Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 伊斯拉仪   段:
وَإِمَّا تُعۡرِضَنَّ عَنۡهُمُ ٱبۡتِغَآءَ رَحۡمَةٖ مِّن رَّبِّكَ تَرۡجُوهَا فَقُل لَّهُمۡ قَوۡلٗا مَّيۡسُورٗا
Ndipo ngati ukuwapewa opempha (pamene ulibe chowapatsa) pamene ukufunafuna chifundo cha Mbuye wako chomwe ukuchiyembekezera, nena kwa iwo mau ofewa (ponena kuti: “Ndikapeza chokupatsani, ndikuninkhani.”)
阿拉伯语经注:
وَلَا تَجۡعَلۡ يَدَكَ مَغۡلُولَةً إِلَىٰ عُنُقِكَ وَلَا تَبۡسُطۡهَا كُلَّ ٱلۡبَسۡطِ فَتَقۡعُدَ مَلُومٗا مَّحۡسُورًا
Ndipo mkono wako usaukhalitse ngati kuti wamangidwa kukhosi kwako, ndiponso usautambasule mosayenera, ungadzakhale wodzudzulidwa ndiwosowa.[255]
[255] Tanthauzo la ndime iyi nkuti mkono wako usakhale wofumbata posiya kugawira ena zomwe ulinazo; ndikutinso usatambasule popatsa mosakaza koma kuchita zapakatikati; osachita umbombo ndiponso osasakaza. Anthu aumbombo ndi osakaza chuma, ndi abale a satana.
阿拉伯语经注:
إِنَّ رَبَّكَ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ وَيَقۡدِرُۚ إِنَّهُۥ كَانَ بِعِبَادِهِۦ خَبِيرَۢا بَصِيرٗا
Ndithu Mbuye wako amamtambasulira rizq amene wamfuna, ndikulichepetsa (kwa amene wamfuna). Ndithu Iye Ngodziwa bwino; wopenya bwino za akapolo Ake.
阿拉伯语经注:
وَلَا تَقۡتُلُوٓاْ أَوۡلَٰدَكُمۡ خَشۡيَةَ إِمۡلَٰقٖۖ نَّحۡنُ نَرۡزُقُهُمۡ وَإِيَّاكُمۡۚ إِنَّ قَتۡلَهُمۡ كَانَ خِطۡـٔٗا كَبِيرٗا
Ndipo musaphe ana anu poopa umphawi. Ife ndi amene tikuwapatsa iwo ndi inu. Ndithu kupha anawo ndi tchimo lalikulu.
阿拉伯语经注:
وَلَا تَقۡرَبُواْ ٱلزِّنَىٰٓۖ إِنَّهُۥ كَانَ فَٰحِشَةٗ وَسَآءَ سَبِيلٗا
Ndipo musachiyandikire chiwerewere; ndithu (icho) ndi uve (chonyansa chachikulu), ndiponso ndi njira yoipa.
阿拉伯语经注:
وَلَا تَقۡتُلُواْ ٱلنَّفۡسَ ٱلَّتِي حَرَّمَ ٱللَّهُ إِلَّا بِٱلۡحَقِّۗ وَمَن قُتِلَ مَظۡلُومٗا فَقَدۡ جَعَلۡنَا لِوَلِيِّهِۦ سُلۡطَٰنٗا فَلَا يُسۡرِف فِّي ٱلۡقَتۡلِۖ إِنَّهُۥ كَانَ مَنصُورٗا
Ndipo musaphe munthu amene Allah waletsa (kumupha) koma mwachoonadi (poweruza oweruza zakuphedwa ngati utam’gwera mulandu woyenera kuphedwa). Ndipo amene waphedwa mopanda chilungamo, tapereka mphamvu kwa mlowammalo wake (wa wophedwayo atafuna angamuphenso kapena kumsiya ndikulandirapo dipo); koma asapyole malire mukuphako. Ndithu iye ngothandizidwa ndi Shariya.
阿拉伯语经注:
وَلَا تَقۡرَبُواْ مَالَ ٱلۡيَتِيمِ إِلَّا بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ حَتَّىٰ يَبۡلُغَ أَشُدَّهُۥۚ وَأَوۡفُواْ بِٱلۡعَهۡدِۖ إِنَّ ٱلۡعَهۡدَ كَانَ مَسۡـُٔولٗا
Ndipo musachiyandikire chuma cha wamasiye (pochidya mosayenera) koma pokhapokha m’njira yomwe ili yabwino, kufikira atakula, (apo tsono apatsidwe chumacho); ndipo kwaniritsani lonjezo, popeza lonjezo lidzafunsidwa (tsiku la Qiyâma).
阿拉伯语经注:
وَأَوۡفُواْ ٱلۡكَيۡلَ إِذَا كِلۡتُمۡ وَزِنُواْ بِٱلۡقِسۡطَاسِ ٱلۡمُسۡتَقِيمِۚ ذَٰلِكَ خَيۡرٞ وَأَحۡسَنُ تَأۡوِيلٗا
Ndipo kwaniritsani mlingo pamene mulinga, ndipo yesani ndi sikelo zabwino, zimenezo ndi zabwino (kwa inu) ndiponso mathero (ake) ngabwino.
阿拉伯语经注:
وَلَا تَقۡفُ مَا لَيۡسَ لَكَ بِهِۦ عِلۡمٌۚ إِنَّ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡبَصَرَ وَٱلۡفُؤَادَ كُلُّ أُوْلَٰٓئِكَ كَانَ عَنۡهُ مَسۡـُٔولٗا
Ndipo usazitsate (pongoziyankhulayankhula kapena kuzichita) zomwe sukuzidziwa; ndithu makutu, maso ndi mtima zonsezo zidzafunsidwa.
阿拉伯语经注:
وَلَا تَمۡشِ فِي ٱلۡأَرۡضِ مَرَحًاۖ إِنَّكَ لَن تَخۡرِقَ ٱلۡأَرۡضَ وَلَن تَبۡلُغَ ٱلۡجِبَالَ طُولٗا
Ndipo usayende padziko modzitukumula; ndithu iwe sungang’ambe nthaka ndiponso sungalifikire phiri m’kutalika.
阿拉伯语经注:
كُلُّ ذَٰلِكَ كَانَ سَيِّئُهُۥ عِندَ رَبِّكَ مَكۡرُوهٗا
Zonsezi kuipa kwake nkonyansidwa kwa Mbuye wako.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 伊斯拉仪
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭