Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 伊斯拉仪   段:
وَمَن يَهۡدِ ٱللَّهُ فَهُوَ ٱلۡمُهۡتَدِۖ وَمَن يُضۡلِلۡ فَلَن تَجِدَ لَهُمۡ أَوۡلِيَآءَ مِن دُونِهِۦۖ وَنَحۡشُرُهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ عَلَىٰ وُجُوهِهِمۡ عُمۡيٗا وَبُكۡمٗا وَصُمّٗاۖ مَّأۡوَىٰهُمۡ جَهَنَّمُۖ كُلَّمَا خَبَتۡ زِدۡنَٰهُمۡ سَعِيرٗا
Ndipo yemwe Allah wamuongola, (chifukwa cha kukonzeka kwake kwa ubwino), iyeyo ndi amene waongoka; ndipo amene wamulekelera kusokera, (chifukwa cha kuipa kwa khalidwe lake), simungampezere athandizi kupatula Iye (Allah). Ndipo pa tsiku la chiweruziro tidzawasonkhanitsa uku akukokedwa ndi nkhope zawo ali osapenya, osalankhula ndi osamva. Malo awo okhala ndi ku Jahannam. Nthawi iliyonse (Motowo) ukatotobwa, tidzauonjezera kwa iwo kuyaka mwaukali.
阿拉伯语经注:
ذَٰلِكَ جَزَآؤُهُم بِأَنَّهُمۡ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَقَالُوٓاْ أَءِذَا كُنَّا عِظَٰمٗا وَرُفَٰتًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ خَلۡقٗا جَدِيدًا
(Chilango) chimenecho ndiyo mphoto yawo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo zisonyezo (zomwe tidasonyeza kwa iwo), ndi kunena kwawo koti: “Kodi tikadzakhala mafupa ndi zidutswa zonyenyekanyenyeka, tidzaukitsidwanso kukhala zolengedwa zatsopano?”
阿拉伯语经注:
۞ أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّ ٱللَّهَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ قَادِرٌ عَلَىٰٓ أَن يَخۡلُقَ مِثۡلَهُمۡ وَجَعَلَ لَهُمۡ أَجَلٗا لَّا رَيۡبَ فِيهِ فَأَبَى ٱلظَّٰلِمُونَ إِلَّا كُفُورٗا
Kodi (onyalanyaza) sadadziwebe kuti Allah Yemwe adalenga thambo ndi nthaka Ngokhoza kulenga ena onga iwo? Ndipo wawaikira nthawi (yodziwika) yopanda chikaiko, (yowaukitsira ku imfa). Koma achinyengo akukana (zonsezi) koma kusakhulupirira basi.
阿拉伯语经注:
قُل لَّوۡ أَنتُمۡ تَمۡلِكُونَ خَزَآئِنَ رَحۡمَةِ رَبِّيٓ إِذٗا لَّأَمۡسَكۡتُمۡ خَشۡيَةَ ٱلۡإِنفَاقِۚ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ قَتُورٗا
Nena (kwa opembedza mafano): “Mukadakhala kuti muli nazo nkhokwe za chifundo cha Mbuye wanga, mukadachita umbombo (posagawira ena) kuopa umphawi. Ndipo munthu ali ndi khalidwe loumira.”
阿拉伯语经注:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَىٰ تِسۡعَ ءَايَٰتِۭ بَيِّنَٰتٖۖ فَسۡـَٔلۡ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ إِذۡ جَآءَهُمۡ فَقَالَ لَهُۥ فِرۡعَوۡنُ إِنِّي لَأَظُنُّكَ يَٰمُوسَىٰ مَسۡحُورٗا
Ndipo ndithu tidampatsa Mûsa zizizwa zoonekera zisanu ndi zinayi (komabe osakhulupirira sadazikhulupirire). Afunse ana a Israyeli pamene adawadzera (Musayo), Farawo adati kwa iye (Mûsa): “Ndithu ine ndikukuona iwe Mûsa kuti walodzedwa.”
阿拉伯语经注:
قَالَ لَقَدۡ عَلِمۡتَ مَآ أَنزَلَ هَٰٓؤُلَآءِ إِلَّا رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ بَصَآئِرَ وَإِنِّي لَأَظُنُّكَ يَٰفِرۡعَوۡنُ مَثۡبُورٗا
(Mûsa) adati: “Ndithu wadziwa kuti palibe amene watumiza (mitsutso) iyi kupatula Mbuye wathambo ndi nthaka kuti zikhale chiphanula maso. Koma ine ndikukuona iwe Farawo kuti waonongeka.”
阿拉伯语经注:
فَأَرَادَ أَن يَسۡتَفِزَّهُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ فَأَغۡرَقۡنَٰهُ وَمَن مَّعَهُۥ جَمِيعٗا
Choncho (Farawo) adafuna kuwatulutsa m’dziko (la Iguputo Mûsa ndi ana a Israyeli) koma tidammiza iye ndi onse omwe adali naye.
阿拉伯语经注:
وَقُلۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِۦ لِبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱسۡكُنُواْ ٱلۡأَرۡضَ فَإِذَا جَآءَ وَعۡدُ ٱلۡأٓخِرَةِ جِئۡنَا بِكُمۡ لَفِيفٗا
(Mûsa ndi anthu ake tidawapulumutsa). Ndipo tidati, kwa ana a Israyeli, pambuyo pake (pommiza Farawo): “Khalani m’dziko (loyera la Shami); ndipo likazadza lonjezo la moyo winawo, tidzakubweretsani nonsenu (muli m’chipwirikiti.)”
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 伊斯拉仪
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭