Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 伊斯拉仪   段:
وَإِذَا مَسَّكُمُ ٱلضُّرُّ فِي ٱلۡبَحۡرِ ضَلَّ مَن تَدۡعُونَ إِلَّآ إِيَّاهُۖ فَلَمَّا نَجَّىٰكُمۡ إِلَى ٱلۡبَرِّ أَعۡرَضۡتُمۡۚ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ كَفُورًا
Ndipo akakupezani masautso pa nyanja, amasowa amene mumakhala mukuwapembedza kupatula Iye (Allah). Koma akakupulumutsirani kumtunda, mukutembenuka ndi kunyoza Allah. Ndithu munthu ndi wokana (mtendere wa Allah sayamika.)
阿拉伯语经注:
أَفَأَمِنتُمۡ أَن يَخۡسِفَ بِكُمۡ جَانِبَ ٱلۡبَرِّ أَوۡ يُرۡسِلَ عَلَيۡكُمۡ حَاصِبٗا ثُمَّ لَا تَجِدُواْ لَكُمۡ وَكِيلًا
Kodi mukudziika pa chitetezo ndi chilango cha Allah (mukafika pa ntunda) kuti Allah sangakulowetseni pansi mbali iliyonse ya pa ntunda, kapena sangakutumizireni chigumula chamchenga (kapena miyala) kenako inu simudzapeza mtetezi (wokupulumutsani ku chilangocho)?
阿拉伯语经注:
أَمۡ أَمِنتُمۡ أَن يُعِيدَكُمۡ فِيهِ تَارَةً أُخۡرَىٰ فَيُرۡسِلَ عَلَيۡكُمۡ قَاصِفٗا مِّنَ ٱلرِّيحِ فَيُغۡرِقَكُم بِمَا كَفَرۡتُمۡ ثُمَّ لَا تَجِدُواْ لَكُمۡ عَلَيۡنَا بِهِۦ تَبِيعٗا
Kapena mwadziika pachitetezo kuti (Allah) sadzakubwezeraninso m’nyanjamo kachiwiri ndipo nkudzakutumizirani chimphepo chaukali ndikukumizani chifukwa cha kusakhulupirira (ndi kusathokoza kwanu,) kenako inu nkusapeza wokutetezani kwa Ife?
阿拉伯语经注:
۞ وَلَقَدۡ كَرَّمۡنَا بَنِيٓ ءَادَمَ وَحَمَلۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِ وَرَزَقۡنَٰهُم مِّنَ ٱلطَّيِّبَٰتِ وَفَضَّلۡنَٰهُمۡ عَلَىٰ كَثِيرٖ مِّمَّنۡ خَلَقۡنَا تَفۡضِيلٗا
Ndipo ndithu tawalemekeza ana a Adam; ndipo tawapatsa zokwera pa ntunda ndi pa nyanja; tawapatsa zopatsa zabwino kwambiri; ndipo tawapatsa ulemelero kuposa zambiri m’zomwe tidalenga; ulemelero waukulu kwabasi.
阿拉伯语经注:
يَوۡمَ نَدۡعُواْ كُلَّ أُنَاسِۭ بِإِمَٰمِهِمۡۖ فَمَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِيَمِينِهِۦ فَأُوْلَٰٓئِكَ يَقۡرَءُونَ كِتَٰبَهُمۡ وَلَا يُظۡلَمُونَ فَتِيلٗا
(Akumbutse za) tsiku lomwe tidzaitana anthu onse m’dzina la mneneri wawo; choncho, amene adzapatsidwe akaundula awo ndi dzanja lamanja iwo adzawerenga akaundula awowo (mwachisangalalo), ndipo sadzaponderezedwa ngakhale pa (kachinthu kakang’ono monga) kaulusi ka mkati mwa njere ya kanjeza.
阿拉伯语经注:
وَمَن كَانَ فِي هَٰذِهِۦٓ أَعۡمَىٰ فَهُوَ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ أَعۡمَىٰ وَأَضَلُّ سَبِيلٗا
Ndipo amene ali wakhungu pano (pa dziko lapansi posapenya zizindikiro) adzakhalanso wakhungu pa tsiku la chimaliziro, ndipo adzakhala wosokera kwambiri njira (kumeneko).
阿拉伯语经注:
وَإِن كَادُواْ لَيَفۡتِنُونَكَ عَنِ ٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ لِتَفۡتَرِيَ عَلَيۡنَا غَيۡرَهُۥۖ وَإِذٗا لَّٱتَّخَذُوكَ خَلِيلٗا
Ndipo ndithu adatsala pang’ono kukusokoneza pa zimene tavumbulutsa kwa iwe kuti utipekere zina zake m’malo mwa izi; pamenepo, akadakusankha kukhala bwenzi (lawo).
阿拉伯语经注:
وَلَوۡلَآ أَن ثَبَّتۡنَٰكَ لَقَدۡ كِدتَّ تَرۡكَنُ إِلَيۡهِمۡ شَيۡـٔٗا قَلِيلًا
Ndipo tikadapanda kukulimbikitsa, ukadapendekera kwa iwo, kupendekera kwa pang’ono.
阿拉伯语经注:
إِذٗا لَّأَذَقۡنَٰكَ ضِعۡفَ ٱلۡحَيَوٰةِ وَضِعۡفَ ٱلۡمَمَاتِ ثُمَّ لَا تَجِدُ لَكَ عَلَيۡنَا نَصِيرٗا
Tero ndithu tikadakulawitsa chilango chachikulu cha moyo (wa pa dziko lapansi) ndi chilango chachikulu utafa; kenako siukadapeza mthandizi wokupulumutsa kwa Ife.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 伊斯拉仪
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭