Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 伊斯拉仪   段:
ذَٰلِكَ مِمَّآ أَوۡحَىٰٓ إِلَيۡكَ رَبُّكَ مِنَ ٱلۡحِكۡمَةِۗ وَلَا تَجۡعَلۡ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ فَتُلۡقَىٰ فِي جَهَنَّمَ مَلُومٗا مَّدۡحُورًا
Izi ndi zina mwa za nzeru zomwe Mbuye wako wakuvumbulutsira. Usakhale ndi mulungu wina ndi kumphatikiza kwa Allah, kuti ungadzaponyedwe ku Jahannam uli wodzudzulidwa ndi wopirikitsidwa apa ndi apo.
阿拉伯语经注:
أَفَأَصۡفَىٰكُمۡ رَبُّكُم بِٱلۡبَنِينَ وَٱتَّخَذَ مِنَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِنَٰثًاۚ إِنَّكُمۡ لَتَقُولُونَ قَوۡلًا عَظِيمٗا
Kodi Mbuye wanu wakusankhirani ana aamuna, ndipo mwini wadzipangira ana aakazi achingelo? Ndithu inu mukunena liwu lalikulu.
阿拉伯语经注:
وَلَقَدۡ صَرَّفۡنَا فِي هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ لِيَذَّكَّرُواْ وَمَا يَزِيدُهُمۡ إِلَّا نُفُورٗا
Ndipo ndithu talongosola lamulo la chinthu chilichonse mwatsatanetsatane m’Qur’an iyi kuti akumbukire, ndipo (oipa) siikuwaonjezera (china) koma kuida ndi kuithawa.
阿拉伯语经注:
قُل لَّوۡ كَانَ مَعَهُۥٓ ءَالِهَةٞ كَمَا يَقُولُونَ إِذٗا لَّٱبۡتَغَوۡاْ إِلَىٰ ذِي ٱلۡعَرۡشِ سَبِيلٗا
Nena: “Pakadakhala milungu ina pamodzi ndi Allah, monga momwe akunenera, ikadafuna njira yomufikira (Mbuye) Mwini Arsh (Mpando wa chifumu, ndi kumthira nkhondo).”
阿拉伯语经注:
سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يَقُولُونَ عُلُوّٗا كَبِيرٗا
Wayera ndipo watukuka Allah ku zimene akunenazo; kutukuka kwakukulu (kwabasi).
阿拉伯语经注:
تُسَبِّحُ لَهُ ٱلسَّمَٰوَٰتُ ٱلسَّبۡعُ وَٱلۡأَرۡضُ وَمَن فِيهِنَّۚ وَإِن مِّن شَيۡءٍ إِلَّا يُسَبِّحُ بِحَمۡدِهِۦ وَلَٰكِن لَّا تَفۡقَهُونَ تَسۡبِيحَهُمۡۚ إِنَّهُۥ كَانَ حَلِيمًا غَفُورٗا
Zonse zakumitambo isanu ndi iwiri ndi nthaka ndi zam’menemo, zikulemekeza Iye; ndipo palibe chilichonse koma chikumlememekeza ndi kumtamanda; koma inu simuzindikira kulemekeza kwawo! Ndithudi Iye (Allah) Ngodekha, Ngokhululuka.
阿拉伯语经注:
وَإِذَا قَرَأۡتَ ٱلۡقُرۡءَانَ جَعَلۡنَا بَيۡنَكَ وَبَيۡنَ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ حِجَابٗا مَّسۡتُورٗا
Ndipo ukamawerenga Qur’an (zikukhala ngati) taika chotchinga chosaonekera pakati pako ndi pakati pa amene sadakhulupirire za tsiku la chimaliziro.
阿拉伯语经注:
وَجَعَلۡنَا عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ أَكِنَّةً أَن يَفۡقَهُوهُ وَفِيٓ ءَاذَانِهِمۡ وَقۡرٗاۚ وَإِذَا ذَكَرۡتَ رَبَّكَ فِي ٱلۡقُرۡءَانِ وَحۡدَهُۥ وَلَّوۡاْ عَلَىٰٓ أَدۡبَٰرِهِمۡ نُفُورٗا
Ndipo (ngati) taika zitsekelero m’mitima mwawo kuti angaizindikire, ndipo (ngati) mmakutu mwawo muli kulemera kwa ugonthi. Ndiponso ukamtchula m’Qur’an Mbuye wako Yekha, iwo akutembenuka ndi misana yawo moipidwa.
阿拉伯语经注:
نَّحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَا يَسۡتَمِعُونَ بِهِۦٓ إِذۡ يَسۡتَمِعُونَ إِلَيۡكَ وَإِذۡ هُمۡ نَجۡوَىٰٓ إِذۡ يَقُولُ ٱلظَّٰلِمُونَ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا رَجُلٗا مَّسۡحُورًا
Ife tikudziwa chifukwa chomwe akuimvetsera (Qur’an), pamene akukumvetsera ndi pamene akunong’onezana awo achinyengo, pamene akunena awo oyipa (kuuza Asilamu kuti): “Inu simutsatira (wina) koma munthu wolodzedwa.”
阿拉伯语经注:
ٱنظُرۡ كَيۡفَ ضَرَبُواْ لَكَ ٱلۡأَمۡثَالَ فَضَلُّواْ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ سَبِيلٗا
Ona momwe akukufanizira ndi mafanizo abodza. (Nthawi zina akuti ndiwe wolodzedwa, nthawi zina akuti ndiwe mfiti!) Choncho asokera, ndipo sangathe kupeza njira (yeniyeni).
阿拉伯语经注:
وَقَالُوٓاْ أَءِذَا كُنَّا عِظَٰمٗا وَرُفَٰتًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ خَلۡقٗا جَدِيدٗا
Ndipo akunena: “Kodi tikadzakhala mafupa odukaduka, tidzaukitsidwanso kukhala zolengedwa zatsopano?”
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 伊斯拉仪
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭