Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 伊斯拉仪   段:
وَإِن كَادُواْ لَيَسۡتَفِزُّونَكَ مِنَ ٱلۡأَرۡضِ لِيُخۡرِجُوكَ مِنۡهَاۖ وَإِذٗا لَّا يَلۡبَثُونَ خِلَٰفَكَ إِلَّا قَلِيلٗا
Ndipo padatsala pang’ono kuti akusowetse mtendere m’dziko ili (la Makka) kuti akutulutse m’menemo; koma pambuyo pako sakadakhala (ndi moyo) kupatula (nthawi) yochepa.
阿拉伯语经注:
سُنَّةَ مَن قَدۡ أَرۡسَلۡنَا قَبۡلَكَ مِن رُّسُلِنَاۖ وَلَا تَجِدُ لِسُنَّتِنَا تَحۡوِيلًا
Chimenechi ndi chikhalidwe cha omwe tidawatuma patsogolo pako mwa atumiki Athu, ndipo supeza kusintha pachikhalidwe Chathu.
阿拉伯语经注:
أَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ لِدُلُوكِ ٱلشَّمۡسِ إِلَىٰ غَسَقِ ٱلَّيۡلِ وَقُرۡءَانَ ٱلۡفَجۡرِۖ إِنَّ قُرۡءَانَ ٱلۡفَجۡرِ كَانَ مَشۡهُودٗا
Pemphera Swala (za Farazi), dzuwa likapendeka mpaka mu mdima wausiku (zomwe ndi Swala za Dhuhri, Asri, Maghrib ndi Isha), ndipo pempheranso Swala ya Fajir: ndithu Swala ya Fajir amaichitira umboni (angelo).
阿拉伯语经注:
وَمِنَ ٱلَّيۡلِ فَتَهَجَّدۡ بِهِۦ نَافِلَةٗ لَّكَ عَسَىٰٓ أَن يَبۡعَثَكَ رَبُّكَ مَقَامٗا مَّحۡمُودٗا
Ndipo pakati pa usiku, dzuka mtulo ndi kupemphera Swala; ilo ndipemphero loonjezera pa iwe, kuti Mbuye wako akakuimike pamalo pa ulemu potamandidwa (ndi zolengedwa zonse pa tsiku la Qiyâma.)
阿拉伯语经注:
وَقُل رَّبِّ أَدۡخِلۡنِي مُدۡخَلَ صِدۡقٖ وَأَخۡرِجۡنِي مُخۡرَجَ صِدۡقٖ وَٱجۡعَل لِّي مِن لَّدُنكَ سُلۡطَٰنٗا نَّصِيرٗا
Ndipo nena (mawu awa pomwe ukupemphera): “Mbuye wanga! Ndilowetseni, kulowetsa kwabwino (paliponse pamene ndikulowa), ndiponso nditulutseni, kutulutsa kwabwino (paliponse pamene ndikutuluka); ndipatseni mphamvu zochokera kwa Inu zondithandiza ndi kugonjetsera adani.”
阿拉伯语经注:
وَقُلۡ جَآءَ ٱلۡحَقُّ وَزَهَقَ ٱلۡبَٰطِلُۚ إِنَّ ٱلۡبَٰطِلَ كَانَ زَهُوقٗا
Ndipo nena: “Choonadi chafika, ndipo chachabe chachoka; ndithu chachabe ndichochoka (ngakhale patapita nthawi yaitali).”
阿拉伯语经注:
وَنُنَزِّلُ مِنَ ٱلۡقُرۡءَانِ مَا هُوَ شِفَآءٞ وَرَحۡمَةٞ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ وَلَا يَزِيدُ ٱلظَّٰلِمِينَ إِلَّا خَسَارٗا
Ndipo tikuivumbulutsa Qur’an yomwe imachiritsa (matenda a mmitima) ndiponso ndi chifundo kwa okhulupirira. Komabe osalungama siikuwaonjezera (kanthu kena) koma kutayika.
阿拉伯语经注:
وَإِذَآ أَنۡعَمۡنَا عَلَى ٱلۡإِنسَٰنِ أَعۡرَضَ وَنَـَٔا بِجَانِبِهِۦ وَإِذَا مَسَّهُ ٱلشَّرُّ كَانَ يَـُٔوسٗا
Ndipo tikampatsa chisomo munthu, (monga moyo wangwiro ndikupeza bwino), amatembenuka (ndikusiya kutikumbukira ndikutipempha), ndipo amadziika kutali (ndi Ife chifukwa chakudzitama ndikudzikuza), koma masautso akamkhudza, (monga matenda ndi umphawi) amataya mtima kwambiri.
阿拉伯语经注:
قُلۡ كُلّٞ يَعۡمَلُ عَلَىٰ شَاكِلَتِهِۦ فَرَبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِمَنۡ هُوَ أَهۡدَىٰ سَبِيلٗا
Nena (iwe Mneneri, kwa osakhulupirira a Chikuraishi,): “Aliyense (wa ife ndi inu) akuchita ntchito (zake ndikuyenda panjira yake) ndipo Mbuye wanu Ngodziwa kwambiri za yemwe ali panjira yolondola (potsatira choonadi).”
阿拉伯语经注:
وَيَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلرُّوحِۖ قُلِ ٱلرُّوحُ مِنۡ أَمۡرِ رَبِّي وَمَآ أُوتِيتُم مِّنَ ٱلۡعِلۡمِ إِلَّا قَلِيلٗا
Ndipo akukufunsa (iwe, Muhammad (s.a.w), anthu ako mokhwiriziridwa ndi Ayuda) za Mzimu. Nena: “Mzimu ndi chinthu chomwe akuchidziwa Mbuye wanga Yekha; ndipo inu simudapatsidwe nzeru (zozindikilira zinthu) koma pang’ono chabe, (poyerekeza ndi nzeru za Allah).”
阿拉伯语经注:
وَلَئِن شِئۡنَا لَنَذۡهَبَنَّ بِٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ ثُمَّ لَا تَجِدُ لَكَ بِهِۦ عَلَيۡنَا وَكِيلًا
Ndipo tikadafuna kufufuta Qur’an (pachifuwa chako) yomwe takuvumbulutsira, (tikadatha kutero). Kenako sukadapeza kwa Ife wokuimilira ndi kukupulumutsa.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 伊斯拉仪
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭