Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 伊斯拉仪   段:
وَبِٱلۡحَقِّ أَنزَلۡنَٰهُ وَبِٱلۡحَقِّ نَزَلَۗ وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا مُبَشِّرٗا وَنَذِيرٗا
Ndipo chifukwa chobweretsa choonadi pa dziko tidaitumiza (Qur’an); ndipo mwachoonadi, yavumbulutsidwa. Ndipo sitidakutume (ndi china) koma kuti ukhale wouza (okhulupirira) nkhani zabwino, ndi wochenjeza (osakhulupirira).
阿拉伯语经注:
وَقُرۡءَانٗا فَرَقۡنَٰهُ لِتَقۡرَأَهُۥ عَلَى ٱلنَّاسِ عَلَىٰ مُكۡثٖ وَنَزَّلۡنَٰهُ تَنزِيلٗا
Ndipo Qur’an iyi taigawa (m’zigawo zosiyanasiyana poivumbulutsa pang’onopang’ono) kuti uwawerengere anthu mwa chifatse ndipo taivumbulutsa pang’onopang’ono.
阿拉伯语经注:
قُلۡ ءَامِنُواْ بِهِۦٓ أَوۡ لَا تُؤۡمِنُوٓاْۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ مِن قَبۡلِهِۦٓ إِذَا يُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ يَخِرُّونَۤ لِلۡأَذۡقَانِۤ سُجَّدٗاۤ
Nena (kwa osakhulupirira a m’Makka mowachenjeza): “Ikhulupirireni (iyi Qur’an) kapena musaikhulupirire, (zonse zili m’chifuniro chanu.) Ndithu amene adapatsidwa nzeru kale (yozindikira za m’mabuku a Allah Qur’an isanadze) ikamalakatulidwa kwa iwo (Qur’aniyi) amagwa ndi zibwano zawo molambira.
阿拉伯语经注:
وَيَقُولُونَ سُبۡحَٰنَ رَبِّنَآ إِن كَانَ وَعۡدُ رَبِّنَا لَمَفۡعُولٗا
Ndipo amanena: “Mbuye wathu Ngoyera! Ndithu lonjezo la Mbuye wathu ndi lokwaniritsidwa!”
阿拉伯语经注:
وَيَخِرُّونَ لِلۡأَذۡقَانِ يَبۡكُونَ وَيَزِيدُهُمۡ خُشُوعٗا۩
Ndipo amagwa ndi zibwano zawo uku akulira, ndipo (Qur’an) imawaonjezera kudzichepetsa.
阿拉伯语经注:
قُلِ ٱدۡعُواْ ٱللَّهَ أَوِ ٱدۡعُواْ ٱلرَّحۡمَٰنَۖ أَيّٗا مَّا تَدۡعُواْ فَلَهُ ٱلۡأَسۡمَآءُ ٱلۡحُسۡنَىٰۚ وَلَا تَجۡهَرۡ بِصَلَاتِكَ وَلَا تُخَافِتۡ بِهَا وَٱبۡتَغِ بَيۡنَ ذَٰلِكَ سَبِيلٗا
Nena (kwa Amushirikina): “Mpempheni Allah, m’dzina la Allah kapena mpempheni m’dzina la Rahman; (dzina) lililonse, limene mungamtchulire (zithandizabe); Iye ali nawo maina abwino. Ndipo usawerenge (Qur’an) pa Swala yako ndi mawu okweza, ndiponso usatsitse mawu kwambiri, koma tsata njira yolingana pakati pa zimenezo (pokweza kwambiri kapena kutsitsa zedi).”
阿拉伯语经注:
وَقُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي لَمۡ يَتَّخِذۡ وَلَدٗا وَلَمۡ يَكُن لَّهُۥ شَرِيكٞ فِي ٱلۡمُلۡكِ وَلَمۡ يَكُن لَّهُۥ وَلِيّٞ مِّنَ ٱلذُّلِّۖ وَكَبِّرۡهُ تَكۡبِيرَۢا
Ndipo nena: “Kutamandidwa kwabwino nkwa Allah, yemwe saadadzipangire mwana, ndipo alibe m’phatikizi mu ufumu (Wake); ndipo alibe mthandizi (womthandiza) mkufooka; ndipo mkuzeni, kumkuza kwakukulu!”
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 伊斯拉仪
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭