Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 伊斯拉仪   段:
مَّن كَانَ يُرِيدُ ٱلۡعَاجِلَةَ عَجَّلۡنَا لَهُۥ فِيهَا مَا نَشَآءُ لِمَن نُّرِيدُ ثُمَّ جَعَلۡنَا لَهُۥ جَهَنَّمَ يَصۡلَىٰهَا مَذۡمُومٗا مَّدۡحُورٗا
Amene afuna zachangu (zosangalatsa za m’dziko ndikumaikirapo mtima pa izo), timpatsiratu mwachangu pa dziko lapansi chimene tikufuna kwa amene tafuna (kumpatsa;) koma (tsiku la chimaliziro) tamkonzera Jahannam adzailowa ali wonyozeka, wopirikitsidwa apa ndi apo.
阿拉伯语经注:
وَمَنۡ أَرَادَ ٱلۡأٓخِرَةَ وَسَعَىٰ لَهَا سَعۡيَهَا وَهُوَ مُؤۡمِنٞ فَأُوْلَٰٓئِكَ كَانَ سَعۡيُهُم مَّشۡكُورٗا
Ndipo amene afuna tsiku la chimaliziro (mzochita zake) ndikuligwilira ntchito yake yeniyeni uku ali okhulupirira, iwowo khama lawo lidzakhala lolandiridwa.
阿拉伯语经注:
كُلّٗا نُّمِدُّ هَٰٓؤُلَآءِ وَهَٰٓؤُلَآءِ مِنۡ عَطَآءِ رَبِّكَۚ وَمَا كَانَ عَطَآءُ رَبِّكَ مَحۡظُورًا
Onse awa, (abwino ndi oipa), timawapatsa awa ndi awa mwazopatsa za Mbuye wako; ndipo zopatsa za Mbuye wako sizotsekerezedwa (kuti zisamfike kapolo Wake).
阿拉伯语经注:
ٱنظُرۡ كَيۡفَ فَضَّلۡنَا بَعۡضَهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖۚ وَلَلۡأٓخِرَةُ أَكۡبَرُ دَرَجَٰتٖ وَأَكۡبَرُ تَفۡضِيلٗا
Taona (ndi diso lolingalira) m’mene tawasiyanitsira mkupeza bwino, ena nkukhala pamwamba pa anzawo (pa chuma ndi pa moyo wangwiro); ndipo pa tsiku la chimaliziro kusiyana kwawo pa masitepe ndi ulemelero, nkwakukulu kwabasi.
阿拉伯语经注:
لَّا تَجۡعَلۡ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ فَتَقۡعُدَ مَذۡمُومٗا مَّخۡذُولٗا
Usadzipangire mulungu wina ndi kumphatika kwa Allah; kuti ungadzakhale wodzudzulidwa (kwa Allah) ndikusiidwa wopanda m’thandizi.
阿拉伯语经注:
۞ وَقَضَىٰ رَبُّكَ أَلَّا تَعۡبُدُوٓاْ إِلَّآ إِيَّاهُ وَبِٱلۡوَٰلِدَيۡنِ إِحۡسَٰنًاۚ إِمَّا يَبۡلُغَنَّ عِندَكَ ٱلۡكِبَرَ أَحَدُهُمَآ أَوۡ كِلَاهُمَا فَلَا تَقُل لَّهُمَآ أُفّٖ وَلَا تَنۡهَرۡهُمَا وَقُل لَّهُمَا قَوۡلٗا كَرِيمٗا
Ndipo walamula Mbuye wako kuti musapembedze (wina) koma Iye Yekha, ndi kuti muchitire zabwino makolo (anu). Ngati m’modzi wa iwo afika msinkhu waukalamba uli naye, kapena onse awiri, usawanenere mawu amnyozo, ndiponso usawakalipire koma yankhula nawo ndi mau aulemu.[254]
[254] M’ndimeyi Allah akulamula anthu Ake kuti apembedze Iye Yekha; asapembedze china chake cholengedwa monga miyala, mitengo, dzuwa, mwezi, nkhalango zowilira, mizimu ya anthu akufa ndi ziwanda. Koma chikhulupiliro chathu chikhale mwa Allah yekha. Tikafuna kudziteteza tidziteteze ndi Allah. Ndiponso Allah watilamula kuchitira zabwino makolo. Tisawanenere mawu amwano ndiponso tisawakalipire. Koma tiwanenere mau aulemu.
阿拉伯语经注:
وَٱخۡفِضۡ لَهُمَا جَنَاحَ ٱلذُّلِّ مِنَ ٱلرَّحۡمَةِ وَقُل رَّبِّ ٱرۡحَمۡهُمَا كَمَا رَبَّيَانِي صَغِيرٗا
Ndipo afungatire ndi phiko lodzichepetsa powachitira chisoni, ndipo nena: “Mbuye wanga achitireni chisoni (makolo anga) monga momwe ankandilelera ku ubwana.”
阿拉伯语经注:
رَّبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِمَا فِي نُفُوسِكُمۡۚ إِن تَكُونُواْ صَٰلِحِينَ فَإِنَّهُۥ كَانَ لِلۡأَوَّٰبِينَ غَفُورٗا
Mbuye wanu akudziwa kwambiri zomwe zili m’maganizo mwanu; ngati muli ofuna kuchita zabwino, (kwa makolo anu Iye akudziwa. Ndipo ngati mutawalakwira, kenako ndikulapa), ndithu Iye ndi Mwini kukhululukira otembenukira kwa Iye.
阿拉伯语经注:
وَءَاتِ ذَا ٱلۡقُرۡبَىٰ حَقَّهُۥ وَٱلۡمِسۡكِينَ وَٱبۡنَ ٱلسَّبِيلِ وَلَا تُبَذِّرۡ تَبۡذِيرًا
Ndipo mnansi wako, masikini ndi wapaulendo (yemwe alibe choyendera) mpatse gawo lake (la chuma chako) ndipo usamwaze (chuma chako) mosakaza.
阿拉伯语经注:
إِنَّ ٱلۡمُبَذِّرِينَ كَانُوٓاْ إِخۡوَٰنَ ٱلشَّيَٰطِينِۖ وَكَانَ ٱلشَّيۡطَٰنُ لِرَبِّهِۦ كَفُورٗا
Ndithu omwaza chuma mosakaza ndiabale a satana (otsatira satana), ndipo satana ngosathokoza kwa Mbuye wake.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 伊斯拉仪
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭