilichonse chobisika mwa inu.
阿拉伯语经注:
فَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِيَمِينِهِۦ فَيَقُولُ هَآؤُمُ ٱقۡرَءُواْ كِتَٰبِيَهۡ
Tsono amene adzapatsidwa kaundula wake chakudzanja lakumanja kwake adzanena (mokondwa kwa amene ali m’phepete mwake): “Tengani! Werengani kaundula wanga!”
阿拉伯语经注:
إِنِّي ظَنَنتُ أَنِّي مُلَٰقٍ حِسَابِيَهۡ
“Ndithudi ine ndidatsimikiza (pa dziko lapansi) kuti ndidzakumana ndi chiwerengero changa.”
阿拉伯语经注:
فَهُوَ فِي عِيشَةٖ رَّاضِيَةٖ
Choncho, iye adzakhala m’moyo wosangalatsa.
阿拉伯语经注:
فِي جَنَّةٍ عَالِيَةٖ
M’munda wapamwamba.
阿拉伯语经注:
قُطُوفُهَا دَانِيَةٞ
Zipatso zake zoyandikira pansi (zosavuta kuzithyola).
阿拉伯语经注:
كُلُواْ وَٱشۡرَبُواْ هَنِيٓـَٔۢا بِمَآ أَسۡلَفۡتُمۡ فِي ٱلۡأَيَّامِ ٱلۡخَالِيَةِ
(Adzawauza kuti:) “Idyani, ndipo imwani mosangalala pa zimene mudatsogoza mmasiku aja adapita (a pa dziko lapansi).”
阿拉伯语经注:
وَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِشِمَالِهِۦ فَيَقُولُ يَٰلَيۡتَنِي لَمۡ أُوتَ كِتَٰبِيَهۡ
Ndipo amene adzapatsidwe kaundula wake kudzanja lake lamanzere, adzanena (modandaula): “Kalanga ine! Ndiponi ndikadapanda kupatsidwa kaundula wangayu!”
阿拉伯语经注:
وَلَمۡ أَدۡرِ مَا حِسَابِيَهۡ
“Nkusadziwa chiwerengero changa!”
阿拉伯语经注:
يَٰلَيۡتَهَا كَانَتِ ٱلۡقَاضِيَةَ
“Ha! imfa ija ikadandimaliziratu (ndi kundilekanitsa ine ndi zimenezi).”
阿拉伯语经注:
مَآ أَغۡنَىٰ عَنِّي مَالِيَهۡۜ
“Chuma changa sichidandithandize!”
阿拉伯语经注:
هَلَكَ عَنِّي سُلۡطَٰنِيَهۡ
“Mphamvu zanga (ndi moyo wanga wathanzi) zandichokera!”
阿拉伯语经注:
خُذُوهُ فَغُلُّوهُ
(Kudzanenedwa kwa angelo oyang’anira Jahena): Mgwireni ndipo mnjateni (pomphatikiza manja ndi khosi)!
阿拉伯语经注:
ثُمَّ ٱلۡجَحِيمَ صَلُّوهُ
Kenako mponyeni ku Moto.
阿拉伯语经注:
ثُمَّ فِي سِلۡسِلَةٖ ذَرۡعُهَا سَبۡعُونَ ذِرَاعٗا فَٱسۡلُكُوهُ
Kenakonso mulowetseni mtcheni lotalika mikwamba makumi asanu ndi awiri!
阿拉伯语经注:
إِنَّهُۥ كَانَ لَا يُؤۡمِنُ بِٱللَّهِ ٱلۡعَظِيمِ
Ndithudi, iye sadali kukhulupirira mwa Allah wamkulu.
阿拉伯语经注:
وَلَا يَحُضُّ عَلَىٰ طَعَامِ ٱلۡمِسۡكِينِ
Sadalinso kulimbikitsa zodyetsa osauka.
阿拉伯语经注:
فَلَيۡسَ لَهُ ٱلۡيَوۡمَ هَٰهُنَا حَمِيمٞ
Basi, lero kuno alibe bwenzi (lomthandiza).
阿拉伯语经注:
وَلَا طَعَامٌ إِلَّا مِنۡ غِسۡلِينٖ
Ngakhale chakudya kupatula mafinya (a anthu a ku Moto).
阿拉伯语经注:
لَّا يَأۡكُلُهُۥٓ إِلَّا ٱلۡخَٰطِـُٔونَ
Zomwe palibe angazidye kupatula ochimwa (mwadala).
阿拉伯语经注:
فَلَآ أُقۡسِمُ بِمَا تُبۡصِرُونَ
Choncho ndikulumbilira zimene mukuziona.
阿拉伯语经注:
وَمَا لَا تُبۡصِرُونَ
Ndi zimene simukuziona.
阿拉伯语经注:
إِنَّهُۥ لَقَوۡلُ رَسُولٖ كَرِيمٖ
Ndithudi iyi (Qur’an) ndiliwu la mthenga wolemekezeka (Jibril).
阿拉伯语经注:
وَمَا هُوَ بِقَوۡلِ شَاعِرٖۚ قَلِيلٗا مَّا تُؤۡمِنُونَ
Ndipo simawu a mlakatuli, ndi zochepa zimene mukuzikhulupirira.
阿拉伯语经注:
وَلَا بِقَوۡلِ كَاهِنٖۚ قَلِيلٗا مَّا تَذَكَّرُونَ
Ndiponso simawu a mlosi, ndizochepa zimene mmakumbukira!
阿拉伯语经注:
تَنزِيلٞ مِّن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
(Ichi ndi) chivumbulutso chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa.
阿拉伯语经注:
وَلَوۡ تَقَوَّلَ عَلَيۡنَا بَعۡضَ ٱلۡأَقَاوِيلِ
Ndipo (Mneneri) akadatipekera bodza linalake.
阿拉伯语经注:
لَأَخَذۡنَا مِنۡهُ بِٱلۡيَمِينِ
Tikadamgwira (mwamphamvu) ndimkono wamanja.
阿拉伯语经注:
ثُمَّ لَقَطَعۡنَا مِنۡهُ ٱلۡوَتِينَ
Ndipo tikadadula mwa iye mtsempha wa moyo (kotero kuti ndikuferatu nthawi yomweyo).
阿拉伯语经注:
فَمَا مِنكُم مِّنۡ أَحَدٍ عَنۡهُ حَٰجِزِينَ
Sipakadapezeka aliyense mwa inu womteteza (kuchilango Chathu).
阿拉伯语经注:
وَإِنَّهُۥ لَتَذۡكِرَةٞ لِّلۡمُتَّقِينَ
Ndithu iyi (Qur’an) ndi phunziro labwino kwa owopa (Allah.)
阿拉伯语经注:
وَإِنَّا لَنَعۡلَمُ أَنَّ مِنكُم مُّكَذِّبِينَ
Ndithu Ife, tikudziwa kuti ena mwa inu ndiotsutsa (Qur’an).
阿拉伯语经注:
وَإِنَّهُۥ لَحَسۡرَةٌ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ
Ndipo ndithu iyi (Qur’an) idzakhala chowadandaulitsa (chachikulu) osakhulupirira (pamene adzaona chilango chawo ndi mtendere wa okhulupirira).
阿拉伯语经注:
وَإِنَّهُۥ لَحَقُّ ٱلۡيَقِينِ
Ndithu iyoyi ndichoonadi Chotsimikizika; (mulibe chikaiko),
阿拉伯语经注:
فَسَبِّحۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلۡعَظِيمِ
Basi, lemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu (pitiriza kutamanda dzina Lake).
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 哈格
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 译解目录

古兰经契瓦文译解,哈利德·伊布拉欣·比德拉翻译,2020年版

关闭